“Funani Yehova, Ofatsa Inu Nonse”
“FUNANI Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:3.
Mneneri Zefaniya ananena mawu amenewo kwa “ofatsa . . . a m’dziko,” ndipo anawalimbikitsa ‘kufuna chifatso’ kotero kuti atetezeredwe mu “tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Zimenezi zikusonyeza mosakayikiritsa kuti chifatso chili chiyeneretso cha chipulumutso. Koma kodi nchifukwa ninji?
Kodi Nkufuniranji Chifatso?
Chifatso ndicho mkhalidwe wa kukhala ndi mtima wodekha, wosanyada kapena kudzigangira. Chimagwirizana kwambiri ndi mikhalidwe ina yaubwino, monga ngati kudzichepetsa ndi kudekha. Zimenezo pokhala ziri choncho, anthu ofatsa ali ophunzitsika ndipo ali ofunitsitsa kulandira chilango kwa Mulungu, ngakhale kuti chingaoneke kukhala chomvetsa chisoni panthaŵiyo.—Salmo 25:9; Ahebri 12:4-11.
Chifatso mwa icho chokha chingakhale chopanda chochita ndi maphunziro a munthu kapena malo m’moyo. Komabe, amene ali ophunzira kwambiri kapena opita patsogolo m’njira yadziko amakhala ndi chikhoterero cha kulingalira kuti ali oyenerera kudzisankhira okha m’chilichonse, ngakhale m’nkhani za kulambira. Zimenezi zingawalepheretse kulola munthu wina kuwaphunzitsa kanthu kena kapena kulandira uphungu ndi kupanga masinthidwe ofunikira m’miyoyo yawo. Ena amene ali olemera mwakuthupi angakhale ndi malingaliro olakwa akuti chisungiko chawo chili m’chuma chawo chakuthupi. Motero, iwo samaona kufunika kwa chuma chauzimu chochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo.—Mateyu 4:4; 5:3; 1 Timoteo 6:17.
Talingalirani za alembi, Afarisi, ndi ansembe aakulu a m’tsiku la Yesu. Panthaŵi ina pamene anyamata otumidwa kukagwira Yesu anabwerako popanda iye, Afasiriwo anati: “Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.” (Yohane 7:45-49) M’mawu ena, kwa Afarisi, osadziŵa ndi osaphunzira okha ndiwo amene akanakhala opulukira kwambiri kotero kuti akakhulupirira Yesu.
Ngakhale zili motero, Afarisi ena anakopeka ndi chowonadi, ndipo anachinjirizadi Yesu ndi Akristu. Pakati pa iwowo panali Nikodemo ndi Gamaliyeli. (Yohane 7:50-52; Machitidwe 5:34-40) Pambuyo pa imfa ya Yesu, “khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” (Machitidwe 6:7) Mosakayikira, chitsanzo chapadera kwambiri chinali cha mtumwi Paulo. Iye anaphunzitsidwa pansi pa uyang’aniro wa Gamaliyeli ndipo anafikira kukhala wochirikiza Chiyuda wolemekezeka ndi wotchuka. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi iye analabadira modzichepetsa chiitano cha Kristu Yesu nakhala wotsatira wake wachangu.—Machitidwe 22:3; 26:4, 5; Agalatiya 1:14-24; 1 Timoteo 1:12-16.
Zonsezi zimasonyeza mwafanizo kuti mosasamala kanthu za mmene chiyambi cha munthu chingakhalire kapena mmene wina angalingalirire tsopano ponena za uthenga wochokera m’Baibulo, mawu a Zefaniya amagwirabe ntchito. Ngati munthu akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu ndi kutsogozedwa ndi Mawu ake, chifatso nchofunika mosalephera.
Awo ‘Ofuna Chifatso’ Lerolino
Mamiliyoni a anthu kuzungulira dziko lonse akulandira mbiri yabwino ya Ufumu. Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo oposa mamiliyoni anayi mlungu uliwonse m’nyumba za anthu oterowo. Ameneŵa ali ndi ziyambi zosiyanasiyana kwambiri ndi mikhalidwe yachuma ndi umoyo m’chitaganya. Komabe, chinthu chimodzi chimene onsewo ali nacho nchakuti iwo ali odzichepetsa mokwanira kotero kuti akulandira uthenga wa Baibulo umene munthu wina anaupereka kwa iwo pakhomo pawo kapena kwina kulikonse. Ambiri a iwo akupita patsogolo bwino lomwe chifukwa chakuti ali ofunitsitsa kuyesayesa kugonjetsa zopinga zimene zili m’njira yawo. Inde, iwo ali pakati pa “ofatsa . . . a m’dziko” lerolino.
Mwachitsanzo, talingalirani za Maria wa ku Mexico. Iye anaphunzira za malamulo kuyunivesite ndipo anali wosungika m’zandalama kaamba ka chuma cha makolo ake. Chifukwa cha zimenezi, iye anakhala ndi malingaliro odzigangira kwambiri amene anamsintha kukhala, monga momwe iyemwini ananenera, munthu “wopanduka, wamwano, wosunga zakukhosi mopambanitsa, ndi wosakhulupirira Mulungu.” Maria anakumbukira kuti: “Ndinayamba kuganiza kuti vuto lililonse linakhoza kuthetsedwa ndi ndalama ndi kuti Mulungu sanali wofunika. Kwenikweni, ndinalingalira kuti iye kunalibeko nkomwe.” Iye anawonjezera kuti: “Kwa ine chipembedzo chinali chinthu choseketsa ndi chofunika cha kakhalidwe chabe.”
Pambuyo pake, Maria anazindikira masinthidwe mwa msuwani wake atakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Maria anafotokoza kuti: “Anali munthu wa makhalidwe oipa, ndipo tsopano anali munthu wamtendere ndi wolungama. Achibale anati iye anali mlaliki ndipo ankaŵerenga Baibulo, motero sanamwenso moŵa kapena kufunanso akazi ochita nawo chisembwere. Chotero ndinafuna kuti abwere kudzandiŵerengera Baibulo chifukwa ndinalingalira kuti mwa njira imeneyi ndikakhoza kupeza mtendere ndi bata zimene ndinafuna kwambiri.” Chotulukapo chake chinali chakuti Maria anavomereza kuphunzira Baibulo ndi Mboni ziŵiri zokwatirana.
Panali zinthu zambiri zimene anafunikira kugonjetsa, ndipo kunalinso kovuta kwambiri kwa iye kuti avomereze lamulo la mkhalidwe Labaibulo la umutu kuti akhale wogonjera kwa mwamuna wake. Koma anapanga masinthidwe aakulu m’moyo ndi maganizo ake. Iye anaulula kuti: “Ndiganiza kuti kuyambira pamene abale analoŵa pakhomo panga ndi kundibweretsera chithandizo cha Yehova, m’nyumba mwanga mwakhala chimwemwe, bata, ndi dalitso la Mulungu.” Lerolino, Maria ali Mboni ya Yehova yodzipatulira ndi yobatizidwa.
M’kulondola kulambira kowona, pali mbali ina mmene chifatso, kapena kusoŵeka kwake, kumachita mbali yaikulu. Kaŵirikaŵiri, mkazi m’banja amalandira chowonadi ndipo amafuna kutumikira Mulungu, komabe mwamuna amazengereza. Mwinamwake kumakhala kovuta kwa amuna ena kuvomereza lingaliro lakuti palinso winawake—Yehova Mulungu—amene mkazi wake tsopano ayenera kugonjera. (1 Akorinto 11:3) Mkazi wina m’Chihuahua, ku Mexico, anapempha phunziro la Baibulo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi iye ndi ana ake asanu ndi aŵiri anabwera m’chowonadi. Poyamba mwamuna wake anali wotsutsa. Chifukwa ninji? Chifukwa sanafune banja lake kulalikira kunyumba ndi nyumba, akumagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo. Mwachionekere, iye analingalira ntchito imeneyi kukhala yonyazitsa kwa iye. Komabe, banja lake linaima nji pachosankha chawo cha kutumikira Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi mwamunayo anayamba kuona phindu la kuvomereza makonzedwe a Mulungu. Koma panapita zaka 15 asanadzipatulire kwa Yehova.
Kuzungulira Mexico yense, padakali zitaganya zakutali zambiri kumene anthu a kumeneko adakali ndi zinenero zachikale ndi miyambo ya Amwenye a ku America. Uthenga wa Baibulo ukufikira anthu ameneŵa ndipo ukuwathandiza kuwongolera mkhalidwe wawo wa moyo, pamene ena akuphunzira kuŵerenga ndi kulemba pophunzira chowonadi. Komabe, chenicheni chakuti anthu siophunzira kwambiri kapena alibe chuma chambiri kwenikweni sichimatanthauza kuti adzakhala omvetsera kwambiri. Kunyada kwaufuko ndi kudzipereka pamiyambo ya makolo nthaŵi zina kumakuchititsa kukhala kovuta kwa ena kulandira chowonadi. Zimenezi zimasonyezanso chifukwa chake m’midzi ina ya Amwenye, awo amene amalandira chowonadi kaŵirikaŵiri amavutitsidwa ndi anthu ena a pamudzi wina. Chotero chifatso chimakhala m’mitundu yambiri.
Labadirani ndi Chifatso
Bwanji ponena za inumwini? Kodi mukulabadira chowonadi cha Mawu a Mulungu? Kapena kodi nkovuta kuti muvomereze mfundo zina za choŵonadi cha Baibulo? Mwinamwake mungafune kudzipenda nokha kuti muone chimene chikukudodometsani. Kodi muli wovutitsidwa maganizo chifukwa chakuti anthu ochuluka amene amakopedwera kuchoŵonadi amachokera kwa anthu osaukirapo? Kodi kunyada mwinamwake kungakhale kukuyambukira malingaliro anu? Ndibwino kulingalira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu; ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.”—1 Akorinto 1:27-29.
Kodi mungakane chuma cha mtengo wapatali kokha chifukwa chakuti mwachipeza m’chotengera chadothi chosakhala cha mtengo wapatali? Ndithudi ayi! Komabe, imeneyo ndiyo njira imene Mulungu wasankha kuperekera kwa ife Mawu ake a chowonadi opulumutsa moyo, monga momwe mtumwi Paulo akufotokozera kuti: “Koma tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7) Chifatso ndi kudzichepetsa zidzatikhozetsa kuona mtengo wake weniweni wa chuma ndipo osati “zotengera zadothi” zokha, kapena atumiki aumunthu, ochibweretsa kwa ife. Mwakutero, tidzakhala tikuwonjezeranso kuthekera kwathu kwa ‘kubisika patsiku la mkwiyo wa Yehova’ ndi kukhala pakati pa ofatsa amene “adzalandira dziko lapansi.”—Zefaniya 2:3; Mateyu 5:5.