Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/1 tsamba 3-5
  • Lonjezo la Dziko Lopanda Kusaona Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lonjezo la Dziko Lopanda Kusaona Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusaona Mtima Kumakuyambukirani
  • Zimene Baibulo Limatiuza
  • Anthu Angathe Kusintha
  • Lonjezo la Yehova
  • N’chifukwa Chiyani Kuli Ziphuphu Zochuluka Chotere?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kuthetsa Ziphuphu ndi Lupanga la Mzimu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Katangale Adzatha M’Boma?
    Nkhani Zina
  • Ziphuphu—Zili Ponseponse
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/1 tsamba 3-5

Lonjezo la Dziko Lopanda Kusaona Mtima

KUSAONA MTIMA kwaloŵerera mbali zonse za chitaganya cha anthu. Kaya mukhale mu boma, zasayansi, zamaseŵero, zachipembedzo, kapena m’zamalonda, kusaona mtima kukuonekera kukhala kosalamulirika.

M’dziko lililonse, mbiri yopsinja maganizo ya nkhani za kusaona mtima imakulitsidwa. Ambiri amene adzipereka kuti atumikire anthu akuvumbulidwa kukhala akumadzilemeretsa mwa kulandira ziphuphu ndi ziwongola dzanja. Upandu wa kusaona mtima kwa a m’maofesi uli wowanda. Anthu omawonjezereka a malo apamwamba m’chitaganya cha anthu kapena achuma amapatsidwa milandu yaikulu ya kuwononga makhalidwe ndi upandu pa ntchito zawo zamasiku onse.

Pali nkhaŵa yomakula pa zimene magazini ena a ku Ulaya anafotokoza kukhala “‘kusaona mtima kwa apamwamba’​—mchitidwe umene akuluakulu a boma, nduna, ndiponso kaŵirikaŵiri, atsogoleri a boma amafuna chiwongola dzanja asanavomereze zogula zazikulu ndi ntchito zina zazikulu zachitukuko.” M’dziko lina “kufufuza kwa zaka ziŵiri kwa apolisi ndi kumanga anthu pafupifupi tsiku lililonse sikunaletse anthu osaona mtima osalamulirikawo,” akutero magazini Achibritishi The Economist.

Chifukwa cha kusaona mtima kofalikira kotero, lerolino ambiri amalingalira kuti palibe munthu amene angamdalire. Amavomerezana ndi malingaliro a wolemba Baibulo Davide pamene anati: “Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.”​—Salmo 14:3.

Kodi mumalimbana motani ndi kusaona mtima kofala kumene kulipo? Lerolino anthu ochuluka amangokunyalanyaza. Koma ngakhale ngati munyalanyaza kusaona mtimako, mudzavutika nakobe. Motani?

Kusaona Mtima Kumakuyambukirani

Kusaona mtima kochitidwa pamlingo waukulu ndi waung’ono komwe kumawonjezera kukwera mitengo kwa zinthu, kumachititsa zinthu kukhala zopangidwa mosalimba, ndipo kumachititsa kuchepa kwa ntchito ndi malipiro otsika. Mwachitsanzo, kukuyerekezeredwa kuti maupandu onga kuba ndalama ndi chinyengo amawonongetsa ndalama zoŵirikiza pafupifupi nthaŵi khumi kuposa ndalama zonse zowonongedwa ndi kuswa nyumba, kulanda, ndi kuba. The New Encyclopædia Britannica (1992) ikunena kuti “mtengo wa upandu wa makampani aakulu mu United States wayerekezeredwa kukhala pa $200,000,000,000 pa chaka​—kuwirikiza katatu mtengo wa upandu wolinganizidwa.” Buku limeneli likufotokoza kuti pamene kuli kwakuti ziyambukiro zake sizingadziŵidwe mosavuta, “maupandu otero ali ndi chiyambukiro chachikulu choipa pa kutetezereka kwa antchito, ogula, ndi malo okhala.”

Zotulukapo zopweteka za kusaona mtima zimatikumbutsa za mawu a Mfumu Solomo: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.”​—Mlaliki 4:1.

Pamenepa, kodi ife tiyenera kungololera kusaona mtima? Kodi nkosapeŵeka? Kodi dziko lopanda kusaona mtima nlosatheka? Tikukondwa kunena kuti ayi! Baibulo limatiphunzitsa kuti chisalungamo ndi kusayeruzika zidzachotsedwa posachedwa.

Zimene Baibulo Limatiuza

Baibulo limatiuza kuti kusaona mtima kunayamba pamene mngelo wina wamphamvu anapandukira Mulungu ndi kusonkhezera anthu oyamba aŵiri kugwirizana naye. (Genesis 3:1-6) Palibe chinthu chabwino chimene chinatuluka m’njira yawo yauchimoyo. M’malo mwake, kuyambira tsiku limene Adamu ndi Hava anachimwira Yehova Mulungu, anayamba kuvutika ndi zotulukapo za kusaona mtima. Matupi awo anayamba kunyentchera, kukumawatsogolera ku imfa yosapeŵeka. (Genesis 3:16-19) Kuyambira pamenepo, mbiri ili ndi zitsanzo zambiri za ziphuphu, kunamiza, ndi chinyengo. Komabe, zimachitika kuti amaliwongo ake ochuluka amazemba chilango.

Mosiyana ndi apandu wamba, akuluakulu amakampani ndi andale osaona mtima kaŵirikaŵiri samaikidwa m’ndende kapena kubweza zinthu zopezedwa molakwazo. Chifukwa cha mkhalidwe wachinsinsi wa ziphuphu, ziwongola dzanja, ndi malipiro, kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kuvumbula kusaona mtima kochitidwa pa mlingo waukulu. Koma zimenezi sizimatanthauza kuti dziko lopanda kusaona mtima nlosatheka.

Kuwonjoledwa pa kusaona mtima kudzachokera kwa Mlengi wa munthu, Yehova Mulungu. Kuloŵerera kwa Mulungu ndiko yankho lokha. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mdani wosaoneka wa anthu, Satana Mdyerekezi, akupitirizabe kusokeretsa anthu. Pa 1 Yohane 5:19 timaŵerenga kuti, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Kodi nchiyaninso chimene chingafotokoze za kuwonjezereka kwa kusaona mtima ​—kumene kochuluka kumachitidwa popanda chilango?

Palibe zoyesayesa za anthu zamtundu uliwonse zimene zingagonjetse Satana ndi ziŵanda zake. Kuloŵerera kwa Mulungu kokha kungapereke kwa anthu omvera “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Yehova akulonjeza kuti posachedwa Satana adzamangidwa kuti asanyengenso anthu. (Chivumbulutso 20:3) Pakali pano, ngati tikufuna kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu lopanda kusaona mtima, tiyenera kukana njira zosaona mtima za dzikoli.

Anthu Angathe Kusintha

M’masiku a Yesu Kristu, munali awo amene anaipitsa ulamuliro wawo ndi kupondereza anthu anzawo. Mwachitsanzo, okhometsa msonkho anali ndi mbiri yoipa chifukwa cha machitidwe awo osaona mtima. Anachita zimenezi mosasamala kanthu za lamulo lomveka bwino la Mulungu: “Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama.” (Eksodo 23:8) Zakeyu, mkulu wa amisonkho, anavomera kuti analanda anthu mwa kuwapatsa mlandu monama. Koma m’malo mwa kuchirikiza kukonzanso zinthu m’chitaganya pa mlingo waukulu, Yesu anadandaulira anthu kulapa ndi kuleka njira zawo zosaona mtima. Chotero, okhometsa msonkho odziŵika kukhala osaona mtima onga Mateyu ndi Zakeyu analeka moyo wawo wakale.​—Mateyu 4:17; 9:9-13; Luka 19:1-10.

Awo amene amaloŵa m’machitachita osaona mtima lerolino nawonso angasiye kusaona mtima kwawoko mwa kuvala “munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:24) Kukhoma msonkho moona mtima kapena kuleka kugwirizana ndi ena m’zinthu zokayikitsa kungakhale kovuta. Komabe, mapindu ake amadza mwa kuyesayesa zolimba.

Pokhala osalamuliridwa ndi dziko losaona mtimali, awo amene ali ndi nkhaŵa ya ubwino wa ena amakhala ndi mtendere mu mtima. Samawopa kugwidwa chifukwa cha kuchita zoipa. M’malo mwake, amakhala ndi chikumbumtima chabwino. Amatsanzira chitsanzo cha m’Baibulo cha mneneri Danieli. Nkhani ya m’Baibuloyo imati nthaŵi zonse akuluakulu a boma anafunafuna kupezera mlandu Danieli. “Koma sanakhoza kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.”​—Danieli 6:4.

Lonjezo la Yehova

Yehova akulonjeza kuti “angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziŵitsadi kuti omwe awopa Mulungu nawopa pamaso pake adzapeza bwino; koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa sawopa pamaso pa Mulungu.”​—Mlaliki 8:12, 13.

Kudzakhala kotonthoza chotani nanga pamene kusaona mtima sikudzadzetsanso chisoni! Lidzakhala dalitso labwino chotani nanga kukhala ndi moyo kosatha m’dziko lopanda kusaona mtima! Zimenezi sizili zosatheka. Baibulo limanena za “chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.” (Tito 1:2) Ngati mumada kusaona mtima ndi kukonda chilungamo, mungadzaonedi kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu la dziko lopanda kusaona mtima.

[Chithunzi patsamba 4]

Kusaona mtima nkofala m’boma ndi m’zamalonda

[Chithunzi patsamba 5]

Kaŵirikaŵiri akuluakulu a boma amakhudzidwa ndi nkhani ya kusaona mtima

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena