Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 12/15 tsamba 23-25
  • Kodi Muyenera Kupemphera kwa Yesu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muyenera Kupemphera kwa Yesu?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pemphero ndi Chiyani?
  • Kuzindikira Yesu m’Mapemphero Athu
  • Kodi Ndimotani Mmene ‘Timaitanira pa’ Dzina la Yesu?
  • Zimene Yesu Angatichitire
  • Kodi Mumamlemekeza Motani Yesu?
  • Mapemphero Olandirika
  • Pankhani ya Mapemphero Amene Mulungu Amamva
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 12/15 tsamba 23-25

Kodi Muyenera Kupemphera kwa Yesu?

ANTHU ena amaona kuti kupemphera kwa Yesu kuli koyenera. Mu Germany ambiri aphunzitsidwa adakali ana kuti asanadye chakudya ayenera kupinda manja awo ndi kuyamika kwa Yesu Kristu.

Malinga ndi kunena kwa Baibulo, Yesu alidi ndi malo okwezeka kwambiri kumwamba. Komabe, kodi zimenezo zimatanthauza kuti tiyenera kupemphera kwa iye? Mwinamwake muli pakati pa awo amene amapereka mapemphero awo kwa Yesu chifukwa cha kumukonda, koma kodi Yesu akulingalira motani ponena za mapemphero oterowo?

Ndi iko komwe, kodi mafunso ameneŵa akubukiranji? Chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ali “Wakumva pemphero.” Pamenepo, nzosadabwitsa kuti atumiki a Mulungu m’nthaŵi zakale, monga Aisrayeli, anapemphera kokha kwa Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse.​—Salmo 5:1, 2; 65:2.

Kodi zinthu zinasintha pamene Yesu, Mwana wa Mulungu, anadza padziko lapansi kudzamasula mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa? Iyayi, mapemphero anaperekedwabe kwa Yehova. Pamene anali padziko lapansi, Yesu iyemwini anapemphera kaŵirikaŵiri kwa Atate wake wakumwamba, ndipo anaphunzitsa ena kuchita chimodzimodzi. Tangolingalirani za pemphero lachitsanzo, nthaŵi zina lotchedwa Pemphero la Ambuye kapena Atate Wathu, limodzi la mapemphero odziŵika koposa m’dziko. Yesu sanatiphunzitse kupemphera kwa iye; iye anatipatsa chitsanzo ichi: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.”​—Mateyu 6:6, 9; 26:39, 42.

Tsopano tiyeni tione nkhaniyi mosamalitsa mwa kupenda chimene pemphero lili kwenikweni.

Kodi Pemphero ndi Chiyani?

Pemphero lililonse lili mtundu wina wa kulambira. The World Book Encyclopedia imatsimikizira zimenezi mwa kunena kuti: “Pemphero lili mtundu wina wa kulambira mmene munthu angasonyeze kudzipereka kwake, kuyamikira, kulapa, kapena kupembedzera kwa Mulungu.”

Panthaŵi ina Yesu anati: “Kwalembedwa, kuti, [Yehova, NW] Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.” Yesu anamamatira ku choonadi cha maziko chakuti kulambira​—kumene kukuphatikizaponso mapemphero​—kuyenera kuperekedwa kwa Atate wake yekha, Yehova Mulungu.​—Luka 4:8; 6:12.

Kuzindikira Yesu m’Mapemphero Athu

Yesu anafa monga nsembe ya dipo ya mtundu wa anthu, anaukitsidwa ndi Mulungu, ndipo anakwezedwa pamalo apamwamba. Monga momwe mungaganizire, zonsezi zinadzetsa kusintha ponena za mapemphero olandirika. Mwa njira yanji?

Mtumwi Paulo akulongosola chisonkhezero chachikulu chimene malo a Yesu ali nacho pa pemphero motere: “Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.”​—Afilipi 2:9-11.

Kodi mawu akuti “m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde” amatanthauza kuti tiyenera kupemphera kwa iye? Iyayi. Mawu Achigiriki panopa “amatanthauza dzina palimene awo opinda bondo amagwirizanapo, pa limene kulambira konse (πᾶν γόνυ) kumagwirizana. Dzina limene Yesu walandira limasonkhezera onse pa kulambira kogwirizana.” (A Grammar of the Idiom of the New Testament, lolembedwa ndi G. B. Winer) Ndithudi, kuti pemphero lilandiridwe, liyenera kuperekedwa “m’dzina la Yesu,” komabe, ilo limaperekedwa kwa Yehova Mulungu ndipo limalemekeza iye. Pachifukwa chimenechi, Paulo anati: “M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”​—Afilipi 4:6.

Monga momwe njira imatsogolerera kumalo amene munthu akupitako, motero Yesu ndiye “njira” yotsogolera kwa Mulungu Wamphamvuyonse. “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine,” Yesu anawaphunzitsa zimenezo atumwi. (Yohane 14:6) Motero, tiyenera kupereka mapemphero athu kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu ndipo osati mwachindunji kwa Yesu iyemwiniyo.a

‘Komabe,’ ena angafunse motero, ‘kodi Baibulo silisimba kuti onse aŵiri wophunzira Stefano ndi mtumwi Yohane analankhula kwa Yesu ali kumwamba?’ Zimenezo nzoona. Komabe, zochitika zimenezi zisinaphatikizepo mapemphero, pakuti aliyense wa iwo Stefano ndi Yohane anaona Yesu m’masomphenya ndi kulankhula naye mwachindunji. (Machitidwe 7:56, 59; Chivumbulutso 1:17-19; 22:20) Kumbukirani kuti kungolankhula ngakhale kwa Mulungu mwa iko kokha sikumakhala pemphero. Adamu ndi Hava analankhula ndi Mulungu, akumapereka zifukwa zodzikhululukira pa tchimo lawo lalikululo, pamene Iye anawaweruza atachimwa mu Edene. Kulankhula kwawo kwa iye m’njira imeneyo sikunali pemphero. (Genesis 3:8-19) Chifukwa chake, kukakhala kulakwa kutchula mawu a Stefano kapena a Yohane kwa Yesu monga umboni wakuti tiyeneradi kupemphera kwa iye.

Kodi Ndimotani Mmene ‘Timaitanira pa’ Dzina la Yesu?

Kodi mukali ndi zikayikiro, mukumakuonabe kukhala koyenera kupemphera kwa Yesu? Mkazi wina analembera ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society kuti: “Pepani kuti ndidakali wosakhutiritsidwa kuti Akristu oyambirira sanapemphere kwa Yesu.” Iye anali kulingalira za mawu a Paulo pa 1 Akorinto 1:2, pamene anatchula za “onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m’malo monse.” Komabe, munthu ayenera kudziŵa kuti, m’chinenero choyambirira mawu akuti “kuitanira pa” angatanthauzenso zinthu zina zosakhala pemphero.

Kodi ndimotani mmene ‘anaitanira pa’ dzina la Kristu kulikonse? Njira ina inali yakuti otsatira a Yesu wa ku Nazarete anamuvomereza poyera kukhala Mesiya ndi “Mpulumutsi wa dziko lapansi,” akumachita ntchito zozizwitsa zambiri m’dzina lake. (1 Yohane 4:14; Machitidwe 3:6; 19:5) Chifukwa chake, The Interpreter’s Bible limanena kuti mawu akuti “kuitanira pa dzina la Ambuye . . . amatanthauza kuvomereza umbuye wake m’malo mwa kupemphera kwa iye.”

Kuvomereza Kristu ndi kusonyeza chikhulupiriro m’mwazi wake wokhetsedwa, umene umatheketsa kukhululukira machimo, kumaphatikizaponso “kuitanira pa dzina la Ambuye wathu, Yesu Kristu.” (Yerekezerani Machitidwe 10:43 ndi 22:16.) Ndipo timatchuladi dzina la Yesu nthaŵi zonse pamene tipemphera kwa Mulungu kupyolera mwa iye. Chotero, pamene kuli kwakuti Baibulo limasonyeza kuti tikhoza kuitanira pa dzina la Yesu, ilo silimanena kuti tiyenera kupemphera kwa iye.​—Aefeso 5:20; Akolose 3:17.

Zimene Yesu Angatichitire

Yesu analonjeza ophunzira ake momvekera bwino kuti: “Chimene chilichonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita.” Kodi zimenezi zimafuna kuti tipemphere kwa iye? Iyayi. Kupemphako kumachitidwa kwa Yehova Mulungu​—koma m’dzina la Yesu. (Yohane 14:13, 14; 15:16) Timapempha Mulungu kuti Mwana Wake, Yesu, agwiritsire ntchito mphamvu yake yaikulu ndi ulamuliro wake kaamba ka ife.

Kodi ndimotani mmene Yesu amalankhulira ndi otsatira ake oona lerolino? Mafotokozedwe a Paulo a mpingo wa Akristu odzozedwa angakhale chitsanzo. Iye anauyerekezera monga thupi ndi Yesu Kristu monga mutu. “Mutu” umagaŵira ziŵalo za thupi lauzimu zosoŵa zawo kudzera mu “mfundo ndi mitsempha,” kapena mwa njira ndi makonzedwe ogaŵira mpingo wake chakudya chauzimu ndi chitsogozo. (Akolose 2:19) M’njira yofananayo, Yesu lerolino amagwiritsira ntchito “mphatso mwa amuna,” (NW) kapena amuna oyeneretsedwa mwauzimu, kutsogolera mpingo, ngakhale kuwongolera pamene kukhala kofunika. Palibe makonzedwe alionse akuti ziŵalo za mpingo zilankhulane mwachindunji ndi Yesu kapena kupemphera kwa iye, koma iwo ayenera​—inde ayeneradi​—kupemphera kwa Atate wake wa Yesu, Yehova Mulungu.​—Aefeso 4:8-12.

Kodi Mumamlemekeza Motani Yesu?

Ponena za chipulumutso cha anthu, ndi mbali yaikulu chotani nanga imene Yesu akuichita! Mtumwi Petro analengeza kuti: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Kodi mumadziŵa kufunika kwa dzina la Yesu?

Mwa kusapemphera mwachindunji kwa Yesu, sikuti timachepetsa malo ake. M’malo mwake, timamlemekeza Yesu pamene tipemphera m’dzina lake. Ndipo monga momwe ana amalemekezera makolo awo mwa kuwamvera, timalemekeza Yesu Kristu mwa kumvera malamulo ake, makamaka lamulo latsopano la kukondana wina ndi mnzake.​—Yohane 5:23; 13:34.

Mapemphero Olandirika

Kodi mukufuna kumapereka mapemphero olandirika? Pamenepo aperekeni kwa Yehova Mulungu, ndipo chitani zimenezo m’dzina la Mwana wake, Yesu. Dziŵani chifuniro cha Mulungu, ndipo lolani kuti mapemphero anu asonyeze kuti mukuchizindikira. (1 Yohane 3:21, 22; 5:14) Pezani nyonga m’mawu a Salmo 66:20 akuti: “Wolemekezeka Mulungu, amene sanandipatutsira ine pemphero langa, kapena chifundo chake.”

Monga momwe taonera, mapemphero ali mtundu wina wa kulambira kumene kuyenera kuperekedwa kokha kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Mwa kupereka mapemphero athu onse kwa Yehova Mulungu, timasonyeza kuti talabadira chilangizo cha Yesu cha kupemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba.”​—Mateyu 6:9.

[Mawu a M’munsi]

a Ena angapemphere kwa Yesu chifukwa amakhulupirira kuti iye ndi Mulungu. Koma Yesu anali Mwana wa Mulungu, ndipo iyemwini analambira Yehova, Atate wake. (Yohane 20:17) Kuti mupeze malongosoledwe atsatanetsatane a nkhaniyi, onani Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena