Mmene Abusa Achikristu Amakutumikirirani
M’MALO ambiri nkosavuta kuona mmene abusa amasamalilira nkhosa. Amatsogolera, kutetezera, ndi kupezera nkhosa chakudya. Zimenezi nzofunika kwambiri kwa akulu achikristu, popeza kuti ntchito yawo imaphatikizapo kuŵeta. Zoonadi, ‘kuŵeta mpingo wa Mulungu’ ndi ‘kuyang’anira nkhosa zonse’ kuli thayo lawo.—Machitidwe 20:28.
Ngati muli chiŵalo cha mpingo wachikristu, kodi abusa auzimu angakutumikireni motani? Ndipo kodi muyenera kuchita motani pa kuyesa kukuthandizani kwawo? Kodi nchifukwa ninji mpingo ufunikira thandizo lawo?
Chitetezero pa Chiyani?
M’nthaŵi zakale mikango ndi nyama zina zakuthengo zinali zangozi pamagulu ankhosa ndipo zinali kugwira nkhosa yoyenda yokha. Abusa anafunikira kuzitetezera. (1 Samueli 17:34, 35) Eya, Satana Mdyerekezi “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Iye akuchita nkhondo mwamkwiyo osati ndi gulu lonse la Yehova la padziko lapansi lokha komanso ndi mtumiki aliyense wa Mulungu. Kodi cholinga cha Satana nchotani? Akufuna kulefula anthu a Yehova ndipo ngakhale kuwaletsa ‘kusunga malamulo a Mulungu’ ndi kuchita “umboni wa Yesu.”—Chivumbulutso 12:17.
Yehova anaimba mlandu abusa aboma la Israyeli wakale wa kunyalanyaza zinthu chifukwa chakuti nkhosa zake zinakhala “chakudya cha zilombo zonse za kuthengo.” (Ezekieli 34:8) Komabe, akulu achikristu ali ndi chikhumbo chachikulu cha kutetezera awo amene ali mumpingo kuti pasatayike aliyense chifukwa cha kunyalanyaza zinthu kwawo kapena chifukwa cha chisonkhezero cha Satana, dziko, kapena “mimbulu” yampatuko. (Machitidwe 20:29, 30) Kodi ndi motani mmene abusawo amathandizira onse a m’gulu la nkhosa kukhala ozindikira ndi amaso? Njira imodzi njakupereka nkhani za m’Malemba zokonzekeredwa bwino papulatifomu ya m’Nyumba ya Ufumu. Ina njamakambitsirano abwino olimbikitsa misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake. Ndiponso njira ina njakuyendera “nkhosa” kunyumba zawo kukaonana nazo maso ndi maso. (Yerekezerani ndi Salmo 95:7.) Koma kodi ulendo wa kuŵeta nchiyani? Kodi kuyendera nkhosa kumeneko kuyenera kuchitidwa motani? Ndipo ndani amene ayenera kuyenderedwa?
Kodi Ulendo wa Kuŵeta Nchiyani?
Ulendo wa kuŵeta suli wa kungoona munthu ndi kucheza pankhani zawamba. Mkulu wina anati: “Ofalitsa ambiri amakondwera kwambiri kuŵerenga lemba kapena kukambitsirana za munthu wina wa m’Baibulo. Zoonadi, mkulu safunikira kumangolankhula yekha. Wofalitsa wa Ufumu amene wayenderedwa kaŵirikaŵiri amakonda kusimba za kukhosi kwake pa Baibulo, ndipo kuchita zimenezi kumalimbitsa chikhulupiriro chake. Mkulu angapite ndi magazini a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! kuti akakambitsirane za nkhani ina yolimbikitsa. Mwinamwake kukambitsirana kumeneku kwauzimu nkumene kumasiyanitsa ulendo wa kuŵeta ndi uja wa kucheza.”
Mkulu wina wodziŵa zinthu anati: “Ulendowo usanakhale, mkulu amathera nthaŵi akumasinkhasinkha za wofalitsa amene akukamuona. Kodi nchiyani chimene chingamangirire wofalitsayo? Chiyamikiro chenicheni chili mbali yofunika ya ulendo wa kuŵeta, popeza chimalimbitsa munthu kupirira.” Inde, ulendo wa kuŵeta umaposa ulendo wakungocheza umene aliyense mumpingo angapange.
Kodi Nchifukwa Ninji Mbusa Amakufikirani?
Pamene mkulu afika panyumba, amakhala wokonzekera kulimbikitsa okhulupirira anzake ndi kuwathandiza kuchirimika m’chikhulupiriro. (Aroma 1:11) Chotero pamene mkulu mmodzi kapena aŵiri afuna kukufikirani, kodi mumachita motani? Woyang’anira woyendayenda wina anati: “Ngati maulendo a kuŵeta apangidwa kokha pamene kanthu kena kalakwika, choyamba munthu woyenderedwayo amalingalira kuti, ‘Ndalakwanji kodi?’” Abusa auzimu achikondi amatsanzira Yehova, amene anasamalira wamasalmo ndi ‘kutsitsimutsa moyo wake,’ makamaka m’nthaŵi za nsautso ndi za kusoŵa kwakukulu.—Salmo 23:1-4.
Cholinga cha ulendo wa kuŵeta ndicho ‘kumangirira, ndipo osati kugwetsa.’ (2 Akorinto 13:10) Mawu a chiyamikiro chifukwa cha kupirira, changu, ndi ntchito yokhulupirika ya munthu wofikiridwayo amakhaladi chinthu cholimbikitsa. Mkulu wina anati: “Paulendo wa kuŵeta, si bwino kupereka lingaliro lakuti munthuwe wafika uli ndi cholinga chakuti udzadziŵe ndi kukambitsirana za mavuto. Zoonadi, mwina wofalitsa mwiniyo angafune kulankhula za vuto lina. Ndipo ngati nkhosayo ikutsimphina kapena ikudzipatula pa gulu lonse, mkuluyo afunikira kuchita kanthu kena kuti athandize.”
Abusa achikristu mosakayikira adzasonyeza chisamaliro chapadera kwa aliyense amene ali ngati aja ofotokozedwa m’mawu awa: “Ndidzafuna yotayika [ine Yehova], ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira tchika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.” (Ezekieli 34:16) Inde, nkhosa zingafunikire kukazifunafuna, kuzibweza, kulukira tchika zothyoka miyendo, kapena kuzilimbitsa. Abusa a Israyeli ananyalanyaza mathayo ameneŵa. Kuchita ntchito imeneyo kumafuna kuti mbusa akhale pafupi ndi nkhosa ina ndi kuisamalira pa zofunika zake. Zimenezi ndizo makamaka zimene ziyenera kusiyanitsa mbali ya ulendo wa kuŵeta uliwonse lerolino.
Nkhosa Zathanzi Zifunikira Chisamaliro
Kodi tiyenera kunena kuti abusa auzimu amakono safunikira kusonyeza chisamaliro chapadera pankhosa zathanzi? Aha, pamene nkhosa yeniyeni iloŵa mu vuto, kumakhala kosavuta kuithandiza ngati imadalira mbusa. Buku lina lamalangizo likunena kuti “mwachibadwa nkhosa zimapeŵa anthu, ndipo nthaŵi zonse nkovuta kuti zidalire munthu.” Pakati pa zinthu zina, buku limodzimodzili limapereka malangizo awa ofunika kuti nkhosa zikudalireni: “Lankhulani ku nyamazo nthaŵi zonse. Zimazoloŵera liwu, limene limazipatsa chidaliro. Yenderani nkhosazo kaŵirikaŵiri kubusa.”—Alles für das Schaf. Handbuch für die artgerechte Haltung (Kuchita Zonse Kaamba ka Nkhosa. Buku la Malangizo Ozisungira Bwino).
Motero kuonana nazo maso ndi maso nkofunika ngati pati pakhale unansi wodalirana pakati pa mbusa ndi nkhosa. Zili chonchonso mumpingo wachikristu. Mkulu wina anati: “Kukhala wodziŵika mumpingo monga mkulu amene amafikira nkhosa nthaŵi zonse kumachititsa kuonana ndi munthu amene ali m’mavuto kukhala kosavuta.” Chifukwa chake, abusa auzimu sayenera kungodyetsa ndi kusamalira nkhosa pa Nyumba ya Ufumu chabe. Malinga ngati mikhalidwe ikulola, akulu ayenera kudziŵa nkhosazo mwa kupanga maulendo a kuŵeta mwa kufika kunyumba zawo. Mkristu wina akukumbukira kuti pamene anali atangoikidwa kumene kukhala mkulu, woyang’anira wotsogoza anamuimbira telefoni ndi kumpempha kukayendera ndi kukatonthonza mbale wina amene mwana wake wamkazi anali atangomwalira kumene mu ngozi yoipa ya galimoto. Mkuluyo akuvomereza kuti: “Ndinadadi nkhaŵa, popeza kuti ndinali ndisanafikirepo mbaleyo ndipo sindinadziŵedi kumene anali kukhala! Ndinatonthozedwa pamene mkulu wina wokhwima anandipempha kuti nditsagane naye.” Inde, akulu amathandizana pamaulendo a kuŵeta.
Pokonzekera ndi kupanga maulendo ena a kuŵeta, mkulu angatsagane ndi mtumiki wotumikira amene akukalimira “ntchito yabwino” ya woyang’anira. (1 Timoteo 3:1, 13) Mmene mtumiki wotumikirayo amayamikirira nanga kuona mmene mkulu amathandizira nkhosa pamaulendo a kuŵeta! Motero akulu ndi atumiki otumikira amayandikirana ndi onse mumpingo, akumalimbitsa zomangira za chikondi ndi umodzi wachikristu.—Akolose 3:14.
Kulinganiza Nthaŵi ya Maulendo a Kuŵeta
Pamene bungwe lina la akulu linasiyira maulendo a kuŵeta kwa ochititsa Maphunziro a Buku a Mpingo, ofalitsa onse m’timagulu tina anafikiridwa mkati mwa miyezi isanu ndi umodzi, pamene kuli kwakuti m’timagulu tina palibe amene anafikiridwa. Zimenezi zinasonkhezera mkulu wina kunena kuti: “Zichitika ngati kuti akulu ena amachitapo kanthu ndipo amachita ntchito yambiri ya kuŵeta, koma ena amafunikira kulimbikitsidwa ndi akulu anzawo kuchita motero.” Mabungwe ena a akulu amapanga makonzedwe akuti ofalitsa onse afikiridwe ndi abusa mkati mwa nthaŵi yoikidwa.
Ndithudi, mkulu kapena wofalitsa wina aliyense angafikire wina mumpingo popanda kuyembekezera kupanga makonzedwe apadera. Asanapange maulendo a kuŵeta, mkulu wina amaimba foni ndi kunena kuti, “Ndimafikira banja limodzi mwezi uliwonse. Kodi ndingadzaonane nanu kwa ola limodzi kapena kuposa pamenepo tsiku lina mwezi wamaŵa? Kodi mudzapeza nthaŵi liti?”
Madalitso a Maulendo a Kuŵeta
Pamene zitsenderezo za dongosolo loipali zikupitiriza kuwonjezereka, maulendo olimbikitsa opangidwa ndi abusa ozindikira amakhaladi opindulitsa kwambiri. Pamene awo onse okhala m’gulu la nkhosa alimbikitsidwa ndi kuthandizidwa kupyolera m’maulendo a kuŵeta, nkhosa iliyonse imamva kukhala yosungika.
Ponena za mpingo wina umene ofalitsa ake onse a Ufumu anafikiridwa nthaŵi zonse ndi abusa, kunasimbidwa kuti: “Ofalitsa anakonda kwambiri maulendo a kuŵeta. Sikunali kwachilendo kuti wofalitsa afikire mkulu wina akumamfunsa za nthaŵi imene adzafikanso, chifukwa chakuti iyeyo anali atasangalala ndi makambitsirano omangirira paulendo watha. Maulendo a kuŵeta anali chochititsa chimodzi chimene chinathandizira kuwongolera mzimu wa mpingo.” Malipoti ena akusonyeza kuti pamene abusa atumikira mwachikondi motero, mpingo ungathe kukula m’chikondi, umodzi, ndi ubwenzi. Ndi dalitso labwino chotani nanga limenelo!
Abusa achikristu amafika kudzalimbikitsa mkhalidwe wauzimu wa nkhosa. Akulu amafuna kulimbikitsa ndi kulimbitsa okhulupirira anzawo. Ngati pabuka vuto lina lofuna uphungu mkati mwa kufikako, kungakhale bwino kwambiri kupanga makonzedwe a kudzakambitsirana panthaŵi ina, makamaka ngati mkuluyo watsagana ndi mtumiki wotumikira. Komabe, pemphero lomalizira ulendo wa kuŵetawo lili loyenera kuchitidwa.
Kodi mbusa wauzimu akufuna kudzafika kwanu posachedwapa? Ngati ndi choncho, khalani wachimwemwe poyembekezera chilimbikitso chimene mudzapatsidwa. Iyeyo akubwera kuti adzakutumikireni ndi kukulimbitsani pa kusankha kwanu kuyendabe panjira yomka kumoyo wosatha.—Mateyu 7:13, 14.
[Bokosi patsamba 26]
MALINGALIRO A MAULENDO A KUŴETA
◻ Pangani lonjezo: Kaŵirikaŵiri ndi bwino kupanga lonjezo. Ngati mkulu alinganiza kusamalira vuto lina lalikulu, kungakhale koyenera kudziŵitsa wofalitsayo za zimenezi pasadakhale.
◻ Kukonzekera: Lingalirani za chibadwa ndi mkhalidwe wa munthuyo. Perekani chiyamikiro chachikondi. Pangani chonulirapo chanu kukhala cha kupereka ‘mtulo wauzimu’ wolimbikitsa ndi wolimbitsa chikhulupiriro.—Aroma 1:11, 12.
◻ Amene mungapite naye: Mkulu wina kapena mtumiki wotumikira woyenera.
◻ Mkati mwa kufikako: Mkulu ayenera kukhala womasuka, wachikondi, wolimbikitsa, ndi wololera. Funsani za banjalo, za ubwino wake, ndi zina zotero. Mvetserani mosamalitsa. Ngati chothetsa nzeru china chachikulu chibuka, kungakhale bwino kwambiri kulinganiza ulendo wina wa kuŵeta wapadera.
◻ Utali wa kufikako: Sungani nthaŵi ya lonjezano, ndipo siyanani ndi munthuyo akali wosangalala ndi kufika kwanu.
◻ Kumaliza kufika: Pemphero lili loyenera ndipo limayamikiridwa.—Afilipi 4:6, 7.
[Chithunzi patsamba 24]
Abusa achikristu amapereka chitetezero chauzimu
[Zithunzi patsamba 26]
Maulendo a kuŵeta amapereka mipata yabwino ya chilimbikitso chauzimu