Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/1 tsamba 3-5
  • Kuthetsa Chinsinsi cha Dzina Lalikulu Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthetsa Chinsinsi cha Dzina Lalikulu Koposa
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunafuna Dzina Lalikulu Koposa
  • Kodi Dzinalo Linakhala Chinsinsi Motani?
  • Dzina Lalikulu Koposa ndi Mtsogolo Mwathu
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kudziwa Dzina la Mulungu
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2004
  • Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2017
  • Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/1 tsamba 3-5

Kuthetsa Chinsinsi cha Dzina Lalikulu Koposa

Nkokondweretsa kuti Koran ya Chisilamu ndi Baibulo la Chikristu lomwe limasonyeza dzina lalikulu koposa. Nkhaniyi ikufotokoza tanthauzo ndi kufunika kwa dzina lalikulu koposalo. Ikusonyezanso mmene dzina limenelo limayambukirira anthu onse ndi mtsogolo mwathu padziko lapansi pano.

MAMILIYONI a amuna ndi akazi padziko lapansi pano akhalako ndi kufa. M’zochitika zambiri maina awo azimiririka limodzi nawo, ndipo aiwalidwa ndi anthu. Koma maina a anthu ena otchuka​—monga ngati Avicenna, Edison, Pasteur, Beethoven, Gandhi, ndi Newton​—amakumbukiridwabe. Maina ameneŵa amagwirizanitsidwa ndi zipambano, kutulukira zinthu, ndi kuyambitsa kupangidwa kwa zinthu ndi anthu amene anali ndi mainaŵa.

Komabe, pali dzina lalikulu koposa maina onse. Zozizwitsa zonse zakale ndi zamakono zimene zili m’chilengedwe chonse nzogwirizanitsidwa nalo. Eya, chiyembekezo cha mtundu wa anthu cha moyo wautali ndi wachimwemwe nchogwirizanitsidwa ndi dzinali!

Anthu ambiri afuna kudziŵa za dzinali. Iwo alifunafuna ndi kufunsa ena za ilo, koma sanalipeze. Kwa iwo lakhala chinsinsi. Kwenikweni, palibe munthu amene angatulukire dzinali ngati Mwiniwake sanamuululire. Mwachimwemwe, chinsinsi cha dzina lobisikali chathetsedwa. Mulungu mwiniyo wachita zimenezi kotero kuti awo amene amamkhulupirira akadziŵe za iye. Iye anavumbula dzina lake kwa Adamu, ndiyeno kwa Abrahamu, kwa Mose, ndi kwa atumiki Ake ena okhulupirika akale.

Kufunafuna Dzina Lalikulu Koposa

Buku la Koran limasimba za munthu wina “amene anali wodziŵa kwambiri Malemba.” (27:40) Pofotokoza vesili, buku la ndemanga lodziŵika kuti Tafsīr Jalālayn limati: “Asaf mwana wa Barkhiyā anali munthu wolungama. Iye anadziŵa dzina lalikulu koposa la Mulungu, ndipo pamene anaitanira pa ilo, anayankhidwa.” Zimenezi zikutikumbutsa za wolemba Baibulo Asafu, amene ananena pa Salmo 83:18 kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.”

Pa Koran 17:2, timaŵerenga kuti: “Tinapatsa Mose Malemba ndi kuwapanga kukhala chitsogozo cha Aisrayeli.” M’Malemba amenewo, Mose akunena ndi Mulungu, akumati: “Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? ndikanena nawo chiyani?” Mulungu anayankha Mose mwakunena kuti: “Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha.”​—Eksodo 3:13, 15.

M’nthaŵi zakale, Aisrayeli anadziŵa dzina lalikulu limeneli la Mulungu. Linagwiritsiridwadi ntchito monga mbali ya maina a iwo eni. Monga momwe tsopano lino munthu angaonere dzina lakuti Abdullah, limene limatanthauza “Mtumiki wa Mulungu,” anthu a Israyeli wakale anali ndi dzina lakuti Obadiya, kutanthauza “Mtumiki wa Yehova.” Amake a mneneri Mose anatchedwa Yokobedi, limene mwina limatanthauza “Yehova Ndiye Ulemerero.” Dzina lakuti Yohane limatanthauza “Yehova Wakhala Wokoma Mtima.” Ndipo dzina la mneneri Eliya limatanthauza “Mulungu Wanga Ndiye Yehova.”

Aneneri anadziŵa dzina lalikulu limeneli ndipo analigwiritsira ntchito ndi ulemu waukulu. Likupezeka nthaŵi zoposa 7,000 m’Malemba Opatulika. Yesu Kristu, mwana wa Mariya, analisonyeza pamene ananena m’pemphero lake kwa Mulungu kuti: “Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine . . . ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo.” (Yohane 17:6, 26) M’ndemanga yake yotchuka ponena za Koran, Bayḍāwī akuthirira ndemanga pa Koran 2:87, akumati Yesu anali “kuukitsa anthu akufa ndi dzina lalikulu koposa la Mulungu.”

Nangano, nchiyani chimene chinachitika kuchititsa dzinalo kukhala chinsinsi? Kodi dzinalo lili nchiyani ndi mtsogolo mwa aliyense wa ife?

Kodi Dzinalo Linakhala Chinsinsi Motani?

Ena amaganiza kuti dzina lakuti “Yehova” m’Chihebri limatanthauza “Allah” (Mulungu). Komatu dzina lakuti “Allah” nlofanana ndi ʼElo·himʹ Wachihebri, mpangidwe wa mawu ochulukitsa a ulemu a liwu lakuti ʼelohʹah (mulungu). Pakati pa Ayuda panabuka mwambo umene unawaletsa kutchula dzina la Mulungu, Yehova. Chifukwa chake, pamene anali kuŵerenga Malemba Opatulika ndi kuona dzina lakuti Yehova, chinali chizoloŵezi chawo kunena kuti ʼAdho·naiʹ, kutanthauza kuti “Ambuye.” M’malo ena, anasinthadi dzina lakuti “Yehova” m’malembo oyambirira Achihebri ndi kuikamo ʼAdho·naiʹ.

Atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anatsatira njira yofananayo. Iwo analoŵetsa mmalo dzina lakuti Yehova ndi “Mulungu” (“Allah” m’Chiluya) ndi “Ambuye.” Zimenezi zinachilikiza kukula kwa chiphunzitso chonyenga cha Utatu, chimene chilibe maziko m’Malemba Opatulika. Chifukwa cha zimenezi, mamiliyoni ambiri molakwa amalambira Yesu ndi mzimu woyera ndipo amalingalira zimenezi kukhala zolingana ndi Mulungu.a

Chifukwa chake, atsogoleri a Chiyuda ndi a Dziko Lachikristu ali ndi mlandu wa kufalikira kwa umbuli wa kusadziŵa dzina lalikulu koposalo. Koma Mulungu analosera kuti: “Ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, . . . ndipo amitundu adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” Inde, Yehova adzadziŵikitsa dzina lake pakati pa mitundu yonse. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti sali Mulungu wa Ayuda okha kapena wa mtundu wina uliwonse kapena anthu. Yehova ali Mulungu wa mtundu wonse wa anthu.​—Ezekieli 36:23; Genesis 22:18; Salmo 145:21; Malaki 1:11.

Dzina Lalikulu Koposa ndi Mtsogolo Mwathu

Malemba Opatulika amati: “Aliyense adzaitana padzina la [Yehova, NW] adzapulumuka.” (Aroma 10:13) Chipulumutso chathu patsiku lachiweruzo chidzagwirizanitsidwa ndi kudziŵa kwathu dzina la Mulungu. Kudziŵa dzina lake kumaphatikizapo kudziŵa mikhalidwe yake, ntchito, ndi zifuno zake ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo ake a mkhalidwe apamwamba. Mwachitsanzo, Abrahamu anadziŵa dzina la Mulungu naitanira pa ilo. Monga chotulukapo chake, anali ndi unansi wabwino ndi Mulungu, anamkhulupirira, anamdalira, ndi kummvera. Motero Abrahamu anafikira kukhala bwenzi la Mulungu. Mofananamo, kudziŵa dzina la Mulungu kumatikokera pafupi naye ndi kutithandiza kukulitsa unansi wathu ndi iye, kumamatira kuchikondi chake.​—Genesis 12:8; Salmo 9:10; Miyambo 18:10; Yakobo 2:23.

M’Baibulo, timaŵerenga kuti: “Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Kodi nchifukwa ninji tiyenera ‘kukumbukira’ dzina lake lalikulu koposalo? Dzina lakuti Yehova kwenikweni limatanthauza “Wochititsa Kukhalako.” Zimenezi zimavumbula Yehova kukhala Uyo amene amadzichititsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo. Nthaŵi zonse iye amakwaniritsa zifuno zake. Iye ndiye Mulungu wamphamvuyonse, Mlengi yekha, amene ali ndi mkhalidwe uliwonse wabwino. Palibe liwu limodzi limene lingafotokoze mokwanira mkhalidwe waumulungu wa Mulungu. Koma Mulungu anadzisankhira dzina lalikulu koposalo​—Yehova​—ndipo limakumbutsa munthu za mikhalidwe yake yonse, ndi zifuno.

M’Malemba Opatulika, Mulungu amatiuza za zifuno zake kwa anthu. Yehova Mulungu analenga munthu kuti asangalale ndi moyo wosatha, wachimwemwe m’Paradaiso. Chifuniro chake kumtundu wa anthu nchakuti anthu onse apange banja limodzi, logwirizana m’chikondi ndi mtendere. Mulungu wachikondiyo adzakwaniritsa chifuno chimenechi mtsogolomu posachedwa.​—Mateyu 24:3-14, 32-42; 1 Yohane 4:14-21.

Mulungu amafotokoza zifukwa za kuvutika kwa mtundu wa anthu ndipo amasonyeza kuti chipulumutso nchothekera. (Chivumbulutso 21:4) Pa Salmo 37:10, 11, timaŵerenga kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Onaninso Koran 21:105.

Inde, Mulungu adzadziŵika ndi dzina lake lalikulu. Mitundu idzadziŵa kuti iye ndiye Yehova. Ndimwaŵi wabwino kwambiri chotani nanga kudziŵa dzina lalikulu koposa limenelo, kulichitira umboni, ndi kulimamatira! Mwanjira imeneyo, chifuno chokondweretsa cha Mulungu chidzakwaniritsidwa kwa aliyense wa ife chakuti: “Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa. Adzandifuulira ine ndipo ndidzamyankha; . . . Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.”​—Salmo 91:14-16.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka umboni wakuti Utatu suli chiphunzitso cha Baibulo, onani brosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? lofalitsidwa mu 1989 ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Chithunzi patsamba 5]

Mose ndi Chitsamba Choyaka Moto, chojambulidwa ndi W. Thomas, Sr.

[Mawu a Chithunzi]

Pachitsamba choyaka moto, Mulungu anadzidziŵikitsa kwa Mose monga ‘Yehova, Mulungu wa Abrahamu’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena