Msonkhano wa Pachaka
OCTOBER 2, 1993
MSONKHANO WA PACHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzakhalako pa October 2, 1993, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Msonkhano woyambirira wa ziŵalo zokha udzayamba ndi 9:30 a.m., kenako padzatsatira msonkhano wa pachaka wa onse pa 10:00 a.m.
Ziŵalo za Bungwelo ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano za kusintha kulikonse kwa keyala kumene kunachitika mkati mwa chaka chatha kotero kuti makalata anthaŵi zonse achidziŵitso ndi zikalata zotumizira chisankho zikhoza kuwafika msanga pambuyo pa August 1.
Zikalata zotumizira chisankho, zimene zidzatumizidwa kwa ziŵalozo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka umenewo, ziyenera kubwezeredwa msanga kotero kuti zifike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite mosachedwera pa August 15. Aliyense amene ali chiŵalo ayenera kudzaza ndi kubwezera chikalata chotumizira chisankho mwamsanga, akunena ngati adzakhalapo pamsonkhano kapena ayi. Zimene alemba pa chikalata chotumizira chisankho ziyenera kumveketsa mfundoyi motsimikizirika, popeza kuti ndizo zidzadaliridwa kudziŵa amene adzapezekapo.
Tikuyembekezera kuti programu yonseyo, kuphatikizapo msonkhano wopenda kagwiridwe ka ntchito ndi malipoti, udzatha pafupifupi ndi 1:00 p.m, kapena kupitirirapo pang’ono. Sipadzakhala gawo la masana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi tikiti okha ndiwo adzaloledwa kuloŵa. Sipadzakhala makonzedwe aliwonse akulunzanitsa msonkhano wa pachaka ndi telefoni ku malo ena osonkhanira.