Zaka Mazana Ambiri za Malekano
LIWU lakuti “schism” (kulekana) (kaŵirikaŵiri loŵerengedwa sizimu, skizimu, kapena shizimu) lalongosoledwa kukhala “kachitidwe m’kamene bungwe lachipembedzo limagawikana kukhala mabungwe aŵiri kapena oposapo odziŵika, odziimira pawokha.”
330 C.E. “Kulekana pakati pa Chikristu Chadziko cha Chigiriki ndi Chilatini. . . . Kukhazikitsidwa kwa Constantinople, ‘Roma watsopano’ (330), akumalowa mmalo ‘Roma wakale’ monga likulu lenileni, kunafesa mbewu za kutetana kwamtsogolo kwatchalitchi pakati pa Kummawa Kwachigiriki ndi Kumadzulo Kwachilatini.”—The Encyclopedia of Religion.
330-867 C.E. “Kuchokera pakuyambika kwa Likulu la pa Constantinople kufikira ku kulekana kwakukulu kwa mu 867 ndandanda ya kupandukira malamulo achipembedzo kosakhalitsaku njowopsa. . . . M’zaka 544 zimenezi (323-867) zaka zosachepera 203 zinatha Constantinople iri mumkhalidwe wolekana [ndi Roma pankhani za kukangana kwa maphunziro aumulungu okhudza Utatu ndi kulambira mafano].”—The Catholic Encyclopedia.
867 C.E. “Likulu la pa Constantinople linasunga kaimidwe kake kotsutsana ndi Roma m’nthaŵi yotchedwa Kulekana kwa Photius. Pamene Papa Nicholas I anatokosa kukwezedwa ku malo apamwamba kwa Photius, . . . mkulu wa ku Byzantium anakana kugonjera. . . . Nicholas . . . anachotsa Photius mumpingo; msonkhano wa pa Constantinople pambuyo pake unayankha chochitikachi (867) mwakuchotsa Nicholas mumpingo. Nkhani zapanthaŵiyo pakati pa malikulu aŵiriwo zinali zokhudza nkhani za ukulu wa chipembedzo, malamulo, ndi kulanga akuluakulu.”—The New Encyclopædia Britannica.
1054 C.E. “KULEKANA KWAKUMMAWA NDI KUMADZULO, chochitika chimene chinazindikiritsa kugawana komalizira kwa pakati pa matchalitchi Achikristu Akummawa [Amwambo] . . . ndi Tchalitchi cha Kumadzulo [Roma Katolika].”—The New Encyclopædia Britannica.
1378-1417 C.E. “KULEKANA [KWAKUKULU] KWA KUMADZULO—Iyi ndi nyengo . . . imene Chikristu Chadziko Chakumadzulo chinagawidwa kukhala ziŵiri, ndipo pambuyo pake kukhala zitatu, chimvero cha papa [ndi apapa opikisana nawo chikumakhala mu Roma, Avignon (Falansa), ndi Pisa (Italiya)].”—New Catholic Encyclopedia.
Zaka za zana la 16 C.E. “Ponena za Kukonzanso kwa Chiprotestanti, . . . Tchalitchi cha Katolika chinagwiritsira ntchito kwakukulukulu liwu lakuti kupatuka mmalo mwa lakuti kulekana.”—Théo—Nouvelle encyclopédie catholique.
1870 C.E. “Msonkhano Woyamba wa Vatican, umene unachilikiza ‘kusalakwa’ kwa papa, unabweretsa kulekana kwa ‘Akatolika Akalekale.’”—La Croix (Nyuzipepala ya ku Paris, Yachikatolika).
1988: Kulekana kwa Akibishopu Lefebvre, amene “anayambitsa kulekana m’Tchalitchi cha Katolika mwa kunyalanyaza kwake Papa ndi lingaliro la Msonkhano wachiŵiri kwa Vatican . . . amene amalingalira Aprotestanti kukhala opatuka, amene amalingalira kusanganizana zipembedzo kukhala ntchito ya mdyerekezi, ndi amene ali wofunitsitsa kumwalira ali wochotsedwa mumpingo mmalo mwa kugwirizanitsidwa ku Tchalitchi ‘chamakono.’”—Catholic Herald.