Anasonkhana Monga Atamandi Achimwemwe
ANTHU a Yehova Mulungu akale anasonkhana kudzalambira, analamulidwa ‘kukondwera monsemo’ pamene anasonkhana kaamba ka kulambira. (Deuteronomo 16:15) Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” wa 1995/96 wapatsadi Mboni za Yehova zifukwa za kukondwerera.
Chiyambire pamene misonkhano imeneyi inayamba, yamanga chikhulupiriro. Yasonyezanso mmene tingapezere chimwemwe m’dziko lopanda chimwemwe. Tiyeni tipende za masiku amsonkhanowo lilonse palokha.
‘Haleluya, . . . Sekerani!’
Mutu watsiku loyamba lamsonkhano wapamwambawu unazikidwa pa Salmo 149:1, 2. Nkhani yakuti “Tili ndi Chifukwa Chofuulira ndi Chimwemwe” inafotokoza kugwira ntchito kwa ulosi wa Yesaya chaputala 35. Unakwaniritsidwa mu Israyeli wakale ndipo makamaka m’tsiku lathu limodzi ndi kubwezeretsedwa kwa olambira Yehova pakulemerera ndi thanzi m’paradaiso wauzimu. Motero, oloŵa msonkhanowo anali ndi chifukwa chofuulira mwachimwemwe chifukwa cha zimene Mulungu walinganizira anthu ake m’paradaiso wauzimu ndi m’Paradaiso wakuthupi amene ali pafupi kwambiri.
Nkhani yaikulu yakuti, “Opatulidwa Monga Atamandi Achimwemwe Padziko Lonse,” inayankha funso lakuti: Kodi nchiyani chimene chimatilekanitsa ndi dzikoli? Ndicho kulambira kwathu Yehova kogwirizana. Mosasamala kanthu za kumene Mboni za Yehova zimakhala padziko lapansili, zimalankhula ndi kuphunzitsa mogwirizana. Zimakondweranso ndi chifuno chachikulu cha Yehova cha kuyeretsa dzina lake lopatulika ndi kuchirikiza ulamuliro wake mwanjira ya Ufumu wake. Komabe, kodi ndi motani mmene Yehova amatithandizira kupeza malo m’chifuno chake? Iye watiikizira choonadi cha Mawu ake opatulika. Mulungu watipatsa mzimu wake woyera. Watidalitsa ndi ubale wapadziko lonse ndi kakonzedwe ka kulambira koyera. Banja lathu lapadziko lonse limatithandiza kutumikira Yehova ndi chimwemwe chachikulu cha mumtima.
Nkhani yakuti “Kukhalabe Olekana ndi Dziko ndi Osachitidwa Nalo Maŵanga” inagogomezera za kufunika kwa kupeŵa kuchitidwa maŵanga a kuchita tsankhu ndi kusankhana magulu. (Yakobo 2:5-9) Ena angamayanjane kokha ndi aja amene ali ofanana nawo m’kakhalidwe kapena m’zachuma, akumasiya Akristu anzawo amene ali osauka kapena opanda mwaŵi. Ena angakonde awo amene ali ndi malo athayo mumpingo. Amaiŵala kuti mwaŵi waukulu koposa umene munthu angakhale nawo ndiwo uja wa kukhala Mboni ya Yehova. Chotero, sitiyenera kulola zikhoterero zadziko kutichita maŵanga ndi kuwononga mtendere wampingo.—2 Petro 3:14.
Nkhani yakuti “Kodi Ndili Wokonzekera Kuloŵa mu Ukwati?” inasonyeza kuti ambiri amaloŵa muukwati mwaphuma. Ena amaloŵa muukwati kuti athaŵe mkhalidwe wovuta panyumba kapena chifukwa chakuti ausinkhu wawo akuloŵa muukwati. Komabe, zifukwa zabwino za ukwati zimaphatikizapo chikhumbo chogwirizana cha kulondola zonulirapo zateokrase, chikondi chenicheni, kufuna ubwenzi ndi chisungiko, ndi chikhumbo cha kubala ana. Maphunziro auzimu ngofunika pokonzekera ukwati. Pakati pa zinthu zina, pamafunika kukulitsa mikhalidwe yokhumbika mwa kuvala umunthu watsopano. Nkwanzerunso kudziŵa kaya ngati woyembekezera kukwatirana nayeyo akupereka umboni wa kukhala ndi unansi weniweni ndi Yehova ndipo amachita mwaulemu ndi ena. Kufuna uphungu kwa Akristu okula msinkhu kulinso kwanzeru.—Miyambo 11:14.
Nkhani yopereka chidziŵitso imeneyi inatsatiridwa ndi ina ya mutu wakuti “Makolo Amene Amapeza Chisangalalo mwa Ana Awo.” Kaŵirikaŵiri kubadwa kwa mwana kuli nthaŵi yachimwemwe chachikulu. Komabe, kubala ana kumabweretsanso thayo lalikulu. (Salmo 127:3) Motero, nkofunika kuti ana aphunzitsidwe kukonda Yehova. Makolo angachite zimenezi mwa kulankhula za Yehova nthaŵi zonse ndi ana awo ndi kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Mawu ake m’banja.
Tsiku loyamba lamsonkhano linamalizidwa ndi chinthu chosayembekezereka—kutulutsidwa kwa brosha latsopano lakuti Mboni za Yehova ndi Maphunziro. Limafotokoza bwino kwambiri kuti Mboni “zimalimbikitsa ana awo kulimbikira ndi kuona ntchito zimene amapatsidwa kusukulu kukhala zofunika kwambiri.” Chofalitsidwa chimenechi chimafotokozanso za zotulukapo zapadera za makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga amene Mboni za Yehova zachititsa kwazaka zambiri ku Nigeria, Mexico, ndi kumaiko ena. Broshalo liyenera kuthandiza aphunzitsi kuona kuti timaŵerengera kwambiri maphunziro.
“Perekani Nsembe ya Chitamando kwa Mulungu Nthaŵi Zonse”
Mutu watsiku lachiŵiri umenewo unazikidwa pa Ahebri 13:15, NW. Programu yammaŵa inali ndi nkhani yosiyirana yakuti “Kuyankha Chiitano cha Kutamanda Yehova.” Usinkhu suli chopinga pa kuyankha chiitano chimenechi. Salmo 148:12, 13 limalimbikitsa anyamata, anamwali, okalamba, ndi ana kutamanda Yehova. Atumiki a Yehova achimwemwe ambiri akhoza kuwonjezera chitamando chawo. Padziko lonse, oposa 600,000 amakhala ndi phande m’ntchito ya kulalikira yanthaŵi yonse, kapena mu utumiki waupainiya. Oposa 15,000 ali m’ntchito yaupainiya wapadera, ndipo osachepera 15,000 ali mu utumiki wa pa Beteli.
“Kutumikira ndi Gulu la Yehova Mokhulupirika” inali nkhani imene inasonyeza kuti kukhulupirika nkofunika kwa atumiki a Mulungu. Kukhala wokhulupirika kwa Yehova kumatanthauza kummamatira limodzi ndi kudzipereka kwamphamvu kumene kumanga ngati gluu yamphamvu. Kukhulupirika kumafuna kuti tipeŵe kuswa dala malamulo a Baibulo, kaya ena akutiona kapena ayi. Kumafunanso kuti tichirikize mokhulupirika ziphunzitso za Baibulo zopezedwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso chakudya china chauzimu choperekedwa ndi Watch Tower Society. Nkhani imeneyi inatsatiridwa ndi nkhani yaubatizo. Panali chimwemwe chotani nanga pamene oyembekezera ubatizo anapereka umboni wa kudzipatulira kwawo kwa Yehova!
Mawu a Hoseya 4:1-3 anatsegulira bwalo nkhani yamasana yakuti “Ukoma Kapena Kuipa—Kodi Mumalondola Ziti?” Ngakhale kuti kaonedwe ka dziko paukoma kaipa, Akristu ayenera kuyesayesa ndi “changu chonse” kulondola makhalidwe okoma. (2 Petro 1:5) Zimenezi zimayamba ndi mmene munthu amaganizirira. Ngati malingaliro ake ali aukoma, amalankhula mawu abwino, okoma ndi omangirira ndipo amayesayesa kukhala woona mtima m’zochita zake ndi ena. Kulondola ukoma kumaphatikizaponso kuyesayesa kukhala womvetsetsa ndi wachifundo kulinga kwa Mkristu mnzathu amene akuvutika ndi chitsenderezo kapena kupsinjika mtima.—1 Atesalonika 5:14.
Nkhani ina yakuti, “Yang’anirani Misampha ya Mdyerekezi,” inachenjeza Akristu pakudziloŵetsa m’zisonkhezero zauchiŵanda. Pankhani ya kuchiritsa nthenda, Akristu afunikira kukhala osamala panjira zake, monga za kugonetsa tulo, kuyeserera kupenduza. Komabe, zimene munthu aliyense payekha amachita kuti achire ndi nkhani yaumwini.
Tsiku lachiŵiri linamalizidwa ndi chinthu chosangalatsa chosayembekezereka—kutulutsidwa kwa chofalitsidwa chokhoza kuloŵa m’thumba cholinganizidwira kuthandiza anthu oona mtima kupita patsogolo mofulumira kufikira pa kudzipatulira ndi ubatizo. Buku latsopano limeneli lamasamba 192 nlotchedwa Knowledge That Leads to Everlasting Life. Buku la Knowledge limafotokoza choonadi m’njira yomangirira. Silimalongosola kwambiri za ziphunzitso zonyenga. Mafotokozedwe ake omveka bwino ndi kulongosoledwa bwino kwa mfundo zidzapangitsa bukuli kukhala losavuta kuchititsira maphunziro a Baibulo ndi kuthandiza anthu kupeza tanthauzo la chidziŵitso chothutsa mtima chonena za Mulungu.
“Khalani Inu Okondwa ndi Kusangalala ku Nthaŵi Zonse”
Mawu ameneŵa a pa Yesaya 65:18 anali mutu watsiku lachitatu lamsonkhano. Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza 1914 kukhala chaka chimene dongosolo loipali linaloŵa m’masiku ake otsiriza. Motero, nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Atamandi Achimwemwe Mkati mwa Mapeto a Dongosolo Lino” inakoka chidwi cha omvetsera. Okamba nkhani anasonyeza mmene anthu miyandamiyanda akutengekera ndi mzimu wadyera ndi chiwawa za dzikoli. Panthaŵi yake, adzapatsidwa chilango monga mbali ya dziko limene Satana ali wolamulira wake. Motero, ino ndiyo nthaŵi yakupanga chosankha. Kodi tikufuna kukhala mbali iti? Kodi tikufuna kutumikira Yehova ndi kuchirikiza ulamuliro wake, kapena kodi tidzalola Satana kukhala wolamulira wathu mwa kuchita zimene zimamkondweretsa? Tonsefe tiyenera kuima kumbali ya Yehova mosakayika.
Nkhani yapoyera yamsonkhanowo yakuti, “Tamandani Mfumu Yamuyaya!” inapatsa omvetsera onse kanthu kena kokasinkhasinkha. Ngakhale kuti lingaliro la umuyaya limaoneka kukhala losatheka kwa anthu ofooka, Yehova amalidziŵa bwino kwambiri. “Yehova ndiye Mfumu ku nthaŵi yamuyaya,” anaimba motero wamasalmo. (Salmo 10:16) Mfumu imeneyi yamuyaya yatsegulira anthu njira yokalandirira moyo wosatha kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 17:3) “Inde, ife anthu ochimwa tingapeze moyo wosatha mwa maphunziro aumulungu ndi chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu,” anatero wolankhulayo.
Pamene msonkhano unayandikira mapeto, awo amene anapezekapo anamangiriridwa ndi nkhani yomaliza, yakuti “Kutamanda Yehova Mwachimwemwe Tsiku ndi Tsiku.” Kunali kothutsa mtima kulandira malipoti onena za kupita patsogolo kwa ntchito yopanga ophunzira padziko lonse lapansi. Ndipo oloŵa msonkhano anasonkhezeredwa ‘kuyamika Yehova masiku onse ndi kulemekeza dzina lake ku nthaŵi za nthaŵi.’—Salmo 145:2.
Machitidwe oipitsitsa auchinyama amalanda anthu chimwemwe. Komabe, anthu odzala ndi chikhulupiriro mwa Yehova angakhale ndi chimwemwe chaumulungu. Motero monga abale apadziko lonse, Mboni za Yehova zingathe kubwereza mawu otsatirawa a Salmo 35:27, 28: “Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa: ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake. Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu, ndi lemekezo lanu tsiku lonse.”
[Zithunzi patsamba 7]
Mabanja adzapindula ndi brosha lakuti “Mboni za Yehova ndi Maphunziro”
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Buku latsopano limeneli, “Knowledge That Leads to Everlasting Life,” limafotokoza choonadi cha Baibulo m’njira yomangirira
[Chithunzi patsamba 9]
Ambiri anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova
[Chithunzi patsamba 9]
Oloŵa msonkhano anasonkhezeredwa kwambiri ndi seŵero lakuti “Kuchitira Ulemu Owuyenerera m’Zaka Zawo za Ukalamba”