Olengeza Ufumu Akusimba
“Chikumbutso cha Mzimu wa Mgwirizano”
PAFUPI ndi kummwera kwenikweni kwa nsonga ya Spain kuli thanthwe lalitali lalikulukulu la njereza lodziŵika monga Rock of Gibraltar. Kwa zaka mazana ambiri, thanthwe limeneli lakhala mboni yosalankhula pa mkangano wa ndale zadziko ndi kusagwirizana kwa maiko. Mosiyana ndi zimenezo, posachedwapa Rock of Gibraltar anali malo a chisonyezero cha mgwirizano ndi umodzi wosaonekaoneka m’dziko lerolino.
Makilomita atatu okha kuchokera kumene kuli Rock kuli tauni ya La Línea, ku Spain. Kumeneko kumangidwa kwa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kunabweretsa pamodzi antchito odzifunira mazana ambiri ofunitsitsa kuchirikiza ndi nthaŵi yawo ndi nyonga. Pamene anali kugwira ntchito zolimba kumanga malo oyenera olambirira Mlengi, Yehova Mulungu, kufunika kwa malo aulemerero a Rock of Gibraltar kunazimiririkadi poyerekezera ndi ntchito imene inalipo.
Olengeza Ufumu ku mbali imeneyo ya dziko akutumiza lipoti lotsatirali:
“Antchito odzifunira osangalala mazana asanu ndi anayi anagwira ntchito usana ndi usiku, kuyambira pa Lachisanu masana, September 24, 1993. Podzafika 7 koloko Lamlungu usiku, chikwangwani chatsopano chodziŵikitsira nyumbayo monga Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova chinali chitaimikidwa, ndipo nyumba yatsopano yokongolayo inali kugwiritsiridwa ntchito kaamba ka msonkhano wake wapoyera woyamba weniweni.
“Mboni zambiri za ku madera apafupi a Gibraltar zinadutsa malire kukathandiza abale awo a ku Spain. ‘Magaŵano a ndale samathetsa ubale wathu wamitundu yonse,’ anafotokoza motero wantchito wina wodzifunira, nzika ya Gibraltar. Anawonjezera kuti: ‘Zaka zingapo zapitazo, mabwenzi a ku La Línea anadzatithandiza kumanga Nyumba yathu Yaufumu mu Gibraltar, chotero tili achimwemwe tsopano kuti tiwachitire mofananamo.’
“Kuti uchirikize zoyesayesa zowoloŵa manjazo za mipingo iŵiri ya Mboni za Yehova ndi othandiza aluso mazana ambiri a ku chigawo cha Andalusia, mzinda wa La Línea unagamula zopereka malo oyenera. ‘Mwamwambo, boma la Spain nthaŵi zonse lapereka malo a nyumba za matchalitchi a Katolika,’ anafotokoza motero meya wa La Línea pochezera malo omangapowo. ‘Kodi tilekerenji kuchita chimodzimodzi kwa magulu ena a zipembedzo? Ndili ndi chidwi kwambiri ndi kusadzikonda kwa antchito odzifunira, ndipo ndikulingalira kuti ayenera kupatsidwa chichirikizo chathu. Tifunikira mzimu wochuluka wamtundu umenewu m’dziko logawanika lalerolino.’
“Anatchula Nyumba Yaufumuyo kukhala ‘chikumbutso cha mzimu wa mgwirizano.’ Ndithudi, mbali yochititsa chidwi kwambiri sinali mamangidwe ake kapena ukulu wa nyumbayo. Mmalo mwake, chimene chinachititsa chidwi ambiri m’chitaganyacho chinali chakuti inamangidwa kokha ndi antchito odzifunira ndipo inaima m’maola 48 okha!”
Nkwachionekere kuti Mboni za Yehova mu La Línea ndi madera ake ozungulira zakhala zokhulupirika pa mawu a Agalatiya 6:10. Pamenepo mtumwi Paulo analangiza okhulupirira anzake kuti: “Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”