Njira Yotakata Yokhala ndi Ufulu Wochepa
Banja lina la anthu atatu—atate, amayi, ndi kamwana kakakazi— linali m’nyumba ku Sydney, Australia, pamene nyumbayo inagwira moto. Anayesa kutulukira m’mazenera, koma iwo anali opingidwa ndi zitsulo. Chifukwa cha zitsulo zopinga zotetezera, ozima moto sanathe kuwapulumutsa. Atate ndi amayiwo anafera mu utsi ndi moto wa malaŵi. Mwana wamkaziyo anakafera kuchipatala pambuyo pake.
NZOMVETSA chisoni chotani nanga kuti banja limeneli linafa chifukwa cha ziŵiya zimene zinalinganizidwira kuwatetezera! Umu ndimo mmene zilili mu nthaŵi yathu ino kwakuti si banja lokhali limene linafuna kutetezera nyumba yake ndi zitsulo zopinga ndi maloko achitetezero. Anansi awo ambiri alinso ndi nyumba ndi malo onga ngati malinga. Chifukwa ninji? Akufuna chisungiko ndi mtendere wamaganizo. Zimenezo zimasokoneza chotani nanga mu chitaganya “chomasuka” mmene anthu amamva kukhala otetezereka kokha ngati adzitsekera monga kuti ali akaidi m’nyumba zawo zomwe! M’madera owonjezereka, ana samaseŵeranso motetezereka m’paki ina yapafupi kapena kupita kusukulu popanda kulondedwa ndi kholo kapena munthu wina wachikhulire. M’mbali zambiri za moyo, ufulu ukuzimiririka ngati mame.
Kusintha kwa Moyo
Masiku a agogo athu anali ena. Pamene anali ana, kaŵirikaŵiri anali kukaseŵera kulikonse kumene anafuna popanda mantha. Pamene anakula, sanasonkhezereke kupeza maloko ndi zitsulo zopinga. Anadziyesa aufulu, ndipo ufuluwo anali nawo pamlingo winawake. Komano agogo athuwo aona mkhalidwe wa anthu ukusintha m’moyo wawo. Pakhala udani ndi dyera kwambiri; m’malo ambiri kukonda mnansi kwaloŵedwa m’malo ndi kuwopa mnansi, kumene kunachititsa chinthu chachisoni chotchulidwa poyambacho. Pamodzi ndi kusoŵa kwa ufulu komakula kumeneku pali kunyonyotsoka kwa makhalidwe abwino kwapang’onopang’ono. Anthu atengeka maganizo ndi “makhalidwe atsopano,” komano kwenikweni, mkhalidwe wafika povuta kudziŵa ngati pali makhalidwe abwino nkomwe.
Yemwe kale anali mphunzitsi pa University of Queensland, Dr. Rupert Goodman, akulemba kuti: “Achinyamata tsopano akulondola moyo wina, wokondetsa chikondwerero . . . umene umachirikiza za ‘iwe mwini’ chabe: kudzikondweretsa, kudziŵerengera kwambiri, kudzikhutiritsa, kudzikonda.” Iye akunenanso kuti: “Makhalidwe onga ngati kudziletsa, kudzimana, kugwira ntchito zolimba, kusawawanya zinthu, kulemekeza ulamuliro, kukonda ndi kulemekeza makolo . . . ali malingaliro osadziŵika kwa ambiri.”
Njira Yotakatadi
Awo amene amadziŵa ulosi wa Baibulo samadabwa ndi kufala kwa mkhalidwe wa kudzikonda umenewu, pakuti Yesu Kristu anachenjeza omvetsera ake kuti: “Njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Njira yoyambayo, yokhala ndi malo aakulu oyendamo anthu ambiri, ndiyo “yotakata” chifukwa chakuti ili yopanda ziletso za malamulo a Baibulo a makhalidwe ndi moyo wa tsiku lililonse. Imakopa awo amene amakonda kuganiza zilizonse zimene akufuna ndi kukhala ndi moyo monga momwe akufunira—mopanda malamulo, mopanda mathayo.
Zoonadi, ambiri amene asankha njira yotakata amanena kuti ali ndi ufulu. Koma ambiri a iwo amasonkhezeredwa ndi mzimu wofala wa dyera. Baibulo limanena kuti amalamuliridwa ndi “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” Mzimu umenewu umawasonkhezera kukhala ndi moyo “m’zilakolako za thupi . . . , ndi kuchita zifuniro za thupi,” kaya zimenezo zikhale makhalidwe oipa, anamgoneka, kapena kufunitsa chuma, kudziŵika, kapena mphamvu.—Aefeso 2:2, 3.
Njira Yotakata Ikumka ku Chiwonongeko
Onani kuti awo amene akuyenda panjira yotakata amasonkhezeredwa kuchita “zifuniro za thupi.” Zimenezi zikusonyeza kuti sali aufulu konse—ali ndi mbuye. Ali akapolo a thupi. Ndipo kutumikira mbuye ameneyu kungadzetse mavuto ochuluka—milili ya nthenda zopatsirana mwa kugonana, mabanja osweka, anthu odwala m’thupi ndi maganizo chifukwa cha anamgoneka ndi kumwetsa zakumwa zaukali, kungotchulapo oŵerengeka. Ngakhale chiwawa, kuthyola nyumba, ndi kugwirira chigololo nzozikika m’kuganiza kodzikonda kokulitsidwa panjira yotakata imeneyi yololera zonse. Ndipo, pamene kuli kwakuti “njira yakumuka nayo kukuwonongeka” ikupitiriza kukhalapo, zipatso zake zidzakhalabe zoŵaŵa.—Miyambo 1:22, 23; Agalatiya 5:19-21; 6:7.
Lingalirani za zitsanzo zenizeni ziŵiri za ku Australia. Mary anagonjera ku chiyeso, akumagwiritsira ntchito anamgoneka ndiponso kuchita chisembwere.a Koma chimwemwe chimene anafunafuna chinamsoŵa. Ngakhale pamene anakhala ndi ana aŵiri, moyo unakhala wopanda pake. Anapsinjika mtima kwambiri pamene anadziŵa kuti anatenga AIDS.
Tom anavutika mwa mtundu wina. “Ndinakulira pa tchalitchi cha mishoni kumpoto kwa Queensland,” iye akulemba motero. “Pausinkhu wa zaka 16, ndinayamba kumwa kwambiri. Atate, achimwene awo, ndi mabwenzi onsewo anali zidakwa, chotero chinali chinthu choyenera kuchita. Ndinafikira pamkhalidwe wa kumwa chilichonse, kuyambira moŵa mpaka ma methylated spirit. Ndinayambanso kutchova juga ya mahachi, nthaŵi zina ndikumataya ndalama zanga zambiri zimene ndinapeza movutikira. Zimenezi zinali ndalama zambiri, pakuti ntchito yanga yodula nzimbe inali ya malipiro abwino.
“Ndiyeno ndinakwatira ndipo tinakhala ndi ana. M’malo mwa kusamalira mathayo anga, ndinachita zimene mabwenzi anga anachita—kumwa, kutchova juga, ndi kuchita ndewu. Kaŵirikaŵiri ndinkatsekeredwa m’ndende ya kwathu. Koma zimenezinso sizinandiphunzitse kanthu. Moyo wanga unali kuipa. Unali wamavuto.”
Inde, mwa kugonjera pa zikhumbo zoipa, Tom ndi Mary anadzivulaza okha ndi mabanja awo. Mwachisoni, achinyamata ena ambiri amakonda kunyengedwa ndi mzimu wonyenga wa ufulu umene umaperekedwa pa njira yotakata. Kukanakhala bwino chikhala kuti achinyamatawo amaona chinyengocho. Kukanakhala bwino chikhala kuti anadziŵa za njira yotakata—zotulukapo zoipa kwambiri zimene onse amene amayendamo amapeza. Zoonadi, iyo njotakata ndi yosavuta kuyendamo. Komano kutakata kwakeko ndiko ngozi. Njira ya nzeru ndiyo kumvetsera choonadi chakuti “wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.”—Agalatiya 6:8.
Komabe, pali njira ina yosankha yabwino kwambiri. Ndiyo njira yochepetsa. Koma kodi njirayo njoletsa motani, kodi iyo njopapatiza ndi yochepetsa motani? Ndipo kodi ikumka kuti?
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa.