Zitsanzo za Kudzichepetsa Zoyenera Kutsanziridwa
“Kudzichepetsa kwanu kudzandikuza ine.”—SALMO 18:35, NW.
1. Kodi ndiumboni wa kudzichepetsa wotani umene unali woonekera mwa prezidenti wakale wa Watch Tower Society?
JOSEPH F. RUTHERFORD anali mwamuna wochititsa chidwi, pakuti anali wamtali woposa masentimita 180 ndi wolemera makilogalamu oposa 90. Analinso ndi liwu lamphamvu, limene anagwiritsira ntchito osati kokha kubukitsira dzina la Yehova kuposa ndi kalelonse komanso kuvumbulira chinyengo cha zipembedzo za atsogoleri a Dziko Lachikristu, akumatcha chipembedzo chawo kukhala “msampha ndi chinyengo.” Komabe ngakhale kuti nkhani zake zinali zamphamvu kwambiri, pamene anapemphera pamodzi ndi banja la Beteli la kumalikulu, iye anamveka monga kamnyamata kamene kakulankhula kwa atate wake, mwa kutero akumapereka umboni wa unansi wake wathithithi ndi Mpangi wake ndi wa kudzichepetsa kwake. Inde, iye anali wodzichepetsa mongadi kamwana.—Mateyu 18:3, 4.
2. Kodi ndim’mbali iti makamaka imene atumiki a Yehova amasiyana kotheratu ndi anthu a dzikoli?
2 Mosakayikira, atumiki owona onse a Yehova Mulungu ali odzichepetsa. M’nkhaniyi iwo amasiyana kotheratu ndi anthu a dziko. Lerolino, kuposa ndi kalelonse, ladzaza ndi anthu onyada. Anthu apamwamba ndi amphamvu, olemera ndi ophunzira, ndipo ngakhale osauka ambiri limodzi ndi awo opanda mwaŵi m’njira zinazake ali onyada.
3. Kodi nchiyani chinganenedwe ponena za zipatso za kunyada?
3 Kunyada kumangowonjezera mikangano ndi mavuto. Ndithudi, masoka onse m’chilengedwe chonse anayamba chifukwa chakuti mngelo wina anakhala wonyada, akumafuna kulambiridwa mwanjira imene inali yoyenera Mlengi yekha, Yehova Mulungu. (Mateyu 4:9, 10) Ndiponso, iyeyo, amene anadzipanga kukhala Mdyerekezi ndi Satana, anapambana m’kunyenga mkazi woyambayo, Hava, mwakumkopa ndi kunyada. Anamlonjeza kuti mwakudya chipatso choletsedwa, iye akafanana ndi Mulungu mwiniyo, akumadziŵa zabwino ndi zoipa. Mkaziyo akanakhala wodzichepetsa, akanati, ‘Ndifunirenji kufanana ndi Mulungu?’ (Genesis 3:4, 5) Pamene tilingalira za mkhalidwe woipitsidwa umene mtundu wa anthu ulimo, mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwamakhalidwe, timaona kuti kunyada kwa anthu kuli kosalungamitsika mpang’ono pomwe! Nzosadabwitsa kuti timaŵerenga kuti Yehova amada “kunyada, ndi kudzikuza”! (Miyambo 8:13) Mosiyana kotheratu ndi anthu onse onyada, pali zitsanzo za kudzichepetsa zopezedwa m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
Yehova Mulungu Ali Wodzichepetsa
4. Kodi ndimalemba ati amene amasonyeza kuti Yehova ali wodzichepetsa?
4 Yehova Mulungu—Wam’mwambamwambayo, Wolamulira Wachilengedwe Chonse, Mfumu yamuyaya—ali wodzichepetsa. (Genesis 14:22) Kodi zimenezo zingakhale zowona? Indedi! Monga momwe kwalembedwera pa Salmo 18:35, Mfumu Davide anati: “Mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu: ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo kudzichepetsa kwanu kudzandikuza ine.” Mwachionekere, Mfumu Davide anayamikira kudzichepetsa kwa Yehova ndiko kunamchititsa iye, Davide, kukhala wamkulu. Ndiyeno, timaŵerenganso pa Salmo 113:6 kuti Yehova ‘amadzichepetsa kuti apenye zam’mwamba ndi za padziko lapansi.’ Matembenuzidwe ena amanena kuti, “aŵerama pansi kuti apenye,” (New International Version) “adzitsitsa kuti apenye zapansi kwambiri.”—The New English Bible.
5. Kodi nzochitika ziti zimene zimachitira umboni kudzichepetsa kwa Yehova?
5 Yehova Mulungu anadzichepetsadi m’njira imene anachitira ndi Abrahamu, akumalola Abrahamu kufunsa za chilungamo Chake pofuna kuwononga mizinda yoipa ya Sodomu ndi Gomora. (Genesis 18:23-32) Ndipo pamene Yehova anasonyeza chifuno chake cha kufafaniza mtundu wa Israyeli—panthaŵi yoyamba kaamba ka kulambira mafano, panthaŵi ina kaamba ka kupanduka—Mose panthaŵi zonse ziŵirizo anakambitsirana ndi Yehova monga ngati kuti anali kulankhula ndi munthu mnzake. Panthaŵi iliyonse Yehova anayankha moyanja. Iye anasonyeza kudzichepetsa povomereza mapempho a Mose onena za anthu Ake Israyeli. (Eksodo 32:9-14; Numeri 14:11-20) Zitsanzo zina za kudzichepetsa kwa Yehova pochita ndi anthu mwachindunji, kunena kwake titero, zingaonedwe m’maunansi ake ndi Gideoni ndi Yona, monga momwe zalembedwera pa Oweruza 6:36-40 ndi Yona 4:9-11.
6. Kodi ndimkhalidwe wa Yehova uti umene umasonyezanso kudzichepetsa kwake?
6 Kwenikweni, pafupifupi nthaŵi zisanu ndi zinayi, Yehova akunenedwa kukhala ‘wolekereza kapena wosakwiya msanga.’a Kuleza mtima kwa Yehova ndi kusakwiya msanga kwake pochita ndi zolengedwa zake zaumunthu zopanda ungwiro kwa zaka zikwi zambiri kuli umboni wowonjezereka wa kudzichepetsa kwake. Anthu onyada ali opupuluma, amafulumira kusonyeza mkwiyo, osaleza mtima konse. Ha, kudzichepetsa kwa Yehova kumanyazitsa anthu onyada chotani nanga! Popeza kuti timauzidwa ‘kukhala akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa,’ tiyenera kukhala odzichepetsa monga momwe iye aliridi wodzichepetsa.—Aefeso 5:1.
Chitsanzo cha Kristu cha Kudzichepetsa
7, 8. Kodi Malemba amanenanji za kudzichepetsa kwa Yesu Kristu?
7 Chitsanzo chachiŵiri chogwira mtima koposa cha kudzichepetsa chomwe tiyenera kutsanzira chikutchulidwa pa 1 Petro 2:21 kuti: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” Kalelo asanabwere padziko lapansi monga munthu, kunaloseredwa ponena za iye pa Zekariya 9:9 kuti: “Fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; [wodzichepetsa, NW] ndi wokwera pa bulu.” Yesu Kristu akadakhala wonyada, akadalandira chopereka cha Mdyerekezi cha maufumu onse a m’dziko mwa kusinthana ndi mchitidwe umodzi wokha wa kulambira. (Mateyu 4:9, 10) Iye anasonyezanso kudzichepetsa kwake mwa kupereka kwa Yehova chitamando chonse cha kuphunzitsa kwake, akumati: “Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.”—Yohane 8:28.
8 Moyenerera, iye anakhoza kunena kwa omvetsera ake kuti: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Mateyu 11:29) Ndipo nchitsanzo chabwino chotani nanga cha kudzichepetsa chimene anachipereka mwakusambitsa mapazi a atumwi ake madzulo omalizira amene anali nawo monga munthu! (Yohane 13:3-15) Moyenerera kwambiri, pa Afilipi 2:3-8, mtumwi Paulo akupatsa uphungu Akristu kuti akhale ‘odzichepetsa mtima,’ akumatchula chitsanzo cha Yesu Kristu kuti: “Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].” Pamene anayang’anizana ndi vuto lalikulu koposa m’moyo wake, iye anapemphera modzichepetsa kwa Atate wake kuti: “Simonga ndifuna ine, koma inu.” (Mateyu 26:39) Mosakayikira konse, kuti ife tikhale otsanzira a Yesu Kristu, tikumalondola mosamalitsa mapazi ake, tiyenera kukhala odzichepetsa.
Mtumwi Paulo, Chitsanzo Chabwino cha Kudzichepetsa
9-12. Kodi ndim’njira zotani zimene mtumwi Paulo anaperekera chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa?
9 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Kodi mtumwi Paulo anatsanziradi Yesu Kristu mwa kukhala wodzichepetsa mtima, mwa kutero akumatipatsa chitsanzo china cha kudzichepetsa choti tichitsanzire? Motsimikizirika, iye anaterodi. Choyamba, iye anavomereza modzichepetsa kuti anali kapolo wa Yesu Kristu. (Afilipi 1:1) Anauza akulu a ku Efeso ponena za ‘kutumikira kwake monga kapolo kwa Ambuye ndi kudzichepetsa mtima kwakukulu ndi misozi ndi mayesero amene adamgwera mwa ziwembu za Ayuda.’ (Machitidwe 20:17-19) Akadakhala wosadzichepetsa, sakadalemba konse mawu opezeka pa Aroma 7:18, 19 akuti: “Ndidziŵa kuti mkati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino . . . Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.”
10 China chosonyezanso kudzichepetsa kwa Paulo ndicho chimene analemba kwa Akristu a ku Korinto, cholembedwa pa 1 Akorinto 2:3 kuti: “Ndinakhala nanu mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.” Akumanena modzichepetsa za njira yake yakale asanakhale Mkristu, analemba kuti: “Kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; . . . Kristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa.”—1 Timoteo 1:13, 15.
11 Chosonyezanso kudzichepetsa kwake ndicho kutamanda kwake Yehova Mulungu kaamba ka chipambano chake chonse m’zoyesayesa zake. Iye analemba ponena za utumiki wake kuti: “Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wowokayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.” (1 Akorinto 3:6, 7) Iye anapemphanso abale ake kumpempherera kuti akhoze kupereka umboni wabwino, monga momwe timaŵerengera pa Aefeso 6:18-20 kuti: “Mupemphere[re] . . . ndi ine ndemwe, kuti andipatse mawu m’kunditsegulira mkamwa molimbika . . . kuti mmenemo ndikalankhule [za chinsinsi chopatulika cha mbiri yabwino] molimbika, monga ndiyenera kulankhula.”
12 Paulo anasonyezanso kudzichepetsa kwake m’njira imene analiri wogwirizana ndi atumwi ena: “Yakobo ndi Kefa ndi Yohane . . . anapatsa ine ndi Barnaba dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa [a]mdulidwe.” (Agalatiya 2:9) Iye anasonyezanso kufunitsitsa kwake kwa kugwirizana ndi akulu a mpingo wa ku Yerusalemu mwakupitira limodzi ndi amuna anayi kukachisi ndi kuwalipirira pamene anakwaniritsa chowinda.—Machitidwe 21:23-26.
13. Kodi nchiyani chinachititsa kudzichepetsa kwa Paulo kukhala kwapadera kwambiri?
13 Kudzichepetsa kwa Paulo kulinso kwapadera kwambiri pamene tiona mmene Yehova Mulungu anamgwiritsirira ntchito mwamphamvu. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti “Mulungu anachita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo.” (Machitidwe 19:11, 12) Ndiponso, iye anapatsidwa masomphenya ndi zivumbulutso zauzimu. (2 Akorinto 12:1-7) Sitiyeneranso kunyalanyaza kuuziridwa kwake kulemba mabuku 14 a mabuku 27 (amene alidi makalata) a Malemba Achigiriki Achikristu. Zonsezo sizinamchititse kukhala wonyada. Iye anakhalabe wodzichepetsa.
Zitsanzo Zamakono
14-16. (a) Kodi ndimotani mmene prezidenti woyamba wa Watch Tower Society analiri chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa? (b) Kodi chitsanzo chake chikusiyana kutalitali ndi chayani?
14 Pa Ahebri 13:7, timaŵerenga uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” Mogwirizana ndi lamulo la mkhalidwe limeneli, tikhoza kutenga prezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society, Charles Taze Russell monga chitsanzo chamakono, amene tingatsanzire chikhulupiriro chake. Kodi iye analidi munthu wodzichepetsa? Ndithudi, iye anali wotero! Monga momwe kwaonedwera bwino lomwe, m’buku lake lakuti Studies in the Scriptures, lokhala ndi mavoliyumu asanu ndi limodzi, onse pamodzi okhala ndi masamba pafupifupi 3,000, palibe ngakhale mpamodzi pomwe pamene anadzitchula iye mwini. Zofalitsidwa za Watch Tower Bible and Tract Society lerolino zimatsatira lamulo la mkhalidwe limeneli mwa kusadziŵikitsa anthu olemba nkhanizo.
15 Mu Watch Tower, Russell panthaŵi ina analemba kuti iye sanadziŵe chinthu chilichonse chotchedwa “Chiraselo” ndi “Araselo,” maina amene anthu omutsutsa anagwiritsira ntchito koma amene iyemwini anawakana kwamtu wagalu. Iye analemba kuti: “Ntchito yathu . . . yakhala yosonkhanitsa pamodzi zidutswa zomwazikana za chowonadi ndi kuzipereka kwa anthu a Ambuye—osati monga zatsopano, osati monga zathuzathu, koma monga za Ambuye. . . . Ntchito imene Ambuye wakhala wokondwa kugwiritsira ntchito luso lathu lochepa siinakhale kwenikweni ntchito ya kuyambitsa koma ntchito ya kumanganso, kuwongolera, kugwirizanitsa.” Ndithudi, iye analankhula malingaliro a mtumwi Paulo, opezeka pa 1 Akorinto 3:5-7.
16 Mkhalidwe wake wamaganizo unali wosiyana kotheratu ndi wa Charles Darwin. M’kope lake loyamba la The Origin of Species mu 1859, Darwin anabwerezabwereza mawu akuti lingaliro “langa,” akumanyalanyaza zimene ena amene anakhalako kale ananena ponena za chisinthiko. Wolemba nkhani wotchuka wa m’zaka za zana limenelo, Samuel Butler, anasuliza Darwin mwamphamvu, akumanena kuti ena ambiri anali atapititsa kale patsogolo malingaliro a chisinthiko; sanayambitsidwe konse ndi Darwin.
17. Kodi ndizitsanzo zina ziti za kudzichepetsa kwa Mbale Rutherford?
17 Mtumiki wina wokhulupirika m’nthaŵi zamakono amene Yehova Mulungu anamgwiritsira ntchito mwamphamvu anali Joseph F. Rutherford, wotchulidwa kuchiyambi kwa nkhani ino. Iye anali wochirikiza chowonadi cha Baibulo wolimba mtima ndipo makamaka wa dzina la Yehova. Ngakhale kuti anadziŵika kwambiri monga Judge Rutherford, iye anali munthu wa mtima wodzichepetsa. Mwachitsanzo, panthaŵi ina anapereka ndemanga zamphamvu ponena za zimene Akristu anayenera kuyembekezera mu 1925. Pamene zochitika sizinagwirizane ndi ziyembekezo zake, iye modzichepetsa anauza banja la Beteli la Brooklyn kuti anadzipusitsa yekha. Mkristu wina wodzozedwa amene anagwirizana naye kwambiri anachitira umboni kuti iye nthaŵi zambiri anamva Mbale Rutherford akupepesa mwa mzimu wa pa Mateyu 5:23, 24, ponse paŵiri poyera ndi mseri, kaamba kokhumudwitsa Mkristu mnzake ndi mawu opweteka. Pamafunikira kudzichepetsa kuti wina wokhala m’malo aulamuliro apepese kwa awo okhala pansi pa ulamuliro wake. Mbale Rutherford anapereka chitsanzo chabwino kwa oyang’anira onse, kaya mukhale mumpingo, m’ntchito yoyendayenda, kapena panthambi iliyonse ya Sosaite.
18. Kodi ndimawu otani osonyeza mkhalidwe wodzichepetsa wa maganizo amene prezidenti wachitatu wa Sosaite ananena?
18 Prezidenti wachitatu wa Watch Tower Bible and Tract Society, Nathan H. Knorr, anasonyezanso kuti, ngakhale kuti anali wotchuka kwambiri pakati pa anthu a Yehova, sanadzione kukhala wokwezeka chifukwa cha udindo wake. Ngakhale kuti anapambana m’luso la kulinganiza zinthu ndi kulankhula kwapoyera, iye anali ndi ulemu waukulu pazimene ena anachita. Chifukwa chake, tsiku lina iye anakachezera chiŵalo cha Komiti Yolemba mu ofesi yake ndi kunena kuti: “Kunoko nkumene kumachitika ntchito yofunika koposa ndi yovuta koposa. Nchifukwa chake ndimachita zochepa m’ntchitoyi.” Inde, iye anali kugwiritsira ntchito modzichepetsa uphungu wa pa Afilipi 2:3, wakuti “ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.” Iye anazindikira kuti ngakhale kuti kutumikira monga prezidenti wa Sosaite kunali kofunika kwambiri, ntchito zinanso zinali zofunika kwambiri. Kunali kudzichepetsa kwake kumene kunamchititsa kulingalira mwanjirayo ndi kukusonyeza moonekera bwino kwambiri. Iye anali chitsanzo chinanso chabwino choyenera kutsanziridwa ndi onse, makamaka awo amene angakhale m’malo auyang’aniro.
19, 20. (a) Kodi nchitsanzo cha kudzichepetsa chotani chimene prezidenti wachinayi wa Sosaite anapereka? (b) Kodi nkhani yotsatira idzatipatsa chithandizo chotani pa kusonyeza kwathu kudzichepetsa?
19 Prezidenti wachinayi wa Sosaite, Fred W. Franz, analinso chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa. Monga wachiŵiri kwa prezidenti wa Sosaite kwa zaka pafupifupi 32, iye analemba nkhani zambiri za m’magazini ndi maprogramu a misonkhano yachigawo; komabe m’mbali zimenezi iye nthaŵi zonse sanafune kutchuka, osafuna kudziŵika. Tikhoza kusonyeza chitsanzo chofanana cha m’nthaŵi zamakedzana. Pamene Yoabu anagonjetsa Aamoni ku Raba, anatsimikiza kuti Mfumu Davide analandira ulemerero wa chilakikocho.—2 Samueli 12:26-28.
20 Ndithudi, zilipo zitsanzo zabwino zambiri, zakale ndi zamakono, zikumatipatsa zifukwa zamphamvu zokhalira odzichepetsa. Komabe, pali zifukwa zina zambiri zimene tiyenera kukhalira odzichepetsa, ndipo zimenezi limodzinso ndi zinthu zotithandiza kukhala odzichepetsa zidzapendedwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Eksodo 34:6; Numeri 14:18; Nehemiya 9:17; Salmo 86:15; 103:8; 145:8; Yoweli 2:13; Yona 4:2; Nahumu 1:3.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi zipatso za kunyada zakhala zotani?
◻ Kodi ndani amene wasonyeza chitsanzo chabwino koposa cha kudzichepetsa?
◻ Kodi nchiyani chimasonyeza amene anali chitsanzo chachikulu koposa chachiŵiri cha kudzichepetsa?
◻ Kodi nchitsanzo chabwino chotani cha kudzichepetsa chimene mtumwi Paulo anapereka?
◻ Kodi nzitsanzo zotchuka zamakono zotani za kudzichepetsa zimene tili nazo?
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anapereka chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa
[Chithunzi patsamba 16]
Paulo anapereka chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa
[Chithunzi patsamba 17]
Mbale Russell sanadzitamande kaamba ka zinthu zimene analemba