Kucheza Kumene Kungakhale Dalitso
1 Zakeyu analandira Yesu kunyumba kwake mokondwera. Ndipo kucheza kumeneko kunalitu dalitso kwambiri!—Luka 19:2-9.
2 Lero, Yesu Kristu monga Mutu wampingo, amatsogolera akulu ‘kuŵeta gulu la Mulungu.’ (1 Pet. 5:2, 3; Yoh. 21:15-17) Kusiyapo kuphunzitsa mumpingo ndi kutsogolera mu utumiki wakumunda, oyang’anira mpingo amathandiza mwachikondi munthu aliyense mumpingo. Choncho, nthaŵi ndi nthaŵi mungamayembekezere kuona akulu akukulankhulani panokha, kaya kunyumba kwanu, pa Nyumba ya Ufumu, muli limodzi mu utumiki wakumunda, kapena kwina. Kodi muyenera kuopa pamene akulu afika kudzakuchezerani? Ayi. Kukufikirani kwawo sikumatanthauza kuti mukulephera mwina ndi mwina. Ndiyeno cholinga cha ulendo waubusa nchiyani?
3 Paulo ananena kuti ankafuna kukachezera abale ‘kukaona mkhalidwe wawo.’ (Mac. 15:36) Inde, monga abusa achikondi, akulu amafuna kwambiri kudziŵa kuti muli bwanji. Amafuna kukuthandizani mwauzimu ndi kukuumbani. Kusamala munthu aliyense choncho nkumene Mbusa wathu wachikondi Yehova amafuna kuti tonsefe tizilandira.—Ezek. 34:11.
4 Yamikirani Akulu Akakuchezerani: Cholinga cha Paulo pochezera abale chinali chakuti ‘awapatse mphatso yauzimu kuti awalimbikitse, ndi kutinso alimbikitsane.’ (Aroma 1:11, 12, NW) Tonsefe timafunikira chilimbikitso chauzimu m’masiku otsiriza ndi ovuta ano, ndipo timafunikira chithandizo kuti tilimbebe pachikhulupiriro. Nzosakayikitsa kuti mukamakondwera ndi ulendo waubusa pamakhala kulimbikitsana.
5 Tiyenera kuyamikira mapindu ambiri amene timapeza m’ntchito ya akulu yaubusa. Ngati pali nkhani ina kapena funso lina limene likukuvutani, kumbukirani kuti akulu alimo mumpingomo kuti athandize. Osamazengereza kukambitsirana nawo nkhani iliyonse imene ingakusoŵetseni mtendere mwauzimu. Yamikirani makonzedwe a Yehova ameneŵa, ngachikondi, ndipo kondwerani ndi madalitso amene kucheza kumeneko kungabweretse.