Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 3/1 tsamba 24-28
  • “Dzanja la Yehova” M’moyo Wanga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Dzanja la Yehova” M’moyo Wanga
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yolalikira Yoyambirira
  • Ntchito Yathu Iletsedwa m’Canada
  • Mbali Zambiri za Utumiki Wanthaŵi Yonse
  • Kulera Ana Athu m’Brazil
  • Kubwerera ku Canada
  • Ndadalitsidwa Moyo Wanga Wonse Chifukwa Chosankha Bwino Zochita
    Nsanja ya Olonda—2007
  • ‘Zingwe Zoyesera Zandigwera Mondikomera’
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kutumikira Yehova Monga Banja Logwirizana
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mulungu Anatisonyeza Kukoma Mtima Kwakukulu M’njira Zambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 3/1 tsamba 24-28

“Dzanja la Yehova” M’moyo Wanga

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI LAWRENCE THOMPSON

USIKU wina mu 1946, ine ndi bambo wanga tinakhala m’galimoto tikumayang’ana cheza choŵala choonekera kuchigawo chakumpoto cha dziko chikung’anima m’mlengalenga. Tinalankhula za ukulu wa Yehova ndi kuchepa kwathu. Tinakumbutsana zochitika za m’zaka zimene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa m’Canada. Atate anamveketsa bwino kwa ine mmene Yehova anachirikizira ndi kutsogoza anthu Ake m’zaka zimenezo.

NGAKHALE kuti ndinali ndi zaka 13 zokha, ndinazindikira kuwona kwa zimene Atate anali kunena. Anamveketsanso kwa ine kufulumira ndi ukulu wa ntchito yolalikira imene inayenera kuchitidwa. Atate anagwira mawu Numeri 11:23 nagogomezera kwa ine kuti, ndithudi, dzanja la Yehova silinafupike. Kusoŵa chikhulupiriro kwathu kokha ndi chidaliro mwa iye ndiko kumachepetsa zimene iye angatichitire. Kunali kukambitsirana kwa atate ndi mwana kwabwino koposa, kumene sindidzaiŵala konse.

Kuphunzira zofalitsa za Watch Tower, makamaka buku la Salvation, lotulutsidwa mu 1939, kunayambukiranso kwambiri moyo wanga wachichepere. Sindidzaiŵala konse fanizo lake lozizwitsa patsamba loyamba: “Sitima yothamanga kwambiri, yodzaza ndi anthu, inali kuthamanga paliŵiro la [makilomita 160] pa ola. Inayenera kuoloka mtsinje pamlatho umene unali wokhota [kwambiri] kwakuti anthu amene anakwera kumbuyo kwa sitimayo anali kuona injini . . . Anthu aŵiri amene anakwera kumbuyo kwa sitimayo . . . anaona kuti mbali yakumapeto kwenikweni ya mlathowo inali kupsa ndi kumagwera m’mtsinjemo. Iwo anazindikira kuti anali pangozi yaikulu. Inali ngozi yeniyenidi. Kodi sitimayo ikanaimitsidwa panthaŵi yabwino kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri amene anakweramo?”

Likumagwiritsira ntchito fanizo limeneli, bukulo linati: “Mofananamo lerolino, mitundu yonse ndi anthu apadziko lapansi akuyang’anizana mwachindunji ndi ngozi yaikulu koposa. Iwo akuchenjezedwa monga momwe Mulungu akulamulira, kuti tsoka la Armagedo lili patsogolopa. . . . Pokhala atachenjezedwa, aliyense wochenjezedwa ayenera kusankha tsopano njira imene adzatenga.”

Sitima yaliŵiroyo, mlatho womapsawo, ndi kufulumira kwa ntchito yolalikira zinazika mizu kwambiri m’maganizo mwanga.

Ntchito Yolalikira Yoyambirira

Ndinayamba kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira mu 1938, pamene ndinali ndi zaka zisanu. Henry ndi Alice Tweed, apainiya aŵiri (atumiki a nthaŵi yonse), ankanditenga kupita nawo, ndipo tinkathera maola 10 mpaka 12 patsiku tikumalankhula ndi anthu. Ndinasangalala kwambiri ndi masiku athunthu amenewo otheredwa muutumiki wa Yehova. Chotero ndinakondwera chaka chotsatira pamene Atate ndi Amayi anandilola kukhala wofalitsa ndi kuperekadi lipoti la ntchito yanga.

M’masiku akale amenewo, tinali kuchita maperete ofalitsa mawu, tikumayenda m’khwalala lalikulu la matauni titavala zikwangwani zokhala ndi mawu amene anavumbula chipembedzo chonyenga ndi kufalitsa Ufumu wa Mulungu. Tinagwiritsiranso ntchito magalamafoni okhoza kunyamulidwa ndi kupereka mauthenga a Baibulo pakhomo penipeni pa eninyumba. Tinkapereka mauthenga a J. F. Rutherford, prezidenti wa Watch Tower Society, ena a mauthengawo ndinawaloŵeza pamtima. Ndimakumbukirabe bwino lomwe ndikumumva akunena kuti: “Kaŵirikaŵiri kwanenedwa kuti, Chipembedzo ndimsampha ndi malonda!”

Ntchito Yathu Iletsedwa m’Canada

Mkati mwa nkhondo yadziko yachiŵiri, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’Canada, monga momwe inaletsedwera ku Nazi Germany ndi maiko ena. Chotero tinagwiritsira ntchito Baibulo lokha koma tinapitiriza ntchito yathu yolamulidwa ndi Mulungu pomvera malangizo a Baibulo. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 5:29) Tinaphunzira kuzemba apolisi pamene anali kulalira misonkhano ndi nyumba zathu. Tinazoloŵeranso kupereka umboni pamaso pa oweruza ndi kuyankha mafunso m’bwalo lamilandu.

Ineyo ndi mkulu wanga Jim tinakhala akatswiri pakuponya timabuku tili m’magalimoto oyenda kutiponyera pamakomo ndi m’makonde. Ndiponso tinali ngati amtengatenga ndipo, nthaŵi zina, monga alonda a awo amene anali kudutsa malire kupita kumisonkhano mu United States.

Nyumba yathu inali kunja kwa Port Arthur (tsopano Thunder Bay), Ontario, pamalo okwanira hekitala imodzi kapena kuposapo ozingidwa ndi mitengo ndi udzu. Tinali ndi ng’ombe yaikazi, mwana wa ng’ombe, nkhumba, ndi nkhuku​—zonsezi zinatumikira monga zinthu zabwino zobisira ntchito yathu yothandiza Akristu anzathu achichepere amene anali kusakidwa kuti awaike m’ndende chifukwa cha kulalikira Ufumu wa Mulungu.

Pofika usiku, magalimoto, malole, ndi ngolo zonyamula Akristu achichepere zinkaloŵa ndi kutuluka m’yadi yathu yokhala kwayokha. Tinkasunga m’nyumba, kubisa, kuzimbaitsa, ndi kudyetsa achichepere ameneŵa ndiyeno nkuwatumiza kumene akupita. Atate ndi amayi, limodzi ndi ogwira ntchito ena oyambirira amenewo, anali atumiki odzipereka ndi mtima wonse amene anaumba mtima wanga wachicheperewo kutumikira ndi kukonda Yehova Mulungu.

Mu August 1941, ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa m’nyanja yaing’ono m’nkhalango. Unyinji wa ife tinasonkhana kaamba ka chochitikachi usiku titayatsa nyali m’chipinda. Mwachionekere apolisi ananyumwa, ndipo anayendera usiku wonse akufunafuna ndi matochi, koma sanatipeze.

Mbali Zambiri za Utumiki Wanthaŵi Yonse

Mu 1951, ndinamaliza maphunziro a sekondale ndipo ndinayenda pafupifupi mtunda wa makilomita 1,600 kukayamba ntchito yaupainiya ku Cobourg, Ontario. Mpingo wake unali waung’ono, ndipo ndinalibe mnzanga wochita naye upainiya. Koma pokumbukira kuti dzanja la Yehova silinafupike, ndinachita lendi chipinda, ndinkaphika ndekha, ndipo ndinali wachimwemwe kutumikira Yehova. Chaka chotsatira ndinaitanidwa kukatumikira paofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu Toronto. Kumeneko ndinaphunzira maphunziro ambiri opindulitsa amene anandiyenga kaamba ka utumiki wa Ufumu wamtsogolo.

Pambuyo potumikira monga mpainiya m’Toronto kwa chaka choposa chimodzi, ine ndi Lucy Trudeau tinakwatirana, ndipo m’nyengo yachisanu ya mu 1954, tinagaŵiridwa kukatumikira monga apainiya ku Levis, Quebec. Kunja kunali kuzizira kwambiri, kusautsa kwa magulu a anthu ndi apolisi kunali kuopseza, ndipo kuphunzira Chifrench kunali kovuta. M’zonsezo dzanja la Yehova silinafupike konse, chotero ngakhale kuti panali nthaŵi zovuta, tinalinso ndi madalitso ambiri.

Mwachitsanzo, tinapemphedwa kuona ngati masitima apamadzi aŵiri (Arosa Star ndi Arosa Kulm) amene Sosaite inafuna kugwiritsira ntchito kunyamula nthumwi kupita kumisonkhano yaikulu ya mitundu yonse ku Ulaya mu 1955 anali mumkhalidwe wabwino. Pofuna kupanga malonda ndi Sosaite, akuluakulu a makampani otumiza zinthu anatichereza mwakamodzikamodzi, umene unali mpumulo wabwino kuutumiki wotsendereza m’Quebec panthaŵiyo.

M’nyengo yaphukuto ya mu 1955, ndinaitanidwa kukatumikira monga woyang’anira woyendayenda, ndipo tinathera nyengo yachisanu ya chakacho tikuchezera mipingo yakutali kumalo ozizira a kumpoto kwa Ontario. Chaka chotsatira tinaloŵa Sukulu ya Baibulo ya Watchtower ya Gileadi mu United States, ndipo pambuyo pake tinagaŵiridwa monga amishonale ku Brazil, South America.

Tinayamba kugwira ntchito m’gawo lathu latsopano ndi mtima wonse ndipo posakhalitsa tinali okhoza kulalikira ndi kuphunzitsa m’chinenero cha Chipwitikizi. Kuchiyambi kwa 1957, ndinagaŵiridwanso kugwira ntchito monga woyang’anira woyendayenda. Tsopano, mmalo mwa kuzizira kowopsa kwa Kumpoto, tinafunikira kulimbana ndi kutentha kwadzaoneni. Nthaŵi zambiri tinkaima ndi kuchotsa michenga yotentha m’nsapato zathu kapena kuthyola nzimbe kuti tidye kubwezeretsa nyonga yathu. Koma panali madalitso.

M’tauni ya Regente Feijo, ndinalankhula ndi mkulu wa apolisi, ndipo iye analamula kuti masitolo onse atsekedwe ndi kuuza aliyense kupita kumalo apakati a tauniyo. Nditaima pamthunzi wa mtengo wamaluŵa wogudira bwino, ndinapereka nkhani ya Baibulo kwa anthu onse a m’tauniyo. Lerolino kumeneko kuli mpingo wa Mboni.

Kulera Ana Athu m’Brazil

Pamene Lucy anatenga pathupi mu 1958, tinakakhala ku Juiz de Fora ndipo tinatumikira monga apainiya apadera. Mkati mwa zaka ziŵiri zotsatira, ana athu aakazi, Susan ndi Kim, anabadwa. Iwo anakhaladi dalitso lenileni muutumiki, nakhala chinthu chatsopano m’tauniyo. Pamene tinkakankha zikuku zawo m’makwalala, anthu anali kubwera kudzawaona. Popeza kuti kunali kusoŵa kwakukulu kwa ofalitsa Ufumu ku Recife, chakummwera kwa equator, tinasamukira kumalo otentha kwambiriwo.

Mu 1961, ndinali wokhoza osati kokha kuthandiza kukonza ulendo wapandege wa Mboni zopita kumsonkhano m’São Paulo koma nanenso ndinafika pamsonkhano wosaiwalikawo. Komabe, pafupifupi mphindi 20 titayamba kuuluka ndegeyo inazolika mwadzidzidzi, ikumagubuduza amene anali mkati mwake. Mkati mwa ndegemo munawonongekeratu; mipando inaguluka m’chimake, ndipo okweramo anasupuka ndipo anali kukha mwazi. Mokondweretsa, woulutsa ndegeyo anakhoza kuitembenuza, ndipo inatera bwinobwino. Palibe aliyense wa ife amene anavulala kwambiri kwakuti nkulephera kupita ku São Paulo pandege ina. Tinasangalala ndi msonkhano wabwino koposa, koma ndinanena kuti sindidzakweranso ndege!

Komabe, pamene ndinafika kunyumba kuchokera kumsonkhanoko, gawo lina linali kundiyembekezera. Ndinayenera kukasamalira msonkhano mkati mwa nkhalango ku Teresina, m’boma la Piauí. Ndinafunikira kupita pandege kumeneko. Ndi mantha angawo, ndinavomera ntchitoyo, ndikumadalira dzanja la Yehova.

Mu 1962, mwana wathu wamwamuna, Greg, anabadwira m’Recife. Ngakhale kuti sindinathenso kuchita upainiya chifukwa chakuti ndinali ndi banja lomakula tsopano, ndinali wokhoza kusonkhezera mpingo waung’onowo. Nthaŵi zonse anawo anali ofunitsitsa kupita nafe muutumiki, popeza kuti timaupanga kukhala wosangalatsa kwa iwo. Aliyense wa iwo, kuyambira pamsinkhu wazaka zitatu, anali wokhoza kupereka ulaliki pamakomo. Tinachipanga kukhala chizoloŵezi kusaphonya misonkhano kapena kukhala ndi phande muutumiki wakumunda. Ngakhale ngati mmodzi m’banjamo anadwala ndipo wina anatsala ndi wodwalayo, ena tonsefe tinapita kumsonkhano kapena kukhala ndi phande muutumiki wakumunda.

M’kupita kwa zaka, tinali kukambitsirana mokhazikika monga banja makosi akusukulu a anawo ndi zonulirapo zawo m’moyo, kuwakonzekeretsa kaamba ka ntchito m’gulu la Yehova. Tinali osamala kuti tisawasonyeze zisonkhezero zofooketsa, monga ngati wailesi yakanema. Tinalibe TV m’nyumba mwathu kufikira pamene anawo anafika zaka zapakati pa 13 ndi 19. Ndipo ngakhale kuti tinali ndi ndalama, sitinasasatitse anawo ndi zinthu zakuthupi. Mwachitsanzo, tinagula njinga imodzi yokha, yoti adzibwerekana atatuwo.

Tinachitira zinthu pamodzi monga momwe tinathera, kuseŵera basketball, kusambira, ndi kutenga banjalo kupita kokayenda. Maulendo athu anali ogwirizana ndi kukapezeka pamisonkhano Yachikristu kapena kukaona nyumba za Beteli m’maiko osiyanasiyana. Maulendo ameneŵa anatipatsa nthaŵi ya kukambitsirana momasuka kotero kuti Lucy ndi ine tidziŵe zimene zinali m’mitima ya ana athu. Tili oyamikira kwambiri kwa Yehova kaamba ka zaka zosangalatsa zimenezo!

Ndiyeno, zaka khumi zimene tinakhala m’Malo Otentha pafupi ndi equator zinali ndi chiyambukiro choipa pathanzi la Lucy. Chotero tinavomereza zosintha gawo kupita kumalo ozizirirako a kummwera, ku Curitiba, m’boma la Paraná.

Kubwerera ku Canada

Mu 1977, pambuyo pokhala m’Brazil pafupifupi zaka 20, Lucy ndi ine tinabwerera ku Canada ndi ana athu kukathandiza kusamalira bambo anga amene anali kudwala. Kunali kusiyana kwamakhalidwe kotani nanga kwa banja lathu! Koma panalibe kusiyana mwauzimu, popeza kuti tinasungabe dongosolo lathu lofananalo pamodzi ndi abale athu achikondi Achikristu.

M’Canada utumiki wanthaŵi yonse unakhala nkhani ya banja lonse pamene ana athu aakazi anasinthanasinthana kuloŵa utumiki wanthaŵi yonse waupainiya. Tonsefe tinathandizana kulipira zowonongedwa za banja lathu. Ndalama zilizonse zolandiridwa pantchito yaganyu zinaikidwa m’thumba la ndalama zogwiritsiridwa ntchito kusamalirira nyumba yathu ndi magalimoto atatu amene tinafunikira kufola gawo lathu lalikulu. Mlungu uliwonse, pamapeto paphunziro lathu la Baibulo labanja, tinali kukambitsirana za makonzedwe athu a banja. Makambitsirano ameneŵa anathandiza aliyense kudziŵa kumene tinali kupita ndi zimene tidzachita ndi miyoyo yathu.

Mwana wathu wamwamuna, Greg, mofanana ndi alongo ake aakulu, anapanganso utumiki wanthaŵi yonse kukhala chonulirapo chake. Kuyambira pamene anali ndi zaka zisanu, iye anafotokoza chikhumbo cha kugwira ntchito paofesi yanthambi ya Sosaite, yotchedwa Beteli. Sanataye konse chonulirapo chimenecho, ndipo atamaliza maphunziro asekondale, anafunsa amayi ake ndi ine kuti: “Kodi muganiza kuti ndifunsire utumiki wa pa Beteli?”

Ngakhale kuti kulola mwana wathu kuchoka kunayambukira maganizo athu, tinayankha mosazengereza kuti: “Sudzalimva konse mwamphamvu dzanja la Yehova monga momwe udzachitira ku Beteli​—paphata penipeni pagulu la Yehova.” Mkati mwa miyezi iŵiri iye anapita ku Beteli ya Canada. Mmenemo munali mu 1980, ndipo wakhala akutumikira kumeneko kuyambira nthaŵi imeneyo.

Ma 1980 anabweretsa masinthidwe ovuta atsopano kwa ine ndi Lucy. Tinabwereranso pamene tinayambira​—kukhalanso aŵiriŵiri. Panthaŵiyo Susan anali atakwatiwa ndipo anali kuchita upainiya ndi mwamuna wake, ndipo Kim ndi Greg anali kutumikira pa Beteli. Kodi tikachitanji? Funso limenelo linayankhidwa mofulumira mu 1981 pamene tinaitanidwa kutumikira m’dera Lachipwitikizi, limene linakuta mtunda wa makilomita pafupifupi 2,000 m’Canada. Tidakasangalalabe ndi ntchito yoyendayenda.

Kim anakwatiwa ndipo analoŵa sukulu ya Gileadi, ndipo tsopano akutumikira ndi mwamuna wake m’ntchito yadera m’Brazil. Susan ndi mwamuna wake adakali ku Canada, akulera ana awo aŵiri, ndipo mwamuna wa Susan akuchita upainiya. Ngakhale kuti banja lathu lasiyana mwakuthupi m’zaka zaposachedwapa chifukwa cha ntchito zathu zosiyanasiyana muutumiki wanthaŵi yonse, tidakali ogwirizana mwauzimu ndi mwamaganizo.

Ine ndi Lucy tikuyembekezera mtsogolo mwachimwemwe ndi banja lathu padziko lapansi loyeretsedwa. (2 Petro 3:13) Mofanana ndi Mose wakale, tadzionera tokha kuwona kwa yankho la funso losafunikira yankho la pa Numeri 11:23 lakuti: “Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? tsopano udzapenya ngati mawu anga adzakuchitikira kapena iyayi.” Ndithudi, palibe chimene chingaletse Yehova kudalitsa atumiki ake kaamba ka utumiki wawo wamtima wonse.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndi mkazi wanga, Lucy

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena