Kukwaniritsa Chosoŵa Chachikulu Chachibadwa cha Kuŵerengeredwa
KUTHOKOZA koona mtima kwakuti “Mwachita bwino!” “Ndikusangalala kuti mwapambana!” kapena kuti “Mwachita zamphamvu; tikunyada nanu” kumathandiza kwambiri kusonkhezera chidaliro cha munthu mwini, makamaka ngati kunenedwa ndi munthu amene mumalemekeza. Anthu amachita bwino zinthu pamene aŵerengeredwa. Atasonyezedwa kuŵerengeredwa, amachita zinthu bwinopo ndipo amakhala achimwemwepo. Indedi, kuŵerengeredwa koyenerera nkofunika kumaganizo ndi mtima monga momwe chakudya chabwino chilili ku thupi.
Dikishonale ina imafotokoza kuŵerengeredwa kukhala “kuvomereza munthu kukhala woyenerera kulingaliridwa kapena kupatsidwa chisamaliro” ndi “kuzindikira kapena chisamaliro chapadera.” Iko kuli kofanana kwambiri ndi ulemu, kumva kukhala wokwezedwa, kumene pamene kuperekedwa kumapatsa lingaliro la kuŵerengera kokhutiritsa kwa munthu ndi mlingo winawake wa kuŵerengera komuyenerera.
Kuŵerengeredwa—Chosoŵa Chachikulu
Kupereka thamo pamene thamolo lili loyenera nkwanzeru ndi koyenera. Yesu anapereka chitsanzo mu fanizo lake la akapolo amene mbuye anawaikizira chuma chake. Poyamikira kusamalira bwino chuma chake, iye anati: “[Wachita bwino, NW], kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika.” (Mateyu 25:19-23) Komabe, kaŵirikaŵiri, khalidwe loyenerera limeneli limanyalanyazidwa. Kusasonyeza kuŵerengera munthu kumapha kutenthedwa maganizo ndi changu. Iona akunena motere: “Kuŵerengeredwa kumakupangitsa kumva kukhala wofunika, wofunidwa, ndi woyamikiridwa . . . Kumakupatsa changu cha kuchita zinthu. Ngati unyalanyazidwa, umaona kukhala wokanidwa ndi wogwiritsidwa mwala.” Patrick akuwonjezera kuti: “Ndiyeno kumakhala kovuta kusunga mlingo wapamwamba wa mkhalidwe ndi zotulukapo zake.” Motero, nkofunika chotani nanga kuti tidziŵe mmene ndi pamene tiyenera kusonyeza kuŵerengera munthu. Tonsefe timakhumba kudziŵa kuti ndife ofunidwa ndi ena. Chimenechi chili chosoŵa chachikulu chachibadwa.
Mawu a chiyamikiro, thayo lowonjezereka, kapena ngakhale mphatso yeniyeni imakusonkhezerani kupitirizabe kuchita bwino koposa. Zimenezi nzoona kaya ndinu kholo, mwamuna, mkazi, mwana, chiŵalo cha mpingo, kapena woyang’anira. “Pamene ndiŵerengeredwa,” akutero Margaret, “ndimamva kukhala wachimwemwe, wofunidwa, ndipo ndimakhala ndi chikhumbo cha kuchita bwinopo.” Andrew akuvomereza, akumati: “Kumanditsitsimula mtima, kukumandisonkhezera kugwira ntchito zolimbadi.” Komabe, kusonyeza kuŵerengera ndi ulemu kwa munthu wina kumafuna kulingalira mosamala ndi nzeru.
Tsanzirani Chitsanzo cha Yehova cha Kusonyeza Kuŵerengera Ena
Chitsanzo chachikulu koposa cha kuŵerengera kufunika kwa ena ndicho Yehova Mulungu. Iye amazindikira awo amene ali oyenerera kuŵerengeredwa. Iye anazindikira anthu onga Abele, Enoke, ndi Nowa. (Genesis 4:4; 6:8; Yuda 14) Yehova anazindikira Davide chifukwa cha kukhulupirika kwake kwapadera. (2 Samueli 7:16) Samueli, amene monga mneneri analemekeza Yehova kwa zaka zambiri, nayenso analemekezedwa ndi Mulungu, amene anayankha mofulumira pemphero lopempha thandizo la Samueli la kugonjetsa Afilisti. (1 Samueli 7:7-13) Kodi simukanaona kukhala wolemekezedwa posonyezedwa kuŵerengeredwa ndi Mulungu koteroko?
Chithokozo ndi chiyamikiro nzofanana kwambiri ndi kuŵerengeredwa. Baibulo limatilimbikitsa ‘kukhala akuyamika’ ndi kukhala othokoza pa zimene ena amatichitira. (Akolose 3:15; 1 Atesalonika 5:18) Pamene kuli kwakuti zimenezi zimanena kwenikweni za kukhala woyamikira kwa Yehova, zili chimodzimodzinso m’nkhani za moyo watsiku ndi tsiku. Mtumwi Paulo anadziŵa zimenezi. Iye anaŵerengera Febe kukhala “wosungira ambiri” ndipo Priska ndi Akula kaamba ka ‘kupereka makosi awo’ kaamba ka iye ndi ena. (Aroma 16:1-4) Tangoganizani mmene anamvera polandira mawu othokoza otero onenedwa mwapoyera. Kunalinso kwabwino kwa Paulo kukhala ndi chimwemwe cha kusonyeza kuŵerengera, ulemu, ndi chilimbikitso. Nafenso tingatsanzire Yehova ndi olambira ake oyamikira mwa kusonyeza kuŵerengera koyenera kwa awo amene akukuyenerera.—Machitidwe 20:35.
Kuŵerengeredwa m’Banja
“Kuŵerengeredwa pang’ono kumathandiza kwambiri kuchititsa moyo kukhala wosangalatsa,” akutero Mitchell, mwamuna wokwatira ndi mkulu Wachikristu. “Kumakuchititsani kukonda munthu amene amakuŵerengeraniyo, mwinamwake kwa nthaŵi yonse.” Mwachitsanzo, mwamuna Wachikristu amasenza thayo lolemera ndi kupanga zosankha zofunika za ubwino wa banja. Iye ayenera kugaŵira zosoŵa za banjalo zauzimu, zakuthupi, ndi zamalingaliro. (1 Timoteo 5:8) Ha, amakhala wothokoza chotani nanga pamene aŵerengeredwa moyenerera kaamba ka gawo lake loperekedwa ndi Mulungu monga mutu wa banja ndi pamene mkazi wake amchitira “ulemu waukulu”!—Aefeso 5:33, NW.
Chinthu china chosafunikira kunyalanyazidwa ndicho ntchito ya mkazi wapanyumba, imene imachitidwa mosaonedwa ndi anthu ambiri. Malingaliro amakono anganyalanyaze ntchito yotero ndi kuilanda ulemu wake ndi kufunika kwake. Komabe, iyo njosangalatsa kwa Mulungu. (Tito 2:4, 5) Nkotsitsimula chotani nanga pamene mwamuna wozindikira atamanda mkazi wake, makamaka m’mbali zonse za moyo zimene amachita bwino, akumamsonyeza kuŵerengera kotero pansi pa umutu wake! (Miyambo 31:28) Ponena za mwamuna wake, Rowena akuti: “Pamene ayamikira zimene ndimachita, ndimaona kukhala kosavuta kugonjera kwa iye ndi kumlemekeza.”
Mphunzitsi wina Wachimereka Christian Bovee panthaŵi ina anati: “Chitamando chabwino kwa ana chili ngati dzuŵa kumaluŵa.” Inde, ngakhale mwana wamng’ono kwambiri amafunikira chitsimikiziro chanthaŵi zonse chakuti iyeyo ali chiŵalo chapadera cha banja. Mkati mwa zaka zaubwana za kuumbika, zodzazidwa ndi kusintha kwa malingaliro ndi kwa kuthupi, mumakhala nkhaŵa ya kuzindikira kaonekedwe kaumwini, limodzi ndi chikhumbo cha kukhala womasuka ndi woŵerengeredwa. Makamaka panthaŵiyi, wachichepere amafuna kumva kukhala wokondedwa ndi makolo ake ndi kuchitiridwa molingaliridwa bwino ndi chifundo chaumunthu. Makolo okalamba ndi agogo nawonso amafuna chitsimikiziro chakuti adakali achithandizo ndi okondedwa, kuti iwo ‘sanatayidwe mu ukalamba.’ (Salmo 71:9; Levitiko 19:32; Miyambo 23:22) Kukhutiritsa moyenerera chosoŵa cha kuŵerengeredwa kumadzetsa chimwemwe chowonjezereka ndi chipambano m’banja.
Kuŵerengeredwa mu Mpingo Wachikristu
Kuli kwa phindu lalikulu kukulitsa chikondwerero chenicheni mwa ena mu mpingo Wachikristu ndi kusonyeza chiyamikiro momasuka pa ntchito ndi zoyesayesa zawo. Akulu Achikristu ayenera kutsogolera mwa kuyamikira ntchito ndi zoyesayesa za ena mu mpingo. “Poyamba sindinadziŵe kuti [mawu osonyeza kuŵerengera] anali othandiza kwambiri pa kupatsa chilimbikitso, chikhutiro ndi chimwemwe, kufikira pamene ndinachezeredwa kangapo pa maulendo aubusa,” anatero Margaret. “Ndinazindikira zimene zimaphonyedwa pamene munthu sanasonyezedwe kuŵerengeredwa.” Ha, chimenechi nchifukwa chabwino chotani nanga chosonyezera chikondwerero chaumwini chenicheni ndi chachikondi kwa onse mu mpingo! Zindikirani ntchito yawo yabwino. Yamikirani momasuka ndi kulimbikitsa. M’mipingo yambiri muli makolo opanda mnzawo wa muukwati amene amagwira ntchito zolimba kuphunzitsa ana awo mikhalidwe yauzimu. Oterowo amayenerera kupatsidwa chiyamikiro chapadera. Tchulani mbali zabwino mmalo mwa zoipa. Lolani ena kuona chikondi chanu chaubale kwa iwo. Aloleni aone kuti mumasamala. Mwanjira imeneyi, oyang’anira achikondi amagwira ntchito yomanga mpingo. (2 Akorinto 10:8) Chiŵalo chilichonse chimachita mofananamo mwa kusonyeza kuŵerengera koyenerera ndi ulemu kwa okhulupirika otero amene amagwira ntchito zolimba kaamba ka iwo.—1 Timoteo 5:17; Ahebri 13:17.
Koma pali mbali inanso, kapena mfundo ina ya nkhaniyi. Zoonadi, chikhumbo cha kufuna kuŵerengeredwa nchamphamvu kwambiri. M’tsiku la Yesu chinakhala nkhaŵa yaikulu pakati pa atsogoleri achipembedzo. Yesu anachita kuwongolera lingaliro lolakwika la ophunzira ake pankhaniyi. (Marko 9:33-37; Luka 20:46) Akristu afunikira kukhala ochita moyenerera ndi achikatikati. Chikhumbo cha kuŵerengeredwa chingakhale changozi mwauzimu ngati sichilamuliridwa. (Yakobo 3:14-16) Mwachitsanzo, kungakhale kwatsoka chotani nanga ngati mkulu afikira kukhala wonyada ndi kuyamba kulamulira ena kuti avomereze malingaliro ake odzitukumula!—Aroma 12:3.
Mtumwi Paulo mwanzeru analangiza Akristu anzake ku Roma kuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Mawu ameneŵa amagwira ntchito makamaka kwa akulu Achikristu, amene nthaŵi zonse ayenera kuzindikira Kristu kukhala Mutu wa mpingo. Kugonjera kudzanja lake lamanja la ulamuliro kumasonyezedwa mwa kufuna chitsogozo cha Kristu mwanjira ya mzimu woyera, malamulo amkhalidwe a Baibulo, ndi chitsogozo choperekedwa ndi Bungwe Lolamulira la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47; onani Chivumbulutso 1:16, 20; 2:1.
Motero, pamene akulu akumana, ndi kupempherera chitsogozo cha Yehova cha kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu, adzayesayesa kupanga zosankha zimene zili zolama mwa Malemba. Kudzichepetsa Kwachikristu, kufatsa, ndi kudzitsitsa kudzaletsa mkulu aliyense kuyesa kudzikweza, kulamulira abale ake, ndi kuika malingaliro ake pa misonkhano imeneyi. (Mateyu 20:25-27; Akolose 3:12) Paliponse pamene pali pothekera, tcheyamani wa bungwe la akulu angachite bwino kupempha malingaliro ochokera kwa akulu anzake pasadakhale ndiyeno kupanga mpambo wa mfundo zokambitsirana pasadakhale kuti alole nthaŵi ya kulingalira kosamalitsa ndi kwapemphero pa mfundo iliyonse yondandalikidwa. Mkati mwa msonkhano wa akulu, iye akayesa, osati kulamulira malingaliro a akulu, koma, kuwalimbikitsa kusonyeza “ufulu wa kulankhula” pankhani zimene akukambitsirana. (1 Timoteo 3:13, NW ) Nawonso akulu anzakewo ayenera kumvetsera mosamalitsa ndemanga za wina ndi mnzake ndi kupindula mokondwera ndi chidziŵitso cha akulu amene ali ndi zaka zambiri m’Chikristu.—Eksodo 18:21, 22.
Komabe, oyang’aniranu zindikirani kuti Kristu angagwiritsire ntchito mkulu aliyense m’bungwelo kupereka malamulo amkhalidwe a Baibulo ofunikira polimbana ndi mkhalidwe winawake, kapena kupanga chosankha chofunika. Mzimu wabwino udzakhala pakati pa bungwelo pamene kuŵerengeredwa koyenera kusonyezedwa kwa mkulu aliyense kaamba ka kuchirikiza kwake kusamalira zinthu zauzimu za mpingo.—Machitidwe 15:6-15; Afilipi 2:19, 20.
Menyerani Nkhondo pa Kusonyeza ndi Kusonyezedwa Kuŵerengera Koyenera
Kuŵerengeredwa kumamangirira. Kumalimbikitsa ndipo nkosonkhezera chikondi. “Ngakhale pamene tidziona kukhala anthu wamba,” akutero Mary, “timafuna chilimbikitso kuti timve kukhala ofunika.” Yamikirani moona mtima zoyesayesa za ena zatsiku ndi tsiku. Kuchita motero kumachititsa moyo kukhala woyenerera ndi wokondweretsa kwambiri kwa iwo. Makolo, ana, oyang’anira, ndi ziŵalo za mpingo Wachikristu, mungapeze kuŵerengeredwa mwa kalankhulidwe kanu ndi mmene mumachitira zinthu. Baibulo limayamikira anthu akhama, ofatsa, ndi odzichepetsa. (Miyambo 11:2; 29:23; Ahebri 6:1-12) Phunzirani kuyamikira mokoma mtima kufunika kwa ena. Lingalirani mmene ena amamvera pamene mugwira nawo ntchito. Mtumwi Petro anapereka chilangizo ichi: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Zimenezi zimafuna kusonyeza kuŵerengera ena, motero tikumakwaniritsa chosoŵa chachikulu chachibadwa.