Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Atamandi Achimwemwe”
Masiku atatu opindulitsa a kuphunzitsidwa za m’Baibulo akukuyembekezani. Pokhala ndi misonkhano yachigawo yokwanira 45 yokonzedwa mu Zambia mokha, ndi ina ku Malaŵi, Mozambique, ndi Zimbabwe, mwachionekere padzakhala msonkhano wachigawo umodzi wochitikira pafupi ndi kumene mukukhala. Dzakhalenipo pamene programu idzayamba ndi nyimbo pa 9:20 a.m. pa tsiku loyamba.
Programu yammaŵa pa tsiku loyamba idzakhala ndi malonje limodzinso ndi nkhani yaikulu yakuti, “Opatulidwa Padera Monga Atamandi Achimwemwe Padziko Lonse.” Programu yamasana idzafotokoza za achichepere, makolo, ndi maphunziro. “Kodi Ndili Wokonzekera Kuloŵa mu Ukwati?” ili nkhani imene achichepere sayenera kuphonya. Makolo ayenera kumvetsera mosamalitsa nkhani yakuti “Makolo Amene Amapeza Chisangalalo mwa Ana Awo.” Programu yamasana idzamalizidwa ndi nkhani yakuti “Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova.” Zimene zidzakambidwa ziyenera kuthandiza achichepere kupita patsogolo pasukulu.
Programu ya pa tsiku lachiŵiri mmaŵa idzakhala ndi ubatizo, ndipo mwaŵi udzaperekedwa kwa aja amene adzayeneretsedwa kubatizidwa. Masana padzakhala kukambitsirana kosabisa kanthu ponena za mmene Satana wagwiritsirira ntchito chikhumbo cha kugonana kunyengera anthu kuyambira m’nthaŵi zakale. Padzakhalanso nkhani yamphamvu yakuti “Peŵani Misampha ya Mdyerekezi.” Programu ya tsikulo idzamalizidwa ndi nkhani yofunika yakuti “Chifukwa Chake Anthu Amafunikira Chidziŵitso Chonena za Mulungu.”
Pa tsiku lachitatu mmaŵa, nkhani yosiyirana yamutu wakuti “Atamandi Achimwemwe Mkati mwa Mapeto a Dongosolo Lino” idzafotokoza zochitika zogwedeza dziko zimene zili patsogolo pathupa. Idzagogomezera kufunika kwamwamsanga kwa kuthaŵira kumalo opulumukirako chisanayambe “chisautso chachikulu” chimene Yesu Kristu ananena, monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 24:21.
Programu ya pa tsiku lachitatu mmaŵa idzamalizidwa ndi seŵero lofunika kwambiri lakuti “Kuchitira Ulemu Ouyenerera m’Zaka Zawo za Ukalamba.” Ndiyeno, masana, padzaperekedwa nkhani yapoyera yakuti, “Tamandani Mfumu Yosatha!” Idzakhala mbali yaikulu ya msonkhanowo.
Pangani makonzedwe tsopano akuti mukakhalepo. Kuti mudziŵe malo apafupi ndi kwanuko, kafunseni pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko, kapena lemberani afalitsi a magazini ano.