Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/1 tsamba 4-7
  • Mulungu Amasamala za Inu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Amasamala za Inu
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chakale
  • Yehova Wakukokani
  • Zozizwitsa za Yesu
  • Yehova Ali Wobwezera Mphotho
  • Kodi Pali Munthu Amene Amasamaladi za Ine?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yehova Amakusamalirani
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Yehova Ndi “Wobwezera Mphoto Iwo Akum’funa Iye”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Yehova Amakuganizirani?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/1 tsamba 4-7

Mulungu Amasamala za Inu

MARY, mkazi wachikristu amene ali kumapeto kwa zaka zake za m’ma 40, wavutika kwambiri m’moyo wake. Kuchita chigololo kwa mwamuna wake kunachititsa chisudzulo zaka zoposa khumi zapitazo. Ndiyeno, Mary anamenya nkhondo ya kukwaniritsa thayo lake kwa ana ake anayi monga kholo lokhala lokha. Koma adakali yekha, ndipo nthaŵi zina kusungulumwa kumaoneka ngati kuti sikungapiririke. Mary amadzifunsa kuti ‘Kodi zimenezi zimatanthauza kuti Mulungu samasamala za ine kapena ana anga opanda atate?’

Kaya munavutikapo m’njira imodzimodziyi kapena ayi, mosakayikira mukuvomerezana ndi malingaliro a Mary. Tonsefe tinapirirapo zochitika zoyesa, ndipo mwina tinadzifunsapo za kuti ndi liti ndipo ndi motani kwenikweni pamene Yehova adzachitapo kanthu kaamba ka ife. Zina za zokumana nazo zimenezi zili zotulukapo zenizeni za kumamatira kwathu ku malamulo a Mulungu. (Mateyu 10:16-18; Machitidwe 5:29) Zina zili zotulukapo za kukhala kwathu anthu opanda ungwiro omakhala m’dziko lolamulidwa ndi Satana. (1 Yohane 5:19) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi.”​—Aroma 8:22.

Komabe, choonadi chakuti mukuyang’anizana ndi chiyeso chachikulu sichimatanthauza kuti Yehova wakusiyani kapena saali wokondweretsedwa ndi ubwino wanu. Kodi ndi motani mmene mungatsimikizirire zimenezi? Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mulungu amasamala za inu?

Chitsanzo Chakale

Baibulo limapereka umboni woonekera bwino wa chisamaliro cha Yehova pa anthu aliyense payekha. Talingalirani za Davide. Yehova anali ndi chikondwerero chaumwini pa mbusa wachichepereyu, akumamuona kukhala “munthu wa pamtima pake.” (1 Samueli 13:14) Pambuyo pake, pamene Davide anayamba kulamulira monga mfumu, Yehova anamlonjeza kuti: “Ndidzakhala nawe kulikonse umukako.”​—2 Samueli 7:9, NW.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Davide anali ndi moyo “wotetezeredwa,” wosakhala ndi mavuto ena alionse? Ayi, Davide anakumana ndi ziyeso zambiri ponse paŵiri asanayambe kulamulira ndiponso mkati mwa kulamulira kwake. Kwa zaka zingapo asanakhale mfumu, Mfumu Sauli inamfunafuna mosaleka kuti imuphe. M’kati mwa nthaŵiyi ya moyo wake, Davide analemba kuti: “Moyo wanga uli pakati pa mikango . . . ndiwo ana a anthu amene mano awo ali nthungo ndi mivi.”​—Salmo 57:4.

Komabe, m’nsautso yonse imeneyi Davide anali wotsimikiza ponena za chisamaliro chaumwini cha Yehova. “Muŵerenga kuthaŵathaŵa kwanga,” anatero m’pemphero kwa Yehova. Inde, kwa Davide zinali ngati kuti Yehova analemba nsautso yonseyo. Ndiyeno Davide anawonjezera kuti: “Sungani misozi yanga m’nsupa yanu; kodi siikhala m’buku mwanu?”a (Salmo 56:8) Ndi fanizo limeneli, Davide anasonyeza chidaliro chakuti Yehova anali kudziŵa osati kokha za mkhalidwewo komanso zimene ungachititse m’malingaliro.

Pamene anali kuyandikira mapeto a moyo wake, Davide anakhoza kulemba kuchokera m’zokumana nazo zaumwini kuti: “Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikatu: pakuti Yehova agwira dzanja lake.” (Salmo 37:23, 24) Inunso mungakhale ndi chidaliro chakuti ngakhale kuti ziyeso zanu sizingathe ndipo nzomakulakulabe, Yehova amaona chipiriro chanu ndipo amachiona kukhala chofunika kwambiri. Paulo analemba kuti: “Mulungu saali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

Ndiponso, Yehova akhoza kuchitapo kanthu kaamba ka inu mwa kukupatsani nyonga imene mufunikira kuti mupirire chopinga chilichonse chimene chili panjira panu. “Masautso a wolungama mtima achuluka,” analemba motero Davide, “koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.” (Salmo 34:19) Zoonadi, Baibulo limatiuza kuti maso a Yehova “ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi iye.”​—2 Mbiri 16:9.

Yehova Wakukokani

Umboni wowonjezereka wa chisamaliro chaumwini cha Yehova umapezeka m’mawu a Yesu. “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine,” iye anatero, “koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Inde, Yehova amathandiza munthu aliyense payekha kugwiritsira ntchito mapindu a nsembe ya Kristu. Motani? Kwakukulukulu, mwa ntchito yolalikira Ufumu. Zoonadi, ntchito imeneyi yakhala ngati “mboni kwa anthu a mitundu yonse,” komabe imafikira munthu aliyense payekha. Choonadi chakuti mukumvetsera ndi kulabadira mbiri ya uthenga wabwino chili umboni wa nkhaŵa yaumwini ya Yehova ponena za inu.​—Mateyu 24:14.

Mwa mzimu woyera, Yehova amakokera anthu kwa Mwana wake ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Chimenechi chimakhozetsa aliyense kudziŵa choonadi chauzimu ndi kuchigwiritsira ntchito mosasamala kanthu za kupereŵera kwachibadwa ndi kuphophonya kulikonse. Ndithudi, munthu sangamvetsetse zifuno za Mulungu popanda chithandizo cha mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 2:11, 12) Monga momwe Paulo analembera Atesalonika, “si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Yehova amapereka mzimu wake kwa awo okha amene amasonyeza kufunitsitsa kukokedwa naye.

Yehova amakoka anthu chifukwa amawakonda monga munthu aliyense payekha ndipo akufuna kuti apeze chipulumutso. Umenewo ndi umboni wolimba chotani nanga wa chisamaliro cha Yehova chaumwini! Yesu anati: “Sichili chifuniro cha Atate wanu wakumwamba kuti mmodzi wa ang’onowa atayike.” (Mateyu 18:14) Inde, pamaso pa Mulungu munthu aliyense ngwofunika monga munthu payekha. Nchifukwa chake Paulo anakhoza kulemba kuti: “Adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake.” (Aroma 2:6) Ndipo mtumwi Petro anati: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye [munthu payekha] ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Zozizwitsa za Yesu

Chikondwerero chaumwini cha Mulungu mwa anthu chinasonyezedwa mogwira mtima m’zozizwitsa zochitidwa ndi Mwana wake, Yesu. Kuchiritsa kumeneku anakuchita ndi chifundo chakuya. (Marko 1:40, 41) Popeza Yesu “sakhoza . . . kuchita kanthu payekha, koma chimene aona Atate achichita,” chifundo chake chimatipatsa chithunzi chogwira mtima cha nkhaŵa ya Yehova pa aliyense wa atumiki ake.​—Yohane 5:19.

Talingalirani nkhani ya chozizwitsa chimene Yesu anachita, yolembedwa pa Marko 7:31-37. Panopa Yesu anachiritsa mwamuna wina amene anali wogontha ndi amene ankadwala matenda a kusalankhula bwino. “Anampatula pa khamu la anthu,” Baibulo limasimba motero. Ndiyeno, “nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko Tatseguka.”

Kodi nchifukwa ninji Yesu anampatula pa khamu la anthu mwamunayu? Eya, mwina chili chifukwa chakuti gonthi amene sanathe kulankhula kwenikweni angamve manyazi pamaso pa openyerera. Yesu ayenera kukhala atadziŵa za manyazi a mwamunayu, ndipo nchifukwa chake anasankha kukamchiritsira payekha. “Nkhani yonse,” akutero katswiri wa Baibulo wina, “imatisonyeza bwino kwambiri kuti Yesu sanaone mwamunayo monga wodwala wina wamba; anamuona monga munthu payekha. Mwamunayo anali ndi kusoŵa kwapadera ndi vuto lapadera, ndipo ndi chifundo chakuya koposa Yesu anachita naye m’njira imene sinapweteke malingaliro ake ndipo m’njira imene anamvetsetsa.”

Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yesu anali ndi nkhaŵa yaumwini pa anthu. Khulupirirani kuti ali wokondweretsedwanso mofananamo ndi inu. Zoonadi, imfa yake inali chisonyezero cha chikondi cha dziko lonse la anthu okhoza kuomboledwa. Komabe, mwinamwake mungatenge chochitika chimenecho mwaumwini, monga momwe Paulo anachitira, amene analemba kuti: ‘Mwana wa Mulungu . . . anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’ (Agalatiya 2:20) Ndipo popeza Yesu anati ‘iye amene anamuona iye anaona Atate,’ tingatsimikize kuti Yehova ali ndi chikondwerero chimodzimodzicho mwa aliyense wa atumiki ake.​—Yohane 14:9.

Yehova Ali Wobwezera Mphotho

Kukhala ndi chidziŵitso cha Mulungu kumaphatikizapo kudziŵa mbali iliyonse ya umunthu wake monga momwe Baibulo limaisonyezera. Dzina lenilenilo lakuti Yehova limatanthauza “Amachititsa Kukhalako,” kutanthauza kuti Yehova angakhale chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse chifuniro chake. M’mbiri yonse, iye wachita mbali zosiyanasiyana, kuphatikizapo zija za Mlengi, Atate, Ambuye Mfumu, Mbusa, Yehova wa makamu, Wakumva pemphero, Woweruza, Mlangizi Wamkulu, ndi Moombolo.b

Kuti tidziŵe tanthauzo lonse la dzina la Mulungu, tiyenera kudziŵanso Yehova monga Wobwezera Mphotho. Paulo analemba kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.”​—Ahebri 11:6.

Yehova walonjeza moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso kwa awo amene tsopano akusankha kumtumikira ndi mtima wonse. Kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo lalikululo sidyera, ndiponso kudziyerekezera kuti muli mmenemo sikudzikweza. Mose “anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:26) Paulo mofananamo anayembekezera mwaphamphu kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu kwa Akristu okhulupirika odzozedwa. Iye analemba kuti: “Ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo [y]a maitanidwe a kumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.”​—Afilipi 3:14.

Inunso mungayembekezere mphotho imene Yehova akuilonjeza kwa awo amene adzapirira. Kuyembekezera mphotho imeneyo kuli mbali yofunika kwambiri ya chidziŵitso chanu cha Mulungu ndi chipiriro chanu mu utumiki wake. Motero tsiku ndi tsiku sinkhasinkhani pa madalitso amene Yehova wakusungirani. Mary, wotchulidwa pachiyambiyo, wayesetsa mwapadera kuchita zimenezi. “Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga,” iye akutero, “ndavomereza posachedwapa kuti nsembe ya dipo ya Yesu imagwira ntchito pa ine. Ndayamba kumva kuti Yehova amandisamalira pandekha. Ndakhala Mkristu kwa zaka zoposa 20, koma ndayamba kukhulupiriradi zimenezi posachedwapa.”

Mwa kuphunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha kuchokera pansi pa mtima, Mary, pamodzi ndi mamiliyoni a ena, adziŵa kuti Yehova amasamala za anthu ake osati kokha monga gulu komanso monga munthu payekha. Mtumwi Petro anakhulupiriradi zimenezi kotero kuti analemba kuti: ‘Tayani pa iye [Mulungu] nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.’ (1 Petro 5:7) Inde, Mulungu amasamala za inu!

[Mawu a M’munsi]

a Nsupa inali choikamo cha chikopa chanyama chimene chinagwiritsiridwa ntchito kusungiramo zinthu zonga madzi, mafuta, mkaka, vinyo, mafuta akudya ndi tchizi. Nsupa zakale zinali zosiyanasiyana mu ukulu ndi mapangidwe, zina za izo zinali matumba achikopa ndipo zina zinali zoikamo zokhala ndi khosi laling’ono zokhala ndi chotsekera.

b Onani Oweruza 11:27; Salmo 23:1; 65:2; 73:28, NW; 89:26; Yesaya 8:13; 30:20, NW; 40:28; 41:14; onaninso New World Translation of the Holy Scriptures​—With References, Appendix 1J, tsamba 1568, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 6]

Chiukiriro​—Umboni Wakuti Mulungu Amasamala

UMBONI wokhutiritsa wa chikondwerero cha Mulungu pa munthu aliyense umapezeka m’Baibulo pa Yohane 5:28, 29 pomwe pamati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”

Mokondweretsa, liwu lachigiriki lakuti mne·meiʹon (manda achikumbukiro) lagwiritsiridwa ntchito pano m’malo mwa taʹphos (manda). Liwu lakuti taʹphos limangopereka lingaliro la kuika maliro. Koma liwu lakuti mne·meiʹon limapereka lingaliro lakuti mbiri ya munthu amene wamwalira ikukumbukiridwa.

Ponena za zimenezi, tangolingalirani za zimene chiukiriro chidzafuna Yehova Mulungu kuchita. Kuti abwezere munthu kumoyo, ayenera kudziŵa zinthu zonse ponena za munthuyo​—kuphatikizapo makhalidwe ake achibadwa ndi zikumbukiro zake zonse. Ndi mwa njirayo mmene munthuyo adzabwezeretsedwa monga momwe anadziŵidwira.

Zoonadi, munthu angaone zimenezi kukhala zosatheka, koma “zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Marko 10:27) Iye angadziŵe kwenikweni ngakhale zimene zili mumtima wa munthu. Ngakhale kuti munthu anakhala wakufa kwa zaka mazana ambiri, chikumbukiro cha Mulungu ponena za iye sichimalephera; sichimazimiririka. (Yobu 14:13-15) Motero potchula Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ngakhale kuti anali atamwalira zaka mazana ambiri, Yesu anakhoza kunena kuti Yehova ‘sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.’​—Luka 20:38.

Motero mabiliyoni amene anamwalira amakumbukiridwa bwinobwino ndi Yehova Mulungu. Ha, ndi umboni wodabwitsa kwambiri chotani nanga wakuti Mulungu amasamala za anthu aliyense payekha!

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu anasonyeza chikondwerero chaumwini mwa awo amene anachiritsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena