Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/1 tsamba 5-7
  • Kufunafuna Kwawo Chipembedzo Cholondola

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Kwawo Chipembedzo Cholondola
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Ena Amakayikira Kwambiri
  • Anadziŵa Choonadi Ponena za Akufa
  • Anapeza Moyo Wokhala ndi Tanthauzo
  • Mpainiya Wopanda Mantha
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • “Wodala Ndiwopeza Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Ndakhala Wokhulupirika kwa Mulungu kwa Zaka Zoposa 70
    Galamukani!—2009
  • Mmene Ena Anapezera Mayankho
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/1 tsamba 5-7

Kufunafuna Kwawo Chipembedzo Cholondola

KUYAMBIRA paubwana anthu ena akhala akufunafuna mayankho okhutiritsa a mafunso awo ponena za moyo. Pamene anali aang’ono, angakhale anafika pa misonkhano yachipembedzo. Koma ambiri a iwo anapeza kuti mayankho operekedwawo kapenanso mwambo wa tchalitchi sizinawathandize kwenikweni kuchita ndi mavuto a moyo.

Iwo anganene kuti adakali a chipembedzo cha makolo awo, ngakhale kuti samafika kaŵirikaŵiri pa misonkhano yachipembedzo. Malinga ndi kunena kwa bishopu wa Church of England, chawocho changokhala chikhulupiriro chochepa chotsalira. Iwo akankhira pambali chipembedzo. Ena, moipidwa ndi chinyengo chimene amaona m’mabwalo achipembedzo, akaniratu chipembedzo. Komabe, mafunso awo onena za moyo amapitiriza.

Chifukwa Chake Ena Amakayikira Kwambiri

Anthu ochuluka amadziŵa kuti matchalitchi ambiri ali ndi magulu othandiza anthu opanda pokhala, ogaŵira chakudya kwa osoŵa, ndi olipirira zochitika za anthu. Koma pafupifupi tsiku lililonse amamvanso malipoti a nkhani za chiwawa ndi kukhetsa mwazi zochititsidwa ndi chipembedzo osati kokha pakati pa amene sali Akristu komanso pakati pa awo amene amadzinenera kukhala Akristu. Kodi ziyenera kutidabwitsa ngati akayikira kuti kaya magulu oloŵetsedwa m’chiwawa choterocho akulondoladi chipembedzo cholondola?

Ambiri amene analeredwera m’mabanja achipembedzo ankaganiza kuti nyumba za ana amasiye zolipiriridwa ndi matchalitchi zinali malo abwino kwambiri. Komabe, m’zaka zaposachedwapa, achititsidwa mantha pamene ansembe a m’malo osiyanasiyana apatsidwa mlandu wakugona ana amene anaikiziridwa m’chisamaliro chawo. Poyamba anthu anaganiza kuti ndi ansembe oŵerengeka okha amene anali ndi liwongo. Tsopano ena a iwo akukayikira ngati pali chinachake cholakwika kwambiri ndi tchalitchi chenichenicho.

Oŵerengeka, monga ngati Eugenia, panthaŵi ina anali odziloŵetsa kwambiri m’chipembedzo chawo. Pamene anali wachichepere m’Argentina, iye anali pakati pa awo amene anapanga maulendo achipembedzo kukalambira Namwali wa ku Itatí. Kwa zaka 14 iye anakhala m’nyumba ya avirigo monga mvirigo. Ndiyeno anachokako kuti akakhale mbali ya gulu lachipembedzo ndi ndale lamitundu yonse limene linachirikiza kusintha kwakukulu kwa mwamsanga, kwa kayendetsedwe ka zinthu zamayanjano ndi zachuma ka chitaganya mwa kupandukira ulamuliro. Monga chotulukapo cha zimene anaona ndi kukumana nazo, anataya chikhulupiriro ndi chidaliro mwa Mulungu. Iye sanali kufunafunadi chipembedzo chimene akanakhulupirira. Zimene anafuna zinali kupeza njira yobweretsera chilungamo kwa awo amene anali osauka​—inde, ndi bwenzi limene akanadalira.

Ena amaona zimene zikuchitika m’matchalitchi ndipo samapitako. Munthu wosakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu amene malingaliro ake anafalitsidwa mu 1991 m’magazini akuti Sputnik ananena mosabisa mawu kuti: “Sindiona kusiyana kwakukulu kulikonse pakati pa mikhalidwe ya nthanthi zachikunja ndi Zachikristu.” Mwachitsanzo, iye analongosola za ligubo m’limene ansembe ovala mikanjo yopetedwa ndi golidi ananyamula bokosi lamaliro lamwala lokhala ndi mtembo akumayenda nalo pang’onopang’ono m’makwalala a Moscow. Unali mtembo wa “woyera Wachikristu wa Orthodox” umene unali kuchotsedwa ku malo osungira zinthu zamakedzana kupita nawo ku tchalitchi, ndipo zinakumbutsa wolembayo za ansembe ndi mitembo ya mu Igupto wamakedzana. Iye anakumbukiranso kuti, ngakhale kuti amene anatenga mbali m’ligubolo mu Moscow anakhulupirira “Utatu Wachikristu,” Aigupto analinso kulambira milungu itatu​—Osiris, Isis, ndi Horus.

Wolemba mmodzimodziyo anatchula za lingaliro Lachikristu la chikondi​—“Mulungu ndiye chikondi,” ndi “uzikonda mnansi wako”​—kukhala lopanda lolingana nalo mu Igupto wachikunja. Koma ananena kuti: “Chikondi cha abale chalephera kupambana m’dziko, ngakhale m’mbali imeneyo ya dziko imene imadzitcha kukhala dziko Lachikristu.” Ndipo anawonjezera ndi ndemanga zonena za zipatso zoipa za kuumirira kwa tchalitchi pa kuloŵa m’nkhani za Boma. Zimene anaona sizinamsonkhezere kulingalira kuti matchalitchi a Dziko Lachikristu anapereka zimene anali kufunafuna.

Mosiyana, ena apeza mayankho okhutiritsa koma osati m’matchalitchi a Dziko Lachikristu.

Anadziŵa Choonadi Ponena za Akufa

Magdalena, amene tsopano ali ndi zaka 37, amakhala m’Bulgaria. Pamene apongozi ake anamwalira mu 1991, anasoŵeratu chochita. Ankadzifunsa kaŵirikaŵiri kuti, ‘Kodi akufa amapita kuti? Kodi apongozi anga ali kuti?’ Anapita ku tchalitchi, ndipo anapemphera pamaso pa fano lachipembedzo kunyumba, komabe sanalandire mayankho.

Ndiyeno tsiku lina mnansi wake anaimba foni kumuitana kupita kunyumba kwake. Mwamuna wachichepere amene anali kuphunzira ndi Mboni za Yehova anali kuchezera mnansiyo. Iye anamvetsera pamene mwamuna wachichepereyo analankhula za Ufumu wa Mulungu ndi chifuno Chake cha kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso kumene anthu angakhale ndi moyo kosatha mwachimwemwe. Pa thebulo panali buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Akumaligwiritsira ntchito, mwamuna wachichepereyo analunjikitsa chidwi cha mkaziyo ku lemba la Baibulo la Mlaliki 9:5, limene limati: “Koma akufa sadziŵa kanthu bi.” Madzulo amenewo mkaziyo anaŵerenga zowonjezereka. Iye anaphunzira kuti akufa sanapite ku moyo wina kumwamba kapena m’helo; iwo sadziŵa kanthu, monga ngati kuti agona tulo. Mosangalala anavomera chiitano cha kufika pamsonkhano wa mpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko. Pambuyo pa msonkhanowo anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo lokhazikika. Pokhala ataona pa msonkhanopo mmene mapemphero anaperekedwera kwa Yehova, nayenso anayamba kupemphera kwa Yehova kaamba ka chithandizo m’kugonjetsa chifooko chachikulu. Pamene pemphero lake linayankhidwa, anadziŵa kuti wapeza chipembedzo cholondola.

Anapeza Moyo Wokhala ndi Tanthauzo

André anakulira m’banja la Akatolika amphamvu m’Belgium ndipo anatumikira monga wothandizira wansembe wa kumaloko. Komabe, mkati mwa nthaŵi imeneyo, anaona zinthu zimene zinamchititsa kusalemekeza tchalitchi. Monga chotsatirapo, iye anali Mkatolika m’dzina lokha.

Kwa zaka 15 ntchito yake inali kuseŵera mpira wachitanyu. Tsiku lina pamene timu yake inaseŵera mpikisano mu Italy, anaitanidwa kukaonana ndi papa. Paulendowo panalibe chilichonse chomangirira mwauzimu, ndipo chuma chakuthupi chimene chinazinga papa chinakhumudwitsa André. Zikayikiro zake zonena za tchalitchi zinakula. Moyo wake wamseri unalinso wopanda chimwemwe chifukwa cha kusweka kwa maukwati aŵiri. Mkhalidwe wa dziko unamgwiritsa mwala. Mu 1989 analemba m’dayale yake kuti: ‘Kodi nchiyani chimene chili tanthauzo la zinthu zonse zopanda pake zimene zikuchitika motizungulira?’ Iye sanapeze mayankho m’chipembedzo chake.

Mu 1990, pamene André anali kugwira ntchito monga mphunzitsi wa mpira wachitanyu mu Iceland, Iiris, mmishonale wa Mboni za Yehova, anamfikira. Iye analandira mabuku ndi kuvomera pempho la mmishonaleyo kuti akabwerenso. Iye anabweranso ndi mwamuna wake, Kjell. Pamene pomalizira pake anakhala okhoza kukhala pansi ndi kulankhula ndi André, kunali koonekeratu kuti anali wokondwerera kwambiri kumvetsetsa Baibulo. Mkazi wake Ásta, anali ndi chikondwerero chofananacho. Pakati pa tsiku, anali ndi maola atatu pakati pa zigawo zake zophunzitsa, ndipo anasankha kugwiritsira ntchito nthaŵi imeneyo kuphunzira Baibulo. “Ndimadzimva kukhala wotsitsimulidwa kwambiri mwa kuphunzira Baibulo kuposa kungopuma basi,” iye anatero. Mwapang’onopang’ono Baibulo linayankha mafunso awo. Pang’onopang’ono chikhulupiriro chawo mwa Yehova ndi Ufumu wake chinakula. Malonjezo aulemerero a Baibulo a dziko latsopano lamtendere, dziko lopanda “zinthu zonse zopanda pake zimene zikuchitika,” linakhala lotsimikizirika kwa iwo. Onse aŵiri André ndi Ásta tsopano akufotokozera ena chikhulupiriro chawo chopezedwa chatsopano.

Magdalena, André, ndi Ásta ali achidaliro kuti pomalizira pake anapeza chipembedzo cholondola. Eugenia nayenso, pambuyo poyesa kuthetsa mavuto a dziko mwa ndale, potsirizira pake anapeza pakati pa Mboni za Yehova chipembedzo chimene chinaonekera kwa iye kukhala cholondola. Koma kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kwenikweni ngati chipembedzo chili cholondola? Chonde onani nkhani yotsatira.

[Chithunzi patsamba 7]

Phunziro lokhazikika la Baibulo ndi Mboni za Yehova likuthandiza anthu oposa mamiliyoni asanu m’kufunafuna kwawo mayankho okhutiritsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena