Kulimbana ndi Mphamvu ya Uchimo pa Thupi Lochimwa
“Chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.”—AROMA 8:6.
1. Kodi anthu analengedwa kaamba ka chifuno chotani?
“MULUNGU ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27) Chifanizo chili chithunzithunzi cha chinthu chinachake kapena chitsanzo chinachake. Chotero, anthu analengedwa kukhala chithunzithunzi cha ulemerero wa Mulungu. Mwa kusonyeza mikhalidwe yaumulungu—yonga ngati chikondi, ubwino, chilungamo, ndi uzimu—m’zochita zawo zonse, amadzetsa chitamando ndi ulemu kwa Mlengi, limodzinso ndi chimwemwe ndi chikhutiro kwa iwo eni.—1 Akorinto 11:7; 1 Petro 2:12.
2. Kodi anthu aŵiri oyambirira anaphonya motani chizindikiro?
2 Anthu aŵiri oyambirira, omwe analengedwa muungwiro, anali okonzekeretsedwa bwino kuchita mbali imeneyi. Mofanana ndi akalirole omwe apukutidwa kukhala ndi maŵalidwe amphamvu, iwo anali okhoza kusonyeza ulemerero wa Mulungu moŵala ndi mokhulupirika. Komabe, iwo analola maŵalidwe amphamvuwo kuipitsidwa pamene mwadala anasankha kusamvera Mlengi ndi Mulungu wawo. (Genesis 3:6) Pambuyo pake, sanakhozenso kusonyeza ulemerero wa Mulungu mwangwiro. Anapereŵera pa ulemerero wa Mulungu, akumaphonya chifuno cha kulengedwa kwawo m’chifanizo cha Mulungu. M’mawu ena, iwo anachimwa.a
3. Kodi mkhalidwe weniweni wa uchimo ndiwotani?
3 Zimenezi zimatithandiza kumvetsetsa mkhalidwe weniweni wa uchimo, umene umawononga chithunzithunzi cha munthu cha chifanefane ndi ulemerero wa Mulungu. Uchimo umachititsa munthu kukhala wosayera, kutanthauza kuti, wodetsedwa ndi woipitsidwa mwauzimu ndi mwamakhalidwe. Mtundu wonse wa anthu, pokhala mbadwa ya Adamu ndi Hava, umabadwira mumkhalidwe woipitsidwa ndi wodetsedwa umenewo, ukumalephera kukwaniritsa zimene Mulungu amayembekezera kwa iwo monga ana ake. Ndi zotulukapo zotani? Baibulo limalongosola kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12; yerekezerani ndi Yesaya 64:6.
Mphamvu ya Uchimo pa Thupi Lochimwa
4-6. (a) Kodi anthu ochuluka lerolino amauona motani uchimo? (b) Kodi nziti zimene zili zotulukapo za lingaliro lamakono la uchimo?
4 Anthu ochuluka lerolino samadzilingalira kukhala odetsedwa, oipitsidwa, kapena ochimwa. Kwenikweni, liwu lakuti uchimo lachokeratu pa mpambo wa mawu wa anthu ochuluka. Mwinamwake iwo akhoza kulankhula za zolakwa, kupanda nzeru, ndi zophophonya. Bwanji ponena za uchimo? Kutalitali! Ngakhale kwa awo amene amanenabe kuti ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, “ziphunzitso zake zinali mpambo wa zikhulupiriro zamakhalidwe mmalo mwa mpambo wa malamulo amakhalidwe, ‘malingaliro 10’ mmalo mwa malamulo 10,” akutero Alan Wolfe, profesa wa zakakhalidwe ka anthu.
5 Kodi zotulukapo za kalingaliridwe kameneka nzotani? Kukana, kapena kunyalanyaza kumlingo wakutiwakuti, kuona kwa uchimo. Zimenezi zatulutsa mbadwo wa anthu okhala ndi lingaliro lopotoka moipa la chabwino ndi choipa, amene amadziona kukhala aufulu kukhazikitsa miyezo yawoyawo ya khalidwe ndi amene amaona kuti sangaimbidwe mlandu ndi munthu aliyense pa chilichonse chimene asankha kuchita. Kwa anthu otero, kumva bwino ndiko muyezo wokha wodziŵira ngati mchitidwe wakutiwakuti uli woyenera kapena ayi.—Miyambo 30:12, 13; yerekezerani ndi Deuteronomo 32:5, 20.
6 Mwachitsanzo, pa programu ya kufunsa pa wailesi yakanema, achichepere anapemphedwa kupereka malingaliro awo ponena za otchedwa machimo asanu ndi aŵiri akupha.b “Kunyada si tchimo,” anatero wotengamo mbali wina. “Uyenera kudziona kukhala kanthu.” Ponena za ulesi, wina anati: “Nkwabwino kukhala wotero nthaŵi zina. . . . Nthaŵi zina nkwabwino kukhala uli phe ndi kukhala ndi nthaŵi yaumwini.” Ngakhale wofotokozayo anapereka ndemanga yachidule yakuti: ‘Machimo asanu ndi aŵiri akupha sali zochita zoipa koma, mmalomwake, ali zikhoterero za munthu aliyense zimene zingakhale zovutitsa ndi zosangalatsa kwambiri.’ Inde, kumva liwongo kwazimiririka pamodzi ndi uchimo, pakuti, ndi iko komwe, liwongo nlosemphana kwambiri ndi kumva bwino.—Aefeso 4:17-19.
7. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, kodi anthu amayambukiridwa motani ndi uchimo?
7 Mosiyana kwambiri ndi zonsezi, Baibulo limafotokoza bwino lomwe kuti: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Ngakhale mtumwi Paulo anavomereza kuti: “Ndidziŵa kuti mkati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichita.” (Aroma 7:18, 19) Panopa Paulo sanali kudzichitira chifundo. Mmalomwake, chifukwa chakuti anazindikira mokwanira ukulu wa kupereŵera kwa mtundu wa anthu pa ulemerero wa Mulungu, anaimva moŵaŵa kwambiri mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa. “Munthu wosauka ine;” iye anatero, “adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?”—Aroma 7:24.
8. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa? Chifukwa ninji?
8 Kodi lingaliro lanu pa nkhaniyi nlotani? Mungavomereze kuti monga mbadwa ya Adamu, inuyo, mofanana ndi ena onse, muli wopanda ungwiro. Koma kodi chidziŵitso chimenecho chimayambukira motani kalingaliridwe kanu ndi njira yanu ya moyo? Kodi mumavomereza kuti zilidi tero ndiyeno kungopitiriza kuchita zimene zimadza mwachibadwa? Kapena kodi mumayesayesa mosalekeza kulimbana ndi mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa, mukumalimbikira kusonyeza kwambiri ulemerero wa Mulungu m’zonse zimene mumachita? Imeneyi ifunikira kukhala nkhani yaikulu kwa aliyense wa ife polingalira zimene Paulo ananena kuti: “Iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.”—Aroma 8:5, 6.
Kusamalira za Thupi
9. Kodi nchifukwa ninji “chisamaliro cha thupi chili imfa”?
9 Kodi Paulo anatanthauzanji pamene ananena kuti “chisamaliro cha thupi chili imfa”? Liwulo “thupi” limagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri m’Baibulo kutanthauza munthu mumkhalidwe wake wopanda ungwiro, ‘wolandiridwa m’mphulupulu’ monga mbadwa ya Adamu wopanduka. (Salmo 51:5, Yobu 14:4) Chotero, Paulo anali kulangiza Akristu kusasumika maganizo awo pa zikhoterero, zisonkhezero, ndi zikhumbo zauchimo za thupi lopanda ungwiro, lochimwa. Ndipo nchifukwa ninji sayenera kutero? Kwinakwake Paulo anatiuza zimene ntchito za thupi zili nawonjezera chenjezoli: “Iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21.
10. Kodi ‘kusamalira’ kumatanthauzanji?
10 Koma kodi sipali kusiyana kwakukulu pakati pa kusamalira kanthu kena ndi kukachita? Zoona, kulingalira kanthu kena nthaŵi zina sikumatsogolera ku kukachita. Komabe, kusamalira nkoposa kungokhala ndi lingaliro lakanthaŵi. Liwu logwiritsiridwa ntchito ndi Paulo ndilo phroʹne·ma m’Chigiriki, ndipo limatanthauza “kalingaliridwe, kusumika (maganizo), . . . cholinga, chikhumbo, kukalimira.” Chotero, ‘kusamalira za thupi’ kumatanthauza kulamuliridwa, kugwidwa, kutsogozedwa, ndi kusonkhezeredwa ndi zikhumbo za thupi lochimwa.—1 Yohane 2:16.
11. Kodi Kaini anasamalira motani za thupi, ndipo chotulukapo chinali chiyani?
11 Mfundoyo ikusonyezedwa bwino lomwe ndi njira imene Kaini anatsatira. Pamene njiru ndi mkwiyo zinabuka mumtima wa Kaini, Yehova Mulungu anamchenjeza kuti: “Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo [iwe, mwiniwe, udzalamulira uwo kodi? NW].” (Genesis 4:6, 7) Kaini anali ndi chosankha. Kodi ‘akachita zabwino,’ ndiko kuti, kuika maganizo ake, cholinga, ndi chikhumbo pa kanthu kena kabwino? Kapena kodi akapitiriza kusamalira za thupi ndi kusumika maganizo ake pa zikhoterero zoipa zimene zinali mumtima mwake? Monga momwe Yehova anafotokozera, uchimo unali ‘kubwatama pakhomo,’ ukumayembekezera kuukira ndi kulikwira Kaini ngati akaulola. Mmalo molimbana ndi chikhumbo chake chakuthupi ndi ‘kuchilamulira,’ Kaini anachilola kumtsogoza—ndi zotulukapo zowononga.
12. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tisayende “m’njira ya Kaini”?
12 Bwanji ponena za ife lerolino? Ndithudi sitifuna kuyenda “m’njira ya Kaini,” monga momwe Yuda anadandaulira ponena za ena pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba. (Yuda 11) Tisachepetse konse zinthu ndi kuganiza kuti kudzikhutiritsa pang’ono kapena kulakwako apa ndi apo nkosavulaza. Mosiyana ndi zimenezo, tiyenera kukhala ogalamuka kuzindikira chisonkhezero chilichonse cha kusapembedza ndi choipitsa chimene chingakhale chitaloŵa mumtima ndi m’maganizo mwathu ndi kuchichotsa mwamsanga chisanazike mizu. Kulimbana ndi mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa kumayambira mkati.—Marko 7:21, 22.
13. Kodi ndimotani mmene munthu ‘anganyengedwere ndi chilakolako chake’?
13 Mwachitsanzo, mungathe kuona chochitika chochititsa kakasi kapena chonyansa kapena chithunzithunzi chodzutsa lingaliro loipa kapena chilakolako cha kugonana. Chingakhale chithunzithunzi m’buku kapena m’magazini, chochitika m’filimu kapena pawailesi yakanema, chidziŵitso pa chikwangwani, kapena ngakhale kupezeka mumkhalidwe weniweniwo. Zimenezo pa zokha sizifunikira kukhala zowopsa, pakuti zingachitike—ndipotu—zimachitika. Komabe, chithunzithunzi chimenecho kapena chochitikacho, ngakhale kuti chingakhale chitatenga timphindi toŵerengeka chabe, mwina chingakhalebe m’maganizo ndi kumakumbukika nthaŵi ndi nthaŵi. Kodi mumachita chiyani pamene zimenezo zichitika? Kodi pomwepo mumachitapo kanthu kulimbana ndi lingaliro limenelo ndi kulitulutsa m’maganizo mwanu? Kapena kodi mumalilola kukhalabe m’maganizo mwanu, mwinamwake mukumasinkhasinkha chochitikacho panthaŵi iliyonse pamene lingaliro limenelo libuka? Kuchita chimene chatchulidwa pomalizirachi ndiko kudziika pangozi yoyambitsa tsatanetsatane wa zochitika zofotokozedwa ndi Yakobo: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” Nchifukwa chake Paulo anati: “Chisamaliro cha thupi chili imfa.”—Yakobo 1:14, 15; Aroma 8:6.
14. Kodi nchiyani chimene timayang’anizana nacho tsiku ndi tsiku, ndipo tiyenera kuchita motani?
14 Kukhala mmene tikukhaliramu m’dziko limene chisembwere, chiwawa, ndi kukondetsa zinthu zakuthupi zimalemekezedwa—zikumasonyezedwa poyera ndi momasuka m’mabuku, m’magazini, m’mafilimu, m’maprogramu apawailesi yakanema, ndi m’nyimbo zotchuka—timakanthidwadi ndi malingaliro ndi njira zolakwa tsiku lililonse. Kodi mumachita motani? Kodi mumasangalala ndi kusanguluka ndi zonsezi? Kapena kodi mumamva monga momwe Loti wolungama anachitira, amene anali “wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja . . . anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika”? (2 Petro 2:7, 8) Kuti tipambane pa kulimbana ndi mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa, tifunikira kutsimikiza mtima kuchita monga momwe anachitira wamasalmo: “Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.”—Salmo 101:3.
Kusamalira za Mzimu
15. Kodi ndi chithandizo chotani chimene tili nacho cholimbanira ndi mphamvu ya uchimo pa ife?
15 China chimene chingatithandize kulimbana ndi mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa ndi chimene Paulo anapitiriza kunena: “Chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6) Chotero, mmalo mwa kulamuliridwa ndi thupi, tiyenera kuchititsa maganizo athu kusonkhezeredwa ndi mzimu ndi kukondwera ndi zinthu za mzimu. Kodi zinthuzo nziti? Pa Afilipi 4:8, Paulo akuzindandalika motere: “Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” Tiyeni tizipende mosamalitsa ndi kumvetsetsa bwino lomwe zimene tiyenera kulingalira.
16. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene Paulo anatilimbikitsa ‘kulingirira,’ ndipo kodi uliwonse umaphatikizapo chiyani?
16 Choyamba, Paulo anandandalika makhalidwe abwino asanu ndi atatu ndipo anayamba ndi liwu lakuti “zilizonse” asanatchule uliwonse. Mawu ameneŵa amasonyeza kuti Akristu samangofunikira chabe kuganizira zinthu za m’Malemba kapena zachiphunzitso nthaŵi zonse. Pali zinthu kapena nkhani zosiyanasiyana zimene tingasumikepo maganizo athu. Koma chofunika nchakuti ziyenera kugwirizana ndi makhalidwe abwino otchulidwa mwachindunji ndi Paulo. Gulu lililonse la “zilizonse” zotchulidwa ndi Paulo lifunikira chisamaliro chathu. Tiyeni tizipende chimodzi ndi chimodzi.
◻ “Zoona” zimaloŵetsamo zoposa kungokhala zoona kapena zonama. Zimatanthauza kuona mtima, kulungama, kukhulupiririka, zinthu zimene zili zenizeni, osati zongopereka chithunzi chakuti zili choncho.—1 Timoteo 6:20.
◻ “Zolemekezeka” zimasonya ku zinthu zoyenera ndi zaulemu. Zimapereka lingaliro la ulemu waukulu, zinthu zokwezeka, zabwino, ndi zoyenerera ulemu osati zamanyazi ndi zonyansa.
◻ “Zolungama” zimatanthauza zokwaniritsa miyezo ya Mulungu, osati ya munthu. Anthu adziko amadzaza maganizo awo ndi njira zosalungama, koma tifunikira kulingalira zinthu zimene zili zolungama m’maso mwa Mulungu ndi kukondwera nazo.—Yerekezerani ndi Salmo 26:4; Amosi 8:4-6.
◻ “Zoyera” zimatanthauza zabwino ndi zosadetsedwa osati m’khalidwe lokha (m’zakugonana kapena zinthu zina) komanso m’maganizo ndi zolinga. “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera,” akutero Yakobo. Yesu, amene ali “woyera,” ali Chitsanzo changwiro chimene tiyenera kulingalira.—Yakobo 3:17; 1 Yohane 3:3.
◻ “Zokongola” ndi zinthu zimene zimafulumiza ndi kusonkhezera chikondi mwa ena. Tiyenera ‘kuganizirana wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,’ mmalo mwa kusumika maganizo athu pa zinthu zimene zimabutsa chidani, mkwiyo, ndi zotetana.—Ahebri 10:24.
◻ ‘Zomveka zokoma’ sizimangotanthauza chabe “zosimbika” kapena “za mbiri yabwino” komanso, m’lingaliro logwira ntchito, kukhala womangirira ndi woyamikira. Timasumika maganizo athu pa zinthu zoyenera ndi zomangirira osati zonyoza ndi zonyansa.—Aefeso 4:29.
◻ “Chokoma” kwakukulukulu chimatanthauza “ubwino” kapena “ubwino woposa wa makhalidwe,” koma chingatanthauze ubwino woposa wa mtundu uliwonse. Chotero, tingayamikire mikhalidwe yabwino koposa, kuyenera, ndi zipambano za ena zogwirizana ndi miyezo ya Mulungu.
◻ Zinthu ‘zotamandika’ zimakhaladi choncho ngati chitamandocho chichokera kwa Mulungu kapena ulamuliro wozindikiridwa moyenerera ndi iye.—1 Akorinto 4:5; 1 Petro 2:14.
Lonjezo la Moyo ndi Mtendere
17. Kodi ndi madalitso ati amene “chisamaliro cha mzimu” chimadzetsa?
17 Pamene titsatira chilangizo cha Paulo ndi ‘kuzilingirira izi,’ tidzapambana mu “chisamaliro cha mzimu.” Zotulukapo sizidzangokhala dalitso la moyo, kutanthauza, moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa, komanso mtendere. (Aroma 8:6) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti maganizo athu ali otetezeredwa ku chisonkhezero choipa cha zinthu za thupi, ndipo sitimakhudzidwanso kwambiri ndi nkhondo yaululu pakati pa thupi ndi mzimu monga momwe yafotokozedwera ndi Paulo. Mwa kukaniza chisonkhezero cha thupi, timapezanso mtendere ndi Mulungu “chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu.”—Aroma 7:21-24; 8:7.
18. Kodi Satana akumenya nkhondo yotani, ndipo ndimotani mmene tingalakire?
18 Satana ndi oimira ake akuchita zilizonse zimene angathe kuti aipitse chithunzithunzi chathu cha ulemerero wa Mulungu. Amayesa kulamulira maganizo athu mwa kuwaukira ndi zikhumbo zathupi, akumadziŵa kuti zimenezi m’kupita kwa nthaŵi zidzatsogolera ku udani ndi Mulungu ndi ku imfa. Koma tikhoza kulakika m’nkhondoyi. Mofanana ndi Paulo, nafenso tingalengeze kuti: ‘Tiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu’ kaamba ka kutipatsa njira yolimbanira ndi mphamvu ya uchimo pa thupi lochimwa.—Aroma 7:25.
[Mawu a M’munsi]
a Kaŵirikaŵiri Baibulo limagwiritsira ntchito mneni Wachihebri wakuti cha·taʼʹ ndi mneni Wachigiriki wakuti ha·mar·taʹno kutanthauza “uchimo.” Mawu aŵiri ameneŵa amatanthauza “kuphonya,” m’lingaliro la kuphonya kapena kusafika pa chonulirapo, chizindikiro, kapena chandamale.
b Mwamwambo, machimo asanu ndi aŵiri akupha ndiwo kunyada, chisiriro, chilakolako, kaduka, kususuka, mkwiyo, ndi ulesi.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi uchimo nchiyani, ndipo kodi ungayambe motani kukhala ndi mphamvu pa thupi lochimwa?
◻ Kodi tingalimbane motani ndi “chisamaliro cha thupi”?
◻ Kodi tingachitenji kuti tichirikize “chisamaliro cha mzimu”?
◻ Kodi “chisamaliro cha mzimu” chimadzetsa motani moyo ndi mtendere?
[Chithunzi patsamba 15]
Kaini analola zikhoterero za thupi kumtsogolera ku chiwonongeko chake
[Zithunzi patsamba 16]
Chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere