Mboni za Yehova Padziko Lonse—Lipabuliki la Philippines
ZISUMBU 7,083 zomwazikanamwazikana za kumalo otentha zopanga Lipabuliki la Philippines zili mbali ya kumtunda ya mtandadza wa mapiri omira pang’ono.a Ndipo nzika 62,000,000 za ku Philippines zimakonda kulankhula za pafupifupi nkhani iliyonse. Mzimu waubwenzi umenewu umachititsa munda wachonde wolalikiramo za Ufumu.
Kuchitira Umboni ku Sukulu
Pachisumbu cha Masbate, wophunzira wina wachichepere wa pasukulu yasekondale anali wokhoza kuchitira umboni kwa mphunzitsi wake ndi kalasi panthaŵi ya mayeso oyankha kuti zowona kapena zonama. Iye akusimba kuti:
“Chiganizocho chinali chakuti, ‘Ngati Mulungu amandikonda, sadzandipatsa mavuto kapena kundilola kuvutika.’ Pamene mphunzitsi wanga anachonga mapepala athu, anapeza kuti onse anayankha kuti zowona kupatulapo ine ndekha. Mphunzitsi wangayo anandilola kufotokozera kalasilo chifukwa chake ndinayankha kuti zonama. Ndinanena kuti Mulungu sindiye amatipatsa mavuto, ngakhale kuti amalola kuvutika ndi kulola kuti tiyesedwe. Ndikumagwiritsira ntchito Baibulo langa, limene ndimamka nalo kusukulu nthaŵi zonse, ndinakambitsirana ndi kalasilo mawu a pa 1 Yohane 4:8, ‘Mulungu ndiye chikondi.’ Nditamaliza kufotokoza, mphunzitsi wanga anakhutira, anagogoda desiki lake, nati: ‘Marilou wakhoza.’ Ndinali ine ndekha amene ndinalemba yankho lolondola pa funso limeneli ndipo ndinalandira mamalikisi ochuluka koposa.”
Uthenga wa Ufumu Uli Ponseponse
Pamene anali muutumiki wakunyumba ndi nyumba kumbali ina ya Philippines, mpainiya wokhazikika (mlaliki wa nthaŵi yonse wa mbiri yabwino) anakumana ndi mayi wina wa ana aang’ono atatu. Mkaziyo anasonyeza chikondwerero chachikulu muuthenga wa Ufumu, ndipo zimenezi zinakuchititsa kukhala kosavuta kuyambitsa phunziro la Baibulo kwa iye. Ngakhale kuti mwamuna wake sanakondwere kuti iye anali kuphunzira Baibulo, makamaka ndi Mboni za Yehova, phunzirolo linapitirizabe.
Mwamunayo anasamutsira banja lake ku mzinda wina, akumaganiza kuti zimenezi zikathetsa kuyanjana kwa mkazi wake ndi Mboni. Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali mkaziyo anapezedwa, ndipo anayambanso phunziro lake la Baibulo. Ndithudi, mwamuna wake anakwiya kwambiri. Anamka kuntchito ndi mkwiyo wakewo, kumene anauza malingaliro ake munthu wina amene ankamkonzera galimoto. Mwamunayo sanadziŵe kuti munthu wokonzeredwa galimotoyo anali mmodzi wa Mboni za Yehova.
Mboniyo inafotokoza kuti kungakhale kopindulitsa kwambiri kwa banja lonselo ngati mkazi wake apitiriza kuphunzira Baibulo. Mkaziyo akhoza kuyamba kugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe a Baibulo m’nyumba. Anaperekanso lingaliro lakuti mwamunayo angapindule ngati nayenso aphunzira za Ufumu wa Mulungu.
Kodi nchiyani chinachitika pambuyo pa kukambitsirana kumeneku? Mkazi wa mwamunayo anali ndi ufulu wokulira wa kuphunzira Baibulo, ndipo mwamunayo anasankha kusamutsa banja lake kubwerera kumalo awo oyamba. Kumeneko mkaziyo anapanga kupita patsogolo kwauzimu kufikira pakukhala wofalitsa Ufumu wosabatizidwa. Mwamuna wake anavomerezanso phunziro la Baibulo, ndipo banja lonse linayamba kufika pamisonkhano Yachikristu.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze mawu owonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.
[Bokosi patsamba 8]
CHIŴERENGERO CHA DZIKO
Chaka Chautumiki cha 1993
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OFALITSA: 116,576
CHIŴERENGERO CHA: Mboni imodzi kwa 549
OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 357,388
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 22,705
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 94,370
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 7,559
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 3,332
OFESI YANTHAMBI: MANILA
[Chithunzi patsamba 9]
Kulalikira pamsika kumabweretsa zotulukapo zabwino
[Chithunzi patsamba 9]
Ofesi yanthambi ya Watchtower Society ku Manila