Lingaliro la Baibulo
Kodi Kuchita Chisoni Nkulakwa?
“NDIMAKHULUPIRIRA MWAMPHAMVU CHIYEMBEKEZO CHA CHIUKIRIRO, NDIPO NDINAGANIZA KUTI KUNGAKHALE KULAKWA KUSONYEZA CHISONI CHANGA PAMASO PA ENA NDI KUTI NDIKAWAPATSA CHIFUKWA CHA KUKAYIKIRA KUTI NDINALI NDI CHIYEMBEKEZO CHAMPHAMVU CHOTERO. NDINAGANIZA KUTI NGATI NDIMAKHULUPIRIRADI CHIUKIRIRO, SINDINGACHITE CHISONI KWAMBIRI NDI KUTAYIKIRIDWAKO.”—CHARLENE, MKRISTU WOBATIZIDWA KWA ZAKA ZOPOSA 21.
PAMENE winawake amene mumakonda amwalira, mungakhale ndi malingaliro ndi makhalidwe a maganizo amene simunayembekezere—mantha, mkwiyo, liwongo, ndi kuchita tondovi. Kwa Mkristu lonjezo lotonthoza mtima la Baibulo lakuti akufa adzauka ndi kukhala ndi moyo padziko lapansi laparadaiso mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu lingathandize kuchepetsa kupweteketsa mtima kwa imfayo. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 21:1-4) Koma monga momwe mawu a Charlene akusonyezera, pamene wokondedwa amwalira, Akristu ena amanyamula chothodwetsa chosayenerera—lingaliro lakuti kulira nkolakwa, kuti kuchita chisoni kumasonyeza mwa njira ina kupanda chikhulupiriro m’lonjezo la Baibulo la chiukiriro.
Komabe, kodi Baibulo limanenanji za kuchita chisoni? Kodi nkulakwa kulira pamene wokondedwa amwalira?
Iwo Anachita Chisoni
Chikhulupiriro cha Abrahamu nchodziŵika bwino kwambiri. Pamene anayesedwa, Abrahamu “anapereka nsembe [mwana wake] Isake.” (Ahebri 11:17; Genesis 22:9-13) Mwachionekere, palibe aliyense amene anali ataukitsidwa isanafike nthaŵi yake, koma Abrahamu anali ndi chikhulupiriro chakuti, ngati kukakhala kofunika, “Mulungu ngwokhoza kuukitsa [mwana wake] ngakhale kwa akufa.” (Ahebri 11:19) Pafupifupi zaka 12 pambuyo pa kuyesedwa kwa chikhulupiriro cha Abrahamu, mkazi wake, Sara, anamwalira. Kodi munthu wa chikhulupiriro ameneyo anachita motani? Baibulo limalongosola kuti iye “anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.”a (Genesis 23:2) Inde, mwamuna amene anali ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu akhoza kuukitsa akufa anasonyeza chisoni poyera. Chikhalirechobe, Abrahamu amatchulidwa kukhala chitsanzo chapadera cha chikhulupiriro.—Ahebri 11:8-10.
Chimodzi cha zitsanzo zokhudza mtima kwambiri za kusonyeza chisoni poyera chifukwa cha kufa kwa wokondedwa chinali cha Yesu Kristu mwiniyo. Ponena za imfa ya Lazaro, bwenzi lapamtima la Yesu, timaŵerenga kuti: “Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, mmene anamuona iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno inu, mlongo wanga sakadamwalira. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. Yesu analira.”—Yohane 11:32-35.
Kulidi kotonthoza mtima kuona kuti Mwana wangwiro wa Mulungu sanachite manyazi kusonyeza chisoni poyera. Liwu la chinenero choyambirira lomasuliridwa “analira” (da·kryʹo) limatanthauza “kukhetsa misozi mwakachetechete.” Chimene chili chapadera kwambiri nchakuti Yesu anali ataukitsapo kale anthu aŵiri—mwana wa mkazi wamasiye wa ku Naini ndi mwana wamkazi wa Yairo—ndipo anafunitsitsa kuukitsa Lazaro. (Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-55; yerekezerani ndi Yohane 11:11.) Mphindi zingapo poyambirirapo anali atauza Malita kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:25) Komabe, malingaliro amphamvu kwambiri otero anagwira Yesu kwakuti maso ake anadzaza ndi misozi.
Palinso chinachake chofunika kwambiri. Yesu ali “chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe [cha Yehova].” (Ahebri 1:3) Motero malingaliro achifundo ndi akuya a Yesu pa imfa ya munthu wokondedwa amasonyeza chithunzi chokhudza mtima cha Atate wathu wakumwamba, Yehova. Iwo amasonyeza Mulungu amene mtima wake umayambukiridwa ndi chisoni cha atumiki ake.—Yerekezerani ndi Salmo 56:8.
Pamenepa, mwachionekere, sikulakwa kuchita chisoni pamene winawake amene mumakonda amwalira. Abrahamu analira imfa ya Sara. Yesu anachita chisoni mwapoyera pamene Lazaro anamwalira. Yehova Mulungu amamvetsetsa kupwetekedwa mtima kwathu chifukwa chakuti ‘amatisamalira.’—1 Petro 5:7.
Komabe, bwanji ponena za chiyembekezo Chachikristu? Kodi chimapanga kusiyana kulikonse?
‘Osalira Monga Otsalawo’
Pamene ena mumpingo Wachikristu wa mu Tesalonika wa m’zaka za zana loyamba anachita chisoni chifukwa cha imfa ya okhulupirira anzawo, mtumwi Paulo anafuna kuwatonthoza. Iye analemba kuti: “Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13) Inde, awo amene ali ndi chidaliro m’lonjezo la Mulungu la kuukitsa akufa ali mumkhalidwe wabwino kwambiri kuposa awo amene alibe chiyembekezo cha chiukiriro.b Motani?
Pamene ayang’anizana ndi imfa, awo amene alibe chiyembekezo cha chiukiriro amataya mtima. Ngakhale ngati amanena kuti amakhulupirira mtundu wina wa moyo wa pambuyo pa imfa, ochepa amapeza chitonthozo chenicheni ku zimenezi. Kwa ena ambiri, chisoni chawo chimachititsidwa osati kokha ndi chenicheni chakuti okondedwa awo achotsedwa pamaso pawo ndi imfa koma ndi chenicheni chakuti kuchoka kwawoko ndi kwachikhalire. Pokhala osamvetsetsa chiukiriro, ziyembekezo zawo zimatha pamene aika akufa awo okondedwa; kwa iwo, zimatanthauza kuti sadzawaonanso.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:12-19, 32.
Komabe, nzosiyana kwa Akristu owona. Paulo analongosola kuti imfa ili ngati tulo—osati kokha chifukwa chakuti ili mkhalidwe wa kusazindikira umene umafanana ndi tulo tofa nato komanso chifukwa chakuti nkotheka kudzutsidwa mwa chiukiriro. (Salmo 13:3; Mlaliki 9:5, 10) Chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo chimenecho chimapanga kusiyana.
Pamene atayikiridwa ndi wokondedwa mu imfa, Mkristu amamva mwamphamvu monga momwe amachitira osakhulupirira kutayikiridwa kwa ubwenzi, kusoŵa kwa nkhope yozolowereka, ndi kusamveka kwa liwu la wokondedwa. Chiyembekezo cha chiukiriro sichimachititsa mtima kukhala wosalingalira. Komabe, chimachepetsa kapena kulinganiza kumva chisoniko. Ayi, chiyembekezo chimenecho sichimachotsa kufunika kwa kuchita chisoni, koma chingachititse kupwetekako kukhala kopiririka mosavuta.
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za liwu Lachihebri lomasuliridwa kuti “maliro,” Theological Wordbook of the Old Testament ikunena kuti: “Onse amene anazindikira kutayika kwa munthu wakufayo anali kubwera kudzagawana chisoni chawo ndi ziŵalo za banjalo. . . . Kulira kofuula kapena kubuma kofuula kaŵirikaŵiri kunatsagana ndi kumva chisoni.” Ponena za liwu Lachihebri lakuti “kulira,” buku limodzimodzilo likulongosola kuti: “Pamene kuli kwakuti misozi imagwirizanitsidwa ndi maso, kulira kumagwirizanitsidwa ndi mawu; a Semite samalira mwakachetechete, koma mofuula. . . . Mu [Chipangano Chakale] chonse kulira kuli chisonyezero chachibadwa ndi chamwadzidzidzi cha malingaliro amphamvu.”
b Akristu a m’zaka za zana loyamba amene Paulo analembera anali ndi chiyembekezo cha chiukiriro cha kumwamba kumene akatumikira monga olamulira anzake a Kristu. (1 Atesalonika 4:14-17; yerekezerani ndi Luka 22:29, 30.) Motero Paulo anaŵalimbikitsa kuti adzitonthozana ndi chiyembekezo chakuti pa kukhalapo kwa Kristu anzawo okhulupirika amene anafa adzaukitsidwa ndipo akagwirizana ndi Kristu ndi wina ndi mnzake. Komabe, kwa unyinji waukulu wa amene amafa, Baibulo limapereka chiyembekezo cha chiukiriro m’dziko lapansi lobwezeretsedwa la paradaiso.—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:1-4.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Jean-Baptiste Greuze, detail from Le fils puni, Louvre; © Photo R.M.N.