Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/11 tsamba 4-6
  • Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungawolokere ku Makedoniya?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mungakatumikire Kudziko Lina?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Ndisamukire Kudziko lina?
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 8/11 tsamba 4-6

Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?

1 Mtumwi Paulo anaona masomphenya ali mumzinda wa Tolowa, womwe uli m’mphepete mwa nyanja ku Asia Minor. Munthu wina wa ku Makedoniya anamupempha kuti: “Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.” Paulo atangoona masomphenyawa, iye ndi anzake omwe ankayenda nawo ‘anatsimikiza kuti Mulungu wawaitana kuti akalengeze uthenga wabwino’ kwa anthu a ku Makedoniya. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Lidiya ndi anthu am’banja lake omwe ankakhala ku Filipi, mzinda waukulu kwambiri ku Makedoniya, anakhala okhulupirira. Ndipo anthu enanso a m’chigawo cha ufumu wa Roma cha Makedoniya anakhalanso okhulupirira.—Mac. 16:9-15.

2 Masiku ano, Mboni za Yehova zimasonyezanso mtima wodzipereka ngati umenewu. Ambiri asamukira kumadera kumene kukufunika olengeza Ufumu ambiri ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito ndalama zawo. Mwachitsanzo, Lisa ankafuna kuti utumiki ukhale chinthu choyamba pa moyo wake. Choncho iye anasamuka ku Canada n’kupita ku Kenya. Trevor ndi Emily omwenso kwawo ndi ku Canada, anasamukira kuno ku Malawi n’cholinga chakuti azichita zambiri mu utumiki. Paul ndi Maggie a ku England, atapuma pa ntchito, anapezerapo mwayi wochita zambiri potumikira Yehova ndipo anasamukira ku East Africa. Kodi inunso muli ndi mtima wodzipereka ngati umenewu? Kodi munaganizirapo zosamuka ngati mmene anthu amenewa anachitira? Ngati ndi choncho, kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti ndiponso malangizo ati amene angakuthandizeni?

3 Dzifufuzeni: Choyamba muyenera kuganizira zolinga zanu. Yesu ananena kuti lamulo lalikulu koposa ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” Tiyenera kukatumikira kudera lina chifukwa chokonda Mulungu ndiponso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwira nawo ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira. Yesu anatinso: “Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” Munthu amasonyeza kuti amakonda anzake ngati ali ndi mtima wofunitsitsa kuwathandiza. (Mat. 22:36-39; 28:19, 20) Nthawi zambiri kutumikira m’dziko lina si ntchito yamasewera ayi ndipo imafuna mtima wodzipereka. Sikuti umangokhala ulendo wokasangalala ngati kuti mwangopita kutchuthi. Chikondi n’chimene chiyenera kukuchititsani kusamuka. Remco ndi Suzanne amene anachokera ku Netherlands, ndipo tsopano akutumikira ku Namibia, anafotokoza mfundo imeneyi ndi mawu akuti: “Chikondi n’chimene chimatichititsa kuti tizikhalabe kuno.”

4 Willie yemwe ndi woyang’anira dera ku Namibia, anati: “Anthu ochokera m’mayiko ena amene atumikira kuno kwa nthawi yaitali sanabwere ndi maganizo akuti abale adzawasamalira. Anabwera ndi cholinga chodzatumikira ndi abale ndiponso kuwathandiza abalewo pa ntchito yolalikira.”

5 Pambuyo pofufuza bwinobwino zolinga zanu, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi maluso otani a utumiki amene ndili nawo omwe angakhale othandiza m’dera lina? Kodi ndimalalikira mogwira mtima? Kodi ndimadziwa zinenero ziti? Kodi ndine wokonzeka kuphunzira chinenero chatsopano?’ Muyenera kukambirana bwinobwino nkhaniyi ndi anthu am’banja lanu. Mukambiranenso ndi akulu a mumpingo wanu. Ndipo musalephere kupempherera nkhaniyi kwa Yehova. Kudzifufuza mwa njira imeneyi kudzakuthandizani kuona ngati mungakwanitse komanso ngati mulidi ndi mtima wofuna kukatumikira kudziko lina.—Onani bokosi lakuti “Dzidziweni Bwino.”

6 Kodi Mungakatumikire Kuti?: Paulo anauzidwa m’masomphenya kuti apite ku Makedoniya. Masiku ano Yehova sationetsa masomphenya kuti atiuze koyenera kupita. Komabe kudzera m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndiponso mabuku ena, atumiki a Mulungu amadziwa madera ambiri amene kukufunika ofalitsa Ufumu ochuluka. Choncho yambani ndi kulemba mayina a madera oterowo. Ngati simuli wokonzeka kuphunzira chinenero china kapena ngati simungakhalitse kudziko lina, mwina mungasankhe kukatumikira kudziko limene chinenero chake chachikulu n’choti inuyo mumachidziwa kale. Kenako fufuzani nkhani zokhudza ziphaso zoyendera, mayendedwe, chitetezo, ndalama zokagwiritsa ntchito ndiponso nyengo ya kumeneko. Zingakhalenso zothandiza ngati mungakambirane ndi anthu amene anasamukira kumeneko. Pemphererani nkhani imeneyi musanasankhe zochita. Kumbukirani za Paulo ndi anzake kuti “mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asia.” Ngakhale kuti anayesetsa kuti apite ku Bituniya, “mzimu wa Yesu sunawalole.” N’chimodzimodzinso ndi inuyo. Pangafunike nthawi ndithu kuti muzindikire dera limene mungakathandizedi.—Mac. 16:6-10.

7 N’kutheka kuti mwaganizirapo zinthu zina zimene mungachite. Ngati mukuganizira zokatumikira kudera lina, lemberani kalata kunthambi. (Onani ndandanda ya mipingo imene ikufunika thandizo) M’kalatayo lembani utumiki wosiyanasiyana umene mwachitapo komanso umene mukuchita panopa. Lembaninso mafunso alionse amene mungakhale nawo okhudza mitengo ya zinthu, nyumba zimene mungakakhalemo, zipatala komanso ngati mungathe kupeza mwayi wa ntchito. Ndiyeno perekani kalata yanuyo ku komiti yautumiki ya mpingo wanu. Iwo adzalembanso kalata yawo yokuvomerezani n’kuitumiza limodzi ndi kalata yanuyo kunthambi. Mayankho amene mungalandire adzakuthandizani kudziwa kumene mungakathandizedi.

8 Willie, amene tam’tchula poyamba uja, anati: “Anthu amene zimawayendera bwino, ndi amene amakayendera kaye dzikolo n’kuona malo amene angathe kukakhalako bwinobwino. Banja lina linaona kuti silingakhale bwinobwino kudera lakumidzi. Choncho linaganiza zokakhala m’katawuni kena kumenenso kunkafunika ofalitsa Ufumu ndipo moyo wake unali wabwinoko.”

9 Mavuto Ake: N’zodziwikiratu kuti kusamuka kwanu n’kukakhala kumalo achilendo kungakhale ndi mavuto ake. Lisa, yemwe tamutchula poyamba uja, anati: “Vuto lalikulu kwambiri limakhala kusowa wocheza naye.” Kodi chimamuthandiza n’chiyani? Kugwirizana kwambiri ndi anthu a mumpingo wake watsopano. Iye anayesetsa kuti adziwe dzina la munthu aliyense. Kuti zimenezi zitheke, ankafika pamisonkhano mwamsanga ndipo ankachoka mochedwa kuti azitha kulankhula ndi abale ndi alongo. Lisa ankayendanso ndi anthu osiyanasiyana mu utumiki, kuitana anthu osiyanasiyana kunyumba kwake ndipo ankayesetsa kupanga mabwenzi atsopano. Iye anati: “Sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Yehova wandidalitsa kwambiri.”

10 Paul ndi Maggie atalera ana awo mpaka kukula, anaganiza zosamuka m’nyumba yawo imene anakhalamo kwa zaka 30. Paul anati: “Kusiya zinthu zathu zonse sikunali kovuta monga mmene tinkaganizira koma kusiyana ndi banja lathu n’komwe kunali kovuta kwambiri. Tinalira kwambiri tili mundege. Zinali zosavuta kuganiza kuti, ‘sitikwanitsa kuchita zimenezi.’ Koma tinadalira kwambiri Yehova. Kupeza mabwenzi atsopano kumathandiza kuti munthu usabwerere m’mbuyo.”

11 Greg ndi Crystal, omwe amalankhula Chingelezi, anaganiza zosamuka ku Canada kupita ku Namibia chifukwa chakuti anthu ambiri opita kusukulu m’dziko limenelo amalankhula Chingelezi. Komabe kenako iwo anaona kuti ndi bwino kuphunzira chinenero chimene anthu ambiri m’dzikolo amalankhula. Iwo anati: “Nthawi zina tinkakhumudwa. Komabe titaphunzira chinenerochi, m’pamene tinayamba kumvetsa bwino chikhalidwe chawo. Kudziwana kwambiri ndi abale akumeneko kunatithandiza kusintha kuti tizolowere malo atsopanowa.” Mtima wodzichepetsa ndiponso wofuna kuthandiza ena ngati umenewu, ungalimbikitsenso kwambiri abale a kumene mwasamukirako.

12 Madalitso a Yehova “Amalemeretsa”: Zimene Paulo anakumana nazo ku Makedoniya zinali zolimbikitsa kwambiri. Patapita zaka 10, iye analembera abale a ku Filipi kuti: “Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira za inu.”—Afil. 1:3.

13 Ndi mmenenso amamvera Trevor ndi Emily, amene anatumikirapo ku Malawi kuno asanapite ku Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Iwo anati: “Nthawi zina tinkakayikira ngati tinaganizadi bwino kusamuka kwathu, komabe tinkasangalala. Tinkakondana kwambiri ndipo tinkaona kuti Yehova akutidalitsa.”

14 N’zoona kuti si aliyense amene angathe kukatumikira kudziko lina. Kwa ena zingakhale bwino kusamukira kudera lina kumene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri m’dera lawo lomwelo. Ena angakwaniritse zolinga zawo potumikira m’mipingo ina yapafupi ndi kwawo. Chofunika kwambiri ndi kutumikira Yehova ndi mtima wonse. (Akol. 3:23) Mukatero, mawu ouziridwa awa adzakwaniritsidwa pa inu: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.”—Miy. 10:22.

15 Kuti mudziwe ngati mungathe kukatumikira m’dziko lina, dzifunseni mafunso amene ali m’bokosi patsamba 5, pempherani ndipo onani bwinobwino ngati mungakwanitsedi kusamuka. Mfundo za m’magazini a Nsanja ya Olonda a m’mbuyomu zingakuthandizeni.

[Bokosi patsamba 5]

Dzidziweni Bwino

• Kodi ndine munthu wokonda zinthu zauzimu?—“Masitepe Opezera Chimwemwe” (October 15, 1997, tsamba 6)

• Kodi ndimalalikira mogwira mtima?—“Mmene Mungapambanire mu Utumiki wa Upainiya” (May 15, 1989, tsamba 21)

• Kodi ndingakwanitse kukakhala kutali ndi anthu a m’banja langa ndiponso anzanga?—“Kulimbana ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu” (May 15, 1994, tsamba 28)

• Kodi ndingakwanitse kuphunzira chinenero china?—“Kutumikira Mumpingo wa Chinenero China” (March 15, 2006, tsamba 17)

• Kodi ndikasamuka, ndikatha kumapeza ndalama zodzisamalira?—“Kodi Ndikatumikire Kudziko Lina?” (October 15, 1999, tsamba  23)

[Bokosi patsamba 6]

Mayina a mipingo imene ikufunika thandizo

Dzina la mpingo: Dera

Chilenje Hill C-12

Chilobwe S-17

Kamkoma C-05

Libuda (Kagulu Kakutali) S-20

Likangala S-09

Mame C-01

Mkombezi N-03

Mwalasi (Kagulu Kakutali) S-07

Rombodzi River C-13

Sichi N-19

Tcharo N-01

Tsendeleke C-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena