Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/15 tsamba 28-29
  • Yehova Amalamulira Mwachifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amalamulira Mwachifundo
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutsanzira Chifundo cha Yehova
  • Chifundo m’Dziko Lankhanza
  • Sonyezani ‘Chifundo Chachikulu’
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Khalani ndi Mtima Wachifundo
    Nsanja ya Olonda—1994
  • “Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/15 tsamba 28-29

Yehova Amalamulira Mwachifundo

KUYAMBIRA kalekale anthu ambiri olamulira akhala akulamulira mosasamala za kuvutika kwa anthu awo. Komabe, Yehova anachita zosiyana ndi zimenezo mwa kusankha mtundu​—Israyeli​—ndi kuulamulira mwachifundo.

Pamene Aisrayeli anali akapolo ku Igupto wakale, Yehova anamva kulira kwawo kaamba ka chithandizo. “M’mazunzo awo onse iye anazunzidwa. . . . M’kukonda kwake ndi m’chisoni chake Iye anawawombola.” (Yesaya 63:9) Yehova anapulumutsa Aisrayeli, anawapatsa chakudya mozizwitsa, ndipo anawaloŵetsa m’dziko lawolawo.

Mkhalidwe wachifundo wa Yehova unasonyezedwanso m’malamulo amene iye anapatsa mtundu umenewu. Iye analamulira Aisrayeli kuti azichitira chifundo ana amasiye, akazi amasiye, ndiponso alendo okhala nawo m’dzikomo. Iwo sanaloledwe kuchitira zinthu zoipa anthu olemala.

Lamulolo linanena kuti anthu osoŵa ayenera kuchitiridwa chifundo. Aumphaŵi anali kuloledwa kukunkha eni ake atatha kukolola. Anali kufafaniza ngongole zonse m’chaka cha Sabata (chaka chachisanu ndi chiŵiri). Malo onse opatsidwa monga choloŵa koma amene anagulidwa anayenera kubwezedwa kwa eni ake m’chaka cha makumi asanu (chaka cha 50). Buku lakuti Ancient Israel​—Its Life and Institutions [Israyeli Wakale​—Moyo ndi Chikhalidwe Chake] likuti: “Ku Israyeli, kunalibe kusankhana malinga ndi mkhalidwe wa zachuma wa anthu monga momwe zilili masiku ano.” “M’masiku oyambirira pamene iwo anakakhala kudziko lawo, pafupifupi Aisrayeli onse anali kukhala mofanana.”​—Levitiko 25:10; Deuteronomo 15:12-14; 24:17-22; 27:18.

Kutsanzira Chifundo cha Yehova

Atumiki a Mulungu ngodzazidwa ndi chifundo chake. Mwachitsanzo, kuyambira kalekale, mafumu ena atsopano apha anthu otsala a m’banja lachifumu la mfumu yapita. Koma Davide mtumiki wa Yehova sanachite zimenezi. Mfumu Sauli atafa, Davide anatetezera Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli amene anatsala ndiponso amene anali woloŵa ufumu. “Mfumu inaleka [“inachitira chifundo,” NW] Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli.”​—2 Samueli 21:7.

Palibe munthu winanso amene anatsanzira chifundo cha Yehova kuposa mmene Yesu anachitira. Iye anachita zambiri za zozizwitsa zake chifukwa chakuti anali ndi chifundo chaumulungu. Nthaŵi ina wakhate anamchonderera kuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Yesu anachita chifundo namkhudza iye, nanena kuti: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” (Marko 1:40-42) Nthaŵi inanso khamu lalikulu la anthu linali kutsatira Yesu. Pakatikati pa phokoso limenelo, Yesu anamvera amuna aŵiri akhungu amene anafuula kuti: “Ambuye, mutichitire chifundo, inu Mwana wa Davide. . . . Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso awo; ndipo pomwepo anapenyanso.”​—Mateyu 20:29-34.

Kuchuluka kwa anthu sikunachititse Yesu kusamvera ena chifundo. “Ndimva nalo chifundo khamulo,” iye anatero nthaŵi ina chifukwa chakuti anthuwo sanadye kwa nthaŵi yaitali. Choncho, iye anawadyetsa mozizwitsa. (Marko 8:1-8) Pamene Yesu anali paulendo wake, iye sanangophunzitsa khamu la anthu koma anali kusamaliranso za zosoŵa zawo. (Mateyu 9:35, 36) Atamaliza ulendo woterowo, Yesu ndi ophunzira ake analibe nthaŵi yopuma ngakhale kudya chakudya. Nkhani ya m’Baibuloyo ikutiuza kuti: “Ndipo anachokera m’ngalaŵa kumka ku malo achipululu padera. Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m’midzi monse, nawapitirira. Ndipo anatuluka iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​—Marko 6:31-34.

Chimene chinachititsa chifundo Yesu si matenda ndi umphaŵi wawo wokha ayi komanso mkhalidwe wawo wauzimu. Atsogoleri awo anali kuwalima pamsana, choncho Yesu ‘anagwidwa chifundo ndi iwo.’ Mawu achigiriki akuti ‘anagwidwa chifundo ndi iwo’ amatanthauza “kumva kuwawa kwa m’matumbo.” Yesu analidi munthu wachifundo!

Chifundo m’Dziko Lankhanza

Tsopano Yesu Kristu ndi Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Yehova. Monga momwe anachitira mu Israyeli wakale, lerolinonso Mulungu akulamulira anthu ake mwachifundo. “Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka [“ndidzawachitira chifundo,” NW].”​—Malaki 3:17.

Anthu amene amafuna kulandira chifundo cha Yehova ayenera kutsanzira njira zake. Zoonadi, tikukhala m’dziko limene anthu amafuna kusamalira njira yawo yokha ya moyo osafuna kusamalira anthu osoŵa. Mabwana nthaŵi zambiri amangofuna mapindu awo mosasamala nkomwe za kutetezera antchito awo ndi anthu amene amagula zinthu zawo. Pa 2 Timoteo 3:1-4, Baibulo likufotokoza bwino lomwe za kuipa kwa makhalidwe kwa m’nthaŵi yathu kumene kwachotsa chifundo m’mitima ya anthu ambiri.

Komabe, ifenso tingapeze mpata wosonyeza chifundo. Kodi tingathandize anansi athu pa zinthu zina zofunikira? Kodi pali munthu wina amene akudwala woti tingakamzonde? Kodi tingatonthoze anthu amene achita tondovi, mogwirizana ndi uphungu wakuti: “Limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka”?​—1 Atesalonika 5:14.

Chifundo chidzatithandizanso kupeŵa kukwiya pamene ena alakwa. Tikuuzidwa kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”​—Aefeso 4:31, 32.

Chifundo chidzatithandiza kupeŵa kulamulira mwankhanza. Baibulo likuti: ‘Valani, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.’ (Akolose 3:12) Kudzichepetsa kumatithandiza kudziona mofanana ndi amene tikuwayang’anira. Kukhala wachifundo kumaphatikizapo kukhala wodzichepetsa ndi wololera osati kukhala munthu wovuta kusangalatsa. Kufuna kuchita zinthu molongosoka sikuyenera kutipangitsa kuona anthu ena monga zipangizo wamba za makina. Ndiponso, m’banja, amuna achifundo amakumbukira kuti akazi awo ali zotengera zochepa mphamvu. (1 Petro 3:7) Kulingalira za chitsanzo cha mmene Yesu anali kuchitira chifundo kungatithandize kukwaniritsa zinthu zonse zimenezi.

Popeza kuti Yesu anawachitira kwambiri chifundo anthu mu utumiki wake wa padziko lapansi, tingakhale ndi chidaliro chakuti iye tsopano ali Wolamulira wachifundo ndipo adzapitiriza kukhala wachifundo. Salmo 72 likunena za iye mwaulosi kuti: “Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphaŵi, nadzaphwanya wosautsa. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja. Ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”​—Salmo 72:4, 8, 13.

Mawu a Mulungu akulosera kuti: “Ndi chilungamo adzaweruza aumphaŵi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka; . . . nadzapha oipa.” Utafotokoza mmene ngakhale anthu ena ankhanza ndi ochita zinthu monga zilombo adzasinthira njira zawo, ulosiwo ukupitiriza kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:4-9) Ulosi umenewu sukulonjeza chinthu chinanso ayi koma za anthu a padziko lonse lapansi odziŵa Yehova ndi kutsanzira njira zake zachifundo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena