Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/1 tsamba 16-22
  • Khalani ndi Mtima Wachifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani ndi Mtima Wachifundo
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito ya Chifundo Imene Sinayambe Yachitikapo
  • Mbali ya Umunthu Watsopano
  • Nsanje​—Chopinga pa Chifundo
  • Zopinga Zina pa Chifundo
  • Kuchitira Chifundo Odwala
  • Kuchitira Chifundo Ofooka
  • Sonyezani ‘Chifundo Chachikulu’
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”
    Yandikirani Yehova
  • Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Yehova Amalamulira Mwachifundo
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/1 tsamba 16-22

Khalani ndi Mtima Wachifundo

“Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima.” ​—AKOLOSE 3:12.

1. Kodi nchifukwa ninji chifundo chili chofunika kwambiri lerolino?

SIZINACHITIKEPO ndi kale lonse m’mbiri kukhala ndi anthu ochuluka monga lerolino ofunikira chithandizo cha chifundo. Poyang’anizana ndi matenda, njala, ulova, upandu, nkhondo, kusayeruzika, ndi masoka achilengedwe, anthu mamiliyoni ambiri amafunikira chithandizo. Komabe pali vuto lina lowopsa kwambiri, ndilo mkhalidwe wauzimu woipa kwenikweni wa mtundu wa anthu. Satana, yemwe akudziŵa kuti nthaŵi yake yachepa, ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9, 12) Motero, makamaka awo okhala kunja kwa mpingo Wachikristu ali pangozi ya kutaya miyoyo yawo, ndipo Baibulo limachotsapo kuthekera kulikonse kwa chiukiriro cha ophedwa mkati mwa tsiku lachiweruzo la Mulungu likudzalo.​—Mateyu 25:31-33, 41, 46; 2 Atesalonika 1:6-9.

2. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanawononge msanga anthu oipa?

2 Komabe, kufikira kumapeto kuno, Yehova Mulungu wapitirizabe kusonyeza kuleza mtima ndi chifundo kwa anthu oipa ndi osayamikira. (Mateyu 5:45; Luka 6:35, 36) Iye wachita zimenezi pachifukwa chimodzimodzi chimene anazengerezera kulanga mtundu wosakhulupirika wa Israyeli. “Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?”​—Ezekieli 33:11.

3. Kodi nchitsanzo chotani chimene tili nacho cha chifundo cha Yehova kwa anthu osakhala ake, ndipo tikuphunziraponji?

3 Chifundo cha Yehova chinasonyezedwanso kwa Anineve oipawo. Yehova anatumiza mneneri wake Yona kukawachenjeza za chiwonongeko choyandikiracho. Iwo analabadira ulaliki wa Yona nalapa. Zimenezi zinachititsa Mulungu wachifundoyo, Yehova, kusawononga mzindawo panthaŵiyo. (Yona 3:10; 4:11) Ngati Mulungu anachitira chisoni Anineve, omwe akanakhala ndi kuthekera kwa kuukitsidwa, koposa chotani nanga mmene ayenera kuchitira chifundo anthu lerolino omwe akuyang’anizana ndi chiwonongeko chosatha!​—Luka 11:32.

Ntchito ya Chifundo Imene Sinayambe Yachitikapo

4. Kodi Yehova amasonyeza motani chifundo chake kwa anthu lerolino?

4 Mogwirizana ndi umunthu wake wachifundo, Yehova watuma Mboni zake kupitirizabe kufikira anansi awo ndi “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Ndipo pamene anthu achitapo kanthu moyamikira ntchito yopulumutsa moyo imeneyi, Yehova amatsegula mitima yawo kuti amvetse uthenga wa Ufumu. (Mateyu 11:25; Machitidwe 16:14) Potsanzira Mulungu wawo, Akristu oona amasonyeza chifundo mwa kubwereranso kwa okondwerera, akumawathandiza mwa phunziro la Baibulo pamene kuli kotheka. Chifukwa chake, mu 1993, Mboni za Yehova zoposa pa mamiliyoni anayi ndi theka, m’maiko 231, zinathera maola oposa pa mamiliyoni chikwi chimodzi zikumalalikira kunyumba ndi nyumba ndi kuphunzira Baibulo ndi anansi awo. Nawonso okondwerera chatsopanoŵa akhala ndi mwaŵi wa kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova ndi kuloŵa pamzera wa Mboni zake zobatizidwa. Motero, iwonso amanyamula thayo la kuchita ntchito imene sinayambe yachitikapo imeneyi yosonyeza chifundo kwa othekera kukhala ophunzira omwe adakali otsekeredwa m’dziko lomafali la Satana.​—Mateyu 28:19, 20; Yohane 14:12.

5. Pamene chifundo cha Mulungu chifika pamalire ake, kodi nchiyani chidzachitikira zipembedzo zimene zimaimira Mulungu monyenga?

5 Tsopano apa Yehova adzachitapo kanthu monga “wankhondo.” (Eksodo 15:3) Chifukwa cha chifundo chake pa dzina lake ndi anthu ake, iye adzafafaniza kuipa konse nadzakhazikitsa dziko latsopano lolungama. (2 Petro 3:13) Matchalitchi a Dziko Lachikristu ndiwo adzakhala oyamba kuyang’anizana ndi tsiku la mkwiyo la Mulungu. Monga momwe Mulungu sanapulumutsire kachisi wake mu Yerusalemu ku dzanja la mfumu ya Babulo, sadzapulumutsanso magulu achipembedzo omwe amuimira monyenga. Mulungu adzaika m’mitima ya ziŵalo za United Nations chifuno cha kupasula Dziko Lachikristu ndi mitundu yake yonse ya chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:16, 17) “Ndipo Inenso,” akulengeza motero Yehova, “diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yawo pamtu pawo.”​—Ezekieli 9:5, 10.

6. Kodi Mboni za Yehova zimasonkhezereka kusonyeza chikondi chawo m’njira zotani?

6 Pamene kudakali nthaŵi, Mboni za Yehova zikupitiriza kusonyeza chifundo kwa anansi awo mwa kulalikira mwachangu uthenga wa Mulungu wa chipulumutso. Ndipo kumene kuli kotheka, mwachibadwa zimathandizanso anthu osoŵa mwakuthupi. Komabe, pambali imeneyi, thayo lawo loyamba ndilo kusamalira zosoŵa za ziŵalo za banja lawo ndi achibale awo a m’chikhulupiriro. (Agalatiya 6:10; 1 Timoteo 5:4, 8) Mautumiki ambiri ochitidwa ndi Mboni za Yehova othandiza okhulupirira anzawo okanthidwa ndi masoka osiyanasiyana akhala zitsanzo zochititsa chidwi za chifundo. Komabe, Akristu sayenera kuyembekezera vuto kuti asonyeze chifundo. Iwo amafulumira kusonyeza mkhalidwe umenewu pazinthu zabwino ndi zoipa za moyo wa masiku onse.

Mbali ya Umunthu Watsopano

7. (a) Pa Akolose 3:8-13, kodi chifundo chagwirizanitsidwa motani ndi umunthu watsopano? (b) Kodi mtima wachifundo umakuchititsa kukhala kosavuta kwa Akristu kuchitanji?

7 Nzoona kuti chibadwa chathu chauchimo ndi chisonkhezero choipa cha dziko la Satana ndizo zopinga pa kukhala kwathu achifundo. Ndicho chifukwa chake Baibulo limatifulumiza kuvula “mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu.” Mmalomwake talangizidwa ‘kuvala umunthu watsopano’​—umunthu umene umagwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu. Choyamba, tikulangizidwa kudziveka “mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” Ndiyeno Baibulo limatisonyeza njira yothandiza yosonyezera mikhalidwe imeneyi. Pitirizani “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso.” Nkwapafupi kukhala wokhululukira ngati takulitsa “mtima wachifundo” kwa abale athu.​—Akolose 3:8-13.

8. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala ndi mzimu wa kukhululukira?

8 Kumbali ina, kulephera kusonyeza mtima wokhululukira mwachifundo kumafooketsa unansi wathu ndi Yehova. Zimenezi zinasonyezedwa mwamphamvu ndi Yesu m’fanizo lake la kapolo wosakhululukira, yemwe anaponyedwa m’ndende ndi mbuye wake “kufikira akabwezere iye mangawa onse.” Kunali komuyenera kapoloyo kuchitiridwa motero chifukwa chakuti modabwitsa analephera kusonyeza chifundo kwa kapolo mnzake yemwe anapempha chifundo. Yesu anamaliza fanizolo mwa kunena kuti: “Chomwecho Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”​—Mateyu 18:34, 35.

9. Kodi mtima wachifundo umagwirizana motani ndi mbali yofunika koposa ya umunthu watsopano?

9 Kukhala ndi mtima wachifundo ndiko mbali yofunika ya chikondi. Ndipo chikondi ndicho chizindikiro cha Chikristu choona. (Yohane 13:35) Motero, Baibulo limamaliza malongosoledwe ake a umunthu watsopano motere: “Koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:14.

Nsanje​—Chopinga pa Chifundo

10. (a) Kodi nchiyani chingachititse nsanje kuzama m’mitima yathu? (b) Kodi nzoipa zotani zimene zingatuluke m’nsanje?

10 Chifukwa cha chibadwa chathu chauchimo, mikhalidwe ya nsanje ingazame m’mitima yathu. Mbale kapena mlongo angakhale ndi mphatso ya maluso kapena zinthu zakuthupi zimene ife tilibe. Kapena wina angalandire madalitso auzimu apadera ndi mathayo. Ngati tichitira nsanje oterowo, kodi tidzakhala okhoza kuwachitira mwa chifundo? Mwinamwake sitingatero. Mmalomwake, nsanje ingaonekere yokha m’kalankhulidwe kosuliza kapena machitidwe osakoma mtima, pakuti Yesu anati za anthu: “M’kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.” (Luka 6:45) Ena angachirikize kusuliza koteroko. Nchifukwa chake mtendere wa banja kapena mpingo wa anthu a Mulungu ukhoza kuwonongedwa.

11. Kodi ndimotani mmene abale khumi a Yosefe anamanira malo chifundo m’mitima yawo, ndipo panakhala zotulukapo zotani?

11 Talingalirani zimene zinachitika m’banja lina lalikulu. Ana aamuna aakulu khumi a Yakobo anachitira nsanje mng’ono wawo Yosefe kaamba kakuti anali mwana wapamtima kwa atate wawo. Chotsatirapo, iwo “sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.” Pambuyo pake, Yosefe anadalitsidwa ndi maloto a kwa Mulungu, akumatsimikiziritsa kuti anali ndi chiyanjo cha Yehova. Zimenezi zinachititsa abale ake ‘kumuda iye koposa.’ Popeza kuti iwo sanachotse nsanje m’mitima yawo, inalanda malo chifundo niwatsogolera m’tchimo lalikulu.​—Genesis 37:4, 5, 11.

12, 13. Kodi tiyenera kuchitanji pamene nsanje iloŵa mumtima mwathu?

12 Mwankhanza, iwo anagulitsa Yosefe monga kapolo. Poyesa kubisa cholakwa chawo, ananyenga atate wawo nawachititsa kukhulupirira kuti Yosefe anaphedwa ndi chilombo. Pambuyo pa zaka zambiri tchimo lawo linavumbuluka pamene njala inawakakamiza kumka ku Igupto kukagula chakudya. Woyang’anira chakudya, yemwe sanamzindikire kuti ndi Yosefe, anawaimba mlandu wa kuzonda dziko nawauza kusafunanso chithandizo chake pokhapo ngati akabweretsa mng’ono wawo, Benjamini. Koma panthaŵiyi Benjamini anali atakhala mwana wapamtima kwa atate wawo, ndipo iwo anadziŵa kuti Yakobo sakafuna konse kumlola amuke.

13 Chotero pamene anali chilili pamaso pa Yosefe, zikumbumtima zawo zinawachititsa kuvomereza kuti: “Tachimwiratu mbale wathu [Yosefe], pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.” (Genesis 42:21) Mwa zochita zake zachifundo komabe zolimba mtima, Yosefe anathandiza abale ake kutsimikizira kuti kulapa kwawo kunali koona mtima. Ndiyeno anadzivumbula kwa iwo nawakhululukira mokoma mtima. Umodzi wa banja unabwezeretsedwa. (Genesis 45:4-8) Monga Akristu, tiyenera kutengapo phunziro pazimenezi. Podziŵa zotulukapo zoipa za nsanje, tiyenera kupempherera thandizo kwa Yehova kuti tichotse nsanje nitikhale ndi “mtima wachifundo.”

Zopinga Zina pa Chifundo

14. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kupenyerera chiwawa?

14 Chopinga china pa kukhala kwathu achifundo chingakhalepo mwa kumapenyerera chiwawa. Maseŵera ndi zosangulutsa zimene zimasonyeza chiwawa zimachititsa kusangulutsidwa ndi chiwawa. M’nthaŵi za Baibulo, anthu akunja kaŵirikaŵiri ankapenyerera mipikisano ya kumenyana kwa kuphana ndi mitundu ina ya kuzunza anthu m’mabwalo a zamaseŵero mu Ufumu wa Roma. Zosangulutsa zoterozo, malinga ndi kunena kwa wolemba mbiri wina, “zinapha mtima wachifundo pa kuvutika umene umasiyanitsa munthu ndi nyama.” Zosangulutsa zochuluka m’dziko lamakono zili ndi chiyambukiro chimodzimodzicho. Akristu omwe akuyesayesa kukhala ndi mtima wachifundo, ayenera kukhala atcheru kwambiri posankha zimene angakonde kuŵerenga, akanema, ndi maprogramu a pa TV. Mwanzeru, amakumbukira mawu a pa Salmo 11:5 akuti: “Moyo wake [Yehova] umuda . . . iye wakukonda chiwawa.”

15. (a) Kodi ndimotani mmene munthu angasonyezere kusoŵa chifundo kowopsa? (b) Kodi Akristu amachitapo kanthu motani pa zosoŵa za okhulupirira anzawo ndi anansi awo?

15 Munthu wodzikonda alinso wothekera kukhala wopanda chifundo. Zimenezi nzowopsa, monga momwe mtumwi Yohane akufotokozera kuti: “Iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?” (1 Yohane 3:17) Kupanda chifundo kofanana ndi kumeneko kunasonyezedwa ndi wansembe wodziyesa yekha wolungama ndi Mlevi m’fanizo la Yesu la Msamariya waunansi. Poona mkhalidwe wa mbale wawo Myuda ali wokomoka, iwowa anadutsira kumbali ina ya msewu napitiriza ndi ulendo wawo. (Luka 10:31, 32) Mosiyana nawo, Akristu achifundo amachitapo kanthu mwamsanga kuthandiza zosoŵa zakuthupi ndi zauzimu za abale awo. Ndipo mofanana ndi Msamariya wa m’fanizo la Yesu, iwo amaderanso nkhaŵa zosoŵa za anthu osawadziŵa. Motero amakhala osangalala kupereka nthaŵi yawo, nyonga, ndi zinthu zakuthupi kuti apititse patsogolo ntchito yopanga ophunzira. Mwa njira imeneyi amakhala akuthandizira mamiliyoni ambiri kulinga ku chipulumutso.​—1 Timoteo 4:16.

Kuchitira Chifundo Odwala

16. Kodi ndi kulephera kotani kumene timakhala nako pochita ndi matenda?

16 Kudwala kuli mkhalidwe wa mtundu wa anthu wopanda ungwiro ndi womafa. Akristu sakupatulidwa, ndipo ambiri a iwo sali madokotala, ndipo sathanso kuchita zozizwitsa monga momwe Akristu oyambirira ena anachitira omwe analandira mphamvu zoterozo kwa Kristu ndi atumwi ake. Pamene atumwi a Kristu ndi anzawo owatsatira anatha kumwalira, mphamvu zozizwitsa zoterozo zinatha. Motero tili ndi mphamvu zochepa chabe za kuthandiza odwala matenda akuthupi, kuphatikizapo ubongo wosagwira bwino ntchito ndi oona zideruderu.​—Machitidwe 8:13, 18; 1 Akorinto 13:8.

17. Kodi timatengapo phunziro lotani pa njira imene Yobu munthu wodwala ndi wofedwa anachitiridwa?

17 Kudwala kaŵirikaŵiri kumachititsa tondovi. Mwachitsanzo, Yobu wowopa Mulungu anachita tondovi kwambiri chifukwa cha nthenda yake yaikulu ndi masoka omwe Satana anadzetsa pa iye. (Yobu 1:18, 19; 2:7; 3:3, 11-13) Iye anafunikira mabwenzi omwe akamchitira mwachifundo ndi amene akalankhula ‘molimbikitsa.’ (1 Atesalonika 5:14) Mmalomwake, otonthoza atatu onyenga anamfikira iye ndi kufulumira kuganiza zolakwa. Iwo anakulitsa mkhalidwe wa tondovi wa Yobu mwa kunena kuti masoka ake anali kaamba ka tchimo lake. Pokhala achifundo, Akristu adzapeŵa kuchita cholakwa chofananacho pamene okhulupirira anzawo akudwala kapena apsinjika mtima. Nthaŵi zina, chachikulu chimene otero amafunikira ndicho kuchezeredwa mokoma mtima kangapo ndi akulu kapena Akristu okhwima omwe adzamvetsera ndi khutu lachifundo, akumasonyeza kumvetsetsa, ndi kupereka uphungu wachikondi wa Malemba.​—Aroma 12:15; Yakobo 1:19.

Kuchitira Chifundo Ofooka

18, 19. (a) Kodi akulu ayenera kuchita motani ndi ofooka kapena olakwa? (b) Ngakhale ngati kungakhale kofunika kupanga komiti yachiweruzo, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa akulu kuchita ndi olakwa mwachifundo?

18 Akulu makamaka ayenera kukhala a mtima wachifundo. (Machitidwe 20:29, 35) “Ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu,” limalamula motero Baibulo. (Aroma 15:1) Pokhala opanda ungwiro, tonse timalakwa. (Yakobo 3:2) Kukoma mtima kuli kofunika pochita ndi ‘munthu wogwidwa nako kulakwa.’ (Agalatiya 6:1) Akulu sayenera konse kufanana ndi Afarisi odzilungamitsa okha omwe anali osalolera pogwiritsira ntchito Chilamulo cha Mulungu.

19 Mosiyana ndi zimenezo, akulu amatsatira zitsanzo za chifundo za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Ntchito yawo yaikulu ndiyo kudyetsa, kulimbikitsa, ndi kutsitsimula nkhosa za Mulungu. (Yesaya 32:1, 2) M’malo mwa kuyesa kuyendetsa zinthu ndi malamulo ambirimbiri, iwo amatsatira miyezo yabwino m’Mawu a Mulungu. Motero, ntchito ya akulu iyenera kukhala kumangirira, kudzetsa chisangalalo ndi chiyamikiro m’mitima ya abale awo kaamba ka ubwino wa Yehova. Ngati wokhulupirira mnzake achita cholakwa chaching’ono, kaŵirikaŵiri mkulu adzapeŵa kumuwongolera pamaso pa ena. Ngati kulidi kofunika kulankhula naye, chifundo chidzachititsa mkuluyo kumtengera pambali ndi kukambitsirana naye vutolo popanda ena kumvako. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:15.) Mosasamala kanthu za mmene munthuyo angakhalire wovuta kuchita naye, kafikidwe ka mkulu kayenera kukhala koleza mtima ndi kothandiza. Sayenera konse kufunafuna zifukwa zochotsera mumpingo woteroyo. Ngakhale ngati kukhala kofunika kupanga komiti yachiweruzo, akuluwo adzasonyeza mtima wachifundo pochita ndi munthu wochita tchimo lalikulu. Kudekha kwawo kungathandize munthuyo kulapa.​—2 Timoteo 2:24-26.

20. Kodi ndiliti pamene machitidwe osonyeza chifundo ali osayenera, ndipo chifukwa ninji?

20 Komabe, pali nthaŵi zina pamene mtumiki wa Yehova sangasonyeze chifundo. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 13:6-9.) Kuti Mkristu aleke ‘kuyanjana’ ndi bwenzi lake lapamtima kapena wachibale yemwe wachotsedwa kungakhale chiyeso chenicheni. M’chochitika choterocho, nkofunika kwambiri kuti munthu asagonje ku chifundo. (1 Akorinto 5:11-13) Kulimba mtima koteroko kungalimbikitse ngakhale wolakwayo kuti alape. Ndiponso, pochita ndi wosiyana naye ziŵalo, Akristu ayenera kupeŵa machitidwe osayenera osonyeza chifundo omwe angatsogolere ku chisembwere.

21. Kodi ndi m’mbali zina ziti mmene tifunikira kusonyeza chifundo, ndipo mapindu ake ngotani?

21 Malo angochepa akuti tifotokoze mbali zonse zofunikira chifundo​—pochita ndi okalamba, ofedwa, omwe akuzunzidwa ndi okwatirana nawo osakhulupirira. Akulu ogwira ntchito zolimba ayeneranso kuchitiridwa mwachifundo. (1 Timoteo 5:17) Alemekezeni ndipo achirikizeni. (Ahebri 13:7, 17) “Khalani nonse . . . ochitirana chifundo,” analemba motero mtumwi Petro. (1 Petro 3:8) Mwa kuchita mwa njira imeneyi m’mikhalidwe yonse yofuna kutero, timapititsa patsogolo umodzi ndi chimwemwe mumpingo ndi kukopera akunja ku choonadi. Choposa zonse, timakhala tikulemekeza Atate wathu wachifundo, Yehova.

Mafunso a Kupenda

◻ Kodi Yehova amasonyeza motani chifundo kwa mtundu wa anthu ochimwa?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala ndi mtima wachifundo?

◻ Kodi pali zopinga zina ziti pa kukhala kwathu ndi mtima wachifundo?

◻ Kodi tiyenera kuwachitira motani odwala ndi ochita tondovi?

◻ Ndayani makamaka ayenera kukhala ndi mtima wachifundo, ndipo chifukwa ninji?

[Bokosi patsamba 19]

AFARISI OPANDA CHIFUNDO

TSIKU lakupuma la Sabata linafunikira kukhala dalitso lauzimu ndi lakuthupi kwa anthu a Mulungu. Komabe, atsogoleri achipembedzo Achiyuda anapanga malamulo ambirimbiri omwe analuluza lamulo la Mulungu la Sabata nalichititsa kukhala lothodwetsa kwa anthu. Mwachitsanzo, ngati aliyense anachita ngozi kapena kudwala, sakalandira chithandizo pa Sabata pokhapo ngati moyo wake unali pangozi.

Kagulu kena ka Afarisi kanali kokhwimitsa zinthu kwambiri pa kutsatira kwawo lamulo la Sabata kotero kuti anati: “Munthu sayenera kukatonthoza olira, kapena kukaona odwala pa Sabata.” Atsogoleri ena achipembedzo analola maulendo oterowo pa Sabata koma analamula kuti: “Misozi siloledwa.”

Chifukwa chake, Yesu molondola anatsutsa atsogoleri achipembedzo Achiyuda kaamba konyalanyaza zofunika zazikulu za Chilamulo, zonga ngati chilungamo, chikondi, ndi chifundo. Nchifukwa chake iye anati kwa Afarisi: “Muyesa achabe mawu a Mulungu mwa mwambo wanu”!​—Marko 7:8, 13; Mateyu 23:23; Luka 11:42.

[Zithunzi patsamba 17]

M’maiko 231 Mboni za Yehova zikuchita ntchito ya chifundo m’nyumba za anthu, pamakwalala, ngakhale m’ndende, imene sinayambe yachitikapo

[Chithunzi patsamba 18]

Kupenyerera chiwawa, konga ngati kwa pa TV, kumafooketsa mtima wachifundo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena