Kodi Mungakatumikire Kudziko Lina?
“NTHAŴI zonse ndinali kulingalira zoyamba ntchito ya umishonale. Monga munthu wosakwatira, ndinkatumikira ku Texas, mu U.S.A., kumene kunali kusoŵa kwakukulu kwa alaliki. Mkazi wanga anabwera komweko pambuyo pomangitsa ukwati wathu. Mwana wathu wamkazi atabadwa, ndinaganiza kuti, ‘Basi, zolinga zanga zonse zathera pamenepa.’ Koma Yehova amakwaniritsadi zokhumba za munthu, makamaka zikakhala zokhudza chifuno chake.”–Jesse yemwe tsopano akutumikira ku Ecuador limodzi ndi mkazi wake ndi ana ake atatu.
“Sindinkadziŵa kuti ndingachite zimenezo popanda kukaphunzira ku sukulu ya amishonale ya Gileadi. Ndikaona mmodzi mwa amene ndimaphunzira nawo Baibulo akupereka nkhani kapena akulalikira, ndinkasangalala kwambiri, ndipo ndinkathokoza Yehova pondipatsa mwayi umenewu.”—Karen, mkazi wosakwatiwa yemwe anachita upainiya kwa zaka zisanu ndi zitatu ku South America.
“Nditagwira ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse kwa zaka 13 ku United States, ineyo ndi mkazi wanga tinali ofunitsitsa kuyamba utumiki watsopano. Tili okondwa zedi kuposa ndi kale lonse; ili njira yabwinodi ya moyo.”–Tom, yemwe akutumikira monga mpainiya limodzi ndi mkazi wake, Linda, kudera la Amazon.
Mawu oyamikira ameneŵa ndi a anthu omwe mikhalidwe yawo sinaŵalole kukapanga nawo maphunziro aumishonale ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Komabe, apeza chimwemwe chachikulu komanso akumana ndi zothetsa nzeru za kutumikira m’mayiko ena. Kodi zimenezo zinatheka motani? Kodi inuyo mungachitenso utumiki wonga umenewo?
Pafunika Zolinga Zabwino
Kuti utumiki wa kudziko lina ukhale wopambana, pafunika zoposa kungokomedwa chabe. Awo amene alimbikirabe ntchitoyo, atero chifukwa chakuti anali ndi zolinga zabwino. Monga mtumwi Paulo, iwo adzilingalira kukhala amangaŵa, osati kwa Mulungu kokha komanso kwa anthu. (Aroma 1:14) Kunali kotheka kukwaniritsa lamulo laumulungu lolalikira mwa kuchitira utumikiwo m’dera lakwawo. (Mateyu 24:14) Koma m’malo mwake iwo anadzimva kukhala amangaŵa ndipo anakakamizika kukafunafuna ndi kukathandiza omwe analibe mwayi wakumva uthenga wabwino.
Chikhumbo chofuna kukagwira ntchito m’gawo lobala zipatso zambiri kaŵirikaŵiri chimakhala chosonkhezera china ndipo n’choyenerera zedi. Ndani wa ife yemwe poona msodzi wina akupha nsomba zambiri sadzapita mbali imeneyo ya dziŵe? Mofananamo, malipoti olimbikitsa a kupita patsogolo kochititsa kaso m’mayiko ena, kwalimbikitsa ambiri kupita komwe kuli “unyinji waukulu wa nsomba.”—Luka 5:4-10.
Ŵerengerani Mtengo Wake
Mayiko ambiri salola antchito za chipembedzo odzifunira ochokera kumayiko ena kugwiranso ntchito yolembedwa m’dzikomo. Choncho omwe akufuna kukatumikira kudziko lina kaŵirikaŵiri ayenera kukhala omwe angakhoze kupeza okha ndalama. Kodi ena achitanji pofuna kuthana ndi vuto la zachuma limeneli? Ambiri agulitsa kapena kuchititsa lendi nyumba zawo kuti apeze ndalama zokwanira. Ena agulitsa mabizinesi awo. Enanso angosunga ndalama kaamba ka cholinga chawocho. Komabe ena amatumikira m’dziko lina kwa chaka chimodzi kapena zaka ziŵiri, ndiyeno n’kubwerera kudziko lakwawo kukagwira ntchito ndi kupeza ndalama, ndipo kenako n’kubwereranso kukapitiriza kutumikira.
Phindu lachidziŵikire lokhala m’dziko lomwe likutukuka kumene n’lakuti kaŵirikaŵiri zinthu sizikhala zokwera mtengo monkitsa poyerekeza ndi m’mayiko otukuka kwambiri. Zimenezi zatheketsa ena amene amadalira ndalama zochepa za penshoni kukhala bwinobwino. Zoona, ndalama zimene munthu amawononga kwakukulukulu zimadalira pa kakhalidwe kamene iye wasankha. Ngakhale m’mayiko omwe akutukuka kumene, nyumba mbambande zimapezeka koma zimakhala zodula kwambiri.
M’posakayikitsa kuti muyenera kuŵerengera ndalama zomwe zingafunike musanachitepo chilichonse. Komabe, pamachitika zambiri zoposa kungoŵerengera ndalama. Mwinatu ndemanga za ena omwe atumikirapo ku South America zingakhale zothandiza.
Vuto Lalikulu
Markku, wochokera ku Finland, pokumbukira anati: “Kuphunzira chinenero cha Chisipanya kunali nkhondo yeniyeni kwa ine. Ndinkaganiza kuti poti chinenerocho sindikuchidziŵa, papita nthaŵi yaitali kuti ndiyambe kutumikira monga mtumiki wotumikira. Koma ndinadabwa kwabasi pamene anandipempha kuchititsa phunziro la buku patangotha miyezi iŵiri yokha! Inde, panachitika zambiri zomwe zinandichititsa manyazi. Ndinkavutika kwambiri potchula mayina. Tsiku lina ndinaitana Mbale Sancho kuti ‘Mbale Chancho (nkhumba),’ ndiponso sindidzaiŵala pamene ndinaitana Mlongo Salamea kuti ‘Malasea (woipa).’ Ubwino wake, abale ndi alongowo anali oleza mtima.” Pomalizira pake, Markku anatumikira kwa zaka zisanu ndi zitatu monga woyang’anira dera limodzi ndi mkazi wake, Celine.
Chris, mkazi wake wa Jesse yemwe tam’tchula poyamba uja akulongosola kuti: “Ndikukumbukira pamene woyang’anira dera anadzatichezera kwa nthaŵi yoyamba, titakhala kuno kwa miyezi itatu yokha. Ndinkadziŵa bwino lomwe kuti mbaleyo akugwiritsa ntchito mafanizo ndipo akunena chinachake chabwino kwambiri poyesetsa kuti atifike pamtima, koma sindinkam’mvetsa zomwe ankanenazo. Ndili m’holo momwemo, ndinagwetsa misozi. Imeneyi sinali misozi yongotsika mwakachetechete ayi; ndinkasisima. Msonkhanowo utatha, ndinayesa kufotokozera woyang’anira derayo za mkhalidwe wangawo. Anandichitira chifundo kwambiri ndipo anandiuza zomwe anthu ambiri ankandiuza kuti, ‘Ten paciencia, hermana’ (‘Lezani mtima, mlongo’). Zaka ziŵiri kapena zitatu pambuyo pake, tinakumananso ndi kulankhulana kwa mphindi 45, ndinasangalala kwambiri chifukwa chakuti tinkamvana bwinobwino.”
“Kuphunzira n’kofunika,” anatero mbale wina. “Pamene tichita khama kwambiri pophunzira chinenero, maluso athu a kulankhula amapitanso patsogolo.”
Onse amavomereza kuti kuyesetsa koteroko kumapindulitsa zedi. Kudzichepetsa, kuleza mtima, komanso khama zimakula pamene munthu akuyesetsa kuphunzira chinenero chatsopano. Khomo lalikulu la mwayi wolalikira uthenga wabwino kwa ena limatseguka. Mwachitsanzo, kuphunzira Chisipanya kungatheketse munthu kumvana ndi ena m’chinenero chomwe chimalankhulidwa ndi anthu oposa 400 miliyoni padziko lonse lapansi. Ambiri omwe anabwerera kumayiko akwawo, pambuyo pake anathanso kugwiritsa ntchito chinenero chatsopanocho pothandiza ena omwe chinenero chawo ndi Chisipanya
Bwanji Ponena za Kukhumba Kumudzi Kwanu?
“Pamene tinabwera ku Ecuador kwa nthaŵi yoyamba mu 1989, ndinkakhumba kwambiri kumudzi,” akukumbukira motero Deborah, yemwe anatumikira limodzi ndi mwamuna wake, Gary, ku dera la Amazon. “Tsopano ndaphunzira kudalira kwambiri abale ndi alongo mu mpingo. Ali ngati banja langa.”
Karen, yemwe watchulidwa poyamba uja, akuti: “Ndinalimbana ndi kulakalaka kumudzi kwathu mwa kudzitanganitsa ndi utumiki tsiku lililonse. Mwa kuchita zimenezi sindinkalota n’komwe za kumudzi. Ndimakumbukiranso bwino kuti makolo anga kumudziko akusangalala ndi ntchito yomwe ndikugwira kunoku. Mayi anga nthaŵi zonse ankandilimbikitsa ndi mawu akuti: ‘Yehova angakusamalire iwe bwino kuposa mmene ine ndingachitire.’”
Makiko, wochokera ku Japan, mwachimwemwe akuwonjezera kuti: “Pambuyo pothera tsiku lonse muutumiki wakumunda, ndimakhala wotopa zedi. Choncho, pamene ndifika kunyumba ndi kuyamba kulakalaka kumudzi, nthaŵi zambiri ndimapha tulo. Chotero, chikhumbocho chimatha mwamsanga.”
Bwanji Nanga Ponena za Ana?
Ngati pali ana, zofunika zawo zazikulu, monga maphunziro, ziyenera kulingaliridwa. Pankhani imeneyi, ena asankha kuti ana awo aziphunzirira panyumba pawo ndipo ena alembetsa ana awo m’sukulu zakomweko.
Al anasamukira ku South America limodzi ndi mkazi wake, ana ake aŵiri, ndi amayi ake. Iye akuti: “Taona kuti kupititsa ana kusukulu kwawathandiza kuphunzira chinenerocho mwamsanga. M’miyezi itatu yokha, anali okhoza kulankhula bwino lomwe.” Kumbali ina, ana aamuna aŵiri a Mike ndi Carrie amaphunzirira panyumba maphunziro omwe amaŵatumizira kuchokera kusukulu yovomerezeka. Makolowo akuti: “Tinaona kuti anaŵa sitingaŵalekere okha maphunziro ameneŵa. Kunali kofunika kuloŵererapo pakosiyo ndi kuonetsetsa kuti anyamataŵa akuphunzira zonse zomwe apatsidwa panthaŵi yake.”
David ndi Janita, ochokera ku Australia, analongosola maganizo awo pa anyamata awo aŵiri. “Tinafuna kuti anyamata athuŵa adzionere okha mmene anthu ena amakhalira. N’chapafupi kulingalira kuti aliyense akukhala m’moyo wofanana ndi omwe ife takula nawowu, koma kunena zoona n’ngochepa zedi amene amakhala m’moyo ngati wathuwu. Aonanso mmene mapulinsipulo ateokalase akugwirira ntchito padziko lonse lapansi, mosasamala kanthu za dziko kapena chikhalidwe.”
“Ndinali ndi zaka zinayi zokha pamene banja lathu linasamukira ku England mu 1969,” anakumbukira motero Ken. “Ngakhale kuti ndinakhumudwa chifukwa choti sitinakakhale m’nyumba yomata, yadenga la udzu, monga momwe ndinaganizira, ndinaona kuti anandilera bwino zedi kuyambira ubwana wanga. Ana ena amene analibe mwayi ngati umenewu ndinawamvera chisoni nthaŵi zonse! Chifukwa chogwirizana kwambiri ndi amishonale komanso apainiya apadera, ndinayamba upainiya wothandiza ndili ndi zaka zisanu ndi zinayi.” Tsopano Ken ndi woyang’anira woyendayenda.
Gabriella, mwana wamkazi wa Jesse, akuvomereza kuti: “Ecuador n’kwathudi tsopano. Ndili wokondwa kwambiri kuti makolo anga anaganiza zobwera kuno.”
Komabe, panali ana ena omwe sanathe kukhala kumalo achilendo kaamba ka zifukwa zina, ndipo mabanja awo anaumirizika kubwerera kudziko lawo. N’chifukwa chake kuli koyenera kupita kukaona dziko linalo choyamba musanasamukire kumeneko. Izi zidzathandiza kuti chosankha chanu chichitike pa maziko a zinthu zomwe mwakadzionera nokha.
Madalitso a Kusamuka
Ndithudi, kusamukira kudziko lina kumaphatikizapo kukumana ndi zothodwetsa, komanso kudzimana. Kodi omwe asamuka asonyeza kuti zikuwapindulira? Aloleni atiuze okha.
Jesse: “M’zaka khumi zomwe takhala m’mzinda wa Ambato, taona chiŵerengero cha mipingo chikukwera kuchokera pa iŵiri kufika pa mipingo 11. Tinali ndi mwayi woyambitsa nawo isanu ya mipingo imeneyo, ndipo tathandiza nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ziŵiri. Tinalinso achimwemwe pothandiza avareji ya ophunzira Baibulo aŵiri pachaka kuti afike pa kubatizidwa. Ndimanong’oneza bondo chifukwa cha chinthu chimodzi chokha—posabwera kuno zaka makumi aŵiri zapitazo.”
Linda: “Kuyamikira kumene anthu amasonyeza chifukwa cha uthenga wabwino ndi khama lomwe tili nalo, kumatilimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, m’tauni ina yomwe ili m’katikati mwa nkhalango, wophunzira Baibulo wina wotchedwa Alfonso anazindikira mmene kukanakhalira kopindulitsa kukamba nkhani zapoyera m’dera lakwawolo. Anali atangosamukira kumene m’nyumba yake yatsopano yamatabwa, imodzi mwa nyumba zoŵerengeka m’mudzimo. Ataganiza kuti nyumba yoyenera Yehova m’tauni yonseyo inali yake yokhayo basi, iye anabwereranso m’kachisakasa kake ka maudzu ndi kupereka nyumba yakeyo kwa abale kuti igwiritsidwe ntchito ngati Nyumba ya Ufumu.”
Jim: “Nthaŵi yomwe timathera tikulankhula ndi anthu muutumiki ndi yoŵirikiza nthaŵi khumi kuposa mu United States. Kuwonjezanso pamenepa, kuno moyo n’ngofeŵa kwabasi. Mosakayikira umakhala ndi nthaŵi yokwanira yochitira phunziro ndi kupita muutumiki wakumunda.”
Sandra: “Kuona mmene choonadi cha Baibulo chikusinthira anthu kukhala abwino, kumandikhutiritsa kwambiri. Panthaŵi ina ndinkaphunzira Baibulo ndi Amada wa zaka 69, yemwe anali ndi sitolo yaing’ono. Nthaŵi zambiri mayiyu ankawonjezamo madzi pang’ono mu mkaka womwe ankagulitsa. Amachitanso chinyengo china kwa makasitomala ake poŵagulitsa mkaka wosungunulawo pamlingo wosadzaza bwinobwino. Koma ataphunzira nkhani ya pamutu waung’ono wakuti ‘Kuona Mtima Kumapatsa Chimwemwe’ mu chaputala 13 cha buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, Amada analeka mchitidwe woipawu. Pambuyo pake, ndinali wosangalala kwabasi kumuona akubatizidwa!”
Karen: “Sindinkadalira kwambiri Yehova kapena kugwiritsidwa ntchito ndi iye monga momwe ndachitira kuno. Ubwenzi wanga ndi Yehova wazama ndiponso walimba kwambiri.”
Bwanji Nanga Inuyo?
M’zaka zambiri zapitazo, mazanamazana a Mboni apita kukatumikira kumayiko ena. Ena amakakhalako chaka chimodzi kapena ziŵiri, ndipo ena amakakhazikika komweko. Amapita ndi zokumana nazo, uchikulire wauzimu, ndiponso njira zopezera ndalama, ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’dziko linalo. Akhoza kutumikira m’dera lomwe ofalitsa Ufumu a kuderalo sakutha kutumikira chifukwa cha kusoŵa kwa ntchito yakuthupi. Ambiri agula galimoto zamphamvu kuti athe kukafika ku zigawo zina zomwe galimoto zina sizingathe kukafikako. Ena omwe akonda kukhala m’mizinda, athandiza kwambiri kulimbikitsa mipingo ikuluikulu yomwe ili ndi akulu oŵerengeka. Komabe, onseŵa akunena motsimikizira kuti alandira madalitso auzimu ambiri kuposa omwe apereka.
Kodi mungakonde kupeza nawo mwayi wokatumikira kudziko lina? Ngati mikhalidwe ikukulolani, bwanji osafufuza mmene mungachitire zimenezo? Mbali yoyamba ndi yofunika zedi ingakhale yolembera kalata ofesi ya nthambi ya Sosaite ya dziko lomwe mukuganiza kuti mungakatumikireko. Chidziŵitso chachindunji chomwe mungalandire chidzakuthandizani kulingalira ngati zingathekedi kwa inu. Komanso, malingaliro ambiri othandiza angapezeke mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1988, m’nkhani yakuti “Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako.” Mutakonzekera bwino komanso ndi madalitso a Yehova, mwina nanunso mungakhale achimwemwe potumikira m’dziko lina.
[Chithunzi patsamba 24]
TOM NDI LINDA M’MSEWU WA KUMIDZI, AKULOWERA KUMUDZI WA AMWENYE A MTUNDU WA SHUAR
[Chithunzi patsamba 25]
AMBIRI AKUTUMIKIRA KU QUITO, LIKULU LA DZIKO LA ECUADOR
[Chithunzi patsamba 25]
MAKIKO AKULALIKIRA M’MAPIRI A ANDES
[Chithunzi patsamba 26]
BANJA LA A HILBIG LAKHALA LIKUTUMIKIRA KU ECUADOR KWA ZAKA ZISANU ZAPITAZI