Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 28-30
  • Kulimbana ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulimbana ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimene Chimayambitsa Chisoni?
  • Kulimbana ndi Malingaliro Anu
  • Pitirizanibe Kuyang’ana Kutsogolo
  • Kodi Mungakatumikire Kudziko Lina?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Micronesia
    Nsanja ya Olonda—2014
  • “Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mungawolokere ku Makedoniya?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 28-30

Kulimbana ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu

YESU KRISTU analamula otsatira ake kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Kwa Akristu ambiri, kuchita ntchito imeneyo kwatanthauza kulimbana ndi mikhalidwe yovuta kumalo akutali ndi kwawo. Oyang’anira oyendayenda, akazi awo, ndi ena amasiya zinthu zambiri kwawo kaamba ka utumiki wa Mulungu. Kulakalaka kumudzi kwawo kungakhale vuto lenileni kwa Mboni za Yehova zonsezi.

Kulakalaka kumudzi kwanu kumadza pamene muyamba kukumbukira za chisungiko ndi chikondi cha m’nthaŵi yakale yokondweretsa. Zimenezi zingachititse kuvutika mtima kwakukulu kwakuti mumaona kukhala wopsinjika mtima ndi wosakhoza kupitirizabe ntchito. Kwenikweni, atagulitsa katundu wawo ndi kuyenda ulendo wodya ndalama zambiri kumka kudziko lachilendo, ena aleka zolinga zawozo ndi kubwerera kumudzi kwawo. Kulakalaka kumudzi kwawo kwawagonjetsa.

Nkhondo ya malingaliro yotero imachitika kaŵirikaŵiri munthu atangosamukira kumene kumalo ena, koma kwa ena imapitirizabe kukhalapo kwa moyo wonse. Zaka zoposa 20 atachoka kwawo, Yakobo ‘anakhumba kunyumba ya atate wake.’ (Genesis 31:30) Kodi ndani amene angayembekezere kuvutika ndi kulakalaka kumudzi kwanu? Kodi chimayambitsa malingalirowo nchiyani? Kodi ndimotani mmene munthu angalimbanire ndi malingaliro otero?

Kodi Nchiyani Chimene Chimayambitsa Chisoni?

Kulakalaka kumudzi kwanu kungathe kuyambukira aliyense. Amytis, mwana wamkazi wa mfumu ya Medi, Astyages, mwachionekere anali ndi chifukwa chabwino chokhalira wachimwemwe: chuma, kulemekezeka, nyumba yokongola. Komabe, analakalaka kwambiri kuona mapiri a kumudzi kwawo ku Media kwakuti mwamuna wake, Mfumu Nebukadinezara, anapanga minda ya maluŵa yopachikidwa ya Babulo poyesayesa kumkondweretsa.

Kulakalaka kumudzi kwanu kungakhale makamaka koyesa kwambiri pamene moyo uonekera kukhala wovuta koposa mmene unalili munthuwe usanamuke. Pamene Ayuda anakhala andende, analira kuti: “Ku mitsinje ya ku Babulo, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukila Ziyoni. Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m’dziko lachilendo?”​—Salmo 137:1, 4.

Zinthu zambiri zingayambitse kupsinjika mtima ndi kulakalaka kumudzi kwanu. Terry, amene anachoka ku Canada, akuti: “Tsiku lina chithunzithunzi cha banja lathu chinagwa m’buku. Pamene ndinachitola, malingaliro ambiri olakalaka kwathu andifikira mwadzidzidzi, ndipo ndinalira.” Chris, amene anasamuka ku England kumka kudziko lina losauka kwambiri, akuvomereza kuti: “Kungozindikira nyimbo ina yakale kapena kununkhira kwa chakudya china chozoloŵereka kunkandipangitsa kukhumba zinthu zimene ndinasiya kwathu.”​—Yerekezerani ndi Numeri 11:5.

Unansi wapafupi wabanja kaŵirikaŵiri umakhala chinthu china chochititsa malingalirowa. Roseli, wa ku Brazil tsopano wokhala m’dziko loyandikana ndi la kwawo, akunena kuti: “Ndimapsinjika mtima pamene ndilandira uthenga woipa kuchokera kwathu ndipo sindingathe kupita kumeneko kuti ndithandize. Nthaŵi zina ndimavutika kwambiri pamene sindilandira uthenga uliwonse ndipo ndimayamba kuyerekezera zinthu.” Janice anasamuka kuchokera ku North America kumka ku tauni ina yaing’ono kumalo otentha a Amazon. Iye akuti: “Ndimalakalaka kwathu pamene ndimva za mbiri yabwino yochokera kumeneko. Ndinamva mmene iwo akusangalalira pamodzi, ndipo ndimakhumba kuti bwenzi ndidakakhala nawo.”

Kusiyana ndi anthu akwanu sindicho chochititsa chokha cha kulakalaka kumudzi kwanu. Linda akufotokoza kuti: “Ndinkakhumudwa kwambiri pamene ndinali wosadziŵa kokagula zinthu zimene ndinafuna. Sindinadziŵe mitengo yake kapena kusinthanitsa zinthu. Magalimoto anali okwera mtengo kwambiri, ndipo nthaŵi zonse ndinali kumangogundanagundana ndi anthu polimbanira kukwera zoyendera za anthu onse. Zimenezi zinangondipangitsadi kukhumba kwathu.” Pothirira ndemanga pa miyambo ndi kusiyana kwa zachuma, Janet akunena kuti: “Umphaŵi ndiwo umene unandinyansa. Ndinali ndisanaonepo anthu akupempha chakudya, kapena mabanja aakulu, onsewo okhala m’chipinda chimodzi chopanda madzi. . . . Zinthu zotero zinandinyansa kwambiri kwakuti ndinalingalira kuti sindingakhoze kupitirizabe kukhala kumeneko.”

Kulimbana ndi Malingaliro Anu

Sitiyenera kuchita manyazi ponena za kukhala ndi malingaliro amphamvu mumtima a anthu amene timakonda kapena a zinthu zotizinga za m’zaka zathu pamene tinali kukula. Yehova Mulungu anatipatsa malingaliro kotero kuti tisangalale ndi maunansi athu abwino. Oyang’anira ampingo Achikristu ku Efeso anali amuna okhwima m’maganizo. Koma kodi n’chiyani chimene chinachitika pamene kucheza nawo kwa Paulo kunali kufika kumapeto? Eya, “onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona”! (Machitidwe 20:37) Zoonadi, chochitika chimenechi sichinaphatikizepo kulakalaka kwawo. Komabe, chimatipatsa malingaliro oti tisinkhesinkhe. Kukhala ndi malingaliro otero n’kwachibadwa, koma sitiyenera kuwalola kutilamulira. Nangano, kodi ndimotani mmene mungalimbanire mwachipambano ndi kulakalaka kumudzi kwanu?

Kuphunzira kulankhula chinenero cha kumaloko ndiko mfungulo ya kukhazikika. Malingaliro a kulakalaka kumudzi kwanu angakule pamene njira yolankhulirana idodometsedwa chifukwa chakuti mukuvutika kulankhula chinenero chachilendo. Chifukwa chake, ngati n’kotheka, phunzirani kuŵerenga ndi kulankhula chinenero cha chigawocho musanasamukireko. Kapena, phunzirani chinenero mkati mwa masabata oŵerengeka oyamba mutafika. Pamenepo mpamene mumakhala ndi chisonkhezero champhamvu ndipo motero mumakhala ndi chiyembekezo chabwino kwambiri cha kuphunzira chinenerocho. Ngati mupatulira masabata ameneŵa kwakukulukulu pa kuphunzira chinenero, inu mofulumira mudzasangalala kukambitsirana ndi ena, ndipo zimenezo zingakuchepetsereni malingaliro a kulakalaka kumudzi kwanu.

Pangani mabwenzi atsopano mofulumira monga momwe mungakhozere, pakuti kumeneku kudzakuthandizani kukhala wolandiridwa. Mpingo wa Mboni za Yehova ndiwo malo abwino koposa opangira mabwenzi enieni. Yambani inuyo kutero ndipo khalani wokondweretsedwa ndi ena. Yesayesani kudziŵa mmene anakulira, banja lawo, mavuto awo, ndi zinthu zimene amakonda. Itanirani okhulupirira anzanu kunyumba kwanu. Mwakutero, mudzapezanso kuti ena adzakukondwererani.

Pakati pa anthu a Mulungu, ubwenzi ukhoza kukhala wathithithi mofanana ndi banja. Yesu anati: “Aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye m’bale wanga, ndi mlongo, ndi amayi.” (Marko 3:35) Kristu anatsimikiziranso otsatira ake kuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.” (Marko 10:29, 30) Pokhala ndi mzimu waubale wokondweretsa chotero, ife sitili tokha, ngakhale m’dziko lachilendo.

Kusunga ubwenzi ndi awo amene munasiya kumudzi kwanu kungakuthandizeninso kulimbana ndi kulakalaka kumudzi kwanu. Inu mungadabwe kupeza kuti tsopano popeza kuti munasamuka, kulankhulana ndi makalata kuli kwatanthauzo kwambiri, popeza kuti mwinamwake mudzalingalira mosamala polemba mawu anu. Padzakhala zinthu zokondweretsa zoti munene. Janet, wotchulidwa poyambirirapo, akupereka lingaliro lakuti: “Kuimba lamya yomka kumalo akutali n’kokwera mtengo, koma kutumiza tepi yojambulidwa mawu ndi positi n’kotsikirako mtengo. Kulankhulira m’makina n’kosazoloŵereka poyamba. Komabe, pamene mukambitsirana ndi munthu wina pamaikolofoni okhala pakati panu, zimakhala zosavuta ndi zokondweretsa.” Mungapemphenso kutumiziridwa uthenga patepi yojambulidwa mawu.

Shirley, amene anasamuka ku United States kumka ku Latin America zaka 25 zapitazo, akunena kuti: “Ndinalemba zokumana nazo zokondweretsa nthaŵi zonse mmalo mwa mavuto. Zimenezi zimalimbikitsa ena kupitirizabe kundilembera.” Komabe, samalani. Kulemba makalata kwambiri kungakuletseni kupanga mabwenzi atsopano. Del, amene anasamuka ku Canada kumka kudziko lina, akuti: “Peŵani kumangokhala panyumba ndi kumaganizira za kwanu ndi kuvutika maganizo pa zinthu zimene mumalakalaka. Mmalo mwake, pitani kokayenda ndi kukasangalala ndi malo anu atsopano.”

Dziŵani miyambo ya m’dziko lachilendolo, mbiri yake, zoseketsa, ndi malo osangalatsa ndi okongola. Zimenezi zidzakuthandizani kupeŵa kuganizira zinthu zosakondweretsa. Ndipo ngati mukulinganiza za kukhala komwe mwasamukira, ndibwino kusafulumira kumka kwanu kukacheza kapena kupitako mwakaŵirikaŵiri. Kupanga mabwenzi atsopano ndi kuzoloŵera malo atsopano kumatenga nthaŵi. Kumka kwanu kukacheza kwanthaŵi yaitali kumasokoneza kusamukako. Pamene mwakhazikika, mungasangalale kumka kwanu kukangocheza​—ndiyeno kubwereranso. Izi zidakali choncho, dzitangwanitseni ndi zokondweretsa za m’malo anu atsopanowo.

Pitirizanibe Kuyang’ana Kutsogolo

Yehova anatipatsa dziko lapansi lonseli kukhala kwathu. (Salmo 115:16) Pokhala ndi mzimu wachisangalalo Wachikristu, moyo ukhoza kukhala wosangalatsa m’dziko lililonse. Ngati musamuka chifukwa cha kuchirikiza zinthu Zaufumu ndi kulalikira mbiri yabwino m’dziko lina kapena kwina kulikonse m’dera la kwanuko, chitani zimenezo ndi chiyembekezo cha chimwemwe. Yembekezerani kupanga mabwenzi atsopano, kuphunzira miyambo yosiyanasiyana, ndi kupanga ophunzira, kapena kuchita zinthu zofupa muutumiki wa Mulungu.

Yehova Mulungu ndiye Bwenzi limene nthaŵi zonse lidzakhala nanu, mosasamala kanthu za kumene muli. (Salmo 94:14; 145:14, 18) Chotero yandikirani kwa iye m’pempherero. (Aroma 12:12) Zimenezi zidzakuthandizani kukumbukira chifuno chanu m’moyo monga mtumiki wa Mulungu. Abrahamu ndi Sara anakumbukira chifuno chawo pamene anasamuka kwawo kwabinoko kumzinda wa Uri. Momvera lamulo la Yehova, iwo anasiya mabwenzi ndi anansi. (Mac. 7:2-4) Ngati akanapitirizabe kukumbukira ndi kulakalaka kumalo kumene anasamuka, akanakhala ndi mpata wa kubwerera. Koma iwo anali kukalimirira malo abwino kwambiri​—moyo padziko lapansi la paradaiso potsiriza pake pansi pa Ufumu wa Mulungu wakumwamba.​—Ahebri 11:15, 16.

Kulalikira kumalo achilendo kapena kumene kusoŵa kwa olengeza Ufumu kuli kokulirapo m’dziko lakwanu kungakhale kovuta. Komanso iko kuli ntchito yobala zipatso ndi yofupa. (Yohane 15:8) Ndipo ngati malingaliro osakondweretsa akufikirani kwakanthaŵi, akhoza kugonjetsedwa mwa kukumbukirabe chonulirapo chanu ndi kuyang’ana kutsogolo. Mlongo wina mmishonale wosakwatiwa anati: “Pamene ndiyamba kuchita chisoni, ndimayesa kuganiza za dziko latsopano ndi mmene mtundu wa anthu udzakhalira banja limodzi.” Malingaliro osangalatsa onga ameneŵa angakuthandizeni kusunga chisangalalo chanu ndi kusagonjera pakulakalaka kumudzi kwanu.

[Chithunzi patsamba 29]

Kulakalaka kumudzi kwanu sikuyenera kudodometsa utumiki Wachikristu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena