Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/1 tsamba 13-18
  • Kudziŵa Chipembedzo Cholondola Kumadzetsa Thayo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudziŵa Chipembedzo Cholondola Kumadzetsa Thayo
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumawalabadira Motani Mawu a Mulungu?
  • Kodi Kudzipereka Kwanu kwa Yehova Kuli Kokwanira?
  • Kodi Chikondi cha Kristu Chimakuyambukirani Mokulira Motani?
  • Kulekana ndi Dziko ​—Kumlingo Wotani?
  • Kodi Chikondi Chanu Chimafika Pati?
  • Umboni Waufumu​—Kodi n’Ngwofunika Motani kwa Inu?
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Chipembedzo
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/1 tsamba 13-18

Kudziŵa Chipembedzo Cholondola Kumadzetsa Thayo

“Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—LUKA 11:28.

1. Atangodziŵa chipembedzo cholondola, kodi ndi anthu amtundu wotani amene amaumba miyoyo yawo pa icho?

SIKULI kokwanira kungodziŵa chipembedzo cholondola. Ngati timakonda chimene chili cholondola ndi choonadi, titangochipeza, tidzaumba miyoyo yathu pa icho. Chipembedzo choona sichimangofunikira kudziŵidwa chabe; chili njira ya moyo.​—Salmo 119:105; Yesaya 2:3; yerekezerani ndi Machitidwe 9:2.

2, 3. (a) Kodi Yesu anagogomezera motani kufunika kwa kuchita chifuniro cha Mulungu? (b) Kodi ndi thayo lotani limene lili pa munthu aliyense amene amadziŵa chipembedzo cholondola?

2 Yesu Kristu anagogomezera kufunika kwa kuchita chimene Mulungu wasonyeza kukhala chifuniro Chake. Pomaliza umene wadziŵika monga Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anadziŵikitsa kuti si onse amene anamutcha Ambuye (motero akumadzinenera kukhala Akristu) akaloŵa mu Ufumu; koma awo okha amene akachita chifuniro cha Atate wake ndiwo akatero. Iye anati ena akakanidwa monga “akuchita kusayeruzika.” Chifukwa ninji kusayeruzika? Chifukwa chakuti monga momwe Baibulo limanenera, kulephera kuchita chifuniro cha Mulungu ndi tchimo, ndipo tchimo lililonse ndi kusayeruzika. (Mateyu 7:21-23; 1 Yohane 3:4; yerekezerani ndi Aroma 10:2, 3.) Munthu angadziŵe chipembedzo cholondola, mwina angayamikire amene amaphunzitsa za icho, ndipo mwina angasimbe za awo amene amachichita, koma alinso ndi thayo la kuchigwiritsira ntchito m’moyo wake. (Yakobo 4:17) Ngati avomereza thayo limenelo, adzapeza kuti moyo wake udzalemerera, ndipo adzapeza chimwemwe chimene sichingadze mwanjira ina.

3 M’nkhani yapapitapo, tinapenda zizindikiro zisanu ndi chimodzi zodziŵira chipembedzo choona. Chilichonse cha zimenezo sichimangotithandiza kudziŵa chipembedzo cholondola komanso chimatipatsa aliyense payekha zitokoso ndi mipata. Motani?

Kodi Mumawalabadira Motani Mawu a Mulungu?

4. (a) Pamene atsopano ayamba kugwirizana ndi Mboni za Yehova, kodi nchiyani chimene iwo mwamsanga amaona ponena za kugwiritsira ntchito Baibulo kwa Mbonizo? (b) Kodi kudyetsedwa bwino mwauzimu kumawayambukira motani atumiki a Yehova?

4 Pamene Mboni za Yehova ziphunzira Baibulo ndi okondwerera chatsopano, ambiri mwa atsopano ameneŵa amazindikira msanga kuti zimene akuphunzitsidwa zikuchokera m’Baibulo. Poyankha mafunso awo, iwo samasonyezedwa ziphunzitso za tchalitchi, miyambo yaumunthu, kapena malingaliro a anthu omveka. Mawu a Mulungu mwiniyo ndiwo muyezo. Pamene apita ku Nyumba Yaufumu, amaonanso kuti kumeneko buku lalikulu lophunziridwa ndilo Baibulo. Ofuna choonadi oona mtima samatenga nthaŵi yaitali kuzindikira kuti mbali yaikulu imene imachititsa chimwemwe chimene amaona pakati pa Mboni za Yehova ndi yakuti izo zimadyetsedwa bwino mwauzimu m’Mawu a Mulungu.​—Yesaya 65:13, 14.

5. (a) Kodi ndi chitokoso chotani chimene chikuperekedwa kwa awo amene amapenyerera Mboni za Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene angakhalire ndi phande m’chimwemwe cha Mbonizo?

5 Ngati mumazindikira zimenezi, kodi mumachitapo kanthu motani? Ngati mudziŵa tanthauzo lake, sikungakhale koyenera kwa inu kungokhala wopenyerera basi, ndipo simuyenera kukhala wotero. Baibulo limasonyeza kuti awo amene ali “akumva okha” koma osati “akuchita mawu” ali ‘kudzinyenga okha.’ (Yakobo 1:22) Iwo amangodzinyenga chifukwa chakuti amalephera kuzindikira kuti mosasamala kanthu ndi zimene anganene, kulephera kwawo kumvera Mulungu kumasonyeza kuti iwo samamkondadi. Chikhulupiriro chongonenedwa chopanda ntchito chili chikhulupiriro chakufa. (Yakobo 2:18-26; 1 Yohane 5:3) Mosiyana ndi amenewo, iye amene asonkhezeredwa ndi chikondi cha pa Yehova kukhala “wakuchita ntchito” adzakhala “wodala m’kuchita kwake.” Inde, monga momwe Yesu Kristu anafotokozera, “odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—Yakobo 1:25; Luka 11:28; Yohane 13:17.

6. Ngati timayamikiradi Mawu a Mulungu, kodi ndi mipata yotani imene ife pa tokha tidzakalimira kugwiritsira ntchito?

6 Chimwemwe chimenecho chidzakula pamene chidziŵitso chanu cha chifuniro cha Mulungu chikula ndi pamene mugwiritsira ntchito zinthu zowonjezereka zimene mumaphunzira. Kodi ndi kuyesayesa kokulira motani kumene mudzachita kuti muphunzire Mawu a Mulungu? Anthu zikwi makumi ambiri amene anali osaphunzira ayesayesa zolimba kuphunzira kuŵerenga, akumachita zimenezi makamaka kuti akhoze kuŵerenga Malemba ndi kuwaphunzitsa kwa anthu ena. Ena amadzuka mmamaŵa tsiku lililonse kuti athere nthaŵi ina pa kuŵerenga Baibulo ndi zothandizira kuphunzira Baibulo, zonga Nsanja ya Olonda. Pamene muŵerenga Baibulo mopitiriza pa nokha kapena kuŵerenga malemba osonyezedwa m’nkhani ina yophunziridwa, zindikirani bwino lomwe malamulo ndi malangizo a Yehova, ndipo yesetsani kuzindikira malamulo ambiri a mkhalidwe amene alimo kaamba ka chitsogozo chathu. Sinkhasinkhani zimene chigawo chilichonse chikuvumbula ponena za Mulungu, chifuno chake, ndi zochita zake ndi mtundu wa anthu. Lolani nthaŵi yakuti zimenezi ziumbe mtima wanu. Lingalirani za njira zimene zingakhalepo zimene mungagwiritsirire ntchito bwino lomwe uphungu wa Baibulo m’moyo wanu.​—Salmo 1:1, 2; 19:7-11; 1 Atesalonika 4:1.

Kodi Kudzipereka Kwanu kwa Yehova Kuli Kokwanira?

7. (a) Kodi chiphunzitso cha Utatu chayambukira motani zoyesayesa za anthu za kulambira Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene chingachitike pamene munthu wadziŵa choonadi ponena za Yehova?

7 Kwa anthu mamiliyoni, kwakhala kotonthoza kudziŵa kuti Mulungu woona sali Utatu. Mafotokozedwe akuti “ndi chinsinsi” sanawakhutiritse konse. Kodi akanayandikira motani kwa Mulungu amene anali wosamvetsetseka? Chifukwa cha chiphunzitso chimenecho, iwo anakhoterera ku kunyalanyaza Atate (amene dzina lake sanalimvepo m’tchalitchi) ndi kulambira Yesu monga Mulungu kapena kulunjikitsa kulambira kwawo kwa Mariya (amene iwo anaphunzitsidwa kuti anali “Amayi wa Mulungu”). Koma mitima yawo inadzala ndi chikondwerero pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anatsegula Baibulo ndi kuwasonyeza dzina laumwini la Mulungu, Yehova. (Salmo 83:18) Mkazi wina wa ku Venezuela anakondwera kwambiri atasonyezedwa dzina laumulungulo kwakuti anafungatira Mboni yachichepere imene inamuuza choonadi chamtengo wapatali chimenecho ndipo anavomereza kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba. Pamene anthu otero aphunzira kuti Yesu ananena za Atate wake kukhala “Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu” ndi kuti Yesu anatcha Atate wake “Mulungu woona yekha,” amazindikira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za Mulungu sizili zosamvetsetseka. (Yohane 17:3; 20:17) Pamene adziŵa mikhalidwe ya Yehova, amadzimva kukhala okokedwera kwa iye, amayamba kupemphera kwa iye, ndipo amafuna kumkondweretsa. Kodi pamakhala zotsatirapo zotani?

8. (a) Chifukwa cha chikondi chawo kwa Yehova ndi chikhumbo chawo cha kumkondweretsa, kodi nchiyani chimene mamiliyoni a anthu achita? (b) Kodi nchifukwa ninji ubatizo Wachikristu uli wofunika kwambiri?

8 M’zaka khumi zapitazo, anthu 2,528,524 m’makontinenti asanu ndi limodzi ndi zisumbu zambirimbiri apatulira miyoyo yawo kwa Yehova nasonyeza kudzipatulira kumeneku mwa ubatizo wa m’madzi. Kodi munali mmodzi wa iwo, kapena kodi mukukonzekera kubatizidwa tsopano? Ubatizo uli sitepe lofunika kwambiri m’moyo wa Mkristu woona aliyense. Yesu analamula atsatiri ake kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse ndi kuwabatiza. (Mateyu 28:19, 20) Nkofunikanso kuzindikira kuti Yesu atangobatizidwa Yehova mwiniyo analankhula ali kumwamba, kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, [ndakuvomereza, NW].”​—Luka 3:21, 22.

9. Kuti tisunge unansi wovomerezedwa ndi Yehova, kodi tiyenera kuchitanji?

9 Unansi wovomerezedwa ndi Yehova uyenera kusamaliridwa. Ngati mwaloŵa muunansi wotero mwa kudzipatulira ndi ubatizo, peŵani chilichonse chimene chingauwononge. Musalole nkhaŵa za moyo ndi za chuma chakuthupi kuukankhira pa malo achiŵiri. (1 Timoteo 6:8-12) Khalani mogwirizanadi ndi uphungu wa pa Miyambo 3:6 wakuti: “Umlemekeze [Yehova] m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.”

Kodi Chikondi cha Kristu Chimakuyambukirani Mokulira Motani?

