Chiwawa Chili Ponseponse
ATAKHALA m’galimoto lake akumayembekezera kuti loboti lisinthe, woyendetsa galimotoyo mwadzidzidzi anaona chimwamuna china chikudza kwa iye, chikumatukwana, ndi kumagwedezera nkhonya yake m’mwamba. Woyendetsayo anafulumira kukhoma zitseko zake ndi kutseka mazenera ake, koma chimwamunacho chinapitiriza kumka kwa iye. Atafika, mwamunayo anagwedeza galimotolo ndi kukoka chitseko chake. Ndiyeno, chifukwa cha ukali anasamula nkhonya yake ndi kuphwanya zenera la kutsogolo, akumalitswanya.
Kodi chimenechi nchochitika cha m’kanema? Ayi! Umenewu unali mkangano wa amagalimoto pachisumbu cha Oahu, ku Hawaii, wotchuka chifukwa cha mkhalidwe wake wabata ndi womasuka.
Zimenezi nzosadabwitsa. Maloko oikidwa pazitseko, zitsulo zopinga m’mazenera, antchito olonda nyumba, ngakhale zikwangwani zoikidwa pamabasi zimene zimati “Woyendetsa sanyamula ndalama”—zonsezo zimasonyeza chinthu chimodzi: Chiwawa chili ponseponse!
Chiwawa pa Nyumba
Panyumba paonedwa kwa nthaŵi yaitali mwapadera kukhala malo othaŵirako munthu. Komabe, chithunzithunzi chabwino chimenechi chikusintha mofulumira. Chiwawa chapanyumba, chimene chimaphatikizapo kuchitira ana nkhanza, kumenya mkazi kapena mwamuna, kupha wina, chili nkhani zazikulu padziko lonse.
Mwachitsanzo, “ana pafupifupi 750,000 ku Britain angadzapsinjike mtima kwa nthaŵi yaitali chifukwa chakuti amaona chiwawa chapanyumba,” ikutero Manchester Guardian Weekly. Lipotilo linazikidwa pa kufufuza kumenenso kunapeza kuti “akazi atatu mwa anayi amene anafunsidwa ananena kuti ana awo anaona zochitika zachiwawa, ndipo pafupifupi ana aŵiri mwa atatu anaona amawo atamenyedwa.” Mofananamo, malinga ndi kunena kwa U.S.News & World Report, Bungwe Lolangiza pa Nkhani ya Kuchitira Ana Nkhanza ndi Kunyanyalidwa la United States likuyerekezera kuti “ana 2,000, ambiri a iwo amene sanafike zaka 4, amafera m’manja mwa makolo kapena owasunga chaka chilichonse.” Chimenechi chikuposa chiŵerengero cha imfa zochititsidwa ndi ngozi za galimoto, kumira m’madzi, kapena kugwa, likutero lipotilo.
Chiwawa chapanyumba chimaphatikizaponso kuchitira nkhanza mkazi kapena mwamuna, kumene kumayambira pa kukankha kapena kugunda kufikira pa kuwombedwa pama, kupondedwa chidyali, kukhamidwa pakhosi, kumenyedwa, kuwopsezedwa ndi mpeni kapena ndi mfuti, kapena ngakhale kuphedwa. Ndipo lerolino mtundu umenewu wa chiwawa umachitidwa ndi amuna ndi akazi omwe. Kufufuza kwina kunapeza kuti pakati pa chiwawa cha okwatirana chimene chinaperekeredwa lipoti, pafupifupi chigawo chimodzi mwa zinayi, mwamuna ndiye amayamba mnzake, chigawo china chimodzi mwa zinayi mkazi ndiye amayamba mnzake, ndipo chigawo chotsalacho chingafotokozedwe kukhala mkangano umene anthu aŵiri onsewo amakhala olakwa.
Chiwawa ku Ntchito
Mwachizoloŵezi kuntchito kwakhala malo amene munthu amapezako dongosolo, ndi ulemu pamene achoka panyumba. Koma zimenezo sizilinso choncho. Mwachitsanzo, ziŵerengero zotulutsidwa ndi Dipatimenti ya Chilungamo ya United States zikusonyeza kuti chaka chilichonse anthu oposa 970,000 amakumana ndi chiwawa kuntchito. Mwanjira ina, “pakati pa antchito anayi mmodzi angakhale wochitiridwa chiwawa cha mtundu winawake kuntchito,” malinga ndi kunena kwa lipoti mu Professional Safety—Journal of the American Society of Safety Engineers.
Chovutitsa maganizo kwambiri nchakuti chiwawa cha kuntchito sichimalekezera pa kukangana kokha ndi kutukwanizana. “Chiwawa chimene makamaka chimachitidwa ndi olembedwa ntchito kwa olemba ntchito ndi olembedwa ntchito ena tsopano chili chochititsa kupha munthu wina chomakula mofulumira ku U.S.,” likutero lipoti limodzimodzilo. Mu 1992, imfa imodzi mwa zisanu ndi imodzi za kuntchito inali yochita kuphedwa ndi munthu wina; kwa akazi, chiŵerengerocho chinali pafupifupi imfa imodzi mwa ziŵiri. Palibe amene angakane kuti chiwawa chikuwanda m’malo antchito amene kale anali adongosolo.
Chiwawa m’Maseŵero ndi Zosangulutsa
Anthu alondola maseŵero ndi zosangulutsa monga chinthu chotayirako nthaŵi kapena chotsitsimutsa munthu pa ntchito zina zovuta kwambiri m’moyo. Lerolino zosangulutsa ndizo malonda opanga ndalama koposa. Kuti apeze phindu lalikulu la ndalama m’malonda andalama ameneŵa, opanga zosangulutsa ameneŵa samaona kukhala aliwongo pogwiritsira ntchito njira iliyonse imene ali nayo. Ndipo imodzi ya njira zimenezo ndiyo chiwawa.
Mwachitsanzo, magazini ena a bizinesi otchedwa Forbes, anasimba kuti okonza maseŵero avidiyo ena ali ndi maseŵero ena ankhondo otchuka amene wankhondo amasakaza mutu ndi msana wa mdani wake pamene oonerera amachemerera kuti, “Mtsiriziretu! Mtsiriziretu!” Komabe, mtundu wa maseŵero amodzimodziwo wopangidwa kaamba ka makampani opikisana, ulibe zochitika zachiwawa zimenezo. Chotulukapo chake? Mtundu wachiwawa kwambiriwo umagulidwa kwambiri mwa kugaŵa atatu pa aŵiri alionse kuposa wopikisana nawo. Ndipo zimenezi zimatanthauza ndalama zochuluka. Pamene mitundu yapanyumba ya maseŵero ameneŵa inayamba kugulitsidwa, makampaniwo anapeza $65 miliyoni padziko lonse m’milingu iŵiri yoyamba! Pamene phindu liloŵetsedwamo, chiwawa chimangokhala nyambo ina kwa makasitomala.
Chiwawa m’maseŵero ena chilinso nkhani ina. Kaŵirikaŵiri oseŵera amanyadira kuvulaza ena kumene amachita. Mwachitsanzo, pamaseŵero ena a hockey mu 1990, panali mapenoti 86—chiŵerengero chapamwamba kwambiri. Maseŵerowo anadodometsedwa kwa maola atatu ndi theka chifukwa cha chiwawa. Woseŵera mmodzi anapatsidwa chisamaliro cha mankhwala chifukwa cha kusweka fupa kumaso, kuvulala diso, ndi kutemeka. Kodi nchifukwa ninji panali chiwawa chimenecho? Woseŵera wina anafotokoza kuti: “Pamene mupambana m’maseŵero ena ovuta kwambiri, andewu zambiri, umamka kwanu ukumva uli wogwirizana kwambiri ndi anzako a m’timu. Ndinaganiza kuti ndewuzo zinakometsa maseŵerowo.” M’maseŵero ochuluka amakono, zichita ngati kuti chiwawa chakhala osati njira yongopezera chipambano komanso kuti ndiko chipambano chenichenicho.
Chiwawa ku Sukulu
Kwa nthaŵi yaitali sukulu yaonedwa monga linga limene achichepere angakhalemo popanda kudera nkhaŵa zinthu zina ndi kuika mtima pa kukulitsa maganizo ndi thanzi lawo. Komabe, lerolino, sukulu sizilinso malo abwino osungika. Kufufuza kwa Gallup mu 1994 kunapeza kuti chiwawa ndi timagulu tachiwawa zinapanga vuto loyambirira m’sukulu zaboma ku United States, zikumawonongetsa ndalama zochuluka kuposa chaka chake chapita. Kodi mkhalidwewo waipa motani?
Pafunso lakuti, “Kodi munachitiridwapo chiwawa m’sukulu kapena pamalo asukulu?” pafupifupi wophunzira mmodzi mwa anayi alionse m’kufufuzako anavomera. Mmodzi mwa aphunzitsi khumi alionse anayankhanso movomereza. Kufufuza kumodzimodziko kunapeza kuti 13 peresenti ya ophunzira, anyamata ndi asungwana, anavomera kuti ananyamulapo chida kumka nacho kusukulu panthaŵi ina yake. Ambiri a iwo ananena kuti anatero kungoti awopseze ena kapena kuti adzitetezere. Koma wophunzira wina wazaka 17 anawombera mfuti mphunzitsi wake pachifuwa pamene mphunzitsiyo anayesa kumulanda mfuti yake.
Chitaganya Chachiwawa
Sitingakane kuti chiwawa chili ponseponse lerolino. Panyumba, pantchito, kusukulu, m’zosangulutsa, timayang’anizanamo ndi chitaganya chachiwawa. Pokhala pakati pake tsiku lililonse, ambiri achivomereza kukhala chozoloŵereka—kufikira pamene aukiridwa. Ndiyeno amafunsa kuti, Kodi chidzathadi? Kodi inunso mungafune kudziŵa yankho lake? Pamenepo chonde ŵerengani nkhani yotsatira.