Kodi Mpikisano Ndiwo Mfungulo ya Chipambano?
“KUPAMBANA sikumaposedwa ndi kalikonse, ndiko chinthu chofunika koposa.” Lerolino ambiri amakhala ndi moyo mogwirizana ndi mawu ameneŵa, onenedwa kaŵirikaŵiri ndi mphunzitsi wa mpira wa ku America, Vince Lombardi. Tsopano, maiko omwe kale anali a Chikomyunizimu agwapo pa kutamanda lingaliro lofala la mpikisano. Kuyambitsa mpikisano m’malonda awo kukumanenedwa kukhala njira yodzetsera kukhupuka. Kummaŵa makolo ambiri amaloŵetsa ana awo mumpikisano ndi ena ndi kuwatumiza kusukulu zakanthaŵi kumene amaphunzitsidwa luso la kupambana mayeso oloŵera. Makolo otengeka maganizo pankhaniyi ali otsimikiza kuti kuloŵa sukulu yotchuka ndiko mfungulo ya kukhupuka kwamtsogolo.
Ambiri amakhulupirira kwambiri kuti mpikisano ndiwo mfungulo ya chipambano. Malinga ndi kuganiza kwawo, anthu apita patsogolo mwa kupikisana wina ndi mnzake. “Mpikisano wopititsa patsogolo malonda ndiwo magwero a nyonga ya mabungwe a makampani a m’Japan,” inatero 65.9 peresenti ya akuluakulu a mabungwe aakulu a makampani amene anafunsidwa ndi Federation of Economic Organizations ya ku Japan. Ndipo kukuoneka ngati kuti makampani a ku Japan akhala akupeza chipambano kwanthaŵi yakutiyakuti. Komabe, kodi mpikisano ulidi mfungulo ya chipambano?
Kodi Umafupadi?
Anthu amene amapikisana ndi ena amasonyeza mzimu wadyera, wa ine choyamba. Iwo amakondwa pamene ena alephera, akumalingalira kuti kulephera kwa enako kudzawadzetsera chipambano. Kuti apeze phindu lawo ladyera, angagwiritsire ntchito njira zovulaza ena. Kodi kulondola chipambano kotero kupyolera mwa mpikisano kumatsogolera kuti? Yasuo, amene anadziloŵetsa mumpikisano wa kukhala wotchuka pakampani yake, akukumbukira njira yake yakale akumati: “Pokhala wodzala ndi mzimu wampikisano ndi malingaliro akukwezedwa pantchito, ndinadziyerekezera ndi ena ndipo ndinadziona kukhala wowaposa. Pamene anthuwo anakwezedwa kundiposa, ndinada nkhaŵa ndipo ndinadandaula masiku onse ndi oyang’anira ntchito pakampanipo. Ndinalibe mabwenzi enieni.”
Mzimu wampikisano ungatsogolerenso ku imfa yamwamsanga. Motani? Mainichi Daily News ya ku Japan ikugwirizanitsa karoshi, kapena imfa yochititsidwa ndi kugwira ntchito kopambanitsa, ndi khalidwe lotchedwa type-A. Mawu akuti type-A amafotokoza mchitidwe wakulimbana ndi kupsinjika mwa kutanganitsidwa mopambanitsa ndi kusawononga nthaŵi, mzimu wampikisano, ndi udani. Akatswiri azamtima a ku America Friedman ndi Rosenman akugwirizanitsa khalidwe la type-A ndi nthenda ya mitsempha ya mtima. Inde, mzimu wampikisano ungakhale wakupha.
Ndiponso mpikisano kumalo antchito ungachititse matenda ena akuthupi ndi amaganizo. Tatengani chitsanzo chimodzi cha Keinosuke, amene anali wosatsa malonda wopambana wa kampani yaikulu yogulitsa magalimoto ku Japan. Iye anapambana mwa kugulitsa magalimoto okwanira 1,250. Chithunzithunzi chake chinaikidwa m’feremu ndi kukoloŵekedwa m’chipinda cha bungwe la oyang’anira ntchito kumalikulu a kampaniyo. Ngakhale kuti ananyansidwa ndi kulima anzake pamsana kuti akwezedwe pantchito, kampani inamsonkhezera kuchita mpikisano. Chotero, m’chaka chimodzi anadwala zilonda za m’chifu ndi m’matumbo. Chaka chimodzimodzicho, akulu antchito 15 m’kampani yake anagonekedwa m’chipatala, ndipo mmodzi anadzipha.
Panyumba, mzimu wofuna kukhala ndi zimene ena ali nazo umasonkhezera anthu kudzitamandira pa zinthu zimene ali nazo mumkangano wosatha. (1 Yohane 2:16) Zimenezi zimangopindulitsa dongosolo la malonda, zikumachititsa amalonda a dziko lapansi kupeza ndalama.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 18:11.
Ngakhale kuti mzimu wamkangano ndi mpikisano ungapititse ntchito patsogolo, mposadabwitsa kuti Mfumu Solomo anati: “Ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndichabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Choncho kodi ndimotani mmene tingasungire mtendere wa maganizo pamene tikukhala m’chitaganya champikisano? Kuti tipeze yankho, tiyeni choyamba tione kumene lingaliro lampikisano linayambira.