10. Kodi nchifukwa ninji kulambira kwathu Yehova sikumatichititsa kunyalanyaza Yesu?

10 Ndithudi, kuzindikira Yehova moyenerera monga Mulungu woona yekha sikumachititsa munthu kunyalanyaza Yesu Kristu. Mmalo mwake, Chivumbulutso 19:10 chimati: “Umboni wa Yesu ndiwo mzimu wa chinenero.” Kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso, maulosi ouziridwa amapereka maumboni onena za mbali ya Yesu Kristu m’chifuno cha Yehova. Pamene munthu adziŵa bwino lomwe maumboni amenewo, nkhani yonseyo imaonekera bwino yopanda zolakwa ndi malingaliro opotoka zochititsidwa ndi ziphunzitso zonyenga za Dziko Lachikristu.

11. Kodi ndimotani mmene kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsadi ponena za Mwana wa Mulungu kunayambukirira mkazi wina ku Poland?

11 Kumvetsetsa choonadi ponena za Mwana wa Mulungu kungakhale ndi chiyambukiro chachikulu pa munthu. Ndi mmene zinaliri kwa Danuta, mkazi wina ku Poland. Iye anakhala akugwirizana ndi Mboni za Yehova kwa zaka zisanu ndi zitatu, anakonda zimene zinaphunzitsa, koma sanali kupanga kulambira koona kukhala njira yake ya moyo. Ndiyeno analandira kope la buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, limene limafotokoza moyo wa Kristu mwanjira yosavuta kumva.a Usiku, iye anatsegula bukulo, ndi cholinga cha kuŵerenga mutu umodzi chabe. Komabe, sanaike bukulo pansi kufikira atamaliza kuliŵerenga mbanda kucha. Anayamba kulira. “Yehova, ndikhululukireni,” anachonderera motero. Chifukwa cha zimene anaŵerenga, iye anaona bwino lomwe koposa ndi kalelonse, chikondi chosonyezedwa ndi Yehova ndi Mwana wake. Anazindikira kuti kwa zaka zisanu ndi zitatu iye mosayamikira anali kukana chithandizo chimene Mulungu anali kumpatsa moleza mtima. Mu 1993 anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova pa maziko a chikhulupiriro mwa Yesu Kristu.

12. Kodi chidziŵitso cholongosoka ponena za Yesu Kristu chimayambukira motani miyoyo yathu?

12 “[Chidziŵitso cholongosoka, NW] cha Ambuye wathu Yesu Kristu” chimagwirizana ndi kukhala Mkristu wachangu ndi wobala zipatso. (2 Petro 1:8) Kodi mudzakhala ndi phande m’ntchito yoteroyo kufikira pati, mukumauza ena uthenga wa Ufumu? Mlingo umene munthu mmodzi ndi mmodzi akhoza kuchita umadalira pa mikhalidwe yambiri. (Mateyu 13:18-23) Mikhalidwe ina sitingaisinthe; ina tingaisinthe. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kuzindikira ndi kupanga masinthidwe amene angapangidwe? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza”; m’mawu ena, chikondi chimene anasonyeza mwa kupereka moyo wake kaamba ka ife nchachikulu kwambiri kwakuti pamene chiyamikiro chathu kaamba ka icho chikula, mitima yathu imasonkhezeredwa kwambiri. Chotero, timazindikira kuti kungakhale kosayenera konse kwa ife kulondolabe zonulirapo zadyera ndi kukhala ndi moyo makamaka wodzikhutiritsa. Mmalo mwake, timasintha zochita zathu kuti tiike pa malo oyamba ntchito imene Kristu anaphunzitsa ophunzira ake kuichita.​—2 Akorinto 5:14, 15.

Kulekana ndi Dziko ​—Kumlingo Wotani?

13. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala ndi mbali ya chipembedzo chimene chadzipanga kukhala mbali ya dziko?

13 Sikovuta kuona mbiri imene Dziko Lachikristu ndi zipembedzo zina zapanga chifukwa chofuna kukhala mbali ya dziko. Ndalama za tchalitchi zagwiritsiridwa ntchito kulipirira machitachita achipanduko. Ansembe akhala zigaŵenga. Tsiku ndi tsiku, manyuzipepala amasimba nkhani za timagulu tachipembedzo m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi timene tikumenyana. Manja awo adzala mwazi. (Yesaya 1:15) Ndipo padziko lonse atsogoleri achipembedzo akupitirizabe kuyesa kusonkhezera mwamachenjera m’zandale. Olambira oona sali ndi mbali m’zimenezi.​—Yakobo 4:1-4.

14. (a) Kodi nchiyani chimene ife pa tokha tiyenera kupeŵa ngati titi tikhale olekana ndi dziko? (b) Kodi nchiyani chimene chingatithandize kupeŵa kugwidwa mumsampha wa mikhalidwe ndi machitachita adziko?

14 Koma kulekana ndi dziko kumaphatikizapo zoposa zimenezo. Dziko ladzala ndi chikondi cha pa ndalama ndi zimene ndalama zingagule, chilakolako cha kumveka kwa munthu mwini, ndi kulondola zokondweretsa kosalekeza, limodzi ndi zinthu zonga kusoŵeka kwa nkhaŵa yeniyeni kaamba ka ena, kunama ndi kutukwana, kupandukira ulamuliro, ndi kulephera kusonyeza kudziletsa. (2 Timoteo 3:2-5; 1 Yohane 2:15, 16) Chifukwa cha kupanda kwathu ungwiro, nthaŵi zina tingasonyeze ina ya mikhalidwe imeneyo. Kodi nchiyani chimene chingatithandize m’nkhondo yathu yofuna kupeŵa misampha imeneyo? Tifunikira kukumbukira amene ali kumbuyo kwa zonsezi. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mosasamala kanthu za mmene njira yakutiyakuti ingakhalire yokopa, mosasamala kanthu za unyinji wa anthu amene amatsatira njirayo, pamene tiona mdani wamkulu wa Yehova, Satana Mdyerekezi, kumbuyo kwake, timazindikira kuipa kwake.​—Salmo 97:10.

Kodi Chikondi Chanu Chimafika Pati?

15. Kodi chikondi chopanda dyera chimene munaona chinakuthandizani motani kudziŵa chipembedzo choona?

15 Pamene munangoyamba kuyanjana ndi Mboni za Yehova, mosakayikira chikondi chosonyezedwa pakati pawo chinakukopani chifukwa cha kusiyana kwake ndi mzimu wa dziko. Kugogomezeredwa kwa chikondi chopanda dyera kumasiyanitsa kulambira koyera kwa Yehova ndi kulambira kwina kwamtundu uliwonse. Mwina zimenezi ndizo zinakukhutiritsani kuti Mboni za Yehova zikuchitadi chipembedzo cholondola. Yesu Kristu mwiniyo anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:35.

16. Kodi ndi mipata yotani ya kufutukula chikondi chathu imene tingakhale nayo aliyense pa yekha?

16 Kodi mkhalidwe umenewo umadziŵikitsanso inu monga mmodzi wa ophunzira a Kristu? Kodi pali njira zina zimene mungafutukulire kusonyeza chikondi kwanu? Ndithudi tonsefe tingatero. Kusonyeza chikondi kumafuna zambiri kuposa kungosonyeza ubwenzi kwa ena pa Nyumba Yaufumu. Ndipo ngati timangokonda awo amene amatikonda, kodi tingakhale osiyana motani ndi dziko? “Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha,” Baibulo limafulumiza motero. (1 Petro 4:8) Kodi nkwayani kumene tingasonyeze chikondi chokulirapo? Kodi nkwa mbale kapena mlongo Wachikristu amene mikhalidwe yake imasiyana ndi yathu ndi amene njira yake yochitira zinthu zina imatikwiyitsa? Kodi nkwa munthu amene, chifukwa cha kudwala kapena ukalamba, wakhala wosakhoza kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse? Kodi nkwa mnzathu wamuukwati? Kapena, mwinamwake, nkwa makolo athu amene akukalamba? Ena amene anali kuchita bwino pa kusonyeza zipatso za mzimu, kuphatikizapo chikondi, anaona ngati kuti anali kuphunziranso zimenezo pamene anayang’anizana ndi mikhalidwe yovuta kwambiri imene ingabuke posamalira, pafupifupi m’zonse, chiŵalo cha banja chimene chinapunduka kwambiri. Ndithudi, ngakhale pamene tiyang’anizana ndi mikhalidwe imeneyi, chikondi chathu chiyeneranso kufalikira kunja kwa banja lathu.

Umboni Waufumu​—Kodi n’Ngwofunika Motani kwa Inu?

17. Ngati ife enife tapindula ndi maulendo a Mboni za Yehova, kodi tsopano tiyenera kudzimva kukhala osonkhezeredwa kuchitanji?

17 Njira yofunika imene timasonyezera chikondi kwa anthu anzathu ndiyo mwa kuchitira umboni kwa iwo ponena za Ufumu wa Mulungu. Gulu limodzi lokha la anthu likuchita ntchito imeneyi imene Yesu ananeneratu. (Marko 13:10) Ndizo Mboni za Yehova. Ife pa tokha tapindula nayo. Tsopano ndi mwaŵi wathu kuthandiza ena. Ngati tili ndi lingaliro la Mulungu pa nkhaniyi, ntchito imeneyi idzakhala yofunika m’miyoyo yathu.

18. Kodi kuŵerenga kwathu buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom kungayambukire motani phande lathu muumboni Waufumu?

18 Mbiri yosangalatsa yonena za mmene uthenga Waufumu waperekedwera ku madera akutali kwambiri a dziko lapansi m’masiku ano otsiriza yasimbidwa m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom. Ngati mudziŵa Chingelezi, musalephere kuliŵerenga. Ndipo pamene mukutero, samalirani kwambiri njira zonse zimene anthu mmodzi ndi mmodzi akhalira ndi phande m’kupereka umboni wonena za Ufumu. Kodi pali ena amene mungatsanzire chitsanzo chawo? Tonsefe tili ndi mipata yambiri yotseguka. Chikondi chathu pa Yehova chitisonkhezeretu kuigwiritsira ntchito bwino.

19. Kodi timapindula motani pamene tilandira thayo limene kudziŵa chipembedzo cholondola kumadzetsa?

19 Pamene tilimbikira motero kuchita chifuniro cha Yehova, timapeza yankho la funso lakuti, Kodi tanthauzo la moyo nchiyani? (Chivumbulutso 4:11) Sitimakhalanso tikupwailapwaila, kudzimva kukhala opanda chifuno. Palibe ntchito iliyonse imene mungaichite modzipereka imene ingadzetse chikhutiro chachikulu kuposa kulimbikira kwanu kwa mtima wonse muutumiki wa Yehova Mulungu. Ndipo ili ndi mtsogolo mwabwino chotani nanga! Umuyaya wa moyo wokhutiritsa m’dziko lake latsopano, kumene tidzakhoza kugwiritsira ntchito bwino lomwe maluso athu mogwirizana ndi chifuno chachikondi chimene Mulungu analengera mtundu wa anthu.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa chipembedzo kulandira Baibulo monga Mawu a Mulungu ndi kulemekeza Yehova monga Mulungu woona?

◻ Kodi chipembedzo choona chimaphunzitsa chiyani ponena za mbali ya Yesu monga Momboli?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala olekana ndi dziko nasonyeza chikondi chopanda dyera?

◻ Kodi umboni Waufumu uli ndi mbali yotani m’chipembedzo cholondola?

[Zithunzi patsamba 16]

Ubatizo ndi sitepe lofunika kwambiri pa kulandira mathayo a kulambira koona. Mwezi uliwonse, anthu pafupifupi 25,000 padziko lonse amatenga sitepe limenelo

Russia

Senegal

Papua New Guinea

U.S.A.

[Zithunzi patsamba 17]

Kuuza ena choonadi cha Baibulo kuli mbali ya kulambira koona

U.S.A.

Brazil

U.S.A.

Hong Kong

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena