Chitonthozo cha Awo a “Mtima Wosweka”
LEROLINO, dziko la Satana lafikira pa ‘kusazindikira kanthu kalikonse.’ (Aefeso 4:19; 1 Yohane 5:19) Chigololo ndi dama nzofala. M’maiko ambiri 50 peresenti kapena kuposa pamenepo ya maukwati amathera m’chisudzulo. Umathanyula umavomerezedwa ndi ambiri. Nkhanza yogona ena—kugwirira chigogolo—kaŵirikaŵiri zimakhala m’nkhani. Zithunzithunzi zaumaliseche zili malonda obweretsa chuma koposa.—Aroma 1:26, 27.
Pakati pa zinthu zoluluza zoipa koposa pali kugona ana osadziŵa kanthu. Monga nzeru ya dziko la Satana, kugona ana ndiko “uchinyama, uchiwanda.” (Yakobo 3:15, NW) Mu United States mokha, akutero magazini a Time, “malipoti otsimikiziridwa oposa 400,000 a kugona ana amaperekedwa kuboma chaka chilichonse ndi aphunzitsi ndi madokotala.” Pamene ochitiridwa nkhanza imeneyi afikira pa uchikulire, ambiri amakhalabe ndi malingaliro opweteka, ndipo malingaliro osautsawo amakhala enieni! Baibulo limati: “Mtima [chikhoterero cha maganizo, malingaliro] wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka [wovulazidwa, wokanthidwa]?”—Miyambo 18:14.
Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umakopa anthu a mtundu uliwonse, kuphatikizapo “osweka mtima” ndi awo ‘opsinjika.’ (Yesaya 61:1-4) Mposadabwitsa kuti ambiri amene ali ovutika mtima amalabadira chiitano chakuti: “Wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Mpingo Wachikristu ungakhale malo otonthoza kwa ameneŵa. Amakondwa kudziŵa kuti posachedwa mavuto adzakhala chinthu chakale. (Yesaya 65:17) Komabe, kufikira nthaŵiyo, afunikira ‘kutonthozedwa’ ndi ‘kumanga’ zilonda zawo. Paulo analangiza Akristu moyenera kuti: “Limbikitsani amantha mtima, chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.”—1 Atesalonika 5:14.
“Zikumbukiro Zotsenderezedwa”
M’zaka zaposachedwapa ena ‘asweka mtima’ pa zifukwa zimene enanso zimawavuta kumvetsa. Iwo ndi anthu achikulire amene, chifukwa cha zimene zafotokozedwa kukhala “zikumbukiro zotsenderezedwa,” amanena kuti anagonedwa mwankhanza pamene anali ana.a Ena sanalingalire kuti anachitiridwa nkhanza, kufikira pamene mwadzidzidzi, anakhala ndi zithunzithunzi m’maganizo ndi “zikumbukiro” zakale za munthu wina wachikulire (kapena anthu ena achikulire) amene anawagona pamene anali aang’ono. Kodi pali aliyense mumpingo Wachikristu amene ali ndi malingaliro ovutitsa oterowo? Inde, m’maiko angapo, ndipo anthu odzipatulira ameneŵa angasautsidwe mtima kwenikweni, kukwiya, kukhala aliwongo, kuchita manyazi, kapena kusukidwa. Monga momwe zinalili kwa Davide iwo angaone ngati kuti atalikirana ndi Mulungu ndi kumafuula kuti: “Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?”—Salmo 10:1.
Mbali zambiri za “zikumbukiro” zimenezi sizimadziŵidwa bwino ndi madokotala aubongo. Komabe, “zikumbukiro” zimenezo zingayambukire mkhalidwe wa Akristu odzipatulira. Chotero timayang’ana ndi chidaliro m’Mawu a Mulungu kaamba ka chitsogozo pochita nazo. Baibulo limapereka “chidziŵitso m’zonse.” (2 Timoteo 2:7; 3:16) Limathandizanso onse okhudzidwa kukhulupirira Yehova, “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Kodi Zinachitikadi?
M’dzikomu, muli mkangano waukulu wonena za chimene chili “zikumbukiro” zimenezi ndi kuti pali umboni wochuluka motani wakuti zinthu zimenezi zinachitikadi. Mboni za Yehova sizili “[z]a dziko lapansi” ndipo sizimakhala ndi phande mu mkangano umenewu. (Yohane 17:16) Malinga ndi kunena kwa malipoti ofalitsidwa, nthaŵi zina “zikumbukiro” zimenezo zakhaladi zoona. Mwachitsanzo, wokonzanso inshuwalansi Frank Fitzpatrick ‘atakumbukira’ kuti anagonedwapo ndi wansembe wina, pafupifupi anthu ena zana limodzi ananena kuti nawonso anagonedwa ndi wansembe mmodzimodziyo. Wansembeyo akuti anavomereza za kugona ena kumeneku.
Komabe, ndi bwino kudziŵa kuti anthu angapo sanathe kuchirikiza “zikumbukiro” zawo. Ena amene avutika mwanjirayi anali ndi zithunzithunzi zamphamvu za munthu wina amene anachita nkhanza kapena za nkhanza imene inachitidwa pamalo ena. Komabe, pambuyo pake umboni wodalirika wosiyana ndi zimenezo unasonyeza bwino kuti zochitika “zokumbukiridwa” zimenezi sizinali zoona.
Kupereka Populumukira
Komano, kodi chitonthozo chingaperekedwe motani kwa awo amene ali ndi “mtima wosweka” chifukwa cha “zikumbukiro” zotero? Kumbukirani fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo. Mwamuna wina anaukiridwa ndi achifwamba, anamenyedwa, ndi kulandidwa zinthu zake. Pamene Msamariya anafika, anachita chifundo ndi mwamuna wovulazidwayo. Kodi anachitanji? Kodi anafunitsitsa kumva zonse za mmene anammenyera? Kapena kodi Msamariyayo anadziŵa achifwambawo nayamba kuwathamangitsa nthaŵi yomweyo? Ayi. Mwamunayo anali atavulala! Chotero Msamariyayo anamanga bwinobwino mabala ake ndi kupita naye mwachikondi kumalo otetezereka kunyumba yofikirako alendo yapafupi kumene anachirira.—Luka 10:30-37.
Zoona, pali kusiyana pakati pa zilonda zakuthupi ndi “mtima wosweka” chifukwa cha kugonedwa kwenikweni kwankhanza kwa paubwana. Koma zonsezo zimapweteka kwambiri. Motero, zimene Msamariya anachita kwa Myuda wovulazidwayo zimasonyeza zimene tingachite kuti tithandize Mkristu mnzathu wovutika. Chinthu choyamba ndicho kupereka chitonthozo chachikondi ndi kumthandiza kuchira.
Mdyerekezi anasautsa Yobu wokhulupirikayo, mwachionekere ali ndi chidaliro chakuti ululu wa mtima kapena wa pathupi udzaswa umphumphu wake. (Yobu 1:11; 2:5) Kuyambira pamenepo, kaŵirikaŵiri Satana wayesa kugwiritsira ntchito kuvutika—kaya mwa kukuchititsa mwachindunji kapena ayi—kufooketsera chikhulupiriro cha atumiki a Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 12:7-9.) Kodi tingakayikire zoti Mdyerekezi tsopano amagwiritsira ntchito kugona ana ndi “kupsinjika” kwa anthu ambiri achikulire amene anachitiridwa zimenezi (kapena amene ali ovutika ndi “zikumbukiro” za kuchitiridwa zimenezi) kuyesa kufooketsa chikhulupiriro cha Akristu? Mofanana ndi Yesu pamene anaukiridwa ndi Satana, Mkristu amene amavutika ndi ululuwo komabe amene mochirimika amakana kusiya umphumphu wake akunena kuti: “Choka Satana”!—Mateyu 4:10.
Khalani Wolimba Mwauzimu
“Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wafalitsa chidziŵitso chothandiza pa kuvulala kwauzimu ndi kwakuthupi kochititsidwa ndi kugonedwa paubwana. (Mateyu 24:45-47) Zochitika zikusonyeza kuti wovutikayo amathandizidwa ngati adalira pa ‘mphamvu ya Ambuye ndi ukulu wa nyonga yake,’ akumavala “zida zonse za Mulungu.” (Aefeso 6:10-17) Zida zimenezi zimaphatikizapo “choonadi” cha Baibulo, chimene chimavumbula Satana kukhala mdani woipitsitsa ndi amene amawanditsa mdima umene iye ndi omchirikiza amagwiramo ntchito. (Yohane 3:19) Ndiyeno pali “chapachifuwa cha chilungamo.” Wovulazidwayo ayenera kumamatira kumiyezo yolungama. Mwachitsanzo, ena ali ndi zisonkhezero zamphamvu za kudzivulaza kapena kuchita chisembwere. Nthaŵi iliyonse imene akaniza zisonkhezero zimenezi, amakhala ndi chipambano!
Zida zauzimu zimaphatikizaponso “uthenga wabwino wa mtendere.” Kuuza ena za zifuno za Yehova kumalimbitsa munthu wolankhulayo ndiponso aliyense womvetsera. (1 Timoteo 4:16) Ngati inu muli mmodzi wa a “mtima wosweka,” zikumakupangitsani kukhala kovuta kwa inu kunena za uthenga wabwino, yesani kutsagana ndi Mkristu wina pamene achita ntchito yofunika imeneyi. Ndipo musaiŵale “chikopa [chachikulu, NW] cha chikhulupiriro.” Khalani ndi chikhulupiriro chakuti Yehova amakukondani ndipo adzabwezera zonse zimene munataya. Khulupirirani kotheratu kuti nayenso Yesu amakukondani, ndipo anasonyeza zimenezi mwa kukuferani. (Yohane 3:16) Satana nthaŵi zonse wanena monama kuti Yehova samasamala atumiki ake. Limeneli langokhala bodza lake lina loipitsitsa.—Yohane 8:44; yerekezerani ndi Yobu 4:1, 15-18; 42:10-15.
Ngati kupweteka kwa mtima kukupatsani vuto pa kukhulupirira kuti Yehova amakuderani nkhaŵa, kuyanjana ndi ena amene amakhulupirira zolimba kuti amadera nkhaŵa kudzakuthandizani. (Salmo 119:107, 111; Miyambo 18:1; Ahebri 10:23-25) Kanani kulola Satana kukulandani mphotho yanu ya moyo. Kumbukirani kuti, “chisoti cha chipulumutso” chili mbali ina ya zida zofunika; monga momwe lilili “lupanga la mzimu.” Baibulo nlouziridwa ndi mzimu woyera, umene sungaletsedwe ndi Satana. (2 Timoteo 3:16; Ahebri 4:12) Mawu ake ochiritsa angatonthoze mtima wopweteka.—Yerekezerani ndi Salmo 107:20; 2 Akorinto 10:4, 5.
Potsirizira pake, pemphererani nyonga ya kupirira mosalekeza. (Aroma 12:12; Aefeso 6:18) Pemphero lochokera mumtima linalimbitsa Yesu kupirira kusautsika mtima kwakukulu, lingathandize inunso. (Luka 22:41-43) Kodi kupemphera kukukuvutani? Pemphani ena kupemphera nanu ndi kukupemphererani. (Akolose 1:3; Yakobo 5:14) Mzimu woyera udzachirikiza mapemphero anu. (Yerekezerani ndi Aroma 8:26, 27.) Monga momwe zilili ndi nthenda yakuthupi yopweteka, ena amene ali ndi zilonda zazikulu za m’maganizo sangachire kotheratu m’dongosolo lino la zinthu. Koma mwa thandizo la Yehova tingapirire, ndipo chipiriro ndicho chilakiko, monga mmene zinalili kwa Yesu. (Yohane 16:33) “Khulupirani pa [Yehova] nyengo zonse, anthu inu: tsanulirani mitima yanu pamaso pake: Mulungu ndiye pothaŵirapo ife.”—Salmo 62:8.
Bwanji Nanga za Wochita Nkhanzayo?
Munthu amene amagonadi mwana ali wogwirira chigololo ndipo ayenera kulingaliridwa motero. Aliyense wochitiridwa nkhanza mwa njira imeneyi ali woyenera kuimba mlandu womchitira nkhanzayo. Komabe, kuimba mlanduko sikuyenera kuchitidwa mwaphuma ngati makamaka kwazikidwa pa “zikumbukiro zotsenderezedwa” za nkhanzayo. Pankhaniyi chinthu chofunika koposa nchakuti wovutitsidwayo akhalenso wolama maganizo. Patapita nthaŵi ina yake, iyeyo angakhale wokhoza kulingalira bwino za “zikumbukiro” zimenezo ndi kusankha zimene akufuna kuchita, ngati zilipo.
Talingalirani za nkhani ya Donna. Akuti anali ndi vuto la kusadya bwino ndipo anapita kwa mlangizi wina—mwachionekere wokayikitsa. Posapita nthaŵi iyeyo anayamba kuimba mlandu atate wake wa kumgona ndipo iwo anatengeredwa kubwalo lamilandu. Oweruza mlanduwo anagometsana, chotero atatewo sanaponyedwe m’ndende, komano anafunikira kulipira $100,000 pa mlanduwo. Ndiyeno zonsezo zitatha, Donna anauza makolo ake kuti sanakhulupirirenso kuti nkhanzayo inachitidwa!
Mwanzeru, Solomo anati: “Usatuluke mwansontho kukalimbana.” (Miyambo 25:8) Ngati pali chifukwa china choyenera cholingalirira kuti wamaliwongo woganiziridwayo akugonabe ana, mwina chenjezo liyenera kuperekedwa. Akulu a mumpingo angathandize pankhani imeneyo. Komano, ndi bwino kuti musachite phuma. Potsirizira pake, mwina mungangokhutira ndi kungonyalanyaza nkhaniyo. Komabe, ngati mukufuna kuimba mlandu wamaliwongo woganiziridwayo (choyamba mutapenda mmene mudzaonera nkhaniyo ponena za zotulukapo zake), muli waufulu kutero.
Mkati mwa nthaŵi imene munthu wokhala ndi “zikumbukiro” akuchira, mungabuke mikhalidwe ina yovuta. Mwachitsanzo, munthu angakhale ndi zithunzithunzi zenizeni za kugonedwapo ndi munthu wina amene amaona tsiku lililonse. Palibe malamulo osamalirira nkhaniyi amene angaikidwe. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Nthaŵi zina munthu angalingalire kuti wachibale wina kapena munthu wina wa m’banja lake ndiye amene akukhudzidwa. Kumbukirani za mkhalidwe wokayikitsa wa “zikumbukiro zotsenderezedwa” zina pankhani ya kudziŵikitsa munthu wolingaliridwa kukhala wamaliwongo. Mu mkhalidwe wotero, malinga ngati nkhaniyo ili yosatsimikiziridwa mwamphamvu, kulankhulana ndi banja—mwinamwake mwa kulichezera panthaŵi ndi nthaŵi, kulilembera kalata, kapena kuliimbira telefoni—kungasonyeze kuti munthuyo akuyesa kutsatira njira ya Malemba.—Yerekezerani ndi Aefeso 6:1-3.
Kodi Akulu Angachitenji?
Ngati akulu afikiridwa ndi chiŵalo cha mpingo chimene chikuvutika ndi zithunzithunzi zakale kapena “zikumbukiro zotsenderezedwa” za kugonedwa paubwana, aŵiri a iwo amasankhidwa kuti athandize. Akulu ameneŵa ayenera kulimbikitsa mokoma mtima wovulazidwayo kuti panthaŵiyo asumike maganizo pa kulimbana ndi kuvutika mtimako. Dzina la munthu aliyense wankhanza “wokumbukiridwayo” liyenera kusungidwa mwachinsinsi.
Thayo lalikulu la akulu ndilo kuchitapo kanthu monga abusa. (Yesaya 32:1, 2; 1 Petro 5:2, 3) Aloleni kukhala osamala kwambiri “[akumadziveka], mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Ayenera kumvetsera m’njira yokoma mtima ndiyeno kugwiritsira ntchito mawu olamitsa ochokera m’Malemba. (Miyambo 12:18) Ena amene akhala ndi “zikumbukiro” zopweteka ayamikira akulu amene amawafikira nthaŵi zonse kapena ngakhale kuwaimbira telefoni kuti adziŵe mmene zinthu zikuyendera kwa iwo. Kulankhulana nawo kotero sikufunikira kukhala kwanthaŵi yaitali, koma kumasonyeza kuti gulu la Yehova limasamala za ena. Pamene munthu wosautsikayo azindikira kuti abale ake Achikristu amamkondadi, zimenezo zingamthandize kuchira kwambiri pa kuvutika kwa mtima.
Bwanji ngati wovutikayo asankha kuti akufuna kuimba mlandu munthuyo?b Pamenepo akulu aŵiri angamlangize kuti, malinga ndi kunena kwa Mateyu 18:15, iyeyo ayenera kufikira mwachindunji woimbidwa mlanduyo ponena za nkhaniyo. Ngati woimba mlanduyo ali wosakhoza kuchita zimenezi maso ndi maso, zimenezi zingachitidwe pa telefoni kapena mwinanso mwa kulemba kalata. Mwa njira imeneyi woimbidwa mlanduyo angapatsidwe mpata wa kuyankha molumbira pamaso pa Yehova za mlanduwo. Iye mwina akhozanso kupereka umboni wakuti sanachite nkhanzayo. Kapena mwina woimbidwa mlanduyo angavomereze, ndipo angayanjane nayenso. Limenelo lingakhale dalitso labwino kwambiri chotani nanga! Ngati munthuyo avomereza, akulu aŵiriwo angasamalire nkhaniyo mowonjezereka mogwirizana ndi malamulo a Malemba.
Ngati chinenezocho chikanidwa, akulu ayenera kufotokozera woimba mlanduyo kuti palibenso zina zimene angachite m’njira ya chiweruzo. Ndipo mpingo udzapitiriza kuona woimbidwa mlanduyo monga munthu wopanda mlandu. Baibulo limati payenera kukhala mboni ziŵiri kapena zitatu munthu asanaimbidwe mlandu. (2 Akorinto 13:1; 1 Timoteo 5:19) Ngakhale ngati anthu oposa mmodzi “akumbukira” za kugonendwa ndi munthu mmodzimodziyo, mkhalidwe wa zikumbukiro zimenezi umangokhala wokayikitsa kwambiri kuti zikhale mlandu wachiweruzo popanda umboni wina wochirikiza. Zimenezi sizikutanthauza kuti “zikumbukiro” zotero zimaonedwa monga zonama (kapenanso kukhala monga zoona). Koma malamulo a Baibulo ayenera kutsatiridwa potsimikizira nkhaniyo kukhala yachiweruzo.
Bwanji ngati munthu woimbidwa mlanduyo—ngakhale kuti angakhale akukana tchimolo—alidi wolakwa? Kodi iye angangozemba chilangocho? Kutalitali! Nkhani ya liwongo lake kapena kupanda liwongo ingangosiyidwa m’manja mwa Yehova. “Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kumka kumlandu; koma enanso ziwatsata.” (1 Timoteo 5:24; Aroma 12:19; 14:12) Buku la Miyambo limati: “Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzawonongeka.” “Pomwalira woipa chidikiro chake chiwonongeka.” (Miyambo 10:28; 11:7) Potsirizira pake, Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu adzapereka chiweruzo chamuyaya mwachilungamo.—1 Akorinto 4:5.
Kukaniza Mdyerekezi
Pamene anthu odzipatulira apirira poyang’anizana ndi mavuto akuthupi aakulu kapena amtima, zimenezi zimapereka umboni wabwino kwambiri chotani nanga wa nyonga yawo ya mkati ndi kukonda Mulungu kwawo! Ndipo umenewu ndi umboni wabwino kwambiri chotani nanga wa mphamvu ya mzimu wa Yehova yowachirikizayo!—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:7.
Mawu a Petro amagwira ntchito kwa anthu amenewo: “Ameneyo [Satana] mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Petro 5:9) Kuchita motero kungakhale kovuta. Nthaŵi zina, kungakhaledi kovuta kuganiza bwino zinthu ndiponso mwanzeru. Koma musalefuke! Posachedwapa, Mdyerekezi ndi machenjera ake sadzakhalakonso. Zoonadi, tikulakalaka nthaŵiyo pamene “Mulungu yekha . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu akuti “zikumbukiro zotsenderezedwa” ndi ena ofanana nawo aikidwa m’mitengero powasiyanitsa ndi zikumbukiro zenizeni zimene tonsefe tili nazo.
b Ndiponso, kungakhale kofunikira kuti sitepe yofotokozedwa m’ndime ino itengedwe ngati nkhaniyo yadziŵika mumpingo.