Sayansi, Chipembedzo, ndi Kufunafuna Choonadi
“Kufalikira kwa zipembedzo zambiri zonyenga . . . kunandiyambukira kumlingo wina wake.”—Charles Darwin
KUCHIYAMBIYAMBI kwa zaka za zana la 19, sayansi ndi chipembedzo zinali ndi unansi wabwino. “Ngakhale m’zolemba za sayansi,” likutero buku lakuti Darwin: Before and After, “olemba ake sanazengereze kulankhula za Mulungu mwanjira imene mwachionekere inali yachibadwa ndi yoona mtima.”
Buku la Darwin la Origin of Species linathandizira kusintha zimenezo. Sayansi ndi chisinthiko zinadzakhala paunansi umene unachititsa chipembedzo—ndi Mulungu—kunyalanyazidwa. “Malinga ndi kulingalira kwa achisinthiko,” akutero Bwana Julian Huxley, “kukhalako kwa wam’mwambamwamba sikulinso kofunikira kapena koyenera.”
Lerolino nthanthi ya chisinthiko imanenedwa kuti ndiyo maziko a sayansi ofunika koposa. Chifukwa chachikulu cha unansiwo chikusonyezedwa ndi katswiri wa physics Fred Hoyle: “Nkhaŵa yaikulu ya asayansi osunga mwambo ili pa kuletsa kubukanso kwa malingaliro onkitsa akale achipembedzo mmalo moyembekezera choonadi mwachidwi.” Kodi ndi malingaliro onkitsa otani amene achititsa sayansi kunyansidwa kwambiri ndi chipembedzo?
Chipembedzo Chidzetsa Mbiri Yoipa pa Chilengedwe
Polingalira kuti akuyesa kuchirikiza Baibulo, “ochirikiza chilengedwe”—mogwirizana kwambiri ndi Aprotesitanti omasulira zinthu mmene zilili—aumirira kuti dziko lapansi ndi chilengedwe chonse zakhalako kwa zaka zosakwanira 10,000. Lingaliro lonkitsa limeneli lachititsa kusuliza kwa akatswiri a geology, openda zakuthambo, ndi akatswiri a physics, popeza kuti limatsutsa zopeza zawo.
Koma kodi Baibulo limanenanji kwenikweni? “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Utali wa nthaŵi imene zimenezo zinatenga sukutchulidwa. “Tsiku loyamba” la kulenga silikutchulidwa konse kufikira pa Genesis 1:3-5. “Kumwamba ndi dziko lapansi” zinaliko kale pamene “tsiku” loyamba limeneli linayamba. Chotero, kodi kumwamba ndi dziko lapansi zingakhale zili ndi zaka mamiliyoni zikwi zambiri, monga momwe asayansi amanenera? Mwina zingakhaledi choncho. Baibulo silimatchula konse nthaŵi imene zochitikazo zinatenga.
Lingaliro lina lonkitsa la chipembedzo limanena za njira imene ena amamasulirira ‘masiku’ asanu ndi limodzi a kulenga. Anthu ena omasulira zinthu mmene zilili amaumirira kuti masiku ameneŵa anali enieni, akumapanikiza kulengedwa kwa za padziko lapansi m’nyengo ya maola 144. Zimenezi zimabutsa chikayikiro cha asayansi, popeza kuti iwo amaona kuti lingaliro limeneli limaombana ndi maumboni a sayansi oonekera bwino.
Komabe, ndi kumasulira Baibulo kochitidwa ndi omasulira zinthu mmene zilili—osati Baibulo lenilenilo—kumene kuli kosemphana ndi sayansi. Baibulo silimanena kuti “tsiku” lililonse la kulenga linali lautali wa maola 24; ndithudi, limaphatikiza pamodzi ‘masiku’ onse amenewo kukhala “tsiku [lotalikirapo] lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba,” kusonyeza kuti si ‘masiku’ onse a m’Baibulo amene anali chabe ndi maola 24. (Genesis 2:4) Ena ayenera kukhala anali azaka zikwi zambiri.a
Motero, ochirikiza chilengedwe ndi omasulira zinthu mmene zilili adzetsa mbiri yoipa pa chikhulupiriro cha chilengedwe. Ziphunzitso zawo ponena za nyengo ya kukhalapo kwa chilengedwe chonse ndi utali wa ‘masiku’ a kulenga nzosagwirizana ndi sayansi yolongosoka ngakhale ndi Baibulo lomwe. Komabe, palinso malingaliro ena onkitsa amene achititsa asayansi kunyansidwa ndi chipembedzo.
Kugwiritsira Ntchito Molakwa Mphamvu
M’mbiri yonse ya anthu, chipembedzo chachititsa chisalungamo chochuluka. Mwachitsanzo, chiphunzitso cha chilengedwe chinapotozedwa m’Nyengo Zapakati pofuna kulungamitsa chichirikizo cha tchalitchi pa ulamuliro wotsendereza wa munthu mmodzi ku Ulaya. Chikhulupiriro chake chinali chakuti Mulungu ndiye anapatsa anthu malo awo, achuma kapena osauka. Buku la The Intelligent Universe limafotokoza kuti: “Ana aamuna ocheperapo a anthu achuma ankauzidwa kuti anali ‘makonzedwe a Mulungu’ kuti iwo azilandira chuma chochepa cha banja kapena kusalandira chilichonse, ndipo munthu wogwira ntchito ankafulumizidwa nthaŵi zonse kukhalabe wokhutira ndi ‘malo amene Mulungu anakonda kumpatsa.’”
Nkosadabwitsa kuti ambiri amawopa kubukanso kwa “malingaliro onkitsa akale achipembedzo”! Mmalo mwa kukhutiritsa kusoŵa kwauzimu kwa munthu, chipembedzo kaŵirikaŵiri chakudyerera. (Ezekieli 34:2) Nkhani ya mkonzi m’magazini a India Today ikuti: “Ndi mbiri imene chapanga m’nyengo zonse, nkodabwitsa kuti chipembedzo chakhalabe choyanjidwa. . . . M’dzina la Mlengi Wamkulu, . . . anthu achitira anthu anzawo nkhanza zonyansa koposa.”
Mbiri yoipa ya chipembedzo chonyenga inayambukiradi kulingalira kwa Darwin. “M’kupita kwa nthaŵi ndinasiya kukhulupirira Chikristu monga vumbulutso la Mulungu,” iye analemba motero. “Kufalikira kwa zipembedzo zambiri zonyenga konga lupsa m’zigawo zazikulu za dziko lapansi kunandiyambukira kumlingo wina wake.”
Kulakika kwa Chipembedzo Choona
Chinyengo chachipembedzo sichili chatsopano m’dziko lino. Yesu anati kwa atsogoleri achipembedzo ofuna mphamvu a m’tsiku lake: “Muoneka ngati anthu abwino kunja—koma mkati mwanu ndinu odzala chinyengo ndi kuipa.”—Mateyu 23:28, Phillips.
Komabe, Chikristu choona ‘sichili cha dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Otsatira ake samatenga mbali m’chipembedzo choipa ndi m’ndale; ndipo samasokeretsedwa ndi nthanthi zimene zimakana kukhalako kwa Mlengi. “Nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu,” analemba motero mtumwi Paulo.—1 Akorinto 3:19.
Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti Akristu enieni alibe chidziŵitso cha sayansi. Mosiyana ndi zimenezo, chipembedzo choona chimakondwera ndi sayansi. “Kwezani maso anu kumwamba, muone,” Yesaya mneneri wakale anauzidwa zimenezo. “[Ndani, NW] amene analenga izo?” (Yesaya 40:26) Mofananamo, kuti adziŵe bwino Mlengi, Yobu anapemphedwa kupenda zodabwitsa za m’chilengedwe za padziko lapansi ndi kumwamba.—Yobu, machaputala 38-41.
Inde, awo okhulupirira mwa Mlengi amaona chilengedwe ndi mantha aulemu. (Salmo 139:14) Ndiponso, amakhulupirira zimene Mlengiyo, Yehova Mulungu, amanena ponena za chiyembekezo chabwino koposa cha mtsogolo. (Chivumbulutso 21:1-4) Mwa kuphunzira Baibulo, anthu mamiliyoni ambiri akuphunzira kuti magwero a munthu kapena mtsogolo mwake sizimadalira pa zinthu zongochitika zokha. Yehova anali ndi chifuno popanga munthu, ndipo chifuno chimenecho chidzakwaniritsidwa—kudalitsa anthu onse omvera. Tikukupemphani kufufuza nkhaniyo inu mwini.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Awake!, November 8, 1982, masamba 6-9, ndi Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 545, zofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Kuti mupeze mawu owonjezereka onena za kukhulupirira chilengedwe ndi kuombana kwake ndi sayansi ndi Baibulo, onani makope a Awake! a March 8, 1983, masamba 12-15, ndi March 22, 1983, masamba 12-15.
[Bokosi patsamba 6]
KODI SADZIŴA UMBONI?
“NGAKHALE Mboni za Yehova zaphunzira zambiri ponena za biology,” analemba motero loyayo Norman Macbeth m’buku lake la mu 1971 la Darwin Retried—An Appeal to Reason. Ataŵerenga nkhani ya mu Galamukani! yonena za chisinthiko, Macbeth anati: “Ndinadabwa kupeza kuti inali ndi zigomeko zanzeru zotsutsa chiphunzitso cha Darwin.” Poona maumboni akuya ndi mawu anzeru onenedwa ndi akatswiri a nkhaniyo, mlembiyo anamaliza kuti: “Simpson salinso wolondola ponena kuti: ‘. . . mwachionekere pafupifupi onse amene samakhulupirira icho [chisinthiko] sadziŵa umboni wa sayansi.’”
[Chithunzi patsamba 7]
Zinthu zongochitika zokha sindizo zidzadzetsa mtsogolo mwa mtundu wa anthu