Kuvutika kwa Anthu Kodi kudzatha konse?
BOMBA litaphulika pa msika wa anthu ambirimbiri wa ku Sarajevo, paoneka zochititsa kakasi; kupha kwauchinyama ndi kupundula dala anthu mu Rwanda; ana owonda ndi njala akulimbanirana chakudya mu Somalia; mabanja ozunguzika maganizo olingalira zimene atayikiridwa nazo pambuyo pa chivomezi mu Los Angeles; anthu osoŵa chochita a ku Bangladesh wosakazidwa ndi kusefukira kwa madzi. Mikhalidwe yotero ya kuvutika kwa anthu imasonyezedwa kwa ife tsiku ndi tsiku pa TV kapena m’magazini ndi m’manyuzipepala.
Chiyambukiro chomvetsa chisoni cha kuvutika kwa anthu nchakuti kumachititsa anthu ena kutaya chikhulupiriro mwa Mulungu. “Nthaŵi zonse kukhalapo kwa kuipa kwakhala chopinga chachikulu koposa pa chikhulupiriro,” malinga ndi kunena kwa mawu ofalitsidwa ndi chitaganya cha Ayuda a ku United States. Olembawo akunena za imfa za m’misasa yachibalo ya Nazi yonga Auschwitz ndi za mabomba onga limene linaphulitsidwa pa Hiroshima. “Nkhani yonena za chifukwa chimene Mulungu wolungama ndi wamphamvu angalolere kupululutsidwa kwa anthu osachimwa ambirimbiri imavutitsa chikumbumtima cha munthu wachipembedzo ndipo imasokoneza maganizo,” akutero olembawo.
Mwachisoni, malipoti atsoka osathawo angachititse anthu kusagunda mtima. Malinga ngati mabwenzi ndi achibale awo sakuphatikizidwa, ambiri samavutika mtima kwambiri ndi kuvutika kwa ena.
Komabe, chenicheni chakuti timatha kuchita chifundo, makamaka ndi okondedwa athu, chiyenera kutidziŵitsa kanthu kena ponena za Mpangi wathu. Baibulo limanena kuti munthu analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu” ndipo “monga mwa chikhalidwe [chake].” (Genesis 1:26, 27) Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu ali ofanana ndi Mulungu m’kaonekedwe. Ayi, pakuti Yesu Kristu anafotokoza kuti “Mulungu ndiye mzimu,” ndipo “mzimu ulibe mnofu ndi mafupa.” (Yohane 4:24; Luka 24:39) Kukhala opangidwa m’chikhalidwe cha Mulungu kumatanthauza kuthekera kwathu kwa kusonyeza mikhalidwe yonga ya Mulungu. Chifukwa chake, popeza kuti anthu oganiza bwino amachitira chifundo awo amene amavutika, tiyenera kunena kuti Mlengi wa munthu, Yehova Mulungu, ngwachifundo ndi kuti amachitira chifundo kwambiri zolengedwa zake zaumunthu zovutika.—Yerekezerani ndi Luka 11:13.
Njira imodzi imene Mulungu wasonyezera chifundo chake ndiyo mwa kupatsa mtundu wa anthu mafotokozedwe olembedwa a chochititsa kuvutika. Iye wachita zimenezi m’Mawu ake, Baibulo. Baibulo limasonyeza bwino kwambiri kuti Mulungu analenga munthu kuti asangalale ndi moyo, osati kuvutika. (Genesis 2:7-9) Limasonyezanso kuti anthu oyamba anadzetsa kuvutika pa iwo eni mwa kukana ulamuliro wolungama wa Mulungu.—Deuteronomo 32:4, 5; Aroma 5:12.
Mosasamala kanthu za zimenezi, Mulungu amachitabe chifundo ndi mtundu wa anthu wovutika. Zimenezi zasonyezedwa bwino kwambiri ndi lonjezo lake la kuthetsa kuvutika kwa anthu. “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4; onaninso Yesaya 25:8; 65:17-25; Aroma 8:19-21.
Malonjezo abwino kwambiri ameneŵa amasonyeza kuti Mulungu amazindikira kwambiri kuvutika kwa anthu ndi kuti ali wotsimikiza kukuthetsa. Koma kodi nchiyani kwenikweni chimene chinachititsa kuvutika kwa anthu poyambirira, ndipo nchifukwa ninji Mulungu wakulola kupitirizabe kufikira m’tsiku lathu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Pachikuto ndi patsamba 32: Alexandra Boulat/Sipa Press
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Kevin Frayer/Sipa Press