Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/10 tsamba 29
  • ‘Kuthetsa Mtima Wodzikonda’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kuthetsa Mtima Wodzikonda’
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • “Lolimba Ngati Thanthwe la Gibraltar”
    Galamukani!—1990
  • “Chikumbutso cha Mzimu wa Mgwirizano”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Anyani Odabwitsa a M’matanthwe
    Galamukani!—2008
  • Mmene Anthu Akuwonjezekera Pakufunika Nyumba Zina Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 1/10 tsamba 29

‘Kuthetsa Mtima Wodzikonda’

● DZIKO la Gibraltar, lomwe lili kum’mwera kwenikweni kwa chilumba cha Iberia, lakhala likuukiridwa ndi asilikali a mayiko ena kwa zaka zambiri. Tsiku lina mu October 2008, kunabwera anthu pafupifupi 1,000 ochokera ku Spain. Koma anthu amenewa anabwerera zamtendere osati kudzachita nkhondo. Iwo anabwera kudzamanga Nyumba ya Ufumu yoti mipingo iwiri ya Mboni za Yehova izigwiritsa ntchito.

Nduna yaikulu ya dziko la Gibraltar inauza olemba Galamukani! kuti anthu a m’dziko lake analandira ndi manja awiri anthu amene anabwera kudzagwira ntchitoyi. Iye ananena kuti zimene anthuwo anabwerera “n’zothandiza kwambiri pa chitukuko cha deralo.” Ananenanso kuti “gulu la Mboni za Yehova limeneli linali lalikulu kuposa magulu ena onse amene anabwerapo m’dzikoli kudzagwira ntchito yotere. Ndipo chochititsa chidwi kwambiri ndi chakuti ntchitoyi inali yongodzipereka.”

Akuluakulu a boma anathandiza pa ntchitoyi kuchokera pamene inayamba. Iwo anapatsa Mboni za Yehova malo abwino oti amangepo nyumbayi. Kodi n’chiyani chinachititsa akuluakuluwa kuti athandize pa ntchitoyi?

Ndunayo inati: “Ndimakhulupirira kuti zinthu zimayenda bwino m’dziko mukakhala anthu oopa Mulungu. Anthu onse kuno ku Gibraltar ali ndi ufulu wopembedza, ndipo boma lili ndi udindo woonetsetsa kuti palibe chipembedzo chimene chikusalidwa. Ndipo nyumba yolambirira imene a Mboniwa amanga ithandiza kwambiri pa chitukuko cha derali.

Iye anawonjezeranso kuti: “Tiyenera kuthetsa mtima wodzikonda. Ndipo gulu la Mboni za Yehova lomwe linabwera kudzagwira ntchito kuno lasonyeza kuti zimenezi n’zotheka.”

Ngakhale kuti mphepo yamkuntho inachititsa kuti ntchitoyi ichedwe kuyamba, Nyumba ya Ufumu imeneyi inatenga masiku atatu okha kuti ithe, kuyambira Loweruka kufika Lolemba. Secundino Nogal, yemwe ankayang’anira ntchitoyi, anati: “Ngakhale kuti ntchitoyi inkafunika kutha Lamlungu, ambiri mwa anthuwa anadzipereka kuti akhalebe ku Gibraltar tsiku lina limodzi n’cholinga choti amalize ntchitoyi. Ife tinazolowera kuthana ndi mavuto. Ntchito yathu imafuna kudzipereka. Komanso kupewa mtima wodzikonda n’kofunika kwambiri kuti tigwire ntchitoyi. N’chifukwa chake timasangalala kwambiri kugwira ntchito zotere.”a

[Mawu a M’munsi]

a Nyuzipepala ina kumeneko inanena kuti: “Panthawi imene mphepo yamkuntho imagwetsa nyumba, Mboni za Yehova zinali zotanganidwa kumanga tchalitchi chawo [Nyumba ya Ufumu]. Panali anthu ambiri ongodzipereka ndipo anamaliza ntchitoyi m’masiku atatu okha.”—Gibraltar Chronicle.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena