Mmene Mungapambanire mu Utumiki wa Upainiya
KODI utumiki wa upainiya uli ntchito yanu? Ngati inu muli mpainiya, kapena mlengezi wa Ufumu wa nthaŵi zonse, mosakaikira inu muli wokondweretsedwa ndi kukhala wachipambano. Koma chipambano chimaitanira pa zoposa kokha kukhala wokhoza kuthera nthaŵi m’ntchito yopatsidwa. Munthu wachipambano ayenera kulandira kuphunzitsidwa ndipo mowumirira kukulitsa kuthekera kwake.
Ndimotani, kenaka, mmene inu mungapitirizire osati kokha monga mpainiya komanso kupanga kupita patsogolo m’ntchito yanu? Pali mafunso okulira osiyanasiyana amene inu mungawalingalire.
Kodi Uli Wolimba Chotani Unansi Wanga Ndi Mulungu?
Chimodzi cha zochititsa zofunika kwambiri m’kupambana monga mpainiya chiri kukhala ndi unansi woyandikana, ndi wolimba ndi Yehova Mulungu. Ponena za ichi, tingaphunzire phunziro kuchokera kwa wamasalmo Davide. Iye anachonderera kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chowonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wachipulumutso changa; inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”—Salmo 25:4, 5.
Davide anadalira kotheratu pa ‘Mulungu wachipulumutso chake.’ Iye anakhumba kuti Yehova amuphunzitse ndi ‘kumpangitsa iye kudziŵa njira Zake.’ Kodi simungazindikire chikhumbo chachangu cha Davide cha kukondweretsa Mulungu? Ichi chinali choposa chifuno wamba, popeza kuti Davide ananena kuti: “Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”
Koma ndimotani mmene mungasungirire unansi woyandikana woterowo ndi Yehova? Dziŵani kuti omwe angotchulidwawo ali malongosoledwe a Davide m’pemphero. Inde, kukambitsirana kupyolera m’pemphero kuli maziko enieni a unansi wabwino ndi Mulungu. Ndipo tingatenge chitonthozo m’kudziŵa kuti palibe chifuno cha kupangana nthaŵi ndi Atate wathu wakumwamba. Ife tingamufikire iye pa nthaŵi iriyonse. Monga mmene Davide ananenera kuti: “Pakuti tsiku lonse ndiitana inu.” (Salmo 86:3) Ngakhale Mwana wa Mulungu weniweni, yemwe anayenda pa dziko lapansi monga munthu wangwiro, anazindikira kuti iye sakapambana popanda thandizo la Atate wake. Yesu analankhula kwa iye m’pemphero tsiku lonse—m’mamawa, mkati mwa tsiku, ndi usiku.—Marko 1:35; Luka 11:1; 6:12.
Monga Akristu, tifunikira kutsatira chitsanzo cha Yesu ngati titi tipambane mu utumiki wathu. (Ahebri 5:7) Ponena za pemphero, mkazi Wachikristu yemwe wakhala mpainiya wachipambano kwa zaka 30 anadzilongosola iyemwini mwa njira iyi: “Ndimapeza kuti pemphero liri loyenerera kwa ine ngati nditi ndipambane monga mpainiya. Landithandiza ine kudalira kotheratu pa Yehova, kuzindikira kuti sindikakhoza kuwuchita pandekha. Ndimafunsa Yehova mosalekeza kuti andithandize ine kupitirizabe.”
Inde, kuti mupambane mu utumiki wa upainiya, inu mufunikira kusungirira unansi wolimba ndi Yehova, kudalira pa iye kotheratu kupyolera m’pemphero. Ngakhale kuli tero, lotsatirali liri funso lina lofunikira kudzifunsa inu eni.
Kodi Ndimokulira Chotani Mmene Ndimakondera Anthu?
Kuchita upainiya kuli kulongosola kwa chikondi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti utumiki wa nthaŵi zonse umaloŵetsamo mzimu wa kudzipereka nsembe. Monga mpainiya, inu mokhazikika mukupereka nthaŵi yanu ndi nyonga kuthandiza ena. Koma ngati muti mupitirize kuchita chimenechi, muyenera kukhala ndi chikondwerero chenicheni m’zosoŵa za ena. Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anasonyeza chikondi choterocho kamba ka anthu. Mwachitsanzo, panali chochitika pamene iye ndi ophunzira ake anali kupita m’bwato ku malo apadera “kupuma kamphindi.” Ngakhale kuli tero, makamuwo anafika kumeneko iwo asanatero. “Ndipo anatuluka Iye, nawona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”—Marko 6:30-34.
Mofanana ndi Yesu, monga apainiya ife tiyenera kukhala ndi chikondi chozikidwa mwakuya kaamba ka anthu. Chikondi choterocho chimatisonkhezera kudzipereka ife eni kaamba ka iwo. Monga mmene mlembi nthaŵi ina ananenera kwa Yesu kuti: “Ndipo, kumukonda Iye [Mulungu] ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsyereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.” (Marko 12:33) Mawu amenewa amatithandiza ife kuyamikira kuti sichiri kokha chomwe timachita mu utumiki wathu chomwe chiri chofunika komanso chifukwa chimene timachitira icho.
Monga mpainiya, inu mumathera nthaŵi yochulukira m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira kuposa ndi mmene ambiri ena amachitira. Koma mumakumananso ndi anthu owonjezereka. Ndimotani mmene mumadzimverera kulinga kwa iwo? Mpainiya wina ananena kuti: “Ndimadziŵa kuti chikondi chiri chipatso cha mzimu wa Mulungu. Chotero popanda icho sindikanakhala m’chowonadi mpang’ono pomwe, kusatchula kupambana monga mpainiya. Chikondi chimandipangitsa ine kukhala wodera nkhaŵa kulinga kwa anthu, kukhala wogalamuka za zosoŵa zawo, ndipo ndimayamikira kuti anthu amavomereza ku chikondi. Ndithudi, pali nthaŵi zimene chikondi chanu kaamba ka anthu chidzayesedwa chifukwa cha makhalidwe ndi maganizo awo. Makamaka pa nthaŵiyo ndi pamene ndimayesera kumvetsera ndi kukhala woleza mtima.”
Kodi mmenemo ndi mmene mumadzimverera ponena za anthu m’gawo lanu? Kuti mukhale mpainiya wachipambano, inu muyenera kukonda anthu. (1 Atesalonika 2:6-8) Kuti mukhale wokhutiritsa m’ntchito yanu ya kuchita upainiya, ngakhale kuli tero, inu mufunikiranso ndandanda yabwino. Chotero, dzifunseni inu eni:
Kodi Ndiri ndi Ndandanda Yolinganizika?
Kuti apitirize mu utumiki wa nthaŵi zonse mwachipambano, mpainiya ayenera kukhala wolinganizika bwino. Popanda ndandanda yabwino yaumwini, kuchita upainiya kungakhale kobwevutsa. Ndithudi, kukhala ndi ndandanda yomwe imalola kuthera ukulu wa nthaŵi yapadera mu utumiki wa m’munda sindicho chokha chomwe chimalowetsedwamo.
Mpainiya amafunikira ndandanda yolinganizika. Kodi inu mulinayo? Mungadzifunse inu eni kuti: Kodi ndikuthera ukulu wa nthaŵi yoyenera mu mbali zosiyanasiyana za utumiki? Kodi ndinganene kuti ndikuika kuyesayesa kulikonse kufikira anthu m’gawo? Kodi ndikupanga kuwongolera kofunikira m’ndandanda yanga kotero kuti ndidziwafikira pamene iwo ali panyumba? Kodi ndimapanga maulendo obwereza okhutiritsa? Yesu ananena kuti: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu . . . mukumawaphunzitsa.” (Mateyu 28:19, 20, NW) Ponse paŵiri kulalikira ndi kuphunzitsa ziri mbali zokulira za utumiki wathu. Kodi muli okhutiritsidwa ndi kugawira mabukhu, kapena kodi mumabwererako kwa onse omwe amasonyeza chikondwerero, kaya alandira mabukhu a Baibulo kapena ayi? Mwachidule, kodi mumapanga nthaŵi yanu kuŵerengera?
Kodi Ndine Mphunzitsi Wopita Patsogolo?
Limenelo liri funso lina lofunika. Pa 2 Timoteo 4:2, Paulo analemba kuti: “Lalikira mawu; chita nawo pa nthaŵi yake, popanda nthaŵi yake; . . . ndi kuleza mtima konse ndi [luso la kuphunzitsa, NW].” Kuti alalikire mawuwo, kaya mkati kapena kunja kwa mpingo, apainiya achipambano amakalamira kupeza ndi kuyenga luso la kuphunzitsa. Nchifukwa ninji Paulo akutcha kuphunzitsa kukhala luso? Chifukwa chakuti kuphunzitsa kumafunikira nzeru ndi kuchita.
Ndimotani mmene mudzawongolera nzeru yanu monga mphunzitsi? Mtumwi Paulo akuyankha kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15) Inde, apainiya ayenera kupereka nthaŵi ku phunziro la Baibulo laumwini, kuwunikira, ndi kusinkhasinkha. Ichi chimaphatikizapo kugwiritsira ntchito malingaliro opezedwa mu zofalitsidwa zoterozo zonga ngati Reasoning From the Scriptures, Utumiki Wathu wa Ufumu, ndi Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki.a
Chotero, kuti mupambane mu utumiki wa upainiya, sungirirani unansi wanu waumwini wolimba ndi Yehova Mulungu. Ichi, pambuyo pake, chidzakusonkhezerani inu kupeza ndi kusonyeza chikondi chozama mwakuya kaamba ka anthu. Ndithudi, kuti mulongosole chikondi chimenechi, simufunikira kokha kukhala wodera nkhaŵa za kuchulukira kwa nthaŵi imene mumathera mu utumiki, koma muyeneranso kufuna kupanga nthaŵi yanu kuŵerengera. Motani? Mwa kuika kuyesayesa kofunikira kufikira anthu ambiri kumene kuli kothekera ndi uthenga wa Ufumu. Chomalizira, pitirizanibe kukhala opita patsogolo monga mphunzitsi mwa kuphunzira njira zosiyanasiyana za kufikira anthu mu utumiki ndipo mwakhama kuphunzira Baibulo m’chiyembekezo cha kuyenga luso lanu la kuphunzitsa.
[Mawu a M’munsi]
a Zofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.