Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/1 tsamba 4-7
  • Anapeza Mtendere M’dziko Lachipwirikiti

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anapeza Mtendere M’dziko Lachipwirikiti
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtendere Weniweni Umene Udzadza
  • Mtendere Pakati pa Chipwirikiti
  • Mtendere Umene Ulipo
  • Anthu Amtendere
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mtendere​—Kodi Mungaupeze Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/1 tsamba 4-7

Anapeza Mtendere M’dziko Lachipwirikiti

CHIKUTO cha magazini ano chikusonyeza nkhondo yowopsa ku Bosnia ndi Herzegovina. Kodi kumalo otero kungakhale mtendere? Chodabwitsa nchakuti yankho lake ndilo inde. Pamene kuli kwakuti Aroma Katolika, a Eastern Orthodox, ndi Asilamu m’dziko latsoka limenelo akulimbirana malo, anthu ambiri akufuna mtendere, ndipo ena aupeza.

Banja la a Djorem linali kukhala ku Sarajevo, ndipo anali Mboni za Yehova. Mkati mwa chipwirikiti chonsecho cha mzindawo, iwo anali ndi chizoloŵezi cha kuchezera anansi awo kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti banja la a Djorem linali kudziŵa kuti Ufumu umenewu uli weniweni, kuti unakhazikitsidwa kale kumwamba, ndi kuti ndiwo chiyembekezo chokha chabwino koposa cha anthu kaamba ka mtendere. Mboni za Yehova zili ndi chidaliro cholimba m’zimene mtumwi Paulo anatcha “uthenga wabwino wa mtendere.” (Aefeso 2:17) Chifukwa cha anthu onga Bozo ndi Hena Djorem, ambiri akupeza mtendere ku Bosnia ndi Herzegovina.

Mtendere Weniweni Umene Udzadza

Pali zambiri zonena pabanja la a Djorem. Koma choyamba, tiyeni tikambitsirane za okwatirana ena amene anakhala ndi chidaliro mu Ufumu wa Mulungu. Maina awo ndi Artur ndi Arina. Iwowo limodzi ndi ana awo aamuna achicheperewo anali kukhala m’dziko limene linali m’dera la dziko limene kale linali Soviet Union. Pamene nkhondo yachiŵeniŵeni inaulika, Artur anamenyako nkhondoyo. Koma posapita nthaŵi, iye anadzifunsa kuti, ‘Nchifukwa ninji ndikumenyana ndi anthu aŵa amene anali anansi anga?’ Anachoka m’dzikolo, ndipo pambuyo pokumana ndi zovuta zambiri, anafika ku Estonia ndi banja lake.

Atapita ku St. Petersburg, Artur anakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anachita chidwi ndi zimene anaphunzira ponena za Ufumu wa Mulungu. Chifuniro cha Yehova nchakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzakhale ulamuliro wokha pa anthu. (Danieli 2:44) Ndiyeno dziko lapansi lidzakhala malo a mtendere, lopandanso nkhondo zachiŵeniŵeni kapena nkhondo za pakati pa maiko. Yesaya analosera za nthaŵiyo kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:9.

Ataona chithunzithunzi chojambulidwa cha dziko lapansi la mtsogolo la mtendere limenelo m’buku lothandizira kuphunzira Baibulo limene Mboni inamsonyeza, Artur anati anali kukhala m’malo onga amenewo. Komano, anali kuwonongedwa ndi nkhondo yachiŵeniŵeni. Ku Estoniako, Artur ndi banja lake akuphunzira zambiri ponena za Ufumu wa Mulungu kupyolera m’phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Mtendere Pakati pa Chipwirikiti

Salmo 37:37 limati: “Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.” Kwenikweni, mtendere wa munthu wangwiro ndi woongoka mtima kwa Mulungu suli wa mtsogolo mwake chabe. Ali nawo ngakhale tsopano. Kodi zimenezo zimatheka bwanji? Talingalirani zimene zinachitikira mwamuna wina wotchedwa Paul.

Paul amakhala kumsasa wakumidzi wa othaŵa kwawo kummwera koma chakumadzulo kwa Ethiopia, ngakhale kuti anachokera ku dziko lapafupi. Ali kudziko la kwawo, anakumana ndi mmodzi wa Mboni za Yehova amene anali kugwira ntchito pakampani ya mafuta, ndipo munthu ameneyu anampatsa buku lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti, Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya.a Paul sanakumanenso nayo Mboniyo, koma anaŵerenga bukulo mosamalitsa. Nkhondo yachiŵeniŵeni inampitikisira kumsasa wa othaŵa kwawo ku Ethiopia, ndipo kumeneko anauza ena zimene anaphunzira. Kagulu kochepa kanalandira zimenezi monga choonadi. Mosonkhezeredwa ndi zimene anaphunzira, iwo posapita nthaŵi anayamba kulalikira kwa ena mumsasawo.

Paul analembera kalata ku malikulu a Watch Tower Society kupempha thandizo. Mtumiki yemwe anatumidwa kuchokera ku Addis Ababa anadabwa kupeza anthu 35 akumyembekezera, okonzeka kuphunzira zambiri ponena za Ufumu wa Mulungu. Makonzedwe anapangidwa akuti thandizolo liziperekedwa nthaŵi zonse.

Kodi tinganene bwanji kuti anthu onga Paul ali ndi mtendere? Moyo wawo ngwovuta, koma ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Pamene akhudzidwa ndi chipwirikiti cha dzikoli, amagwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wakuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Chotero, amakhala ndi chikhutiro chosapezekapezeka lerolino. Mawu a mtumwi Paulo kumpingo wa Afilipi amagwira ntchito pa iwo: “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Inde, amakhala paunansi wathithithi ndi Yehova, “Mulungu wa mtendere.”​—Afilipi 4:6, 7, 9.

Mtendere Umene Ulipo

Mfumu yokhazikidwa pa mpando wachifumu ya Ufumu wa Mulungu ndi Yesu Kristu, wotchedwa “Kalonga wa Mtendere” m’Baibulo. (Yesaya 9:6) Ponena za iye, mneneri wakale anati: “Adzanena za mtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, kuyambira ku Mtsinje kufikira kumalekezero a dziko.” (Zekariya 9:10) Mawu ouziridwa onga ameneŵa anakhudza kwambiri mtima wa mwamuna wina wotchedwa José.

Panthaŵi ina José anali m’ndende. Iye anali chigaŵenga ndipo anagwidwa pamene anali kukonzekera zokaphulitsa malo a apolisi. Anaganiza kuti chiwawa chokha ndicho chimene chingasonkhezere boma kuwongolera mkhalidwe wa dziko lawo. Pamene anali m’ndende, Mboni za Yehova zinayamba kuphunzira Baibulo ndi mkazi wake.

José atamasulidwa, nayenso anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo posapita nthaŵi mawu a Salmo 85:8 anayamba kugwira ntchito pa iye: “Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake.” Komabe, vesi limenelo limamaliza ndi chenjezo lakuti: “Asabwererenso kuchita zopusa.” Chotero, munthu amene afuna mtendere wa Yehova sadzayesa kudzigangira kapena kutsutsa chifuniro Chake.

Lerolino, José ndi mkazi wake ali atumiki achikristu. Iwo amasonyeza ena Ufumu wa Yehova monga njira yothetsera mavuto amene José poyamba anayesa kuthetsa ndi mabomba opangidwa panyumba. Iwo ali okonzeka kukhulupirira Baibulo, lomwe limati: “Yehova adzapereka zokoma.” (Salmo 85:12) Inde, José posachedwapa anapita ku malo aja amene anafuna kuwononga. Chifukwa? Kuti akauze mabanja akumeneko za Ufumu wa Mulungu.

Anthu Amtendere

Pa Salmo 37:10, 11, Baibulo limati: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Ndi chiyembekezo chabwino chotani nanga chimenecho!

Koma onani kuti mtendere wa Yehova uli kokha wa “ofatsa.” Aja ofunafuna mtendere ayenera kuphunzira kukhala amtendere. Ndi mmene zinalili kwa Keith, amene amakhala ku New Zealand. Keith anafotokozedwa monga “munthu wojintcha ndi waukali, wachiwawa, ndi wamakani.” Iye anali m’kagulu kena kaupandu ndipo ankakhala panyumba imene inali ngati linga ndithu, agalu atatu akumalonda pabwalo pake kuletsa anthu kuloŵa. Mkazi wake, mayi wa ana ake asanu ndi mmodzi, anali atamsudzula.

Pamene Keith anakumana ndi Mboni za Yehova, uthenga wabwino unamkhudza mtima kwambiri. Posapita nthaŵi iye ndi ana ake anayamba kumapezeka pamisonkhano ya Mboni. Anameta tsitsi lake lalitali lofika m’chuuno nayamba kuuza amene kale anali mabwenzi ake za Ufumu wa Mulungu. Enanso a iwowa anayamba kuphunzira Baibulo.

Mofanana ndi mamiliyoni a anthu oongoka mtima padziko lonse, Keith anayamba kugwiritsira ntchito mawu a mtumwi Petro akuti: “Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino . . . apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.” (1 Petro 3:10, 11) Mkazi uja amene anali atalekana ndi Keith anavomereza kukwatirananso naye, ndipo tsopano akuphunzira ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola.’

Mtendere wa Yehova wapulumutsa miyoyo ya anthu ambiri, kuphatikizapo yemwe kale anali wamaseŵero wobadwira ku dziko lomwe kale linali U.S.S.R. Mwamuna ameneyu anapata mendulo za mpikisano wa Olympic, koma anagwiritsidwa mwala nayamba kumwa anamgoneka ndi moŵa. Pambuyo pa zaka 19 za zochitachita zimene zinaphatikizapo zaka zitatu mumsasa wachibalo ku Siberia, ulendo wa ku Canada atabisala m’ngalaŵa, ndi kupulumuka imfa kaŵiri chifukwa cha chizoloŵezi chake cha anamgoneka, anapemphera kwa Mulungu kaamba ka thandizo kuti apeze chifuno chenicheni cha moyo. Phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova zolankhula Chirasha linamthandiza kupeza yankho la mafunso ake. Lerolino mwamuna ameneyu, mofanana ndi anthu ena mamiliyoni ambiri, wapeza mtendere ndi Mulungu ndi wa iye mwini.

Chiyembekezo cha Chiukiriro

Pomaliza, tiyeni titembenukire kwa Bozo ndi Hena Djorem ku Sarajevo. Okwatirana ameneŵa anali ndi mwana wamkazi dzina lake Magdalena wazaka zisanu. M’July wapita, onse atatu anali kuchoka panyumba kupitanso ku ntchito yolalikira pamene onse anaphedwa ndi bomba. Nanga bwanji za mtendere umene iwo analalikira kwa ena? Kodi bomba limene linatenga miyoyo yawo linasonyeza kuti umenewo sunali mtendere weniweni?

Kutalitali! M’dongosolo lino la zinthu, kumagwa masoka. Anthu amaphedwa ndi mabomba. Ena amafa ndi matenda kapena ngozi. Ambiri amafa ndi ukalamba. Aja amene ali ndi mtendere wa Mulungu sali otetezereka, koma kutheka kwake kwa zochitika zimenezo sikumawatayitsa chiyembekezo.

Yesu analonjeza bwenzi lake Marita kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:25) Banja la a Djorem linakhulupirira zimenezi, mofanana ndi Mboni za Yehova zonse. Ndipo banja la a Djorem linakhulupirira kuti akamwalira, adzaukitsidwira padziko lapansi limene panthaŵiyo lidzakhaladi malo a mtendere. Yehova Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

Ali pafupi kumwalira, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mtendere ndikusiyirani inu. . . . Mtima wanu usavutike.” (Yohane 14:27) Tikukondwa nalo limodzi banja la a Djorem limene linali ndi mtendere umenewo ndi limenenso lidzasangalala nawo kwambiri pachiukiriro. Tikukondwa limodzi ndi onse amene akulambira Yehova, Mulungu wa mtendere. Anthu otero ali ndi mtendere wamaganizo. Ali ndi mtendere ndi Mulungu. Amakhala pa mtendere ndi ena. Ndipo ali nacho chidaliro chakuti mtsogolo muli mtendere. Inde, apeza mtendere, ngakhale kuti akukhala m’dziko lachipwirikiti. Ndithudi, onse amene akulambira Mulungu mumzimu ndi m’choonadi akusangalala ndi mtendere. Inunso mupezetu mtendere wotero.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Zithunzi patsamba 7]

Apeza mtendere ngakhale kuti akukhala m’dziko lachipwirikiti

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena