Lipoti la Olengeza Ufumu
Kuchirimika Kudzetsa Mfupo Zazikulu
YESU ananeneratu kuti otsatira ake akazunzidwa, ndipo nayenso mtumwi Paulo anatero, monga momwe kwanenedwera pa 2 Timoteo 3:12 kuti: “Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” Koma kuchirimika potumikira Yehova Mulungu kumadzetsa mfupo zazikulu.
◻ Zimenezi zinali choncho m’tauni ina ya kugombe la kumpoto koma cha kummaŵa kwa Malaysia. Ngakhale kuti anali Mbuddha wolimba amene anaphunzitsa ana ake kwambiri, atateyo analephera kuletsa ana ake aakazi atatu ndi ana aamuna atatu kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ngakhale mkazi wake anakondwereranso chowonadi. Ndiyeno tsiku lina mnansi wake wina anamnyodola akumati: “Kodi mungalephere motani kulamulira ana anu ndi kuwalola kukhala Mboni za Yehova? Inetu ana anga onse amandimvera ndipo ali m’chipembedzo cha Chibuddha cha makolo athu. Mumachititsa chisoni kwambiri!”
Atatewo anamka kunyumba kwawo mofulumira akumawopseza kukamenya mlongo amene anali kuchititsa maphunziro kwa ana akewo. Komabe, anawo anawaletsa kuchita motero napitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kufika pamisonkhano mochirikizidwa ndi amayi awo.
Komabe, potsirizira pake, atatewo anaitana banja lonselo pamaso pawo. “Sankhani,” iwo analamula motero, “pakati pa ine ndi kukhala panyumba pano ndi kukhala Akristu ndi kuchoka panyumba pano.” Mwana wamkulu wamwamuna, mnyamata wolankhula mofatsa kwambiri, nthaŵi yomweyo anayamba kulongedza katundu kuti achoke. “Ayi!” atatewo anafuula motero. “Popeza kuti nonsenu ndinu ana opanduka, kuli bwino kuti ndingofa.” Ndiyeno anatuluka m’nyumbamo mofulumira, banjalo likumawalondola, ndi kuwachonderera kuti asadziphe. Atachita chidwi ndi kuchonderera kwawo, anabwerera kunyumba.
Panapita nthaŵi. Atateyo anayamba kuona chiyambukiro chabwino cha chowonadi Chabaibulo pakhalidwe la ana ake. Tsiku lina anakumana ndi bwenzi lake lomnyodola lija, limene tsopano linali lachisoni, limene linati: “Ndagwiritsidwa mwala kwambiri ndi ana anga. Amandinamiza ndi kundibera zinthu.” Koma atate amene ana awo anali kuphunzira chowonadi ndi Mboni za Yehova anati: “O, ana anga sachita zimenezo! Iwo ngokoma mtima kwambiri kwa ine ndipo anandithandizadi kulipirira ndalama za galimoto langa pamene sindinali pantchito.”
Lerolino, ana aakazi atatu ndi amayi awo ngobatizidwa. Mwana wamwamuna mmodzi ndimpainiya wapadera. Ndipo bwanji za amene kale anali atate wotsutsa ndi waukali kwambiriyo? Iye tsopano ngwaubwenzi ndipo anafika pa Chikumbutso.
Yehova anafupa mwana wamwamunayo ndi alongo ake atatu limodzinso ndi amayi awo chifukwa cha kuchirimika kwawo kwa Iye. Iwo tsopano ali alaliki Aufumu achangu, akumakondweretsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.