Mtendere wa Maganizo m’Chitaganya Champikisano
“NGATI munthu afuna kukhala woyamba,” Yesu Kristu analangiza atumwi ake, “akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.” Atumwiwo anali kutsutsana ponena za amene anali wamkulu mwa iwo. Iwo anadziŵa kuti Yesu anada mzimu wa mtundu umenewo. Palibe ndi tsiku limodzi lomwe pamene iye anachititsa ophunzira ake kupikisana monga njira yochirikizira kupita patsogolo kwauzimu.—Marko 9:33-37.
Asanadze kudziko lapansi, Yesu Kristu anali ndi mbali m’kulengedwa kwa anthu aŵiri oyamba ndipo anadziŵa mmene anapangidwira. (Akolose 1:15, 16) Anthu oyamba analengedwa ndi kukhoza kwa kupita patsogolo popanda kuchita mpikisano wa wafawafa watsalawatsala ndi ena. Anthu sanafunikire kumenyana kuti aone amene anali mtsogoleri wawo, ndipo sanapikisane ndi zinyama kulimbirana kukhalapo kwawo.—Genesis 1:26; 2:20-24; 1 Akorinto 11:3.
Magwero a Mzimu Wampikisano
Pamenepa, kodi ndimotani mmene mzimu wampikisano wa wafawafa watsalawatsala unakhalira mphamvu yolamulira m’chitaganya cha anthu? Mlandu woyamba wambanda m’mbiri ya anthu umapereka yankho. Mzimu wampikisano mwa Kaini, mwana wachisamba wa banja laumunthu loyamba, unachititsa tsokalo. Kaini anapha mbale wake Abele chifukwa nsembe ya Abele inakondweretsa Mulungu, pamene ya Kaini sinatero. Ndipo Baibulo limati Kaini anali “wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:12; Genesis 4:4-8.
Inde, woipayo, Satana Mdyerekezi, ndiye woyambitsa ndi wochirikiza mzimu wampikisano. Ngakhale kuti anali mwana waungelo wa Mulungu wokhala ndi mwaŵi waukulu, anafuna zowonjezereka. (Yerekezerani ndi Ezekieli 28:14, 15.) Pamene ananyenga Hava, anavumbula chikhumbo chake. Iye ananena kuti mwa kudya chipatso choletsedwa, mkaziyo ‘akakhala ngati Mulungu.’ (Genesis 3:4, 5) Kunena zowona, anali Satana amene anafuna kukhala ngati Mulungu, akumapikisana ndi Yehova. Mzimu wakupikisana ndi Mulungu unamsonkhezera kupanduka.—Yakobo 1:14, 15.
Mzimu umenewu umayambukira. Chifukwa cha chisonkhezero cha Satana, mtendere woperekedwa ndi Mulungu wa m’kakonzedwe koyambirira ka banja unatayika. (Genesis 3:6, 16) Kuyambira pamene anapandukira Mulungu, Satana Mdyerekezi walamulira mtundu wa anthu, akumachirikiza mzimu wampikisano, ngakhale kunyenga amuna ndi akazi kukhulupirira kuti mpikisano wa wafawafa watsalawatsala ndiwo mfungulo ya chimwemwe. Komabe, Baibulo limafotokoza kuti: “Pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.” (Yakobo 3:14-16) Motero Satana wabera munthu chimwemwe ndi mtendere wake wa maganizo.
Chipambano Popanda Mpikisano
Mosiyana ndi chisonkhezero cha Satana, Baibulo limapereka zitsanzo za chipambano popanda mpikisano. Choposa ndichija cha Yesu Kristu. Ngakhale kuti anali ndi maonekedwe a Mulungu, sanaganize za kukhala wolingana ndi Mulungu koma anatenga maonekedwe a kapolo nadza kudziko lapansi. Kuposa zimenezo, iye anadzichepetsa nakhala womvera kufikira imfa ya pamtengo wozunzirapo. Mkhalidwe wamaganizo wakumvera umenewu, wopanda mzimu uliwonse wampikisano, unamchititsa kupeza chiyanjo cha Mulungu. “Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse.” (Afilipi 2:5-9) Kodi nchipambano chachikulu chiti choposa chimenecho chimene cholengedwa china chilichonse chingapeze? Anakondweretsa Atate wake kufikira kumlingo umene palibe cholengedwa china chingaufikire, ndipo anachita zimenezi popanda mzimu uliwonse wampikisano.—Miyambo 27:11.
Angelo okhulupirika ambirimbiri kumwamba amasonyeza mkhalidwe wamaganizo umodzimodziwo. Ngakhale kuti Yesu, amene anali mkulu wa angelo, anakhala wochepa pang’ono kwa iwo pamene anadza kudziko lapansi, iwo mofunitsitsa anatumikira zosoŵa zake. Mwachionekere, iwo analibe lingaliro lililonse la kugwiritsira ntchito mkhalidwewo kuyesa kumlanda malo monga Mngelo Wamkulu.—Mateyu 4:11; 1 Atesalonika 4:16; Ahebri 2:7.
Kunyansidwa kwawo ndi mkhalidwe wampikisano kumaoneka bwino koposerapo pamene tilingalira njira imene alabadirira chifuno cha Mulungu cha kukweza anthu ena opanda ungwiro kuwapatsa moyo wauzimu wosafa, mkhalidwe umene ‘adzaweruziramo angelo.’ (1 Akorinto 6:3) Angelo ali ndi nkhokwe ya chidziŵitso m’kutumikira Yehova ndipo ali ndi kukhoza kwakukulu kwa kuchita chabwino kuposa anthu opanda ungwiro. Komabe, angelo mokondwa amatumikira odzozedwa padziko lapansi, popanda konse kusirira zimene iwowa adzalandira. (Ahebri 1:14) Mkhalidwe wawo wabwino wamaganizo, wa kusapikisana umawakhozetsa kupitiriza kutumikira patsogolo pa mpando wachifumu wa Mfumu Ambuye Yehova.
Ndiyeno, talingalirani za atumiki akale okhulupirika a Mulungu amene adzaukitsidwa padziko lapansi. Abrahamu anali chitsanzo chapadera cha chikhulupiriro ndipo anatchedwa “kholo la onse akukhulupira.” (Aroma 4:9, 11) Yobu anapereka chitsanzo chopambana cha chipiriro. (Yakobo 5:11) Mose, “wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi,” anatsogolera mtundu wa Israyeli ku ufulu. (Numeri 12:3) Kodi ndani mwa anthu opanda ungwiro amene wapereka chitsanzo chabwinopo cha chikhulupiriro, chipiriro, ndi chifatso kuposa amuna ameneŵa? Komabe, iwo ali mumzera wa kudzalandira gawo la padziko lapansi la Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 25:34; Ahebri 11:13-16) Iwo, mofanana ndi Yohane Mbatizi, adzaikidwa pansi pa “amene ali wochepa mu Ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 11:11) Kodi iwo adzaganiza nkomwe za kunyinyirika, akumaumirira kuti chikhulupiriro, chipiriro, kapena chifatso chawo chinalingana kapena nthaŵi zina kuposa chija cha awo opatsidwa moyo kumwamba? Motsimikizirikadi ayi! Iwo adzakhala nzika za padziko lapansi zachimwemwe za Ufumu wa Mulungu.
Lerolinonso, anthu opanda mkhalidwe wamaganizo wampikisano ngabwino kukhala nawo. Yasuo, wotchulidwa m’nkhani yoyamba, analoŵa m’ngongole zowopsa chifukwa cholingalira kupeza phindu m’malonda a golide ndipo anatayikiridwa ndi chuma chake chonse. “Mabwenzi” ake anamnyanyala. Popeza kuti mkazi wake anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anapita kumisonkhano yawo chifukwa cha kudzimva waliŵongo kaamba ka kuvutika kumene anadzetsera banja lake. M’kupita kwa nthaŵi, anadzichotsera mzimu wampikisano nakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Tsopano ali wokondwa kukhala ndi mabwenzi Achikristu, omwe ali ofunitsitsa kumthandiza m’nthaŵi ya mavuto.
Mmene Tingasungire Mtendere wa Maganizo
Nthaŵi zina nkovuta kusunga mtendere wa maganizo m’chitaganya champikisano, chopanda chifundo. Tingachite mwanzeru kuzindikira kuti Baibulo limatsutsa “madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru” kukhala “ntchito zathupi” zimene zimaletsa anthu kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Ntchito zonsezi zimagwirizana kwambiri ndi mzimu wampikisano. Nchifukwa chake mtumwi Paulo analimbikitsa Agalatiya kuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.”—Agalatiya 5:19-21, 26.
M’nkhani imeneyi, kalata ya Paulo inasonyeza mfungulo yolakira mpikisano wakudzikuza. Iye anati: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.” (Agalatiya 5:22, 23) Zipatso za mzimu zimatithandiza kuchotsa mpikisano m’maganizo mwathu. Mwachitsanzo, talingalirani mkhalidwe wa chikondi. “Chikondi sichidukidwa,” akufotokoza motero Paulo. “Sichidziŵa kudzitamandira, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” (1 Akorinto 13:4-7) Mwa kukulitsa chikondi, tingachotse kaduka, mphamvu yosonkhezera mzimu wampikisano. Zipatso zina za mzimu zimatithandizanso kuchotseratu m’mitima mwathu ndi maganizo kambali kalikonse kotsalira ka mzimu wampikisano wa wafawafwa watsalawatsala. Eya, mwa kudziletsa chikhoterero chilichonse cha kupikisana ndi ena kuti tipambane zivute zitani chingathetsedwe mosataya nthaŵi!—Miyambo 17:27.
Komabe, kuti tikulitse mikhalidwe imeneyi, tiyenera kulola mzimu wa Mulungu kugwira ntchito mwa ife. Tingachirikize kugwira ntchito kwabwino kumeneku kwa mzimu woyera mwa kulimbikira kupemphera ndi kupempha mzimu wa Mulungu kutithandiza. (Luka 11:13) Poyankha pemphero lathu, kodi nchiyani chimene Mulungu adzatipatsa? Baibulo limayankha kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
Zimenezi zinali zachionekere kwa atumwi a Yesu. Ngakhale pambuyo pakuti Yesu anayambitsa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pausiku wake womalizira ndi atumwi ake, iwo anali kutsutsanabe ponena za amene anali wamkulu koposa pakati pawo. (Luka 22:24-27) Panthaŵi zosiyanasiyana Yesu anayesa kuwathandiza kuwongolera kalingaliridwe kawo, koma mkhalidwe wamaganizo wopikisana umenewu unali ndi mizu yakuya mwa iwo. (Marko 9:34-37; 10:35-45; Yohane 13:12-17) Komabe, atalandira mzimu woyera pambuyo pa masiku pafupifupi 50 kuyambira pamkangano umenewo, mkhalidwe wawo wamaganizo unasintha. Panalibe mkangano wakuti ndani akawaimira polankhula kwa khamu la anthu ochita chidwi losonkhana patsiku la Pentekoste limenelo.—Machitidwe 2:14-21.
Palibe munthu analoledwa kulamulira mpingo Wachikristu. Pamene anafunikira kuthetsa vuto la mdulidwe, Yakobo, amene sanali nkomwe wophunzira panthaŵi ya imfa ya Yesu, anali tcheyamani pamsonkhano wofunika umenewo. Palibe umboni wakuti panali mkangano wonena za amene akatsogolera pamsonkhano umenewo wa bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu. Zinthu zinasintha chotani nanga kuchokera panthaŵi imene atumwiwo anali odetsedwa ndi mzimu wampikisano! Mothandizidwa ndi mzimu woyera, anakumbukira ziphunzitso za Yesu nayamba kuzindikira tanthauzo la maphunziro ake.—Yohane 14:26.
Ndimmenenso zingakhalire ndi ife. Mothandizidwa ndi mzimu woyera, tikhoza kulaka chikhoterero chilichonse chotsalira cha kupikisana ndi ena kuti tipite patsogolo mwa kuwalima pamsana. Mmalomwake, tingapeze mtendere wa maganizo wakupambana chidziŵitso chonse. Baibulo limatitsimikizira kuti magwero a mpikisano wa wafawafa watsalawatsala, Satana Mdyerekezi, posachedwapa adzaponyedwa m’phompho, kusiyitsidwa kugwira ntchito. (Chivumbulutso 20:1-3) Mpikisano pakati pa anansi sudzakhalakonso. Kodi padzakhala chitaganya chopanda kupita patsogolo kulikonse? Kutalitali! Anthu adzafikira ungwiro, osati mwa kupikisana kulikonse pakati pawo, koma mwa kugwiritsiridwa ntchito kwa nsembe yadipo ya Yesu pa iwo.—1 Yohane 2:1, 2.
Keinosuke, wotchulidwa poyamba, amene kale anali ndi ulemerero wa chipambano cha dziko mwa kugulitsa magalimoto ochuluka koposa wina aliyense, anadzitopetsa ponse paŵiri mwamaganizo ndi mwakuthupi, koma pomalizira pake anasiya ntchito yake. “Tsopano, moyo wanga ngwodzala ndi chimwemwe chenicheni,” iye akutero. Anafikira pakuzindikira chifukwa chimene moyo wa Yesu unalili wachipambano chenicheni. Tsopano amapeza mpumulo m’chilichonse chimene angachite mumpingo wa padziko lonse wa Mulungu. Motero akukonzekeretsedwera dziko latsopano, limene lidzakhala lopanda mpikisano. Nanunso mungalaŵe chitaganya cha dziko latsopano chimenechi mwa kupita ku imodzi ya Nyumba Zaufumu m’dera lanu ndi kuyanjana ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 7]
Chitaganya cha anthu chidzakhala pamtendere ndi kugwirizana m’dziko latsopano la Mulungu