Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/15 tsamba 8-9
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Colombia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Colombia
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Akuluakulu Amalonda Anachita Chidwi
  • Choonadi Chifikira a Mitundu Yonse
  • Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo
    Galamukani!—2001
  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Chionetsero Chokhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Ufulu Wauzimu m’Colombia
    Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/15 tsamba 8-9

Mboni za Yehova Padziko Lonse​—Colombia

COLOMBIA ndi dziko lapadera la ku South America. Nyanja zazikulu zamchere ziŵiri za Atlantic ndi Pacific zimakhudza gombe la dziko la volcano limeneli. Kutentha kwa magombe otsika a kumalo otentha ndi zigwa kumasiyana ndi kuzizira kwa kumalo okwera, a mapiri okutidwa ndi chipale chofeŵa a Andes.a

Ngakhale kuti Colombia ngwotchuka chifukwa cha golidi ndi ma emerald, anthuwo ndiwo chuma chake chamtengo koposa. Lerolino, Yehova akudzaza nyumba yake yauzimu ndi ulemerero. Olambira okongola, ofunika akuthamangiramo m’mbali zonse za dziko lapansi, kuphatikizapo Colombia.​—Hagai 2:7.

Akuluakulu Amalonda Anachita Chidwi

Sande, November 1, 1992, linali deti la kupatuliridwa kwa ofesi yanthambi yatsopano ya Watch Tower Society ndi nyumba yosindikizira pa Facatativá, makilomita 42 kumpoto koma chakumadzulo kwa Bogotá. Maulendo oyendera nthambiyo akhala ndi chiyambukiro chachikulu pa alendo. Pamene anabwerera ku fakitale kumene amagwira ntchito, mlendo wina motenthedwa maganizo anasonkhezera amanijala ake kupita ndi kukaona gulu limene lili ‘chozizwitsa cha kugwira bwino ntchito, dongosolo, ndi mzimu wantchito wosonyezedwa ndi antchito.’ Mkati mwa ulendo wawo woyendera wotsatira, akuluakuluwo anasonyeza chikondwerero chachikulu ndipo anafunsa mafunso ambiri.

Akuluakulu ameneŵa anafuna kutumiza oyang’anira, olangiza, ndi akapitawo awo​—kwenikweni, antchito awo onse​—pa ulendo wodzayendera. Mlungu uliwonse, anandandalika antchito 15 kufikira 25 kudzayendera kufikira gulu lonse la antchito 1,300 litaona kugwira bwino kwa gulu koteroko.

Mazana a antchito awo anayendera malo a nthambiyo ndi kuona vidiyo ya Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name. Atachita chidwi ndi ukulu wa gululo ndi kufalikira padziko lonse kwa ntchito yolalikira Ufumu, iwo anadabwa ndi kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga limene limagwiritsiridwa ntchito ndi Sosaite. Pamene anali kuchoka, ambiri anamvedwa akunena kuti akumva ngati kuti ‘akuchoka m’Paradaiso kubwerera ku dziko la msokonezo.’

Choonadi Chifikira a Mitundu Yonse

Mitundu yonse ya anthu ikufikiridwa ndi mbiri yabwino. (1 Timoteo 2:3, 4, NW) Mwachitsanzo, yemwe kale anali wolemba nyimbo ndi mtsogoleri wa gulu loimba la roko la heavy-metal analandira choonadi cha Baibulo, anapanga masinthidwe m’moyo wake, ndipo posakhalitsa anakhala mpainiya wokhazikika. Pambuyo pake anaikidwa kukhala mtumiki wotumikira. Anthu angapo omwe anali ziŵalo za magulu opandukira aphunzira kuika chidaliro ndi chiyembekezo chawo mu Ufumu wa Yehova. Iwo tsopano ali odziloŵetsa mokangalika m’kulalikira uthenga wa dziko latsopano lamtendere.

Omwerekera ndi ogulitsa mankhwala oledzeretsa atembenukiranso ku choonadi. Mwamuna wina wachichepere amene tsopano ndi Mboni anakhala akusamalira munda wa mankhwala oledzeretsa ndi laboratory ya cocaine m’nkhalango kwa zaka zisanu asanamasuke ku moyo wa mtundu umenewo. Iye wapeza chimwemwe m’kuphunzira ndi kuchita malamulo a mkhalidwe a Baibulo. M’nyumba yandende akupha anthu mwachiwembu oweruzidwa osonkhezeredwa ndi phunziro loona mtima la Baibulo akupemphera moona mtima kuti Yehova awakhululukire machimo awo ndi kuwalandira monga atumiki ake.

Ndi mmene zilili kuti anthu a mitundu yonse akulandira uthenga wa Ufumu. Mu Colombia, limodzinso ndi kwina konse, Yehova akudzazadi nyumba yake ndi ulemerero.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.

[Bokosi patsamba 8]

ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO

Chaka Chautumiki cha 1993

CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 60,854

KUGAŴA: Mboni 1 kwa 558

OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 249,271

AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 8,487

AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 100,927

CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 5,183

CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 751

OFESI YA NTHAMBI: FACATATIVÁ

[Chithunzi patsamba 9]

Ogwira ntchito pa ofesi ya nthambi ndi amishonale mu 1956

[Chithunzi patsamba 9]

Chinthunzi chojambulidwira m’mlengalenga cha ofesi yanthambi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena