Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 10/1 tsamba 3-4
  • Ziphuphu—Zili Ponseponse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ziphuphu—Zili Ponseponse
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Lonjezo la Dziko Lopanda Kusaona Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuthetsa Ziphuphu ndi Lupanga la Mzimu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Katangale Adzatha M’Boma?
    Nkhani Zina
  • N’chifukwa Chiyani Kuli Ziphuphu Zochuluka Chotere?
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 10/1 tsamba 3-4

Ziphuphu​—Zili Ponseponse

“Boma limapatsa kampani yathu ntchito yoti tigwire. Koma nthawi zambiri timayembekezera kwa miyezi iwiri kapena itatu kuti atipatse malipiro a ntchito imene tagwira. Komabe posachedwapa ndinalandira foni kuchokera kwa munthu wina wogwira ntchito m’boma. Iye anandiuza kuti akhoza kutithandiza kuti tizilandira mofulumira malipiro athu ngati titam’patsa ndalama.”—JOHN.a

KODI anthu ena anayamba akuuzani kuti mupereke ziphuphu? Mwina zimene tatchulazi sizinakuchitikireni, komabe n’kutheka kuti munavutikapo chifukwa cha ziphuphu zimene ena anachita.

Malinga ndi lipoti limene bungwe lina loona za katangale linatulutsa m’chaka cha 2011 (Transparency Internationalb) “pa mayiko komanso madera okwana 183, mayiko ambiri anaonetsa kuti sanachite bwino pa nkhani yolimbana ndi katangale.” Komanso lipoti limene bungweli linatulutsa m’chaka cha 2009, linasonyeza kuti katangale sanasiye malo. Lipotilo linati: “Zikuonekeratu kuti palibe dziko limene simuchitika zakatangale.”

“Kuchita ziphuphu n’kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa n’cholinga chofuna kupeza kenakake. Ziphuphu zimachititsa kuti anthu azivutika chifukwa choti anthu ena audindo sakuchita zinthu mwachilungamo.”​—TRANSPARENCY INTERNATIONAL

Nthawi zina kuchita katangale kapena ziphuphu kumabweretsa mavuto aakulu. Mwachitsanzo, magazini ina inanena kuti “ziphuphu komanso kuchita zinthu mosasamala” ndi zina mwa zimene zinachititsa kuti anthu ambiri afe pa chivomezi chachikulu chimene chinachitika ku Haiti m’chaka cha 2010. Magaziniyi inanenanso kuti: “Nyumba zambiri m’dzikoli sizinamangidwe bwino chifukwa anthu amene ankayang’anira ntchitoyo ankalandira ziphuphu.”—Time.

Kodi ziphuphu zidzatha? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyenera kudziwa kaye zimene zimachititsa anthu kuti azichita ziphuphu. Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

a Dzina lasinthidwa.

b Bungweli limandandalika mmene mayiko achitira pa nkhani ya katangale potengera zakatangale zimene zimachitika m’mabungwe a boma.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena