Kodi Nchifukwa Ninji Mantha Akugwira Dziko?
KODI ndani amene amafuna kukhala m’mantha? Munthu aliyense amafuna chisungiko, popanda chiwopsezo ku moyo wake kapena chuma. Chifukwa chake, ambiri amasamuka ku madera odzaza ndi upandu. Komabe, zochititsa mantha zili ponseponse.
Ngozi za zida za nyukliya ndi zipangizo zotulutsira ndi kulamulira mphamvu yake zimadzetsa mantha a kusakaza kwa mtundu wa anthu. Kuwonjezereka kwakukulu kwa chiwawa kumakulitsa mantha. Ambiri akuchita mantha kuti AIDS idzakhala mliri wakupha koposa wa zaka za zanali. Kuwonongedwa kwa malo athu okhala kuli pakati pa zochititsa mantha zina. Kodi mantha ameneŵa ali apadera kwambiri? Ndipo kodi tingayembekezere konse kukhala m’dziko lopanda mantha otero?
Mantha Apadziko Lonse Ngapadera
Kufalikira kwa mantha kwa lerolino kuli kwapadera chifukwa cha zimene zinanenedweratu m’Baibulo. Mu ulosi wake wonena za masiku otsiriza, Yesu Kristu anatchula mikhalidwe imene ikachititsa mantha. Iye anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akuti akuti.” Yesu analankhulanso za “kuchuluka kwa kusayeruzika.” Chiyambire 1914, nkhondo, njala, zivomezi, ndi kusayeruzika zosayerekezereka zachititsa mantha aakulu ndi kutayika kwa moyo.—Mateyu 24:7-14.
Ngakhale mikhalidwe ya maganizo ya anthu imachititsa mantha lerolino. Pa 2 Timoteo 3:1-4, timaŵerenga mawu aulosi a mtumwi Paulo awa: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Popeza kuti tazingidwa ndi anthu otero m’masiku otsiriza ano, nzosadabwitsa kuti pali mantha aakulu motero!
Zimene Dzikoli Lingayembekezere
Yesu anayerekezera nyengo ino ndi masiku otsiriza a dziko la nthaŵi ya Nowa. Mosakayikira, mantha anali aakulu panthaŵiyo, popeza kuti cholembedwa cha mbiri ya Baibulo chimati: “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” Motero, “Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa.” (Genesis 6:11, 13) Dziko loipa limenelo linali lachiwawa kwambiri kwakuti Mulungu analithetsa mwa Chigumula chapadziko lonse. Komabe, chifukwa cha chikondi, Yehova Mulungu anasunga Nowa wolungama ndi banja lake.—2 Petro 2:5.
Chotero kodi dziko lachiwawa lilipoli lingayembekezere chiyani? Chabwino, Mulungu amanyansidwa ndi kusalingalira ubwino wa ena mwa kuwachitira chiwawa. Zimenezi zimaonekera m’mawu a wamasalmo akuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Yehova anathetsa dziko lachiwawa la m’tsiku la Nowa. Chotero, pamenepa, kodi sitiyenera kuyembekezera kuti Mulungu adzathetsa dziko lino lokanthidwa ndi chiwawa chochititsa mantha?
Mtumwi Petro anauziridwa mwaumulungu kulankhula za kukhalapo kwa Kristu ndi kulosera tsoka la dziko loipa lilipoli. Iye analemba kuti: “Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” Ndiyeno Petro anagwiritsira ntchito liwu lakuti “miyamba” kuimira dongosolo la ulamuliro wopanda ungwiro pa mtundu wa anthu ndi liwu lakuti “dziko lapansi” kaamba ka chitaganya cha anthu osalungama. “Pakuti,” iye anatero, “ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja [a Nowa], pomizika ndi madzi, lidawonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:3-7.
M’lingaliro lofananalo, Paulo anasonyeza kuti Kristu ndi angelo ake amphamvu ‘akabwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.’ (2 Atesalonika 1:6-9) Buku lomalizira la Baibulo limalankhula za kusonkhanitsidwa kwa mitundu ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” ndi kutitsimikizira kuti Yehova ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18; 16:14-16.
Nthaŵi ya Kusangalala, Osati Kuwopa
Mmalo mochita mantha ndi zimene Baibulo limaneneratu za dziko lino, anthu olungama ali ndi chifukwa cha kusangalalira. Posachedwapa Yehova adzathetsa dziko loipali, koma zimenezi zidzachitidwa kaamba ka ubwino wa awo amene amakonda chilungamo. Kodi nchiyani chidzatsatira kuthetsedwa kwaumulungu kwa dongosolo la zinthu lilipoli? Eya, dongosolo latsopano pansi pa Ufumu wakumwamba wa Mulungu, umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuupempherera! Iye anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi ndi masinthidwe otani amene tingayembekezere pamene chifuniro cha Mulungu chichitidwa padziko lapansi?
Nkhondo ndi zowopsa zake zidzatha. Salmo 46:9 limati: “[Yehova Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.” Ndiyeno anthu “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Mika 4:4.
Matenda akupha sadzakhalanso ochititsa mantha ndi kupha miyoyo. Lonjezo laumulungu nlakuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Nchochititsa chisangalalo chotani nanga!
Mantha a upandu ndi chiwawa adzakhalanso zinthu zakale. Salmo 37:10, 11 limalonjeza kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”
Kodi mantha alerolino adzaloŵedwa m’malo motani ndi mtendere weniweni ndi chisungiko? Mwa njira ya boma limodzi lolungama—Ufumu wa Mulungu. Ponena za nthaŵi yathu, Danieli 2:44 amati: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. nudzakhala chikhalire.” Mfumu yoikidwa ya Yehova, Yesu Kristu, ‘ayenera kulamulira kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake.’ (1 Akorinto 15:25) Ulamuliro wa Yesu wa Zaka Chikwi udzakwaniritsa chifuno choyambirira cha Mulungu cha kukhala ndi dziko lapansi laparadaiso lokhalidwa kwamuyaya ndi anthu achimwemwe.—Luka 23:43; Chivumbulutso 20:6; 21:1-5.
M’dziko lapansi Laparadaiso limenelo, mudzakhala mantha oyenera amodzi. Adzakhala “kuwopa Yehova.” (Miyambo 1:7) Ndithudi, tiyenera kukhala ndi mantha ameneŵa ngakhale tsopano, popeza kuti ali ulemu wakuya ndi mantha limodzi ndi kuwopa kusakondweretsa Mulungu chifukwa chakuti timayamikira ukoma ndi ubwino wake. Mantha ameneŵa amafuna kuti tikhulupirire Yehova kotheratu ndi kummvera mokhulupirika.—Salmo 2:11; 115:11.
Zochitika zowopsa zikuzindikiritsa ano kukhala masiku otsiriza. Komabe, ngati tisonyeza chikondi chathu pa Mulungu, tingasangalale mmalo mwa kukhala amantha. Maulosi a Baibulo akusonyeza kuti kuthetsa kwaumulungu kwa dziko lino kuli pafupi. Lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lachilungamo lolonjezedwa ndi Yehova Mulungu. (2 Petro 3:13) Indedi, pansi pa ulamuliro wa Ufumu posachedwapa padzakhala dziko lopanda mantha osayenerera.
[Bokosi patsamba 6]
MPHAMVU YA KOPE LIMODZI
TOMASZ, mwamuna wachichepere wa ku Poland, anapalamula mlandu wakuswa lamulo umene unamchititsa kuthaŵa m’dzikolo. Kwa miyezi isanu ndi umodzi anakwera matola kudutsa Ulaya, akumagona m’hema ndi kugwira ntchito zosiyanasiyana. Panthaŵiyo, funso limodzi linali m’maganizo mwake nthaŵi zonse: Kodi chifuno cha moyo nchiyani?
Funso la Tomasz linayankhidwa pamene anapatsidwa kope la Nsanja ya Olonda la Chipolishi. Iye analiŵerenga nthaŵi zingapo ndi kuzindikira kuti magaziniwa anali ndi choonadi chimene anakhala akuchifunafuna. Tomasz anakwera matola mtunda wa makilomita 200 kupita ku ofesi yanthambi ya Watch Tower ku Selters/Taunus, Germany. Akumafika pa Lolemba madzulo, iye anatulutsa magazini ake a Nsanja ya Olonda ndi kunena kuti: “Ndingakonde kuti munthu wina alongosole zochuluka ponena za zimene zili m’magazini awa. Kodi ndifunikira kuchita chiyani?”
Madzulo amenewo, Mboni za Yehova ziŵiri zinalankhula ndi Tomasz ponena za chifuno cha moyo, zikumagwiritsira ntchito Baibulo monga maziko a kukambitsirana kwawo. Pokhala wofunitsitsa kuphunzira zambiri, Tomasz anabwerera ku ofesi yanthambiyo tsiku lililonse mlungu umenewo, akumaphunzira Baibulo ndi buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.
Tomasz anasankha zobwerera ku Poland, ngakhale kuti akakumana ndi mavuto kumeneko. Chotero, pa Lachisanu, masiku anayi okha pambuyo pa kufika kwake pa ofesi yanthambi ya Selters, Tomasz ananyamuka kubwerera kwawo. Panthaŵi yomweyo anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova mu Poland. Tomasz anapita patsogolo mofulumira ndipo anayamba kulankhula mwachangu kwa ena ponena za zimene anali kuphunzira. Mu October 1993, miyezi inayi yokha pambuyo pa ulendo wake woyamba ku Selters, anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova.
Kope limodzi lokha la Nsanja ya Olonda linathandiza mwamuna wachichepere ameneyu kufufuza chifuno cha moyo!
[Chithunzi patsamba 7]
Pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Yesu Kristu, mantha sadzagwiranso dziko