Yehova Sanatisiye
YOSIMBIDWA NDI NASHO DORI
Mbreshtan ndi mudzi waung’ono wa kumapiri kummwera kwa Albania, pafupi ndi ku Greece. Nkumene ndinabadwira mu 1907. Pamene ndinali ndi zaka zisanu, ndinayamba kupita kusukulu yachigiriki, komano kuphunzira kwanga kunadodometsedwa pamene magulu ankhondo achitaliyana analanda Albania mu Nkhondo Yadziko I. Nkhondoyo itatha, ndinapitiriza kuphunzira kusukulu komano m’chinenero cha Chialabaniya.
NGAKHALE kuti makolo anga sanali okonda chipembedzo kwambiri, anali kusunga miyambo ya Albanian Orthodox Church. Agogo awo a atate anali wansembe mu Mbreshtan, chotero ndinali kugwira ntchito m’tchalitchi ndi kuona zochita za tchalitchicho. Miyambo yake inaoneka yopanda tanthauzo, ndipo mkhalidwe wachinyengo unandivutitsa maganizo.
Mogwirizana ndi mwambo wathu, makolo anga anandisankhira mkazi woti ndikwatire. Argjiro anali wapamudzi wina woyandikana nafe wa Grabova, ndipo tinakwatirana mu 1928, pamene anali ndi zaka 18.
Kuphunzira Choonadi cha Baibulo
Panthaŵiyo ndinadandaula ponena za Tchalitchi cha Orthodox kwa mbale wanga wina amene anafika kudzacheza kuchokera ku United States. “Ku America, pafupi ndi nyumba yanga,” iye anayankha motero, “pali kagulu kena ka anthu kamene kalibe tchalitchi, koma kamaphunzira Baibulo.” Lingaliro la kuphunzira Baibulo popanda tchalitchi ndinalikonda. Chotero ndinampempha kuti akanditumizire mabuku ena ofotokoza Baibulo.
Ndinali nditaiŵaliratu za kukambitsirana kwathuko kufikira patapita pafupifupi chaka chimodzi pamene ndinalandira phasulo kuchokera ku Milwaukee, Wisconsin. Mkati mwake munali buku la Zeze wa Mulungu m’Chialabaniya ndi Nsanja ya Olonda m’Chigiriki. Ndinasuzumira m’buku lonselo ndi kuona mawu otchula za tchalitchi choona. Zimenezo zinandikhumudwitsa. Ndinati, ‘sindikufunanso za tchalitchi.’ Chotero sindinaŵerenge bukulo mokwanira.
Mu 1929, ndinaloŵa usilikali ndipo ananditumiza kumzinda wa Tiranë, likulu la Albania. Kumeneko ndinakumana ndi Stathi Muçi, amene anali kuŵerenga Baibulo lachigiriki. “Kodi umapita ku tchalitchi?” ndinamfunsa motero. “Ayi,” iye anayankha motero. “Ndinachoka m’tchalitchi. Ndine mmodzi wa Ophunzira Baibulo Apadziko Lonse.” Ineyo ndi msilikali wina tinapita kumsonkhano ndi Stathi pa Sande. Kumeneko ndinaphunzira kuti tchalitchi choona si nyumba kapena chipembedzo, koma nchopangidwa ndi atumiki a Kristu odzozedwa. Tsopano ndinazindikira zimene Zeze wa Mulungu anali kunena.
Nasho Idrizi ndi Spiro Vruho anali atabwerera ku Albania kuchokera ku United States chapakati pa ma 1920 ndipo anali kufalitsa choonadi cha Baibulo chimene anaphunzira kumeneko. Ndinayamba kuloŵa misonkhano ku Tiranë, pamodzi ndi Ophunzira Baibulo angapo. Posapita nthaŵi ndinazindikira kuti ndinali nditapeza gulu la Yehova. Chotero pa August 4, 1930, ndinabatizidwa mu mtsinje wina wapafupi.
Pambuyo pake ndinabwerera ku Mbreshtan kukagwira ntchito yanga yopanga nsapato. Koma chofunika koposa, ndinayambanso kuuza ena choonadi cha Baibulo chimene ndinaphunzira. Ndinali kuwauza kuti: “Yesu Kristu sali ngati mafano a m’tchalitchi. Iye ngwamoyo!”
Kulalikira Mosasamala Kanthu za Chitsutso
Ahmed Bey Zogu analanda boma mu 1925, nadzipanga Mfumu Zog I mu 1928, ndi kulamulira kufikira 1939. Nduna yake ya zoyenera zamunthu inavomereza ntchito yathu yachikristu. Komabe, tinali ndi mavuto. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Musa Juka, nduna yoona nkhani za mkati mwa dziko, inali yogwirizana kwambiri ndi papa ku Rome. Juka analamula kuti zipembedzo zitatu zokha ziloledwe m’dziko—Asilamu, a Orthodox, ndi Aroma Katolika. Apolisi anayesa kulanda mabuku athu ndi kutiletsa kulalikira, koma sanakhoze kutero.
Mkati mwa ma 1930, ndinali kupita ku Berat kaŵirikaŵiri, mzinda waukulu mu Albania kumene Mihal Sveci anali kuyang’anira ntchito yathu yolalikira. Tinalinganiza maulendo okalalikira m’dziko lonseli. Panthaŵi ina ndinatumizidwa kutauni ya Shkodër kwa milungu iŵiri, ndipo ndinagaŵira mabuku ambiri. Mu 1935 kagulu kathu kena kanachita haya basi kuti tikalalikire m’tauni ya Këlcyrë. Ndiyeno ulendo wina wokulirapo wa mu Albania unalinganizidwa kaamba ka matauni a Përmet, Leskovik, Ersekë, Korçë, Pogradec, Elbasan. Tinamalizira ulendowo mu Tiranë nthaŵi ya Chikumbutso cha imfa ya Kristu itatsala pang’ono kukwana.
Kuperekedwa kwa chakudya chauzimu kunatithandiza kukhala olimba mwauzimu, chotero sitinamve kukhala osiyidwa. Kuyambira 1930 kudzafika 1939, ndinalandira Nsanja ya Olonda yachigiriki mokhazikika. Chonulirapo changa chinalinso kuŵerenga Baibulo pafupifupi ola limodzi patsiku, zimene ndinachita kwa zaka 60 maso anga asanachite khungu. Baibulo lapezeka m’chinenero cha Chialabaniya posachedwapa, chotero ndili wokondwa kuti ndinaphunzira Chigiriki pamene ndinali mwana. Mboni zina zachialabaniya m’masiku oyambirira amenewo zinaphunziranso kuŵerenga Chigiriki kuti nawonso aŵerenge Baibulo lonse.
Mu 1938, Argjiro anabatizidwa. Podzafika 1939 ana athu asanu ndi aŵiri mwa khumi anali atabadwa. Mwachisoni, ana athu atatu mwa asanu ndi aŵiri oyamba anamwalira pamene anali aang’ono.
Mavuto m’Nkhondo Yadziko II
Mu April 1939, Nkhondo Yadziko II ili pafupi kuyamba, magulu ankhondo achifasisti achitaliyana anaukira Albania. Posapita nthaŵi ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa, koma kagulu kathuko ka olengeza Ufumu 50 kanapitiriza kulalikira. Mabuku athu ndi timabuku pafupifupi 15,000 zinalandidwa ndi kuwonongedwa m’Nkhondo Yadziko II.
Jani Komino anali ndi malo aakulu osungiramo mabuku ogwirizanitsidwa ndi nyumba yake. Pamene magulu ankhondo achitaliyana anadziŵa kuti mabukuwo anasindikizidwa ku United States, anakwiya. “Inu ndinu amanong’onong’o eti! United States wadana ndi Italy!” iwo anatero. Abale ena achinyamata achangu apachibale Thomai ndi Vasili Cama anamangidwa, ndipo pamene kunadziŵika kuti mabuku amene anali kugaŵira anachokera kwa Komino, nayenso anamangidwa. Posakhalitsa ndinaitanidwa kupolisi kuti ndikafunsidwe.
“Kodi anthuŵa ukuwadziŵa?” iwo anandifunsa choncho.
“Inde,” ndinawayankha.
“Kodi umagwira nawo ntchito?”
“Inde,” ndinayankha. “Ndife Mboni za Yehova. Sitilimbana ndi maboma. Tilibe mbali m’ndale.”
“Kodi mwakhala mukupereka kwa anthu mabuku awa?”
Pamene ndinavomera motsimikiza, anandimanga ndi unyolo, ndipo anandiika m’ndende pa July 6, 1940. Mmenemo ndinagwirizana ndi ena asanu ochokera m’mudzi wakwathu—Josef Kaci, Llukan Barko, Jani Komino, ndi anyamata aŵiriwo apachibale a a Cama. Pamene tinali m’ndende tinakumana ndi Mboni zina zitatu—Gori Naçi, Nikodhim Shyti, ndi Leonidas Pope. Asanu ndi anayi tonsefe tinaikidwa mopanikizana m’chipinda cha mamita 1.8 m’bwambi ndi 3.7 muutali!
Titakhala mmenemo masiku oŵerengeka, tinamangidwa muunyolo pamodzi ndi kutengeredwa ku mzinda wa Përmet. Patapita miyezi itatu anatisamutsira ku ndende ya ku Tiranë ndi kukhala kumeneko kwa miyezi inanso isanu ndi itatu popanda kuimbidwa mlandu.
Potsirizira pake, tinakaonekera pabwalo lamilandu la asilikali. Ine ndi Mbale Shyti tinapatsidwa chilango cha miyezi 27 m’ndende, Mbale Komino cha miyezi 24, ndipo enawo anamasulidwa pambuyo pa miyezi khumi. Anatisamutsira ku ndende ya ku Gjirokastër, kumene Mbale Gole Flloko anatithandiza pakumasulidwa mu 1943. Pambuyo pake banja lathu linasamukira mu mzinda wa Përmet, kumene ndinakhala woyang’anira mpingo waung’ono.
Ngakhale kuti ntchito yathu inali yoletsedwa ndipo Nkhondo Yadziko II inali kulilima m’maiko otizinga, tinapitiriza kuchita zimene tinatha kuti tikwaniritse utumiki wathu wa kulalikira uthenga wa Ufumu. (Mateyu 24:14) Mu 1944 Mboni zokwanira 15 zinali m’ndende. Komabe, mkati mwa nthaŵi zovuta zimenezi, sitinamve kukhala osiyidwa ndi Yehova.
Kuyesedwa Pankhani ya Kusakhalira Mbali
Ngakhale kuti nkhondoyo inatha mu 1945, mavuto athu anapitiriza ndipo ngakhale kukula kwambiri. Lamulo la kuponya voti moumiriza linakhazikitsidwa m’chisankho cha December 2, 1946. Aliyense amene anayesa kukana anaonedwa ngati mdani wa Boma. Anthu a mpingo wathu ku Përmet anayamba kufunsa kuti, “Kodi tiyenera kuchitanji?”
“Ngati mukhulupirira Yehova,” ndinkayankha motero, “simudzandifunsa zochita. Mukudziŵa kale kuti anthu a Yehova ali osakhalira mbali. Sali a dziko lapansi.”—Yohane 17:16.
Tsiku la chisankho linafika, ndipo nthumwi za boma zinafika panyumba pathu. Anayamba kulankhula modekha kuti, “Aha, tiyeni tizimwa kofi tikumalankhula. Kodi mukudziŵa kuti lero ndi tsiku lanji?”
“Inde, chisankho chikuchitika lero,” ndinawayankha choncho.
“Ndiyetu mufulumire, chifukwa mwina mungachedwe,” ofesala wina anatero.
“Ayi, sindikupita kumeneko. Tinasankha Yehova,” ndinamuyankha choncho.
“Chabwino, tiyenitu mukavotere zipani zotsutsa boma.”
Ndinalongosola kuti Mboni za Yehova sizikhalira mbali konse. Pamene kaimidwe kathu kanadziŵika kwa onse, tinatsenderezedwa kwambiri. Anatilamulira kuleka kusonkhana, chotero tinayamba kusonkhana mobisa.
Kubwerera Kumudzi Kwathu
Mu 1947 ine ndi banja langa tinabwerera ku Mbreshtan. Posakhalitsa, pamasana ena ozizira a December, ndinaitanidwa ku ofesi ya Sigurimi (apolisi achinsinsi). Ofesala wake anafunsa kuti, “kodi ukudziŵa chifukwa chake ndakuitana?”
“Ndiganiza kuti nchifukwa chakuti mwamva zimene anthu andineneza,” ndinayankha motero. “Koma Baibulo limati dziko lidzatida, chotero zinenezo sizikundidabwitsa.”—Yohane 15:18, 19.
“Usalankhule za Baibulo kwa ine,” iye anatero mwaukali. “Ndingakuumbuze.”
Ofesalayo ndi anyamata ake anachoka koma anandiuza kuti ndiime kunja kozizirako. Patapita kanthaŵi kochepa anandiitana mu ofesi mwake ndi kundilamula kuleka kuchita misonkhano panyumba panga. “Kodi m’mudzi wakwanuwo muli anthu angati?” anafunsa motero.
“Anthu zana limodzi ndi makumi aŵiri,” ndinatero.
“Kodi iwo ngachipembedzo chiti?”
“Cha Albanian Orthodox.”
“Nanga iwe?”
“Ndine mmodzi wa Mboni za Yehova.”
“Anthu zana limodzi ndi makumi aŵiri atenga njira imodzi, koma iwe yakoyako eti?” Ndiyeno anandilamula kukayatsa makandulo m’tchalitchi. Pamene ndinanena kuti sindingachite zimenezo, anayamba kundimenya ndi ndodo. Kunali cha ku ma 1 koloko mmamaŵa pamene ndinamasulidwa.
Mitokoma ya Mabuku Ileka Kufika
Nkhondo Yadziko II itatha, tinayambanso kulandira Nsanja ya Olonda pa positi, koma m’kupita kwa nthaŵi magazini analeka kufika. Ndiyeno, usiku wina pa 10 koloko, ndinaitanidwa ndi apolisi achinsinsi. Anandiuza kuti “magazini ena achigiriki afika ndipo tikufuna kuti ulongosole kuti ngachiyani.”
“Sindimachidziŵa bwino Chigiriki,” ndinatero. “Mnansi wanga wina ndiye amene amachidziŵa bwino. Mwinamwake angakuthandizeni.”
“Ayi, tikufuna kuti iweyo ulongosole zimenezi,” ofesala wina anatero pamene analikutulutsa makope a Nsanja ya Olonda achigiriki.
“Oho, izi nzanga!” ndinatero. “Zoonadi, ndikhoza kulongosola zimenezi. Mwaona nanga, magaziniŵa amachokera ku Brooklyn, New York. Kumeneko nkumene kuli likulu la Mboni za Yehova. Ine ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Koma ndikuona ngati kuti analakwitsa keyala yake. Magazini ameneŵa akanayenera kutumizidwa kwa ine, osati kwa inu.”
Sanandipatse magaziniwo, ndipo kuyambira pamenepo kufikira mu 1991, zaka zoposa 40 pambuyo pake, sitinalandire buku lililonse lofotokoza Baibulo mu Albania. M’zaka zonsezo, tinapitiriza kulalikira, tikumagwiritsira ntchito Baibulo lokha. Mboni pafupifupi 20 zinali m’ndende mu 1949; ena anapatsidwa zilango za zaka zisanu.
Mavuto Awonjezereka
M’ma 1950, anthu analamulidwa kukhala ndi ziphaso zosonyeza kuti anali kuchirikiza magulu ankhondo. Koma Mboni za Yehova zinakana kukhala ndi ziphaso zimenezo. Chifukwa cha zimenezi, ine ndi Mbale Komino tinathera miyezi iŵirinso m’ndende.
Panthaŵi imene Boma linalola zipembedzo zina, tinali aufulu pang’ono. Komano, mu 1967 zipembedzo zonse zinaletsedwa, zikumapangitsa Albania kukhaliratu dziko losakhulupirira Mulungu mwalamulo. Mboni zinapitiriza kuyesayesa kusonkhana, koma zimenezi zinakhala zovuta kwambiri. Ena a ife tinasoka thumba lapadera m’nsalu yamkati mwa majekete athu kuti tizibisamo ma Baibulo. Ndiyeno tinkapita kuthengo kukaliŵerenga.
Mboni za ku Tiranë zinagwidwa, ndipo atatu a iwo anapatsidwa chilango cha zaka zisanu kumsasa wachibalo wina wakutali. Chifukwa cha zimenezo, mabanja awo anavutika. Ena a ife ochokera m’midzi yaing’ono yakutali sanatipereke kumeneko chifukwa chakuti anationa kukhala osawopseza boma kwenikweni. Koma anatichotsa m’kaundula wa chakudya chifukwa cha kusakhalira mbali kwathu. Motero, moyo unali wovuta kwambiri. Ndiponso, ana athu enanso aŵiri anamwalira. Komabe sitinamve kukhala osiyidwa ndi Yehova.
Mantha anali ofala mu Albania. Munthu aliyense anali kulondedwa, ndipo apolisi achinsinsi anali kulemba malipoti onena za aliyense amene anayesa kunena lingaliro losiyana ndi la chipani cholamulira. Chotero tinali osamala kwambiri ponena za kulemba malipoti a ntchito yathu. Tinali kusonkhana m’magulu a anthu osaposa aŵiri kapena atatu kuti tilimbikitsane mwauzimu. Komabe, sitinaleke kulalikira.
Poyesayesa kuchititsa msokonezo pakati pa abale, apolisi achinsinsi anawanditsa mphekesera yakuti Mboni ina yodziŵika ku Tiranë inali kazitape. Zimenezi zinapangitsa ena kutaya chidaliro chawo ndi kusokoneza umodzi wathu pang’ono. Chifukwa cha kusakhala ndi mabuku atsopano alionse ofotokoza Baibulo ndiponso posoŵa njira yolankhulana ndi gulu la Yehova looneka, angapo anagonja chifukwa cha mantha.
Ndiponso, akuluakulu a boma anawanditsa mphekesera yakuti Spiro Vruho, mkulu wolemekezedwa kwambiri wachikristu ku Albania, anali atadzipha. “Mwaonatu,” iwo anatero, “ngakhale Vruho wagonja.” Pambuyo pake tinadziŵa kuti Mbale Vruho anachita kuphedwa.
Mu 1975, ine ndi Argjiro tinakhala ndi mwana wathu wamwamuna ku Tiranë kwa miyezi ingapo. M’nthaŵi ya masankho, akuluakulu a boma mu mzindawo anatiumiriza mwa kutiwopseza kuti: “Ngati simuponya voti, tidzathamangitsa mwana wanu pantchito.”
“Mwana wangayu wakhala pantchito pake kwa zaka 25,” ndinayankha motero. “Inu muli ndi umboni watsatanetsatane wolembedwa ponena za iye ndi banja lake. Ine sindinaponye voti pa zaka zoposa 40 zapitazi. Umboni umenewu uli m’mabuku anu a antchito. Ngati mulibemo, ndiye kuti mabuku anu sali m’dongosolo labwino. Ngati zimenezi zili m’mabuku anu, ndiye kuti mwakhala osakhulupirika kuchipani mwa kumlola kugwira ntchito zaka zambirimbiri zonsezi.” Atamva zimenezi, akuluakuluwo ananena kuti ngati tibwerera ku Mbreshtan, iwo sadzatchulanso nkhaniyo.
Kusintha Kwadzidzidzi
Mu 1983 tinasamuka ku Mbreshtan kumka ku mzinda wa Laç. Posakhalitsa, mu 1985, wolamulira woponderezayo anafa. Iye anali atalamulira kuyambira pa masankho oumiriza aja mu 1946. M’kupita kwa nthaŵi, chipirala chake choumbidwa, chimene chinali chotchuka pa bwalo lochezerako anthu ku Tiranë, ndi chija cha Stalin zinagwetsedwa.
Mkati mwa zaka makumi ambiri zimenezo za kuletsedwa kwa ntchito yathu, Mboni zambiri zinachitiridwa mwankhanza, ndipo zina zinaphedwa. Mwamuna wina anauza Mboni zina pakhwalala kuti: “Mu nthaŵi ya Akomyunisiti, tonsefe tinamsiya Mulungu. Ndi Mboni za Yehova zokha zimene zinakhala zokhulupirikabe kwa iye ngakhale kuti zinakumana ndi mayeso ndi mavuto.”
Pamene ufulu wowonjezereka unaperekedwa, anthu asanu ndi anayi anachitira lipoti utumiki wachikristu mu June 1991. Mu June 1992, patapita mwezi chiletsocho chitachotsedwa, anthu 56 anakhala ndi phande mu ntchito ya kulalikira. Kuchiyambiyambi kwa chakacho tinasangalala kwambiri kukhala ndi anthu 325 ofika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Kuyambira pamenepo chiŵerengero cha olalikira chakula kuposa pa anthu 600, ndipo chiwonkhetso cha anthu 3,491 anafika pa Chikumbutso pa April 14, 1995! M’zaka zaposachedwapa ndakhala ndi chimwemwe chosaneneka kuona achichepere ambiri akumawonjezereka kumipingo yathu.
Argjiro wakhala wokhulupirikabe kwa Yehova ndipo wakhala wodalirika kwa ine zaka zonsezi. Pamene ndinali m’ndende kapena kuyenda ulendo wa ntchito yolalikira, iyeyo anasamalira banja lathu mopirira popanda kudandaula. Mmodzi wa ana athu aamuna ndi mkazi wake anabatizidwa mu 1993. Zimenezo zinatikondweretsa kwambiri.
Kaamba ka Ufumu wa Mulungu Wokha
Ndili wokondwa kuona gulu la Yehova mu Albania lili logwirizana kwambiri ndi kusangalala ndi kulemerera kwauzimu. Ndimamva ngati Simeoni wokalamba mu Yerusalemu amene anapatsidwa mwaŵi wamtengo wapatali wa kuona Mesiya wolonjezedwa kwanthaŵi yaitaliyo, asanafe. (Luka 2:30, 31) Tsopano pamene ndifunsidwa za mtundu wa boma umene ndimakonda, ndimati: “Sindikonda Chikomyunizimu kapena chikaputolizimu. Zilibe kanthu kuti kaya anthu ndiwo eni malo kapena Boma. Maboma amamanga misewu, kupititsa magetsi kumidzi yakutali, ndipo amachititsa zinthu kukhala zadongosolo pang’ono. Komabe, boma la Yehova, Ufumu wake wakumwamba, ndiwo chothetsera chokha cha mavuto amene Alabaniya ndiponso dziko lonse likukumana nawo.”
Zimene atumiki a Mulungu akuchita padziko lonse lapansi polalikira za Ufumu wa Mulungu si ntchito ya munthu wamba. Imeneyi ndi ntchito ya Mulungu. Ife ndife atumiki ake. Ngakhale kuti tinali ndi zovuta zambiri ku Albania ndipo tinalibe njira yolankhulirana ndi gulu la Yehova looneka kwa nthaŵi yaitali, iyeyo sanatisiye. Nthaŵi zonse mzimu wake unali nafe. Anatitsogolera m’njira monse. Zimenezi ndaziona m’moyo wanga wonse.