Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 9/1 tsamba 5-7
  • Njira Yochepetsa ya ku Ufulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Yochepetsa ya ku Ufulu
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Njira Yochepetsa Imamasulira
  • Thandizo la Mulungu Latsimikiziridwa kwa Ife
  • Analeka Kuyenda pa Njira Yotakata
  • Njira Yotakata Yokhala ndi Ufulu Wochepa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Zipembedzo Zonse N’zabwino?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Pitirizani ‘Kumumvera’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Lolani Yehova Kukutsogolerani ku Ufulu Weniweni
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 9/1 tsamba 5-7

Njira Yochepetsa ya ku Ufulu

ANTHU anzeru oŵerengeka amatsutsa zoti chilengedwe chimalamuliridwa ndi malamulo achibadwa. Malamulo ameneŵa amalamulira kanthu kalikonse kuyambira pa ma atomu ochepetsetsa kufikira ku milalang’amba yaikulu ya nyenyezi miyandamiyanda. Zikadapanda kutero, si bwenzi pali kulinganiza ndipo si bwenzi pali kumvetsetsa; moyo weniweniwo sukanakhalako. Mwa kuzindikira malamulo achibadwa ndi kuchita mogwirizana nawo, munthu wakhoza kuchita zinthu zodabwitsa, monga ngati kuyenda pamwezi ndi kusonyeza zithunzithunzi zamaonekedwe achibadwa kuchokera kumalo alionse pa dziko lapansi kapena ngakhale mu mlengalenga pa wailesi yakanema m’nyumba zathu.

Koma bwanji nanga za malamulo a makhalidwe abwino? Kodi kuwatsatira nkopindulitsanso? Ambiri amachita ngati kuti palibe malamulo a makhalidwe abwino ndipo amasankha makhalidwe olola zonse kapena chipembedzo chimene chimayenerana ndi zikhumbo za iwo eni.

Komabe, pali ena amene amasankha njira ina, ‘njira yochepetsa yakumuka nayo kumoyo’ monga momwe yalongosoledwera m’Baibulo. Sitiyenera kudabwa kuti amene amasankha imeneyi ali oŵerengeka chabe, pakuti Yesu ananena za njira yochepetsayo kuti: ‘Akuipeza imeneyo ali oŵerengeka.’ (Mateyu 7:14) Kodi nchifukwa ninji ali oŵerengeka chabe?

Chifukwa chakuti njira yochepetsayo ili ndi malamulo a Mulungu oletsa. Imangokopa kokha munthu amene akufunadi kugwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Mulungu. Mosiyana kwambiri ndi njira yotakata, imene imapereka ufulu wonyenga koma kwenikweni uli ukapolo, njira yochepetsa, imene imakhala ngati yoletsa, imamasula munthu pa mbali iliyonse yofunika. Malire ake aikidwa ndi “lamulo langwiro, ndilo laufulu.”​—Yakobo 1:25.

Mmene Njira Yochepetsa Imamasulira

Zoonadi, kuyenda panjira yochepetsa nthaŵi zina nkovuta. Munthu aliyense wamoyo ngwopanda ungwiro ndipo ali ndi chikhoterero chachibadwa cha kuchita cholakwa. Chotero munthu angafune kupatuka pang’ono. Komabe, mapindu akumamatira pa ‘njira yopapatiza’ ngoyenerera kudzilanga kulikonse kapena masinthidwe, pakuti Mulungu ‘amatiphunzitsa kuti tipindule.’​—Yesaya 48:17; Aroma 3:23.

Mwachitsanzo: Makolo anzeru amalinganiza ‘njira yopapatiza’ ya kadyedwe kaamba ka ana awo. Nthaŵi zina zimenezi zimafuna kukhwimitsa zinthu panthaŵi ya chakudya. Koma pamene ana akula, amayamikira mwambo wachikondi wa makolo awo. Monga achikulire, iwo amakhala atadziŵa ubwino wa chakudya chopatsa thanzi. Ndipo chifukwa chakuti pali chakudya chomanga thupi chosiyanasiyana sadzakhala opanikizika.

M’njira yauzimu, Mulungu amachita chimodzimodzi kwa awo amene amayenda panjira yochepetsa ya ku moyo. Amakulitsa mwa ofatsa zikhumbo zabwino zimene zimadzetsa chimwemwe ndi ufulu weniweni. Amachita zimenezi mwa kupereka Mawu ake, Baibulo. Ndiponso, amatiuza kupempherera mzimu wake kuti utithandize, ndipo amatilamulira kuyanjana ndi Akristu anzathu, amene angatilimbikitse kuyendabe panjira yochepetsa. (Ahebri 10:24, 25) Inde, Mulungu ndiye chikondi, ndipo mkhalidwe wapamwamba umenewu ndiwo maziko a zolinga zake ndi njira zake zonse.​—1 Yohane 4:8.

Pamene chikondi, mtendere, ubwino, kudziletsa, ndi zipatso zina za mzimu wa Mulungu zikhalapo, njira yochepetsayo simakhala yoletsa. Kuli monga momwe lemba limanenera kuti, “pokana zimenezi palibe lamulo.” (Agalatiya 5:22, 23) “Pamene pali mzimu wa [Yehova, NW] pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Ngakhale tsopano, Akristu enieni akulaŵa ufulu umenewu. Ali omasuka pamantha ambiri amene amagwira anthu lerolino, onga kuwopa zamtsogolo ndi miyambo ya kuwopa imfa. Nkokondweretsa chotani nanga kusinkhasinkha zamtsogolo pamene “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja”! (Yesaya 11:9) Panthaŵiyo, ngakhale kuwopa upandu kudzatha. Maloko ndi zopinga zachitsulo zidzachokeratu. Onse adzakhala aufulu ndi otetezereka​—masana ndi usiku, panyumba ndi kwina. Umenewo udzakhaladi ufulu!

Thandizo la Mulungu Latsimikiziridwa kwa Ife

Zoonadi, kutsatira miyezo ya Mulungu kumafuna kuyesayesa, komabe “malamulo ake sali olemetsa,” ngakhale kwa anthu opanda ungwiro. (1 Yohane 5:3) Pamene tizoloŵera njira yochepetsa ndi kulandira mapindu a kuyendamo, timakulitsa kuda njira ndi kaganizidwe kamene kamasonyezedwa ndi awo amene amayenda panjira yotakata. (Salmo 97:10) Kumvera lamulo la Mulungu kumasonkhezera chikumbumtima chathu tonsefe. M’malo mwa kukhala ndi “mtima wachisoni” ndi “kusweka mzimu” kumene ambiri ali nako, Mulungu akulonjeza kuti: “Taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala.” Inde, mtima wophunzitsidwa ndi Yehova ngwosangalala ndi womasuka.​—Yesaya 65:14.

Yesu anafa kuti ufulu weniweni ukhale wotheka kwa ife. Baibulo limati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Tsopano, Yesu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, akupereka mapindu a nsembe imeneyo. Posachedwapa, “chisautso chachikulu” chitapita, pamene njira yotakatayo ndi awo oyendamo awonongedwa, adzayamba kutsogolera anthu omvera moleza mtima pambali yotsala ya njira yochepetsa kufikira mapeto ake, ungwiro wa anthu. (Chivumbulutso 7:14-17; Mateyu 24:21, 29-31) Potsirizira pake tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo laulemerero lakuti: “Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” Ufulu wopatsidwa ndi Mulungu umenewu sungaposedwe ndi wina uliwonse. Ngakhale imfa idzachotsedwa.​—Aroma 8:21; Chivumbulutso 21:3, 4.

Mwa kuona ndi kuzindikira bwino kumene njira yochepetsa ikumka, munthu amakhala wokhoza kusankha njira imeneyi ndi kuyendabe mmenemo. Makamaka achinyamata amathandizidwa kuona patali ndi kusaipidwa ndi zimene amaona kukhala ziletso zoikidwa ndi miyezo ya Mulungu. Amaphunzira kuona zimenezi monga umboni wa chikondi cha Mulungu ndipo monga chitetezero pa zoipa za njira yotakata. (Ahebri 12:5, 6) Ndithudi, munthu afunikira kukhala woleza mtima, akumakumbukira kuti pamafunika nthaŵi kuti mikhalidwe yaumulungu ndi zikhumbo zikule, monga momwe pamafunikira nthaŵi kuti mtengo wa zipatso ubale zipatso zabwino. Koma mtengowo umabala ngati usamaliridwa ndi kuthiriridwa.

Chotero phunzirani Mawu a Mulungu, yanjanani ndi Akristu ena, ndipo ‘pemphererani mzimu woyera kosaleka.’ (1 Atesalonika 5:17) Khulupirirani Mulungu kuti akuthandizeni ‘kuwongola mayendedwe anu.’ (Miyambo 3:5, 6) Koma kodi zonsezi zingachitike? Kodi zimathekadi? Inde, zinatheka kwa Tom ndiponso kwa Mary, amene atchulidwa m’nkhani yapitayo.

Analeka Kuyenda pa Njira Yotakata

Tom akulemba kuti: “Pakati pa ma 70, tinaonana ndi Mboni za Yehova pamene mmodzi wa iwo anafika panyumba pathu. Kukambitsirana kwathu kunayambitsa phunziro la Baibulo. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuyeretsa moyo wanga. Ndinabatizidwa mu 1982 ndipo tsopano ndikutumikira mumpingo wa kwathu kuno. Tsopano nayenso mwana wathu wamwamuna ngwobatizidwa. Ndithokoza mkazi wanga chifukwa chopirira nane zaka zonsezi ndisanaphunzire choonadi. Ndipo koposa zonse ndikuthokoza Yehova ndi Mwana wake, Kristu Yesu, chifukwa cha zonse zimene atipatsa ndi chiyembekezo cha mtsogolo chimene tili nacho tsopano.”

Bwanji nanga za Mary? Eya, iye analingalira kuti Mulungu sangamkhululukire, koma anafuna kudziŵa za iye kaamba ka ana ake. Pamene anamva kuti Mboni za Yehova zinali kuphunzitsa mnansi wake Baibulo, nayenso anapempha thandizo. Komabe, zizoloŵezi zake zoipa zokhomerezekazo zinapangitsa kupita patsogolo kwake kukhala kovuta. Phunzirolo nthaŵi zina linali kupita patsogolo ndipo nthaŵi zina kuima. Komabe, mwana wake wamkazi wazaka zisanu ndi ziŵiri, anapitiriza kumlimbikitsa. “Limbikirani Amayi. Mudzadziŵa!” mwanayo ankatero. Ndiyeno Mary ankalimbikira kwambiri.

Pamene mwamuna wake wongotolana naye panjira, yemwe nayenso anali wa anamgoneka, anabwera panyumba, anadziphatika pa phunzirolo. Pomalizira pake aŵiriwo anagonjetsa zizoloŵezi zawo zoipazo. Ndiyeno atalembetsa ukwati wawo ndi kubatizidwa, anali ndi chimwemwe chachikulu nakhaladi banja lenileni kwa nthaŵi yoyamba. Mwachisoni, AIDS inapha Mary potsirizira pake, koma iyeyo anafa mtima wake uli pa lonjezo la Baibulo la chiukiriro ndi moyo wa pa dziko lapansi la paradaiso, pochotsedwa njira yotakata yakuphayo.

Inde, kuchoka panjira yotakata imene ikumka ku chiwonongeko nkotheka. Kristu Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Nangano, bwanji osatsimikiza kuyenda panjira yochepetsa imene ikumka kumoyo? Mwa kulabadira ndi kugwiritsira ntchito zimene mumaphunzira m’Mawu a Mulungu, mungadzionere inu mwini lonjezo la Baibulo lokondweretsa mtima lakuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena