Makanda, Mwazi, ndi AIDS
POSACHEDWAPA The New York Times inali ndi lipoti lowopsya iri patsamba lake lakutsogolo: “Ana a ku Romania akuwopsyezedwa ndi mliri wa AIDS, yofalikira kwambiri m’nyumba zodzala zosungira ana amasiye ndi zipatala, oyambukitsidwa ndi kachitidwe kamakedzana ka kuthira mwazi ana obadwa kumene.”—February 8, 1990.
Mwachiwonekere adokotala ena a ku Romania mwachizoloŵezi ankathira mwazi wochepera panchombo wa ana obadwa kumene akumayembekezera kuti “kuthira mwazi wocheperawu” kukafulumiza mwanayo kukula. Kachitidweko kanatsimikizira kukhala njira yokhutiritsa kwabasi ya kuyambukitsa AIDS; painti imodzi ya mwazi woipitsidwa imakhala ndi mlingo wokwanira wa makanda ambiri.
World Health Organization, imene inatumiza gulu la adokotala a m’nthaŵi yangozi ku Romania, ikuyerekeza kuti ana 700 a ku Romania apezedwa kale ali ndi kachilombo ka AIDS, ndipo 50 owonjezera pa awa ngodwaliratu AIDS. Mkulu wa gululo wa programu ya AIDS anauza Times kuti chiŵerengero cha oyambukiridwa ndi AIDS pakati pa ana ameneŵa chiri pakati pa ziŵerengero zazikulu zadziko.
Pansi pa ulamuliro wolandidwa mphamvu posachedwapa wa Ceausescu, Romania siinali ndi chiwopsyezo cha AIDS chodziŵika mwalamulo. Nyuzi iriyonse ya kufalikira kwamatendawa inabisidwa kotheratu monga chinsinsi chaboma. Opereka mwazi sankapimidwa AIDS. Tsopano izi zasintha. Koma m’chaka chimodzi ndi theka kusinthaku kusanachitike, adokotala ambiri a ku Romania sanalingalirepo konse za AIDS pamene anayamba kuwona ana ambirimbiri oyambukiridwa ndi matenda omwe sankachiritsika. Monga mmene mmodzi wa iwo ananenera kuti: “Ngati munthu auzidwa kuti mu Romania mulibe kachirombo kotereka, nkukaphunziriranji?”