Wachimwemwe mu Ubale Weniweni wa Padziko Lonse
YOSIMBIDWA NDI WILLIE DAVIS
Mu 1934 Kugwa kwa Chuma Kwakukulu kunali pa dziko, ndipo United States anali m’mavuto aakulu a zachuma. Kunja kwa malo otchedwa Prospect Relief Station mu Cleveland, Ohio, kunali ndewu pakati pa wapolisi ndi Wakomyunizimu wokangalika. Wapolisiyo anawombera ndi kupha Wakomyunizimuyo ndi wina woima pambali, agogo anga aakazi, a Vinnie Williams.
AKOMYUNIZIMU anayesa kutembenuza imfazo kukhala mkangano wa fuko, popeza kuti agogo angawo anali akuda ndipo wapolisiyo anali mzungu. Iwo anafalitsa mapepala olembedwapo mitu yankhani yonga wakuti “Polisi ya Cleveland Yatsankho la Fuko” ndi wakuti “Bwezerani Kupha Kumeneku.” Akomyunizimuwo anakonza ndi kusamalira maliro a agogo anga. Ndili nacho chithunzi cha onyamula bokosi la maliro—onsewo azungu ndipo onsewo ziŵalo za chipani. Aliyense wa iwo ataumba nkhonya atainyamula m’mwamba mwa kachitidwe kamene pambuyo pake kanadzatengedwa kukhala chizindikiro cha Black Power.
Pamene agogo anga anamwalira, mwana wawo wamkazi anali ndi ine m’mimba mwake, ndipo pambuyo pa miyezi inayi ndinabadwa. Ndinakula ndi ulema wa kulankhula. Sindinkatha kulankhula popanda kuchita chibwibwi, motero sukulu yanga yoyambirira inaphatikizapo chithandizo cha kulankhula.
Makolo anga analekana pamene ndinali ndi zaka zisanu, ndipo ine ndi mlongo wanga tinaleredwa ndi amayi athu. Pamene ndinali ndi zaka khumi, ndinayamba kugulitsa malonda a zinthu zogwiritsira ntchito panyumba nditaŵeruka kusukulu kuti ndithandize kupeza ndalama za banja. Pambuyo pa zaka ziŵiri ndinayamba kugwira ntchito ndisanapite kusukulu ndi pambuyo pake pomwe, ndikumakhala wodyetsa banja. Pamene Amayi anasungidwa m’chipatala nafunikira maopaleshoni angapo, ndinaleka sukulu ndi kuyamba kugwira ntchito ya tsiku lonse.
Kudziŵitsidwa Ubalewo
Mu 1944 mmodzi wa Mboni za Yehova anasiira mkazi wa msuwani wanga buku lakuti “The Truth Shall Make You Free,” ndipo ndinadziloŵetsa m’phunziro la Baibulo limene linayambidwa kwa iye. Chaka chimodzimodzicho ndinayamba kufika pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki mu Mpingo wa Eastside. Mlangizi wa sukulu, Albert Cradock, anali ndi vuto lakulankhula limene ndinali nalo, koma anaphunzira kulilamulira. Anandilimbikitsa chotani nanga!
Anthu ochuluka kumalo omwe tinkakhala anali Ataliyana, Apolishi, Ahangariya, ndi Ayuda, ndipo mpingo unapangidwa ndi anthu a mafuko ameneŵa ndi ena. Mkazi wa msuwani wanga ndi ine tinali pakati pa Amereka Achiafirika oyamba kuyanjana ndi mpingo umenewu wa azungu okhaokha, koma Mbonizo sizinasonyeze konse tsankhu la fuko kwa ife. Ndiponso, iwo anandiitana nthaŵi zonse kunyumba zawo kuchakudya.
Mu 1956, ndinasamukira kummwera kwa United States kukatumikira kumene kusoŵa kwa atumiki kunali kokulira. Pamene ndinabwerera kumpoto m’chilimwe china ku msonkhano wachigawo, abale ambiri mu Cleveland anadzandiona ndi kusonyeza chidwi chachikulu pa ntchito zanga. Kudera nkhaŵa kwawo kunandiphunzitsa phunziro lofunika kwambiri: Nthaŵi zonse “munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”—Afilipi 2:4.
Utumiki Wanthaŵi Yonse Wofutukulidwa
Nditagwira ntchito kwa zaka zitatu m’ntchito yolalikira yanthaŵi yonse monga mpainiya, mu November 1959, ndinaitanidwa kukagwira ntchito pa Beteli ya Brooklyn, malikulu a padziko lonse a Mboni za Yehova mu New York. Ndinagaŵiridwa ku Dipatimenti ya Mitokoma. Woyang’anira wa dipatimenti yathu, Klaus Jensen, ndi mnzanga wa m’chipinda, William Hannan, onse azungu, anakhala atate anga auzimu. Aliyense wa iwo anali atatumikira kwa zaka pafupifupi 40 pa Beteli pofika panthaŵi imene ndinafika.
Kuchiyambi kwa ma 1960, ziŵalo za banja la Beteli zinali pafupifupi 600, ndipo pafupifupi 20 anali Amereka Achiafirika. Panthaŵiyo, mkangano wa fuko unayamba kukula mu United States, ndipo maunansi a mafuko anayamba kuipa. Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti “Mulungu alibe tsankhu,” ndipo nafenso sitiyenera kukhala nalo. (Machitidwe 10:34, 35) Makambitsirano a zauzimu amene tinali nawo pa Beteli m’mawa uliwonse analimbikitsa kufunitsitsa kwathu kulandira lingaliro la Mulungu pankhani zimenezo.—Salmo 19:7.
Pamene ndinali kutumikira pa Beteli ya Brooklyn ndinakumana ndi Lois Ruffin, mpainiya wa ku Richmond, Virginia, ndipo tinakwatirana mu 1964. Chifuno chathu chinali cha kukhalabe mu utumiki wanthaŵi yonse, motero titakwatirana tinabwerera kummwera kwa United States. Choyamba tinatumikira monga apainiya apadera, ndiyeno mu 1965, ndinapemphedwa kuyamba ntchito ya dera. Kwa zaka khumi zotsatira, tinachezera mipingo m’maboma a Kentucky, Texas, Louisiana, Alabama, Georgia, North Carolina, ndi Mississippi.
Chiyeso pa Ubale Wathu
Zaka zimenezo zinali za kusintha kwakukulu. Tisanasamukire Kummwera, mafuko anali atagaŵanika. Anthu akuda analetsedwa ndi lamulo kuloŵa masukulu amodzimodzi ndi azungu, kudyera m’malesitiranti amodzimodzi, kugona m’mahotela amodzimodzi, kugula kumasitolo amodzimodzi, ngakhale kumwera pampopi umodzimodzi. Koma mu 1964 bwalo la United States Congress linapereka lamulo la Civil Rights Act limene linaletsa tsankhu m’malo aunyinji, kuphatikizapo m’zoyendera. Motero panalibenso maziko alamulo a tsankhu la fuko.
Motero funso linali lakuti, kodi abale ndi alongo athu m’mipingo ya akuda okhaokha ndi ya azungu okhaokha akagwirizana ndi kusonyezana chikondi kapena kodi chitsenderezo chochokera kwa anthu m’chitaganya ndi udani waukulu wakale zikawachititsa kukana kugwirizana kumeneko? Linali vuto kulabadira lamulo la m’Malemba lakuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.”—Aroma 12:10.
Kwa nthaŵi yaitali kwambiri, lingaliro lofala, makamaka Kummwera, linali lakuti akuda anali apansi. Lingaliro limeneli linali litakhomerezedwa kwambiri m’maganizo mwa anthu m’mbali iliyonse ya chitaganya, kuphatikizapo matchalitchi. Motero sikunali kopepuka kwa azungu ena kuona akuda monga olingana nawo. Ndithudi, imeneyo inali nthaŵi ya kuyesedwa kwa ubale wathu—kwa akuda ndi azungu omwe.
Mokondweretsa, ambiri analandira bwino lomwe kugwirizanitsidwa kwa mipingo yathu. Malingaliro a tsankhu la fuko ophunzitsidwa mwakhama kwa zaka mazana ambiri sanafafanizike mofulumira. Komabe pamene kugwirizanako kunayamba, kunalandiridwa bwino lomwe ndi abale athu, ndipo ambiri anasangalala kukhala okhoza kusonkhana pamodzi.
Mosangalatsa, ngakhale osakhala Mboni kaŵirikaŵiri anachirikiza kugwirizana kwa mipingo yathu. Mwachitsanzo, mu mzinda wa Lanett, Alabama, okhala pafupi ndi Nyumba Yaufumu anafunsidwa ngati iwo anali otsutsa lingaliro lakuti akuda azibwera ku misonkhano. Mzungu wina wokalamba wamkazi anagwirana chanza ndi mbale wakuda, akumati: “Tabwerani kuno kwathu ndi kudzalambira Mulungu wanu mmene mufunira!”
Abale Okhulupirika mu Ethiopia
Mu 1974 tinasangalala kulandira maphunziro a miyezi isanu ndi theka a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu New York City. Ndiyeno tinatumizidwa ku dziko la mu Afirika la Ethiopia. Haile Selassie, mfumuyo, anali atangochotsedwa kumene pa ufumu ndi kumangidwira panyumba. Popeza kuti ntchito yathu yolalikira inali italetsedwa, tinayamikira kwambiri umodzi wachikondi wa ubale wathu Wachikristu.
Tinakhala pamodzi ndi kutumikira ndi ambiri amene pambuyo pake anaponyedwa m’ndende chifukwa cha kumamatira kwawo ku kulambira koona. Ena a mabwenzi athu apamtima ananyongedwadi. Adera Teshome anali mkulu mnzanga mu mpingo wa likulu la Ethiopia, Addis Ababa.a Patapita zaka zitatu ali m’ndende, ananyongedwa. Mwachibadwa, mkazi wake anagwidwa ndi chisoni kwambiri. Kunali kosangalatsa chotani nanga kumuona pambuyo pa zaka zambiri ali ndi nkhope yachimwemwe akutumikira monga mpainiya!
Worku Abebe, mbale wina wokhulupirika, anapatsidwa chiweruzo cha imfa kasanu ndi katatu.b Koma iye sanawopsezedwe! Pamene ndinamuona kwa nthaŵi yotsirizira, anandisonyeza makutu ake amene alonda a m’ndende anawatswanya ndi thendere za mfuti. Iye ananena moseka kuti anadya thendere za mfuti monga mfisulo, chakudya chamasana, ndi mgonero. Ngakhale kuti anamwalira kalelo, abale amamkumbukirabe mwachikondi.
Hailu Yemiru ali mbale wina yemwe ndimakonda kumkumbukira.c Iye anasonyeza chikondi chapadera kwa mkazi wake. Mkazi wakeyo adamangidwa, koma popeza kuti anali ndi pathupi ndipo anali pafupi kuona mwana, Hailu anapempha akuluakulu a ndende kuti atenge malo a mkazi wake m’ndende. Pambuyo pake, pamene anakana kulolera molakwa chikhulupiriro chake, ananyongedwa.—Yohane 15:12, 13; Aefeso 5:28.
Chifukwa cha mkhalidwe wa ndale woipiraipira mu Ethiopia, tinasamukira ku Kenya mu 1976. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri tinatumikira m’ntchito yoyendayenda, tikumachezera abale m’maiko ambiri a ku East Africa—kuphatikizapo Kenya, Ethiopia, Sudan, zisumbu za Seychelles, Uganda, ndi Tanzania. Ndinapitanso ku Burundi ndi Rwanda kangapo monga mmodzi wa gulu lokakambitsirana ndi akuluakulu a boma ponena za kulembetsa mwalamulo ntchito yathu m’maiko amenewo.
Kunali kosangalatsa kubwerera ku Ethiopia mu January 1992 kukapezeka pa msonkhano wachigawo woyamba kuchitidwa kumeneko pambuyo pa kuchotsedwa kwa chiletso pa ntchito yathu. Ambiri a oposa 7,000 opezekapo sanadziŵane, popeza kuti kalelo abalewo ankangosonkhana m’timagulu tating’ono. Tsiku lililonse la msonkhanowo, ambiri anali kufika maola aŵiri programu isanayambe ndipo pambuyo pake anakhalapobe kufikira madzulo kwambiri, akumasangalala ndi ubale wathu wachikondi.
Kusankhana Mtundu Kugonjetsedwa
Kwa zaka mazana ambiri kusankhana mtundu kwakhala kwakukulu mu Afirika. Mwachitsanzo, mu Burundi ndi Rwanda, mitundu yaikulu, Ahutu ndi Atutsi, akhala paudani kwa nthaŵi yaitali. Chiyambire pamene maikowa anapata ufulu kuchokera kwa Belgium mu 1962, anthu a mitundu iŵiriyo aphana nthaŵi ndi nthaŵi mwa zikwi zambiri. Chotero, nkosangalatsa chotani nanga kuona anthu a mitundu imeneyi omwe akhala Mboni za Yehova akumagwirira ntchito pamodzi mwamtendere! Chikondi chenicheni chimene amasonyeza kwa wina ndi mnzake chalimbikitsa ambiri kumvetsera zoona za Baibulo.
Mofananamo, mitundu ina mu Kenya inali ndi mikangano yawo. Pali kusiyana kwakukulu chotani nanga ndi ubale Wachikristu wa anthu a Yehova m’Kenya! Mungathe kuona anthu a mafuko osiyanasiyana akumalambira mogwirizana pa Nyumba Zaufumu. Ndakhala wokondwera kwabasi kuona ambiri a ameneŵa akutaya udani wawo wa pa mtundu ndi kusonyeza chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo awo a mafuko ena.
Wachimwemwe Kaamba ka Ubale Wathu
Pamene ndiyang’ana kumbuyo kwa zaka zoposa 50 za kuyanjana ndi gulu la Mulungu, chiyamikiro kwa Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, chimadzaza mtima wanga. Kwakhala kodabwitsa kuona zimene iwo achititsa padziko lapansi! Iyayi, sinthaŵi zonse pamene mikhalidwe yakhala bwino pakati pa anthu a Mulungu, ndipo siili motero lerolino. Koma sikungayembekezeredwe kuti maphunziro osankhana fuko ophunzitsidwa ndi dziko la Satana kwa zaka mazana ambiri angafafanizidwe tsiku limodzi. Ndi iko komwe, tidakali opanda ungwiro.—Salmo 51:5.
Pamene ndiyerekezera gulu la Yehova ndi dziko, mtima wanga umasefukira ndi chiyamikiro kaamba ka ubale wathu wenieni wa padziko lonse. Ndimakumbukirabe mokondwera abale aja mu Cleveland, onse azungu, omwe anandisamalira m’choonadi. Ndipo pamene ndinaona abale athu kummwera kwa United States, onse azungu ndi akuda omwe, akumavula mzimu wa tsankho ndi kuvala chikondi chaubale, mtima wanga unasangalala kwambiri. Ndiyeno, kupita ku Afirika ndi kudzionera ndekha mmene Mawu a Yehova angafafanizire maudani a pakati pa mafuko kwandichititsa kuzindikira bwino koposa ubale wathu wa padziko lonse.
Ndithudi, Mfumu Davide wakaleyo analongosola bwino lomwe pamene anati: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!”—Salmo 133:1.
[Mawu a M’munsi]
a Zithunzi za Adera Teshome ndi Hailu Yemiru zili patsamba 177 la 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses; chokumana nacho cha Worku chasimbidwa pamasamba 178-81.
b Zithunzi za Adera Teshome ndi Hailu Yemiru zili patsamba 177 la 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses; chokumana nacho cha Worku chasimbidwa pamasamba 178-81.
c Zithunzi za Adera Teshome ndi Hailu Yemiru zili patsamba 177 la 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses; chokumana nacho cha Worku chasimbidwa pamasamba 178-81.
[Chithunzi patsamba 23]
Maliro a agogo anga
[Chithunzi patsamba 24]
Mboni Zachitutsi ndi Zachihutu zikugwira ntchito pamodzi mwamtendere
[Chithunzi patsamba 25]
Limodzi ndi mkazi wanga, Lois