Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/1 tsamba 23
  • “Mawu a Mulungu Anakula”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mawu a Mulungu Anakula”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Ntchito Zabwino Zimene Zimalemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Otsimikiza Mtima Kutumikira Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/1 tsamba 23

Olengeza Ufumu Akusimba

“Mawu a Mulungu Anakula”

MPINGO wachikristu unakula mofulumira kwambiri kuchokera pa anthu 120 kufikira pa oposa 3,000 utangopangidwa. (Machitidwe 1:15; 2:41) Baibulo limafotokoza kuti “mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu.” (Machitidwe 6:7) Zaka zoŵerengeka zokha zitapita, mpingo wopangidwa chatsopanowo unakhala gulu la padziko lonse lokhala ndi Akristu mu Afirika, Asia, ndi Ulaya.

Lerolinonso mpingo wachikristu ukukula mofulumira. Mwachitsanzo, chiŵerengero cha olengeza Ufumu ku Mexico chawonjezereka m’zaka zisanu zokha kuchokera pa oposa 130,000 kufika pa 443,640! Mu 1995 munthu mmodzi mwa 59 alionse ku Mexico anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu chimene chimasungidwa ndi Mboni za Yehova. Komabe, kututa kwauzimu m’dziko limenelo sikunathe, monga momwe chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.​—Mateyu 9:37, 38.

M’tauni ina m’boma la Chiapas, palibe amene anavomera kuchita phunziro la Baibulo lapanyumba ndi Mboni za Yehova, ngakhale pamene anali atalalikira uthenga wabwino pafupifupi kwa zaka 20 m’deralo. Mwachionekere, anthu ambiri a m’tauniyo anali kuwopsezedwa ndi mwamuna wina amene anadziŵika kukhala wachiwawa. Ankawopa mmene adzachitira ngati adzatulukira kuti anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni.

Mboni ziŵiri zolimba mtima zimene zinasamukira m’deralo zinasankha zolimbana ndi vutolo mwa kupita mwachindunji kwa mwamuna ameneyo. Pamene zinafika panyumba pake, mkazi wake anatuluka pakhomo ndipo anamvetsera uthenga wawo mosamala. Mkaziyo anachita chidwi makamaka ndi zimene Baibulo limafotokoza ponena za kukhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi. Komano ananena kuti mwamuna wake angamvutitse kwambiri ngati atayamba kuphunzira Baibulo. Mbonizo zinafotokoza kuti ngati iyeyo adzapenda mosamala zimene Baibulo limanena, mpamene adzaphunzira mmene angatumikirire Mulungu ndi kulandira moyo wosatha padziko lapansi. Mkaziyo anavomera phunziro la Baibulo.

Monga momwe anayembekezerera, mwamuna wakeyo anakhumudwa ndi chosankha chake. Anamletsa kuyendetsa galimoto lake kumka kumisonkhano yachikristu, ngakhale kuti anamlola kuligwiritsira ntchito pa zifuno zina. Ngakhale kuti anamtsutsa, iyeyo nthaŵi zonse anali kuyenda ndi miyendo kumka ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya pafupi naye, imene inali pamtunda wa makilomita 10. Posapita nthaŵi ena m’tauniyo anaona kulimba mtima ndi kutsimikiza kwakeko. Anthu anayamba kumvetsera pamene Mboni zinafika panyumba zawo. Ena anayambadi kutsagana ndi mkaziyo kumisonkhano. Posapita nthaŵi, Mboni zinali kuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 20 m’tauni imeneyo!

Bwenzi la mkazi ameneyu nalonso linasankha kuphunzira Baibulo ngakhale kuti mwamuna wake anamtsutsa. Modabwitsa, iyeyo analimbikitsidwa kuchita motero ndi mwamuna wa mkazi woyamba uja. Mwamunayo atalankhula ndi mwamuna wa mkaziyo, analeka kumtsutsa. Zinali motero kuti patapita zaka 20, mbewu ya choonadi cha Baibulo inaphuka, ndi anthu oposa 15 akumaphunzira Baibulo ndi kufika pamisonkhano yachikristu, kuphatikizapo akazi aŵiriwa, amene tsopano akufalitsa uthenga wabwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena