Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/1 tsamba 6-10
  • Ngakhale Tilira, Sitili Opanda Chiyembekezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngakhale Tilira, Sitili Opanda Chiyembekezo
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Imfa Iloŵa m’Banja la Munthu
  • Okhulupirika Amene Analira
  • Chisoni m’Nthaŵi ya Yesu
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akufa?
  • Chithandizo Chogwira Ntchito kwa Olira
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Kuchita Chisoni Nkulakwa?
    Galamukani!—1994
  • Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Kodi Kulira Maliro N’kulakwa?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/1 tsamba 6-10

Ngakhale Tilira, Sitili Opanda Chiyembekezo

“Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” ​—1 ATESALONIKA 4:13.

1. Kodi nchiyani chimene anthu amakumana nacho nthaŵi zonse?

KODI mwataya wokondedwa wanu mu imfa? Mosasamala kanthu za msinkhu, ambirife tagwidwa ndi chisoni pamene tataya wachibale kapena bwenzi. Mwinamwake anali agogo, kholo, mnzanu wa muukwati, kapena mwana. Ukalamba, matenda, ndi ngozi nthaŵi zonse zimatenga miyoyo. Upandu, chiwawa, ndi nkhondo zimawonjezeranso nsautso ndi chisoni. Kuzungulira dziko lonse, avareji ya anthu oposa 50 miliyoni amafa chaka chilichonse. Avareji ya tsiku ndi tsiku mu 1993 inali 140,250. Chisoni cha pa imfa chimakhudza mabwenzi ndi banja, ndipo chisoni cha kutayikidwa chimakhala chachikulu.

2. Kodi nchiyani chimene chimaoneka kukhala chachilendo ponena za kufa kwa ana?

2 Kodi sitingamvere chisoni makolo a ku California, U.S.A., amene anataya mwana wawo wamkazi wokhala ndi pakati m’ngozi yomwaza mtima yagalimoto? Panthaŵi imodzi chabe, iwo anataya mwana wawo yekha wamkazi ndi khanda limene likanakhala mdzukulu wawo woyamba. Mwamuna wa wakufayo anataya mkazi ndi mwana wake wachisamba mwamuna kapena mkazi. Kwa makolo, kufedwa mwana, kaya wamng’ono kapena wamkulupo, kuli kosazoloŵereka. Sikuli kozoloŵereka kuti ana ayambirire makolo kufa. Tonsefe timakonda moyo. Chifukwa chake, imfa ilidi mdani.​—1 Akorinto 15:26.

Imfa Iloŵa m’Banja la Munthu

3. Kodi imfa ya Abele iyenera kuti inakudza motani Adamu ndi Hava?

3 Uchimo ndi imfa zalamulira monga mafumu kwa zaka pafupifupi zikwi zisanu ndi chimodzi za mbiri ya anthu, chiyambire chipanduko cha makolo athu aumunthu oyamba, Adamu ndi Hava. (Aroma 5:14; 6:12, 23) Baibulo silimatiuza mmene iwo anachitira pamene mwana wawo Abele anaphedwa ndi mbale wake Kaini. Pazifukwa zambiri, chiyenera kukhala chinali chochitika chokhwethemula maganizo kwa iwo. Panopo, kwanthaŵi yoyamba, iwo anadzionera ndi maso imfa ya munthu, yochitikira mwana wawo weniweni. Iwo anaona chipatso cha chipanduko ndi kupitiriza kwawo kugwiritsira ntchito ufulu molakwa. Kaini, mosasamala kanthu za machenjezo ochokera kwa Mulungu, anasankha kuchita mbanda yapaubale yoyamba. Timadziŵa kuti Hava ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri ndi imfa ya Abele chifukwa pamene anabala Seti, anati: “Mulungu wandiloŵezera ine mbewu ina m’malo mwa Abele amene Kaini anamupha.”​—Genesis 4:3-8, 25.

4. Kodi nchifukwa ninji nthanthi ya moyo wosafa sinakhale yotonthoza pa imfa ya Abele?

4 Makolo athu oyamba aumunthu anadzioneranso chotulukapo cha chiweruzo cha Mulungu pa iwo​—chakuti ngati akapanduka ndi kukhala osamvera, ‘akafa ndithu.’ Mosasamala kanthu za bodza la Satana, mwachionekere nthanthi ya moyo wosafa inali isanakhalepo, choncho iwo sanapeze chitonthozo mwa iyo. Mulungu adati kwa Adamu: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” Iye sanatchulepo za kukhalako kwa pambuyo pake monga moyo wosafa kumwamba, m’helo, Limbo, purigatoriyo, kapena kwina kulikonse. (Genesis 2:17; 3:4, 5, 19) Monga miyoyo imene inachimwa, potsirizira pake Adamu ndi Hava akamwalira ndi kusakhalakonso. Mfumu Solomo anauziridwa kulemba kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika. Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano.”​—Mlaliki 9:5, 6.

5. Kodi chiyembekezo chenicheni cha akufa nchiyani?

5 Ha, mawuwo ngoona chotani nanga! Ndithudi, ndani amene angakumbukire makolo okhalako zaka mazana aŵiri kapena atatu zapitazo? Kaŵirikaŵiri ngakhale manda awo sadziŵikanso kapena anaiŵalika. Kodi zimenezo zimatanthauza kuti palibe chiyembekezo cha akufa athu okondedwa? Kutalitali! Marita anati kwa Yesu ponena za mlongo wake wakufa, Lazaro: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:24) Anthu Achihebri anakhulupirira kuti Mulungu akaukitsa akufa m’nthaŵi ya mtsogolo. Komabe, zimenezo sizinawaletse kulira imfa ya wokondedwa.​—Yobu 14:13.

Okhulupirika Amene Analira

6, 7. Kodi Abrahamu ndi Yakobo anachita motani pa imfa?

6 Pafupifupi zaka zikwi zinayi zapitazo, pamene Sara mkazi wa Abrahamu anamwalira, “Abrahamu anadza ku maliro a Sara kuti amlire.” Mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ameneyo anasonyeza chisoni chachikulu pa imfa ya mkazi wake wokondedwa ndi wokhulupirika. Ngakhale kuti anali mwamuna wochita zinthu wolimba mtima, sanachite manyazi kusonyeza chisoni chake ndi misozi.​—Genesis 14:11-16; 23:1, 2.

7 Chochitika cha Yakobo chinali chofanana. Kodi iye anachita motani pamene ananyengedwa ndi kukhulupirira kuti mwana wake Yosefe anaphedwa ndi chilombo? Timaŵerenga pa Genesis 37:34, 35 kuti: “Yakobo ndipo anang’amba malaya ake, navala chiguduli m’chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri. Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.” Inde, kuli kwaumunthu ndi kwachibadwa kusonyeza chisoni pamene wokondedwa amwalira.

8. Kodi ndimotani mmene Ahebri kaŵirikaŵiri anasonyezera chisoni chawo?

8 Ena angalingalire kuti malinga ndi miyambo yamakono kapena ya kwanuko, kachitidwe ka Yakobo kanali kopambanitsa ndi kodzionetsera. Koma iye anali mbadwa ya nyengo ina ndi mwambo wina. Kusonyeza kwake chisoni​—kuvala chiguduli​—ndiko kuyamba kutchulidwa kwa kachitidwe kameneka m’Baibulo. Komabe, monga momwe kwalongosoledwa m’Malemba Achihebri, kulira kunasonyezedwanso mwa kubuula, mwa kupeka nyimbo zamaliro, ndi mwa kukhala pansi m’mapulusa. Mwachionekere, Ahebri sanaletsedwe kusonyeza chisoni chawo m’njira zoyenera.a​—Ezekieli 27:30-32; Amosi 8:10.

Chisoni m’Nthaŵi ya Yesu

9, 10. (a) Kodi Yesu anachita motani pa imfa ya Lazaro? (b) Kodi chimene Yesu anachita chimatiuzanji ponena za iye?

9 Kodi tinganenenji za ophunzira oyambirira a Yesu? Mwa chitsanzo, pamene Lazaro anafa, alongo ake Marita ndi Mariya analira maliro ake ndi misozi. Kodi munthu wangwiroyo Yesu anachita motani pamene anafika pamalopo? Nkhani yolembedwa ndi Yohane imati: “Mariya, pofika pamene panali Yesu, mmene anamuona iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno inu, mlongo wanga sakadamwalira. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumaperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, nati, mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. Yesu analira.”​—Yohane 11:32-35.

10 “Yesu analira.” Mawu aŵiri chabe ameneŵa amatiuza zochuluka ponena za umunthu wa Yesu, chifundo chake, ndi malingaliro ake. Ngakhale kuti anadziŵa bwino lomwe za chiyembekezo cha chiukiriro, “Yesu analira.” (Yohane 11:35) Nkhaniyo ikupitiriza kunena kuti oona zimenezo anati: “Taonani, anamkondadi [Lazaro]!” Ndithudi, ngati munthu wangwiro Yesu analira ndi kutayika kwa mnzake, sikuli konyazitsa ngati mwamuna kapena mkazi alira momveka kapena ndi misozi lerolino.​—Yohane 11:36.

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akufa?

11. (a) Kodi tingaphunzirenji pa zitsanzo za m’Baibulo za kulira maliro? (b) Kodi nchifukwa ninji sitimalira monga aja opanda chiyembekezo?

11 Kodi tingaphunzirenji pa zitsanzo za m’Baibulo zimenezi? Kuti kuli kwaumunthu ndi kwachibadwa kulira ndipo sitiyenera kuchita manyazi kusonyeza chisoni chathu. Ngakhale pamene tili ndi chitonthozo cha chiyembekezo cha chiukiriro, imfa ya wokondedwa imakhalabe kutayika kovutitsa maganizo, kumene kumasautsa kwambiri. Zaka zambiri, ndipo ngakhale makumi a zaka, za kuyanjana kwachikondi ndi kuchitira zinthu pamodzi zimaduka mwadzidzidzi ndi mwatsoka. Zoona, ife sitilira monga aja opanda chiyembekezo kapena aja okhala ndi ziyembekezo zonama. (1 Atesalonika 4:13) Ndiponso, sitimasochezedwa ndi nthanthi zilizonse zakuti munthu ali ndi moyo wosafa kapena wopitiriza kukhalako mwa kubadwanso. Timadziŵa kuti Yehova walonjeza ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene mudzakhala chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Mulungu ‘adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso [pathu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’​—Chivumbulutso 21:4.

12. Kodi Paulo anasonyeza motani chikhulupiriro chake cha chiukiriro?

12 Kodi pali chiyembekezo chotani kwa aja amene anafa?b Mlembi Wachikristu Paulo anauziridwa kutipatsa chitonthozo ndi chiyembekezo pamene analemba kuti: “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:26) The New English Bible imati: “Mdani wotsiriza amene adzafafanizidwa ndiye imfa.” Kodi nchifukwa ninji Paulo anakhala wotsimikiza motero? Chifukwa chakuti iye anadzatembenuzidwa ndi kuphunzitsidwa ndi munthu amene anaukitsidwa kwa akufa, Yesu Kristu. (Machitidwe 9:3-19) Chimenecho ndicho chifukwa chakenso Paulo ananena kuti: “Pakuti monga imfa inadza mwa munthu [Adamu], kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu [Yesu]. Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.”​—1 Akorinto 15:21, 22.

13. Kodi mboni zoona ndi maso zinachita motani pakuutsidwa kwa Lazaro?

13 Chiphunzitso cha Yesu chimatipatsa chitonthozo chachikulu ndi chiyembekezo cha mtsogolo. Mwachitsanzo, kodi iye anachitanji m’chochitika cha Lazaro? Anapita kumanda kumene thupi la Lazaro linali litatha masiku anayi. Iye anapereka pemphero, “ndipo mmene adanena izi, anafuula ndi mawu aakulu, Lazaro, tuluka. Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nawo, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.” Kodi mukuona m’maganizo mwanu nkhope zodabwa ndi zachisangalalo za Marita ndi Mariya? Ha, anansiwo ayenera kuti anadabwa chotani nanga poona chozizwitsa chimenechi! Mposadabwitsa kuti oona ambiri anakhulupirira mwa Yesu. Komabe, adani ake achipembedzo, “anapangana kuti amuphe iye.”​—Yohane 11:41-53.

14. Kodi chiukiriro cha Lazaro chinali chisonyezero cha chiyani?

14 Yesu anachita chiukiriro chosaiŵalika chimenecho pamaso pa mboni zambiri zoona ndi maso. Chinali chisonyezero cha chiukiriro chamtsogolo chimene ananeneratu pachochitika china poyamba, pamene anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake [a Mwana wa Mulungu], nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”​—Yohane 5:28, 29.

15. Kodi ndi umboni wotani umene Paulo ndi Hananiya anali nawo wa chiukiriro cha Yesu?

15 Monga momwe tatchulirapo kale, mtumwi Paulo anakhulupirira chiukiriro. Pamaziko otani? Iye poyamba anali Saulo uja wambiri yoipa, wozunza Akristu. Dzina lake ndi mbiri yake inachititsa mantha pakati pa okhulupirira. Ndi iko komwe, kodi sindiye amene anavomereza kuti Mkristu wofera chikhulupiriro Stefano aponyedwe miyala mpaka imfa? (Machitidwe 8:1; 9:1, 2, 26) Komabe, panjira yopita ku Damasiko, Kristu woukitsidwayo anachititsa Saulo kuzindikira, akumamkantha ndi khungu la kanthaŵi. Saulo anamva liwu likumuuza kuti: “Saulo, Saulo, undilondalonderanji? Koma anati, ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, ndine Yesu amene umlondalonda.” Ndiyeno Yesu mmodzimodzi woukitsidwayo analangiza Hananiya, wokhala m’Damasiko, kupita kunyumba kumene Saulo anali kuphemphera kuti akabwezeretse kuona kwake. Chotero, mwa chokumana nacho cha iwo eni, onse aŵiri Saulo ndi Hananiya anali ndi chifukwa chokwanira chokhulupirira za chiukiriro.​—Machitidwe 9:4, 5, 10-12.

16, 17. (a) Kodi timadziŵa motani kuti Paulo sanakhulupirire lingaliro Lachigiriki la kusafa kwa moyo wa munthu? (b) Kodi Baibulo limapatsa chiyembekezo cholimba chotani? (Ahebri 6:17-20)

16 Onani mmene Saulo, mtumwi Pauloyo, anayankhira pamene anabweretsedwa pamaso pa Kazembe Felike monga Mkristu wozunzidwa. Timaŵerenga pa Machitidwe 24:15 kuti: “[Ndili] nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Mwachionekere, Paulo sanakhulupirire lingaliro Lachigiriki la kusafa kwa moyo wa munthu, umene unalingaliridwa kuti unali kusamukira ku moyo wapambuyo pa imfa yanthanthi kapena ku dziko la mizimu ya akufa. Iye anakhulupirira ndi kuphunzitsa za chikhulupiriro cha chiukiriro. Zimenezo zinatanthauza kuti ena akalandira mphatso ya moyo wosafa monga zolengedwa zauzimu kumwamba pamodzi ndi Kristu ndipo kwa unyinji kubwereranso ku moyo pa dziko lapansi langwiro.​—Luka 23:43; 1 Akorinto 15:20-22, 53, 54; Chivumbulutso 7:4, 9, 17; 14:1, 3.

17 Motero Baibulo limatipatsa lonjezo lomveka bwino ndi chiyembekezo cholimba chakuti mwa chiukiriro, ambiri adzaonanso okondedwa awo pompano pa dziko lapansi m’mikhalidwe yosiyana kwambiri.​—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-4.

Chithandizo Chogwira Ntchito kwa Olira

18. (a) Kodi ndi chiŵiya chothandiza chotani chimene chinatulutsidwa pa Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu”? (Onani bokosi.) (b) Kodi ndi mafunso otani tsopano amene akufuna mayankho?

18 Pakali pano tili ndi zikumbukiro zathu ndi zisoni zathu. Kodi tingachitenji kuti tipirire m’nyengo ino yopereka chiyeso ya kufedwa? Kodi ena angachitenji kuti athandize olira? Ndiponso, kodi tingachitenji kuti tithandize aja oona mtima amene tikumana nawo mu utumiki wathu wakumunda amene alibe chiyembekezo chenicheni ndi amenenso akulira? Ndipo kodi ndi chitonthozo china chotani chimene tingapeze m’Baibulo ponena za okondedwa athu omwe agona mu imfa? Nkhani yotsatira idzapereka malingaliro ena.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe zowonjezereka za kulira maliro m’nthaŵi za Baibulo, onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 446-7, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Kuti mudziŵe zochuluka pa chiyembekezo cha chiukiriro chopezeka m’Baibulo, onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 783-93.

Kodi Mungayankhe?

◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti imfa ndi mdani?

◻ Kodi atumiki a Mulungu a m’nthaŵi za Baibulo anasonyeza motani chisoni chawo?

◻ Kodi pali chiyembekezo chotani cha okondedwa akufa?

◻ Kodi Paulo anali ndi maziko otani okhulupirira chiukiriro?

[Bokosi patsamba 8, 9]

Chithandizo Chogwira Ntchito kwa Olira

Pa Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu” mkati mwa 1994-95, Watch Tower Society inalengeza kutulutsidwa kwa brosha latsopano lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Chofalitsa cholimbikitsa chimenechi chakonzedwa kuti chipatse chitonthozo anthu a mitundu yonse ndi a zinenero zonse. Monga momwe mungakhale mutaonera kale, ilo limapereka malongosoledwe osavuta a Baibulo a za imfa ndi mkhalidwe wa akufa. Chofunika koposa nchakuti, limasonyeza lonjezo la Mulungu, kupyolera mwa Kristu Yesu, la kuukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi loyeretsedwa laparadaiso. Limapatsadi chitonthozo kwa olira. Chifukwa chake, liyenera kukhala chiŵiya chothandiza mu utumiki Wachikristu ndipo liyenera kuthandiza kudzutsa chidwi, likumayambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba owonjezereka. Mafunso a phunziro aikidwa mwanzeru m’mabokosi cha kumapeto kwa chigawo chilichonse kotero kuti kupendanso mfundo zophunziridwa kosavuta kuchitidwe ndi wolira aliyense woona mtima.

[Chithunzi patsamba 8]

Pamene Lazaro anamwalira, Yesu analira

[Chithunzi patsamba 9]

Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

First Mourning, ndi W. Bouguereau, chojambulidwa pa chithunzi choyambirira cha pagalasi cha mu Photo-Drama of Creation, 1914

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena