Kusonkhana ndi Owopa Mulungu
“ANTHU kulikonse amakhumba ufulu ku mantha—mantha a chiwawa, mantha a ulova, ndi mantha a matenda owopsa. Nafenso timakhumba zimenezo. . . . Nanga, nchifukwa ninji tikulankhula za mmene tingakulitsire mantha?” Funso lokopa limenelo linafunsidwa ndi wokamba nkhani yaikulu pa uliwonse wa Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu” imene inayamba mu June 1994.
Anthu mamiliyoni ambiri amene anapezekapo—choyamba ku North America, ndiyeno pambuyo pake ku Ulaya, Central ndi South America, Afirika, Asia, ndi ku zisumbu zapanyanja—anali ofunitsitsa kudziŵa mmene angakulitsire mantha amenewo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kupeza kwathu madalitso amene Yehova Mulungu wasungira anthu ake kumadalira pa kukhala kwathu ndi mantha aumulungu. Osonkhanawo anasonkhana pamodzi kuti aphunzire mantha aumulungu, ndipo m’programu yamasiku atatu, anadziŵa zambiri ponena za mkhalidwe umenewu Wachikristu wofunika kwambiri.
‘Opani Mulungu ndi Kusunga Malamulo Ake’
Umenewo ndiwo unali mutu wa tsiku loyamba la msonkhano, wozikidwa pa Mlaliki 12:13. Kodi kuwopa Mulungu kumatanthauzanji? M’mbali yoyamba ya programu, tcheyamani wa msonkhano wachigawo anafotokoza kuti mantha aumulungu amasonyeza kuwopa ndi ulemu waukulu kaamba ka Yehova ndi kunyansidwa koyenera kwa kumkwiyitsa. Mantha aumulungu otero sali ofooketsa; ali mantha abwino ndi oyenera.
Kodi ndimotani mmene mantha abwino ameneŵa amatipindulitsira? Nkhani yotsatira yakuti, “Musaleme ndi Kuleka,” inafotokoza kuti mantha aumulungu adzatisonkhezera kusunga malamulo a Mulungu mwachimwemwe. Kuwonjezera pa chikondi chathu kwa Mulungu ndi anansi, mantha amenewo amatipatsa nyonga yauzimu. Inde, mantha aumulungu angatithandize kupeŵa kulefuka m’makani a moyo wosatha.
Ndiyeno panatsatira kufunsa, kumene kunapereka umboni wooneka wakuti mantha aumulungu amatichirikiza. Ofunsidwawo anafotokoza mmene kuwopa Mulungu kwaulemu kunawasonkhezerera kupitiriza ndi utumiki mosasamala kanthu za mphwayi, kuipidwa kwa anthu, kapena chizunzo ndi mmene kunawathandizira kupirira ngakhale kuti anakumana ndi ziyeso zovuta zaumwini.
Nangano, nchifukwa ninji anthu ena ali ndi mantha aumulungu pamene ena alibe? M’nkhani yakuti “Kukulitsa Mantha Aumulungu ndi Kupindula Nawo,” wokamba nkhani yaikulu anafotokoza kuti pa Yeremiya 32:37-39, Yehova analonjeza kuti akapatsa anthu Ake mtima wowopa Mulungu. Yehova amaika mantha aumulungu m’mitima yathu. Motani? Mwa mzimu wake woyera ndi Mawu ake ouziridwa, Baibulo. Komabe, mwachionekere, tiyenera kuyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kugwiritsira ntchito bwino lomwe zogaŵira zauzimu zochuluka zimene wapereka. Zimenezi zimaphatikizapo misonkhano yathu yachigawo ndi yampingo, imene imatithandiza kuphunzira kumuwopa iye.
Programu yamasana inayamba ndi chilangizo cha kudalira Yehova ndi Mawu ake. Chimenechi chinatsatiridwa ndi nkhani yonena za njira zazikulu zimene Ufumu uyenera kuyambukirira miyoyo yathu monga Akristu.
Ndiyeno panatsatira nkhani yosiyirana yoyamba mwa zitatu zoperekedwa pa msonkhano. “Mantha Aumulungu Amatisonkhezera Kumvera Zofunika Zaumulungu” ndiwo unali mutu wa nkhani yosiyirana imeneyi, imene inasumika maganizo pa banja. Wotsatirawu ndi uphungu wachidule wa m’Malemba ndi wogwira ntchito umene unaperekedwa.
□ Wa amuna: Mantha aumulungu ayenera kusonkhezera mwamuna kukonda mkazi wake monga thupi la iye mwini. (Aefeso 5:28, 29) Mwamuna samavulaza dala thupi lake, kudzinyazitsa pamaso pa mabwenzi ake, kapena kudyerera miseche zophophonya zake. Nchifukwa chake, ayenera kupatsa mkazi wake ulemu umene amadzipatsa iye mwini.
□ Wa akazi: Mantha aumulungu a Yesu anamsonkhezera ‘kukondweretsa Mulungu nthaŵi zonse.’ (Yohane 8:29) Akazi ayenera kutsanzira mzimu wabwino umenewu pochita ndi amuna awo.
□ Wa makolo: Makolo Achikristu angasonyeze mantha aumulungu mwa kuona mathayo awo aukholo mwamphamvu, akumaona ana awo monga choloŵa cha kwa Yehova. (Salmo 127:3) Chonulirapo chachikulu chimene makolo ayenera kukhala nacho ndicho kulera ana awo kuti akhale Akristu enieni.
□ Wa ana: Yehova amalangiza ana kumvera ‘akuwabala mwa Ambuye.’ (Aefeso 6:1) Chotero, kumvera kwawo makolo kumatanthauza kumvera Mulungu.
Nkhani yomaliza patsikulo inakhudza mtima wathu, pakuti inafotokoza chisoni chachikulu chimene tonsefe timakhala nacho pamene wokondedwa wathu amwalira. Komabe, chapakati pa nkhaniyo, panali zosangalatsa. Wokamba nkhaniyo anakondweretsa omvetsera mwa kulengeza kutulutsidwa kwa brosha latsopano Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Chofalitsidwa chimenechi chamasamba 32, cha zithunzi zamaonekedwe achibadwa, chimanena zambiri zimene zingathandize amene ali ndi maliro kumvetsetsa ndi kuchita ndi chisoni chimene chimakhalapo wokondedwa atamwalira. Kodi zinachitikapo kuti munasoŵa chonena kwa munthu amene wafedwa? Chigawo china cha brosha limeneli chimafotokoza mmene tingathandizire amene akulira maliro. Pamene anali kumvetsera kwa wokamba nkhaniyo, ambiri mwa omvetsera anali kulingalira za wina amene angapindule nalo brosha latsopano limeneli.
‘Perekani Utumiki Wopatulika ndi Mantha Aumulungu ndi Kuwopa’
Umenewo unali mutu wa tsiku lachiŵiri, wozikidwa pa Ahebri 12:28 (NW). Programu yammaŵa inali ndi nkhani yachiŵiri yosiyirana yakuti, “Mipingo Yomayenda m’Mantha Akuwopa Yehova.” Mbali yoyamba inanena za kupezeka pamisonkhano. Kukhalapo kwathu pamisonkhano kumasonyeza ulemu wathu kwa Mulungu ndi zogaŵira zake zauzimu. Mwa kupezekapo, timasonyeza kuti timawopa dzina lake ndi kuti tikufunitsitsa kugwirizana ndi chifuniro chake. (Ahebri 10:24, 25) Wokamba nkhani wachiŵiri anafotokoza kuti, kuti mipingo yonse iyende m’kuwopa Yehova, munthu aliyense ayenera kuchita mbali yake ya kusunga mayendedwe okoma. Wokamba nkhani yomaliza analankhula za thayo ndi ntchito imene Akristu onse ali nayo—kulengeza mbiri yabwino mosalekeza. Kodi tidzapitirizabe kulalikira mpaka liti? Kufikira Yehova atanena kuti zakwanira.—Yesaya 6:11.
Nkhani yotsatira inali ndi mutu wakuti “Chimwemwe cha Yehova Ndicho Linga Lanu,” umene ukulongosoledwa m’nkhani zophunzira m’magazini ano. (Nehemiya 8:10) Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova ali achimwemwe? Wokamba nkhaniyo anapereka zifukwa zingapo. Chapadera kwambiri nchakuti unansi wathu wolimba ndi Mulungu umatichititsa kukhala anthu achimwemwe koposa padziko lapansi. Tangolingalirani, wokamba nkhaniyo anakumbutsa osonkhanawo, tili ndi mwaŵi wa kukhala pakati pa anthu amene Yehova wawakokera kwa Yesu Kristu. (Yohane 6:44) Ha, chimenecho nchifukwa champhamvu chotani nanga chokhalira achimwemwe!
Chapadera pa msonkhano uliwonse ndicho ubatizo, ndipo umenewo unalipo pa Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu.” M’nkhani yakuti “Kudzipatulira ndi Ubatizo m’Kuwopa Yehova,” wokamba nkhani anafotokoza kuti mathayo aumwini a anthu obatizidwa ali anayi: (1) Tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mothandizidwa ndi zofalitsidwa zimene zimatithandiza kuwamvetsetsa ndi kuwagwiritsira ntchito; (2) tiyenera kupemphera; (3) tiyenera kuyanjana ndi okhulupirira anzathu pamisonkhano ya mpingo; ndipo (4) tiyenera kuchitira umboni dzina la Yehova ndi Ufumu wake.
Programu ya pa Loŵeruka masana inayamba ndi nkhani yolimbikitsa yakuti “Anthu Osasiyidwa ndi Yehova.” Zaka mazana 35 zapitazo, pamene mtundu wa Israyeli unayang’anizana ndi nthaŵi zovuta, Yehova anapereka chitsimikizo kupyolera mwa Mose, kuti: “Yehova Mulungu wanu . . . sadzakusoŵani, kapena kukusiyani.” (Deuteronomo 31:6) Yehova anachitadi zimene anawatsimikizirazo mwa kutetezera Aisrayeli pamene analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa ndi kulilanda. Lerolino, pamene tiyang’anizana ndi ziyeso zovuta, nafenso tingakhale ndi chidaliro cholimba chakuti Yehova sadzatisiya, malinga ngati timamatira kwambiri ndi kulabadira uphungu wa Mawu ake.
Kodi ndimotani mmene mungapezere chikondwerero poŵerenga Baibulo? M’nkhani yakuti “Ŵerengani Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika, Tsiku ndi Tsiku,” wokamba nkhaniyo anapereka lingaliro la kuŵerenga ndi maganizo ofufuza ndi kufunsa mafunso onga otsatirawa: Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsanji ponena za mikhalidwe ya Yehova ndi njira zake? Kodi ndingakhale bwanji wofanana kwambiri ndi Yehova m’mbali zimenezi? Kuŵerenga Baibulo motero kuli kokondweretsa ndi kofupa.
Ndiyeno maganizo anasumikidwa pa nkhani yachitatu yosiyirana paprogramu, yakuti, “Zogaŵira Zothandiza Awo Owopa Yehova.” Ngakhale kuti Yehova sangachitire zozizwitsa atumiki ake lerolino, iye amathandizadi iwo akumuwopa iye. (2 Petro 2:9) Nkhani yosiyirana imeneyi inafotokoza zogaŵira zinayi zochokera kwa Yehova zotithandiza m’nthaŵi zino zovuta: (1) Mwa mzimu wake, Yehova amatipatsa mphamvu yochitira ntchito imene sitingaichite mwa nyonga ya ife eni. (2) Mwa Mawu ake, amapereka uphungu ndi chitsogozo kwa ife. (3) Mwa dipo, amatipatsa chikumbumtima choyera. (4) Mwa gulu lake, kuphatikizapo akulu, amatipatsa chitsogozo ndi chitetezo. (Luka 11:13; Aefeso 1:7; 2 Timoteo 3:16; Ahebri 13:17) Mwa kugwiritsira ntchito bwino lomwe zogaŵira zimenezi, tidzakhoza kupirira ndi kupeza chiyanjo cha Yehova.
Nkhani yomaliza pa Loŵeruka masana inali yamutu wakuti “Tsiku Lochititsa Mantha la Yehova Lili Pafupi,” yozikidwa pa ulosi wa Malaki. Analiko masiku ochititsa mantha m’mbiri yakale, monga pamene chiweruzo chinaperekedwa pa Yerusalemu mu 70 C.E. Koma tsiku lochititsa mantha koposa limene anthu sanalionepo lidzakhala tsiku lilinkudza la Yehova pamene ‘chilango chidzabwezeredwa kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.’ (2 Atesalonika 1:6-8) Kodi zimenezo zili pafupi motani? Wokamba nkhaniyo anati: “Mapeto ali pafupi! Yehova akudziŵa tsiku limenelo ndi ola. Sadzasintha ndandanda yake ya nthaŵi. Tikupemphedwa kupirira modekha.”
Zinali zovuta kukhulupirira kuti masiku aŵiri anali atatha kale. Kodi tsiku lomaliza likabweretsanji?
“Opani Mulungu, Mpatseni Ulemerero”
Mutu wa tsikulo unazikidwa pa Chivumbulutso 14:7. M’programu yammaŵa, mpambo wa nkhani unafotokoza zina za ziphunzitso zamaziko zimene zimasiyanitsa Mboni za Yehova ndi magulu ena onse achipembedzo.
M’nkhani yakuti “Kudzakhala Kuuka kwa Olungama,” wokamba nkhaniyo anafunsa funso lochititsa chidwi lakuti: “Mkati mwa Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi limenelo, kodi ndiliti pamene awo amene anafa ali okhulupirika m’zaka zino zomalizira za dongosolo la zinthu la Satana adzaukitsidwa?” Yankho lake? “Baibulo silimanena,” anafotokoza motero wokamba nkhaniyo. “Komabe, kodi si kwanzeru kunena kuti awo amene akufa m’tsiku lathu akayamba kuukitsidwa kotero kuti adzagwirizane ndi khamu lalikulu la opulumuka Armagedo mu ntchito yaikulu ya kuphunzitsa imene idzachitika m’Tsiku Lachiweruzo lonse? Inde, ndithudi!” Kodi padzakhala opulumuka? Adzakhalapodi. Ziphunzitso za Baibulo ndi zitsanzo zake zimene zimatitsimikizira zimenezi zinafotokozedwa bwino lomwe m’nkhani yotsatira yakuti, “Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu.”
Kwa nthaŵi yaitali Mboni za Yehova zakhulupirira kuti Baibulo limapereka ziyembekezo ziŵiri—moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso kwa anthu mamiliyoni osaŵerengeka ndi moyo wosafa wakumwamba kwa anthu ochepa amene adzalamulira ndi Kristu mu Ufumu wake. Chiyembekezo chakumwamba chinafotokozedwa m’nkhani yakuti “Musawopa, Kagulu ka Nkhosa Inu.” (Luka 12:32) Polingalira za mkhalidwe umene ulipo padziko, kagulu ka nkhosa kayenera kukhala kolimba mtima; aliyense wa iwo ayenera kupirira kufikira mapeto. (Luka 21:19) “Kupanda mantha kwawo,” anatero wokamba nkhaniyo, “kumalimbikitsa awo a khamu lalikulu. Nawonso ayenera kukulitsa mkhalidwe wa maganizo wopanda mantha pamene akuyembekezera chiwomboledwe mkati mwa nthaŵi ya mavuto aakulu koposa amene dziko lapansi silinaonepo.”
Pamapeto a programu yammaŵa, omvetsera anaonerera mokondwera seŵero la m’Baibulo lakuti Zosankha Zimene Mukuyang’anizana Nazo. M’masiku a Yoswa, ndiponso a mneneri Eliya, Aisrayeli anafunikira kugamulapo. Anafunikira kupanga chosankha. Eliya anati: “Mukayikakayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo.” (1 Mafumu 18:21) Lerolinonso, mtundu wa anthu uyenera kugamulapo. Ino sindiyo nthaŵi ya kumakayikakayika. Kodi chosankha cholondola nchiti? Chimene chija chimene Yoswa wakale anapanga. Iye anati: “Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.
Zinaoneka ngati kuti nthaŵi ya nkhani yapoyera yamutu wakuti “Chifukwa Chake Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano” inakwana msanga pa Sande masana. Pa Chivumbulutso 14:6, 7, mtundu wonse wa anthu ukulangizidwa kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero.” Kodi nchifukwa ninji kuwopa Mulungu kuli kofunika mwamsanga tsopano? Chifukwa chakuti, monga momwe lembalo likupitirizira kunena, “yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” Kupyolera mwa Mwana wake, woikidwa pa mpando wachifumu tsopano monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, Yehova adzathetsa dongosolo la zinthu lodetsedwa ndi lopanduka lilipoli. Wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti imeneyi ndiyo njira yokha yodzetsera mpumulo kwa owopa Mulungu limodzinso ndi kupulumutsa ndi kusungitsa dziko lathu lapansili. Popeza kuti ano ndi masiku omalizira a dongosolo la zinthu limeneli, kuli kofunika mwamsanga kuwopa Mulungu woona tsopano!
Pambuyo pa phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda ya mlungu umenewo, wokamba nkhani womaliza anapita papulatifomu. Chifukwa cha programu ya msonkhano wachigawo, mantha aumulungu anakhala ndi tanthauzo lokulirapo kwa osonkhanawo, iye anafotokoza motero. Anagogomezera mapindu ochuluka amene owopa Mulungu amapeza. Wokamba nkhaniyo analengeza kutulutsidwa kwa vidiyo yatsopano—United by Divine Teaching. Imasonyeza mbali zapadera za Misonkhano Yamitundu Yonse ya “Chiphunzitso Chaumulungu” yochitidwa mu 1993-94. Pamene nkhaniyo inali kufika kumapeto ake, ambiri anasinkhasinkha m’maganizo kuti, ‘Kodi chaka chamaŵa chidzadzetsanji?’ Misonkhano yachigawo yamasiku atatu m’malo ambiri.
Pomaliza, wokamba nkhaniyo anatsegula pa Malaki 3:16, amene amati: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” Osonkhanawo anapita ali ndi chikhumbo chotsimikizirika cha kusinkhasinkha dzina la Yehova ndi kumtumikira ndi mantha aumulungu.
[Chithunzi patsamba 24]
Obatizidwa afunikira kupitiriza kusonyeza mantha aumulungu
[Chithunzi patsamba 25]
Seŵero lakuti “Zosankha Zimene Mukuyang’anizana Nazo” linakhomereza mwa omvetsera kufunika kwa kukhala otsimikiza potumikira Yehova
[Chithunzi patsamba 26]
Osonkhana anakondwera kulandira brosha latsopano lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira”