Kodi Kukambitsirana za Chipembedzo Kuli ndi Ubwino Wotani?
MAKOLO amakhala akuyembekezera mwachidwi kumva mawu oyamba a mwana wawo. Pamene amamva liwu lobwerezabwereza m’kukamba kwachibwana longa “Mama” kapena “Tata,” amakondwera kwambiri. Mwamsanga amauzako bwenzi lawo ndi anansi zimenezo. Kumva za kulankhula koyamba kwa mwana kulidi uthenga wabwino umene umakondweretsa.
Mawu omvedwa, zinthu zoonedwa, ndi mafungo amachititsa mwana kuchitapo kanthu. Ndithudi, iwo amachita mosiyana. Koma ngati nthaŵi ingopita popanda mwanayo kuchitapo kanthu pa zimenezi, pamenepo makolo adzayamba kuda nkhaŵa kuti mwina mwana wawo sadzakula bwino.
Makanda amachita bwino kwa anthu amene amawadziŵa. Pamene mayi afukata khanda lake, kaŵirikaŵiri limamwetulira mwachisangalalo. Komabe, lingalire pamene wachibale wodzacheza aligwira, ngakhale kukaniratu kuti ameneyo alinyamule. Achibale ambiri amene zimenezo zimawachitikira samaleka. Pamene khandalo liwazoloŵera, amakondwera kuona kuti vutolo limatha, ndipo pang’onopang’ono khandalo limayamba kumwetulira.
Mofananamo, achikulire ambiri amazengereza kukambitsirana poyera za zikhulupiriro zawo za chipembedzo ndi munthu amene sanamzoloŵere kwa nthaŵi yaitali. Iwo angakhale akudabwa kuti munthu wosamdziŵa angafunirenji kukambitsirana nkhani yaumwini—ya chipembedzo. Mwakutero, iwo amalola chopinga pakati pa iwo ndi aja olankhula za Mlengi. Amakana kukambitsirana chimene kwenikweni chili mkhalidwe wachibadwa wa anthu, chikhumbo cha kulambira.
Kwenikweni, tiyenera kukhala ofuna kuphunzira za Mlengi wathu, ndipo kukambitsirana ndi ena kungatitheketse kuphunzira. Zili motero chifukwa chakuti kuyambira kalekale, Mulungu walankhula ndi anthu poyera. Tiyeni tione mmene wachitira chimenecho.
‘Mvetserani ndi Kuphunzira’
Mulungu analankhula ndi munthu kwa nthaŵi yoyamba pamene analankhulana ndi Adamu m’munda wa Edene. Komabe, Adamu ndi Hava atachimwa, anakabisala pamene Mulungu anawaitana, pamene anafuna kulankhulanso nawo. (Genesis 3:8-13) Komabe, Baibulo lili ndi nkhani zonena za amuna ndi akazi amene anakondwera kulankhula ndi Mulungu.
Mulungu analankhula ndi Nowa ponena za chiwonongeko choyandikiracho cha dziko loipa la m’nthaŵi yake, pamene Nowayo anakhala “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Monga wolankhulira Mulungu ku mbadwo wake, Nowa sanangosonyeza chikhulupiriro pa zochita za Mulungu ndi munthu komanso anadzionetsera poyera kuti anali kumbali ya Yehova. Kodi Nowa anaona anthu akuchita motani pa zimenezo? Mwachisoni, ochuluka a m’nthaŵi yake “sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:37-39) Koma ife tinachita mwaŵi kuti ziŵalo zisanu ndi ziŵiri za banja la Nowa zinamvetsera, zinamvera malangizo a Mulungu, nizipulumuka Chigumula cha dziko lonsecho. Kwa iwowo ndi kumene kunachokera anthu onse omwe alipo lerolino.
Pambuyo pake, Mulungu analankhula ndi mtundu wonse wa anthu, Israyeli wakale. Kupyolera mwa Mose, Mulungu anawapatsa Malamulo Khumi ndi malamulo enanso pafupifupi 600 ogwira ntchito mofananamo. Yehova anafuna kuti Aisrayeli awamvere onsewo. Mose analangiza kuti nthaŵi zonse patapita zaka zisanu ndi ziŵiri, pa Madyerero a Misasa apachaka, Chilamulo cha Mulungu chinayenera kuŵerengedwa mofuula. Iye analangiza kuti, “sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu.” Ndi cholinga chotani? “Kuti amve, ndi kuti aphunzire kuwopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi.” Onse anafunikira kumva ndi kuphunzira. Tangolingalirani za chisangalalo chachikulu chimene anakhala nacho pokambitsirana zimene anamva!—Deuteronomo 31:10-12.
Patapita zaka zoposa mazana asanu, Mfumu ya Yuda Yehosafati inasonkhanitsa akalonga ndi Alevi kuchita mkupiti wa kuyambitsanso kulambira Yehova koyera. Amuna ameneŵa anayenda kuzungulira m’mizinda yonse ya Yuda akumaphunzitsa okhala mmenemo malamulo a Yehova. Mwa kukambitsirana zimenezo poyera, mfumuyo inasonyeza kulimba mtima kwake pa kulambira koona. Ponena za anthu ake, iwo anafunikira kumva ndi kuphunzira.—2 Mbiri 17:1-6, 9.
Kuchitira Umboni mwa Kukambitsirana
Mulungu anatumiza Mwana wake, Yesu, kudza pa dziko lapansi kudzatumikira monga Womlankhulira Wake. (Yohane 1:14) Pamene ophunzira ake atatu anaona Yesu akusandulika pamaso pawo, anamva liwu la Mulungu lenilenilo likulengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” (Mateyu 17:5) Iwo anamvera mosavuta.
Mofananamo, Yesu analamula atumwi ake kulengeza zifuno za Mulungu kwa anthu ena. Koma pamene kunatsala miyezi isanu ndi umodzi ya utumiki wake pa dziko lapansi, Yesu ananena kuti ntchito yolalikira Ufumu wa kumwamba inali yaikulu kwambiri kwakuti pakafunikira ophunzira owonjezereka. Iye anaphunzitsa okwanira 70 njira yokambitsirana ndi anthu achilendo za Ufumu wa Mulungu, nawatumiza kukalalikira poyera uthengawo. (Luka 10:1, 2, 9) Atakhala pafupi kubwerera kumwamba kwa Atate wake, Yesu anasonkhezera otsatira ake kuyamba kulankhula kwa ena za uthenga umenewu, nawalamulira kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Kuzungulira dziko lonse, Akristu oona lerolino akuchita ntchito imeneyo mwa kukambitsirana uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi anansi awo. Makambitsirano ameneŵa amawakhozetsa kuchitira umboni choonadi chonena za Mlengi, Yehova.—Mateyu 24:14.
Makambitsirano Omangilira ndi Amtendere
Kodi ophunzira a Yesu anayenera kukambitsirana ndi ena zikhulupiriro zawo m’njira yotani? Iwo sanafunikire kukwiyitsa otsutsa, ngakhale kukangana nawo. M’malo mwake, anafunikira kufunafuna aja amene anali ofuna kulandira uthenga wabwino, ndiyeno kupereka umboni wa Malemba wouchirikiza. Ndithudi, Mulungu anaona machitidwe a aja omwe analankhulana ndi ophunzira a Mwana wake, monga momwe Yesu analengezera: “Iye wakulandira inu, andilandira ine, ndi wakundilandira ine, amlandira iye amene ananditumiza ine.” (Mateyu 10:40) Unali mwano wotani nanga pamene okhala m’nthaŵi ya Yesu ambiri anakana uthenga wake!
“Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu,” analangiza motero mtumwi Wachikristu Paulo. M’malo mwake, “akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi.” (2 Timoteo 2:24, 25) Njira imene Paulo analengezera uthenga wabwino kwa anthu a ku Atene, mu Girisi, imapereka chitsanzo chabwino. Iye anakambitsirana ndi Ayuda m’sunagoge wawo. Masiku onse m’bwalo la malonda analankhula ndi “iwo amene anakomana nawo.” Ngakhale kuti ena, mosakayikira, anangokonda kumvetsera malingaliro atsopano, Paulo analankhula molunjika ndi m’njira yokoma mtima. Iye anakambitsirana ndi omvetsera ake uthenga wa Mulungu, umene unafuna kuti iwo alape. Kachitidwe kawo kanali kofanana ndi ka anthu lerolino. “Ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.” Paulo sanafune kungopitiriza makambitsirano amenewo. Pokhala atalalikira uthenga wake, “anatuluka pakati pawo.”—Machitidwe 17:16-34.
Pambuyo pake, Paulo anauza ziŵalo za mpingo Wachikristu ku Efeso kuti ‘sanawabisira zinthu zopindulira, osazilalikira kwa iwo, ndi kuwaphunzitsa pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.’ Ndiponso, anali ‘atachitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye Yesu Kristu.’—Machitidwe 20:20, 21.
Zitsanzo za m’Malemba zimenezi zimasonyeza mmene atumiki a Mulungu okhulupirika a m’nthaŵi za Baibulo anakambitsirana za chipembedzo. Mofananamo lerolino, momvera lamulo Mboni za Yehova zimakambitsirana chipembedzo ndi anansi awo.
Makambitsirano Omwe Amapindula Zambiri
‘Mverani Mawu a Mulungu.’ ‘Mverani malamulo ake.’ Mawu osonkhezera amenewo amapezeka kaŵirikaŵiri chotani nanga m’Baibulo! Mukhoza kulabadira zitsogozo za Baibulo zimenezi pamene Mboni za Yehova zifikanso kudzalankhula nanu. Mvetserani uthenga wa m’Baibulo umene zikubweretserani. Uthenga umenewo suli wa nkhani za ndale koma umachirikiza boma la Mulungu lakumwamba, Ufumu wake. Imeneyi ndiyo njira ya Mulungu yochotsera zochititsa mikangano imene ilipo. (Danieli 2:44) Pambuyo pake, ulamuliro wa Mulungu umenewu wochokera kumwamba udzakonza makonzedwe akuti dziko lonse lapansi lisandulizidwe paradaiso monga munda wa Edene.
Yemwe kale anali tekitivi wa polisi ankakana nthaŵi zonse kumvetsera pamene Mboni za Yehova zinalankhula kwa iye za Baibulo. Koma poona kuwonjezeka kwa upandu umene anali kukumana nawo, anagwiritsidwa mwala ndi moyo. Motero anauza Mboni imene inamfikira ulendo wotsatira kuti akafufuza umboni wa uthenga wa Baibulo. Chotstirapo chinali makambitsirano a nthaŵi zonse. Ngakhale kuti wapolisiyo ankasamukasamuka, Mboni zinamfunafuna ndi kumpeza kumalo atsopano aliwonse amene anapitako kuti zipitirize naye makambitsirano. Potsirizira pake wapolisiyo anavomereza kuti: “Umboni umene ndinkafunafuna unalipo pafupi nthaŵi yonseyi m’Malemba Oyera. Mboni zija zikadapanda kulimbikira kulankhula nane, bwenzi ndidakali kuja kunja ndisakudziŵabe chifuno cha moyo. Koma mmene zakhaliramu, ndaphunzira choonadi, ndipo ndidzawonongera masiku anga otsalawo pa kufunafuna ena amene akufunafuna Mulungu muja ndinachitira ine.”
Omvetsera a mtima wofunadi amafuna kudziŵa zochuluka. Moyenerera, iwo amafuna kumva zifukwa za ziphunzitso zolalikidwa kwa iwo. (1 Petro 3:15) Monga momwe mwana wamng’ono amafunsira makolo ake mafunso ochuluka ndi kufuna kuti iwo ayankhe, inunso muli woyenera kufuna kuti Mboni zikupatseni mayankho omveka bwino. Mungakhale ndi chidaliro chakuti iwo adzakhala okondwa kufikanso kudzakambitsirananso nanu uthenga wa m’Baibulo.
Mwinamwake mumadziŵa zina za m’Baibulo. Mwina mukudziŵa kuti zimene Mulungu amafuna kwa inu zidzafuna kuti musinthe zinthu zina pa moyo wanu. Musazengereze pa kuchitapo kanthu chifukwa chowopa kuti zofuna za Mulungu zidzakutayitsani zambiri. Zidzangokupatsani chimwemwe chenicheni. Mudzazindikira zimenezi pamene mupita patsogolo pang’onopang’ono.
Choyamba, talingalirani za amene Yehova ali, zimene amafuna kwa inu, ndi zimene walonjeza. Funsani Mboni kuti zikusonyezeni zimene Baibulo limanena pa zimenezi. Tsimikizirani zimene Mboni zikunena mwa kuona m’Baibulo lanu. Mutadziŵa kuti Mboni zimalingalira bwino pa zimene zimalalikira monga choonadi ponena za chipembedzo, mosakayika mudzafuna kuphunzira zinthu zambiri zimene izo zingakambitsirane nanu m’Malemba.—Miyambo 27:17.
Mukuitanidwa kukadzionera nokha mmene Mboni zimachitira pa malo osonkhanira a kwanuko, pa Nyumba Yaufumu. Kumeneko mudzamva makambitsirano opindulitsa a Mawu a Mulungu. Mudzaona mmene aja okhalapo amasangalalira polankhuzana za zifuniro za Mulungu. Lolani Mboni zimenezi zikuthandizeni kuphunzira choonadi chonena za chifuniro cha Mulungu kwa ife lerolino. Yankhani chiitano cha Mulungu cha kukambitsirana za kulambira koona ndi kupeza chivomerezo chake, ngakhaletu moyo wosatha m’Paradaiso.—Malaki 3:16; Yohane 17:3.
[Chithunzi patsamba 5]
Nowa analankhula poyera za chifuno cha Mulungu
[Zithunzi patsamba 7]
Monga momwe Paulo anachitira ku Atene wakale, Mboni za Yehova zimaphunzitsa ena choonadi cha Baibulo