Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/1 tsamba 4-9
  • Kummaŵa ndi Kumadzulo, Yehova Akulimbikitsa Anthu Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kummaŵa ndi Kumadzulo, Yehova Akulimbikitsa Anthu Ake
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupita Patsogolo Pansi pa Chiletso
  • Bwanji Ponena za ku America?
  • Mu Afrika Wokanthidwa ndi Nkhondo
  • Mu “Dziko la Chiwombankhanga”
  • “Tanimphitsa Zingwe Zako”
  • Yehova Sanatisiye
    Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/1 tsamba 4-9

Kummaŵa ndi Kumadzulo, Yehova Akulimbikitsa Anthu Ake

M’MAGAWO mmene ntchito yolalikira ili yoletsedwa, m’maiko okanthidwa ndi chiwawa, ndi m’maiko mmene ziletso zachotsedwa posachedwapa​—ndithudi, kuzungulira munda wa padziko lonse​—Yehova akupitiriza kupatsa Mboni zake “ukulu woposa wamphamvu.”​—2 Akorinto 4:7.

Kupita Patsogolo Pansi pa Chiletso

Pa kagulu ka zisumbu za ku Far East, ntchito yolalikira yakhala yoletsedwa kwa zaka 17 tsopano. Kodi Mbonizo zikulefulidwa? Kutalitali! May wapitayu, zinafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 10,756, okwanira 1,297 a iwo anali kutumikira monga atumiki anthaŵi yonse. Pamene mikhalidwe yadziko ikuipiraipira, anthu a pachisumbupo ali oyedzamira kwambiri kumvetsera chowonadi. Chotero iwo akhala akuchitira lipoti maphunziro Abaibulo 15,654 amene amachititsidwa m’nyumba za anthu okondwerera. Kuchiyambiko, 25,397 anafika pamisonkhano imene inachitidwa mwamseri kukumbukira imfa ya Yesu.

Pamene Misonkhano Yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu” inachitidwa​—kachiŵirinso mochenjera mogwirizana ndi mikhalidwe ya kumaloko​—abalewo anasangalala kulandira, m’chinenero cha kumaloko, makope awo a mabuku otulutsidwa amodzimodzi amene anatulutsidwa ku United States. Otembenuza, oŵerenga mopenda, ndi ena anadzipereka kugwira ntchito maola owonjezereka kotero kuti akonze chotulutsidwa chachikulu, chokhala ndi masamba mazana ambiricho, panthaŵi yake. Ndipo kampani yosindikiza yogwirizanika inali yachimwemwe kuchita ntchito yabwino yosindikiza ndi kumamatiza. Osonkhanawo anasangalala kulandira bukulo, lokhala ndi zithunzithunzi zokongola zoposa chikwi chimodzi. Akuluakulu aboma ambiri amalemekeza Mboni za Yehova, ndipo chitsutso chimachokera makamaka kwa atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Kukuyembekezeredwa kuti posachedwapa chiletsocho chidzachotsedwa.

Bwanji Ponena za ku America?

Mboni za Yehova m’maiko a Kumadzulo ameneŵa zili zogwirizana ndi abale awo a Kummaŵa m’kulimbana ndi mavuto awo molimba mtima, ndipo mzimu woyera wa Yehova umawathandiza kulaka mikhalidwe yovuta. Mwachitsanzo, talingalirani za lipoti lotsatirali lochokera ku dziko la ku Latin-America kumene magulu ochita malonda a anamgoneka amayendayenda m’nkhalango.

Kagulu ka Mboni kanakwera basi kupita kugawo lakutali. Pamene anatsika basi, anaona msewu waung’ono wopita kunja kwa mudzi. Chotero abale asanu anapita kukaona kumene kamsewu kafumbiko kanapita, akumagaŵira alongo ndi ana kugwira ntchito m’mudzimo. Mmodzi wa abalewo akusimba kuti:

“Titayenda kwa maola aŵiri pamsewuwo tinapeza nyumba zoŵerengeka zokha. Ndiyeno, amuna asanu ndi atatu onyamula zida ovala zophimba kumutu anatulukira mwadzidzidzi kuchokera m’thengo. Ena anali ndi mfuti zachiwaya, ndipo ena anali ndi zikwanje. Kodi tinakumana ndi chiyani? Tinayamba kufunsa zimene anafuna, koma tinauzidwa kukhala chete osalankhula​—koma kungoyenda kumka kutsogolo. Tinachita zimenezo! Patapita maola aŵiri owonjezereka tikuyenda m’nkhalango yowirira tinafika pamalo olambulidwa bwino amene mwachionekere anali msasa wa anthu onyamula zida. Alonda okhala ndi mfuti anali ponseponse. Pakati pake panali nyumba yomangidwa bwino kumene tinauzidwa kupita.

“Titakhala pansi tinafunsidwa ndi mmodzi amene mwachionekere anali mtsogoleri wa msasawo. Iye anali wovala mwaukhondo, wophunzira, ndipo wolemekezeka. Analoza mmodzi m’kagulu kathu ka abale ndi kumuuza kuimirira. Ndiyeno anamfunsa kuti: ‘Kodi ukuganiza motani za gulu [lathu]?’ Atazindikira kotheratu kumene tinali, mbaleyo anayankha kuti: ‘Eya, tikudziŵa za gulu lanu, koma sitili okondweretsedwa nalo kapena ngakhale gulu lina lililonse landale. Chifukwa chokha chimene tadzera kuno ndicho kulalikira za Ufumu wa Yehova Mulungu m’manja mwa Kristu Yesu. Posachedwapa udzawononga maboma onse andale ndi dongosolo ili la zinthu ndi kubweretsa madalitso abwino koposa kwa anthu padziko lapansili pansi pa mikhalidwe Yaparadaiso​—chinthu chimene palibe munthu kapena gulu la anthu limene lingakhoze kuchita.’

“Mkhalidwe wamaganizo wa munthuyo unasintha. Anayamba kufunsa mafunso. ‘Kodi munaphunzira kuti zonsezi? Kodi munakonzekeretsedwa motani kulankhula motere?’ Kwa ola limodzi ndi theka, tinakhoza kupereka umboni wabwino ponena za mikhalidwe yadziko ndi kusonyeza kuti Baibulo limatchula chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu. Tinalongosolanso za lemba la Aroma chaputala 13​—kuti timamvera maulamuliro olamulira, koma pamene pali kuwombana pakati pa Mawu a Yehova ndi awo, timamvera Mulungu wathu, Yehova, choyamba. Pomalizira pake, tinamgaŵira mabuku amene tinali nawo. Iye anatenga atatu a iwo ndi Baibulo ndipo, motidabwitsa kwambiri, anatipatsa chopereka chake. Ananena kuti akawaŵerenga.

“Kenako, mtsogoleriyo anauza mmodzi wa amunawo kutuluka nafe mu msasamo. Posakhalitsa tinali paulendo wathu wobwerera, tikumathokoza Yehova chifukwa cha chilaliko chimene tinali nacho m’munda wina wolalikira.”

Mu Afrika Wokanthidwa ndi Nkhondo

Chapakati pa Far East ndi Kumadzulo pali dziko la Afrika. Nkhondo za mafuko zasintha maiko ena kumeneko kukhala mikuntho yamphamvu yachiwawa. Ku Liberia, anthu a Yehova ayambukiridwanso kwambiri ndi kuyambika kwa nkhondo yachiweniweni. Poyamba kunali kumenyana mkati ndi kunja kwa mzinda waukulu mkati mwa October ndi November wa 1992. Ndiyeno, pamene nkhondoyo inafalikira dziko lonse, mipingo yathunthu inapasulidwa pamene abale anathaŵira m’tchire limodzi ndi anthu ena onse. Komabe, changu chawo chakhalabe chosathetsedwa. Pamene anali kuthaŵa, analalikira, ndipo zimenezi zinachititsa umboni waukulu kuperekedwa m’mbali zakutali kwambiri za mkatimo.

Mpingo wina wa abale obalalitsidwa unamanga Nyumba Yaufumu yakanthaŵi pakati pa munda wa mitengo yampira. M’tauni ina yapafupi ndi malo omenyanirana nkhondo, nthaŵi yamasana anthu ankathaŵira m’minda ya mitengo yampira yapafupi kuthaŵa mabomba oponyedwera m’mlengalenga. Abale a kumaloko (kuphatikizapo ofalitsa ambiri obalalitsidwa a kumalikulu, m’Monrovia) analinganiza utumiki wakumunda ndipo anali kuonedwa nthaŵi zonse akulalikira kwa zikwi zambiri zobisala pansi pa mitengo yampira! Nthaŵi iliyonse pamene ndege inayandikira, abale ndi alongowo anadumphira m’ngalande yapafupi ndiyeno, ngoziyo itapita, anapitiriza kulalikira kwawoko.

Modabwitsa, ofalitsa ampingo oposa chikwi chimodzi amene ali okhoza kutumiza malipoti awo ku Sosaite, afikira avareji ya maola 18.1 muutumiki wakumunda ndipo akuchititsa maphunziro Abaibulo 3,111 mwezi ndi mwezi, mosasamala kanthu za mikhalidwe ya nkhondo yachiweniweni imeneyi.

Mu Afrika mkati mwa zaka zinayi zapitazi, ziletso zachotsedwa pa ntchito ya Mboni za Yehova m’maiko 18. Ndipo nchisangalalo chopambana chotani nanga! Pa August 12, chiletso chimene chinaikidwa pa Mboni m’Malaŵi mu October 1967, chinachotsedwa. Kulalikira mbiri yabwino mobisa nthaŵi zonse kwakhala kukukula mowonjezereka, koma tsopano Mbonizo zili zokhoza kupitabe patsogolo mwaufulu, ngakhale kuti adzafunikira kuyembekezera chiukiriro cha kudzalandiranso atsamwali awo ambiri okondedwa amene anaphedwa ndi otsendereza.

M’Mozambique, pangano la mtendere linayamba kugwira ntchito pa October 4, 1992. Madera amene kale anali osafikika chifukwa cha nkhondo yosakaza ya zaka 16 akufikiridwa. M’dera la Carioco, kulankhulana kunayambiranso ndi abale ndi alongo 375 amene analephera kulankhulana ndi gulu kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapita. Tsiku la msonkhano wapadera linachitidwa ku Milange, likulu la chigawo chimene kale chinadziŵika monga malo a msasa wachibalo ndi malo “ophunzitsiranso” a Mboni za Yehova, zambiri za izo zinali zothaŵa ku Malaŵi. Chiwonkhetso chodabwitsa cha anthu 2,915 chinafikapo, kuphatikizapo woyang’anira tauni, amene analandira Mboni za Yehova. Chotero malo akale “ophunzitsiranso” ameneŵa anakhala malo a chiphunzitso chaumulungu patsikulo.

Mmishonale wina akulemba kuti: “Ponena za abale athu amene anali m’misasa ya othaŵa kwawo ku Tete Province, ndemanga yokondweretsa inaperekedwa ndi woimira wa bungwe la UNHCR (United Nations High Commissioner for Refugees.) Iye anati Mboni za Yehova zinalinganiza misasa yawo, patali ndi magulu ena. ‘Msasa wawo,’ iye anatero, ‘ unali umodzi wokhawo umene unasamaliridwa bwino,’ nawonjezera kuti, ‘Mboni za Yehova ndizaudongo, zolinganizika, ndi zophunzira.’ Ndiyeno anadzipereka kunditenga paulendo wapandege kudutsa thengo kuti ndikaone ndekha. Ndili mumlengalenga, woulutsa ndege analoza misasa iŵiri. Umodzi unali wosasamaliridwa bwino ndi wauve, wokhala ndi nyumba zomata zoyandikana kwambiri zosalinganizidwa bwino. Winawo unali wolinganizidwa bwino, wokhala ndi nyumba zokhala m’mizera yogawidwa ndi misewu. Nyumbazo zinali ndi maonekedwe audongo, zokhala ndi mabwalo osesedwa. Zina zinapakidwa utoto wopangidwa panyumba. ‘Kodi ungatchule kuti msasa wa anthunu ndiuti?’ anatero woulutsa ndegeyo. Ndinakondwera kwambiri kukumana ndi abale mumsasawu. Tsopano pali mipingo isanu ndi itatu m’mudzi wa Mboni umenewu.”

Mu “Dziko la Chiwombankhanga”

Ayi, chimenechi sichiwombankhanga cha ku United States! Pakati pa Kummaŵa ndi Kumadzulo pali dziko lina la ku Ulaya, Albania, dzina lake m’chinenero chaboma, lakuti Shqipëria, limatanthauza “Dziko la Chiwombankhanga.” Posachedwapa, chiletso chankhalwe cha utali wa zaka 50 pa Mboni za Yehova m’dzikoli chinachotsedwa, ndipo zili zokhoza kugwirizana ndi abale awo a Kummaŵa ndi a Kumadzulo m’kusangalala kwawo ndi ufulu wa kulambira. Iwo alidi “kuchita machawi.” (Aefeso 5:16) Msonkhano woyamba m’mbiri ya Albania, msonkhano wa tsiku limodzi, unachitidwira pa National Theater, m’likulu la dzikolo, Tiranë, pa Sande, March 21. Loŵeruka masana kagulu ka Mboni zodzipereka modzifunira 75 kanasintha malo osonkhanira owonongeka kukhala holo yosonkhanira yowala, yaudongo. Oyang’anira malowo anachita kakasi. Ndipo muyenera kudziŵa kuti pa anthu 75 odzipereka modzifunirawo, pafupifupi 20 okha ndiwo anali obatizidwa!

Kunja kunacha bwino. Pamene nthumwi zochokera kutsidya kwanyanja zinafika, kupatsana moni​—makamaka wa majesichala ndi kukupatirana​—kunachititsa tsiku la msonkhano wapadera limenelo kukhala lapadera kwambiri. Zikhato zitakwezedwa m’mwamba, Mbale Nasho Dori anapereka pemphero lotsegulira. Iye anabatizidwa mu 1930 ndipo tsopano amawona mwachimbuuzi. Programu inaperekedwa m’chinenero cha ku Albania, mbali yaikulu inaperekedwa ndi apainiya apadera a kumaiko ena. Ofikapo 585 anaimba nyimbo yakuti “Kudzipatulira Kwachikristu”​—imodzi ya nyimbo zisanu ndi imodzi zimene zinamasuliridwa m’chinenero cha ku Albania kaamba ka chochitikacho​—pamene abale ndi alongo atsopano 41 anapita kudziŵe limene abale a ku Greece mokoma mtima analipanga m’Nyumba Yaufumu yamomwemo. Ha! kunali kusintha kotani nanga! Kale, kukhala ndi Baibulo kunatanthauza kutumizidwa kumisasa yachibalo, ndipo misonkhano inachepetsedwa kukhala ya anthu aŵiri kapena atatu.

Tsiku lotsatira la msonkhanowo, ofesi ya Watch Tower inalandira foni kuchokera kwa mkulu wa malo azamaseŵerawo. Kaŵirikaŵiri iye amasonyeza chikondwerero chochepa mwa amene amagwiritsira ntchito malo azamaseŵerawo. Imeneyo ndintchito ya wothandiza wa mkuluyo. Koma anati: “Ndangofuna kukuimbirani foni kuti ndikuthokozeni. Sindinaonepo maloŵa ali audongo motere. Nditati ndiwalongosole, ndinganene kuti mphepo yochokera kumwamba inaomba pa malo athu azamaseŵera dzulo. Nthaŵi iliyonse imene mudzafuna kugwiritsira ntchito malo athu, chonde dzabwereninso, ndipo mudzakhala oyamba. Mudziŵa, tiyeneradi kukulolani kubwera miyezi itatu iliyonse kwaulere.”

Mbonizo zinabwerera kumatauni awo zili zolimbikitsidwa ndi zoyamikira ndipo zinayamba kukonzekera Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Masiku 15 okha pambuyo pake, Lachiŵiri, pa April 6, Chikumbutso choyamba chapoyera chinachitidwa m’malo asanu ndi aŵiri.

M’tauni ya Berat, ofika pamsonkhano awonjezeka kufika pafupifupi 170, ndipo wansembe wakumaloko wakwiya. Pa ofalitsa Ufumu 33 m’Berat, 21 anabatizidwa pamsonkhano wadera. Berat anachitira lipoti ofika pa Chikumbutso 472. Ziŵerengero zina za ofika pa Chikumbutso zinalinso zapadera, kwakukulukulu monga chotulukapo cha chitsogozo chabwino choperekedwa ndi apainiya apadera.

M’tauni Yachikatolika ya ku Albania ya Shkodër, kumene kuli tchalitchi chachikulu, tchalitchi chinayamba kusindikiza kalata yamwezi ndi mwezi, ndipo kope lililonse linali ndi nkhani yakuti “Mmene Mungapeŵere Mboni za Yehova.” Kope lomaliza linati: “Mboni za Yehova zalanda Shkodër”! Khamu lalikulu la Mboni ziŵiri kumeneko linasonkhanitsa anthu akhalidwe labwino ndi olama maganizo okwanira 74 kufika pa Chikumbutso. Pambuyo pomvetsera nkhani Yachikumbutso, mabanja 15 anapempha maphunziro Abaibulo. M’tauni ina, ya Durres, kumene kuli khamu la Mboni zinayi, chiŵerengero cha ofikapo chinali chosangalatsa cha 79.

Chifukwa cha chitsutso chochitidwa ndi achichepere Achikatolika, amene anawopseza kupitikitsa Mboni ndi miyala, msonkhano wa Chikumbutso m’mudzi wa ku phiri wa Kalmeti i Vogel unasamutsidwira kunyumba ya mbale wakomweko, kumene 22 anafikapo mwamtendere. Pali ofalitsa asanu m’kagulu kameneka, atatu a iwo anabatizidwa pamsonkhanopo ku Tiranë.

Ku Vlorë anyamata ena aŵiri analandira kope la Nsanja ya Olonda, analiŵerenga, ndi kulembera Sosaite kuti: “Tsopano timadzitcha Mboni za Yehova chifukwa cha chowonadi chimene taphunzira mu Nsanja ya Olonda. Chonde titumizireni thandizo.” Apainiya apadera aŵiri anagaŵiridwa kumeneko, ndipo mmodzi wa anyamata ameneŵa anayeneretsedwa mwamsanga kukhala wofalitsa. Anali wachimwemwe kukhala pakati pa 64 amene anafika pa Chikumbutso ku Vlorë.

Mbale wina wa ku Albania amene anaphunzira chowonadi ku United States anabwerera m’ma 1950 ku tauni yakwawo ya Gjirokastër, kumene anatumikira kumlingo wothekera kufikira imfa yake. Iye anafesa mbewu za chowonadi mumtima mwa mwana wake wamwamuna. Pamene chiletso chinachotsedwa, mwanayu anapempha thandizo ku Watch Tower Society. Wokondwerera wina wokhala m’mudzi wa kumpoto kwake anali atalembanso kupempha thandizo, chotero apainiya apadera anayi anatumizidwa kumeneko. Lachitatu mmaŵa pambuyo pa Chikumbutso, mmodzi wa iwo anaimbira foni ofesi ya Sosaite ku Tiranë nati: “Sindikanatha kukhala chete osakuuzani zinthu zochuluka zimene mzimu wa Yehova wachita. Ndife achimwemwe kwambiri! Chikumbutso chinachitika bwino kwambiri.” Chiŵerengero cha ofikapo chinali 106, kuphatikizapo gulu la ofalitsa Ufumu asanu ndi aŵiri.

Kodi chiwonkhetso cha ofika pa Chikumbutso chinali chotani? Mu 1992, pamene kunali ofalitsa Ufumu 30 okha, ofikapo anali 325. Mu 1993, ofalitsa 131 anasonkhana pakati pa ofikapo 1,318. M’zaka zonse ziŵiri, ofikapo aŵirikiza nthaŵi khumi kuposa chiŵerengero cha ofalitsa. Nkokondweretsa chotani nanga kuona ‘wamng’ono akusanduka chikwi’ m’nyengo yanthaŵi yochepa chotero!​—Yesaya 60:22.

“Tanimphitsa Zingwe Zako”

Pamene ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova ikufutukuka kumbali zonse za dziko, chiitano ichi chikuperekedwa: “Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za [chihema chako chachikulu, NW]; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako. Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere.” (Yesaya 54:2, 3) Kufutukuka kwa “chihema . . . chachikulu” cha Mulungu kumeneku​—koimiridwa ndi mpingo wapadziko lonse wa olambira ake​—kwakhaladi koonekera Kummaŵa kwa Ulaya, makamaka m’maiko amene kale anali a Soviet Union. Pambuyo pochirikiza atumiki ake m’zaka makumi ambiri a chitsenderezo, Yehova tsopano akupatsa Mboni zake nyonga yamphamvu yofunikira kufutukula ndi kulimbitsa gulu.

Ku Moscow, Russia, pa Locomotive Stadium, pa July 22-25, chiŵerengero chapamwamba cha 23,743 chinafika pamsonkhano wamitundu yonse wapadera wa mpambo wa chaka chatha wa “Chiphunzitso Chaumulungu.” Kodi ndani akanalingalira zimenezi kukhala zotheka, ngakhale zaka ziŵiri zapitazo? Komatu zinachitika! Oposa 1,000 anabwera kuchokera ku Japan ndi Korea, pafupifupi 4,000 anachokera ku United States ndi Canada, ndipo zikwi zina zinachokera ku maiko oposa 30 a ku South Pacific, Afrika, Ulaya, ndi madera ena​—ndithudi kukumana kwa Kummaŵa ndi Kumadzulo. Kunali kolimbikitsa chotani nanga kwa onsewa kukhalira pamodzi mwaufulu ndi abale ndi alongo awo oposa 15,000 a ku Russia! Panali chikondwerero chosaneneka.

Chiwonkhetso chodabwitsa cha Mboni zatsopano 1,489 chinabatizidwa. Ubatizowo unafalitsidwa kwambiri ndi oulutsa nkhani kuzungulira padziko lonse, kuphatikizapo chithunzi chabwino kwambiri patsamba loyamba la The New York Times. Ngakhale kuti panthaŵi yaubatizoyo panali kuwomba m’manja kwamphamvu, iko kunaposedwa ndi kuwomba m’manja kumene kunachitidwa m’nkhani yomaliza pamene, wokamba nkhani anali atathokoza odzipereka modzifunira 4,752 ndi akuluakulu amene anali atathandiza kuchititsa msonkhanowo kukhala wachipambano, anati: “Koposa onse, tikuthokoza Yehova!” Inde, mzimu wa Yehova unali utaletsa chitsutso champhamvu chochokera kwa achipembedzo cha Orthodox ndi kupereka nyonga yofunikira imene inachititsa msonkhanowo kukhala wosangalatsa kwambiri.

Komabe, zambiri zinali mtsogolo, mu mzinda wa Kiev wa ku Ukraine, pa August 5-8. Kachiŵirinso, odzipereka modzifunira ofunitsitsa anakonza kotheratu sitediyamu, ndipo m’Nyumba Yaufumu yaikulukulu imeneyi munaloŵa anthu 64,714 monga chiŵerengero chapamwamba cha ofikapo. Kachiŵirinso, Mboni zinachokera Kummaŵa ndi Kumadzulo ndi kumbali zonse zadziko. Nkhani zazikulu zinamasuliridwa m’zinenero 12. Nthumwi pafupifupi 53,000, zimene zinafika ndi zoyendera zosiyanasiyana, zinakachingamiridwa ku masiteshoni a sitima ndi mabwalo andege ndipo zinaperekedwa kumalo awo ogona ku mahotela, sukulu, ndi nyumba za anthu, ndiponso m’masitima apamadzi. Zonsezi zinachitidwa ndi ndalama zochepa ndi kulinganizika kwadongosolo kumene kunadabwitsa ndi kuchititsa apolisi mumzindawo kupereka chitamando.

Mbali yokondweretsa kwambiri pa programu ya msonkhanoyo inali ubatizo, umene unachitidwa kwa maola aŵiri ndi theka onsewo. Chiwonkhetso cha abale ndi alongo atsopano 7,402 anachitira chizindikiro kudzipatulira kwawo kwa Yehova, pamene kuwomba m’manja kunachita namalowe kuzungulira m’sitediyamu yaikuluyo. Chimenechi chinali chiŵerengero chapamwamba kuposa chiŵerengero chachikulu koposa cha ubatizo cha 7,136 cholembedwa pamene osonkhana 253,922 anasonkhana mu New York City mu 1958.

Pamene nyengo yachiweruzo ino ikuyandikira mapeto ake, anthu onga nkhosa a Kummaŵa, Kumadzulo, ndipo ngakhale ku “malekezero ake a dziko” akusonkhanitsidwa mu umodzi wosayerekezereka m’mbiri yonse ya anthu. Ndithudi, “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” akugwirizana ndi Israyeli wauzimu m’kulengeza chikhulupiriro chawo m’nsembe yamtengo wapatali yadipo ya Yesu, maziko a zonse zimene zikukwaniritsidwa m’kulemekezedwa kwa ulamuliro wa ufumu wa Yehova.​—Machitidwe 1:8; Chivumbulutso 7:4, 9, 10.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Akummaŵa agwirizana ndi Akumadzulo ku Moscow ndi Kiev

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena