Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi mtumwi Paulo anatanthauzanji pamene anati anali ‘kuiŵaladi zammbuyo, ndi kutambalitsira zamtsogolo’? (Afilipi 3:13) Kodi munthu akhoza kuiŵala chinthu modzifunira?
Ayi, nthaŵi zambiri sitingaiŵalire modzifunira chinthu china. Choonadi ndicho chakuti, timaiŵala zambiri zimene timafuna kukumbukira ndi kukumbukira zinthu zambiri zimene tingakonde kuiŵala. Motero, kodi nchiyani chimene Paulo anatanthauza pamene analemba mawu a pa Afilipi 3:13? Nkhani yake yonse imatithandiza kumvetsetsa.
Mu Afilipi chaputala 3, Paulo akufotokoza za “kukhulupirira m’thupi” kwake. Akunena za mbiri yake yachiyuda yabwino kwambiri ndi changu chake pa Chilamulo—zinthu zimene zikanampatsa mapindu ochuluka mumtundu wa Israyeli. (Afilipi 3:4-6; Machitidwe 22:3-5) Komabe, anafulatira mapindu oterowo, akumawaona ngati chitayiko, titero kunena kwake. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anali atapeza chinachake chabwinopo—“mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu.”—Afilipi 3:7, 8.
Chonulirapo chachikulu cha Paulo chinali kufikira “kuuka [koyamba, NW] kwa akufa” osati malo apamwamba a m’dziko lino. (Afilipi 3:11, 12) Motero, akulemba kuti: “Poiŵaladi za m’mbuyo, ndi kutambalitsira zamtsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 3:13, 14) Pamene Paulo ananena kuti anali ‘kuiŵaladi za m’mbuyo,’ sanali kutanthauza kuti mwa njira ina anafafaniza “za m’mbuyo” m’maganizo mwake. Mwachionekere iye ankazikumbukira, popeza anali atangozitchula kumene. Ndiponso, m’chigiriki choyamba, iye akugwiritsira ntchito mtundu wina wa verebu wosonyeza chinthu chimene chili kuchitika, osati chimene chachitika kale. Iye akunena kuti “poiŵaladi,” osati “pokhala nditaiŵala.”
Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “iŵala” (e·pi·lan·thaʹno·mai) lili ndi matanthauzo ambiri, limodzi la iwo ndilo “kusadera nkhaŵa za,” kapena “kunyalanyaza.” Malinga ndi Exegetical Dictionary of the New Testament (lolinganizidwa ndi Horst Balz ndi Gerhard Schneider), izi nzimene ‘kuiŵala’ kumatanthaza pa Afilipi 3:13. Paulo sankalingalira nthaŵi zonse za zinthu zimene anasiya. Anaphunzira kuziona monga zosafunika kwenikweni. Zinali monga “chitayiko” pozilinganiza ndi chiyembekezo cha kumwamba.—Afilipi 3:8.
Kodi mawu a Paulo tingawagwiritsire ntchito motani lerolino? Eya, monga Paulo, Mkristu angakhale atadzimana kuti atumikire Mulungu. Angakhale atasiya ntchito yapamwamba kaamba ka utumiki wanthaŵi yonse. Kapena angakhale wambanja lolemera limene laleka kugaŵana naye chumacho chifukwa chakuti iwo sakonda choonadi. Kudzimana kotero nkoyamikirika, koma sikuli chinthu chodera nacho nkhaŵa nthaŵi zonse. Mkristu ‘amaiŵala,’ amaleka kudera nkhaŵa za, “m’mbuyo” poona mtsogolo mwaulemerero mmene amayembekezera.—Luka 9:62.
Pulinsipulo la mawu a Paulo mwinamwake tingaligwiritsire ntchito m’njira ina. Bwanji ponena za Mkristu amene anali ndi makhalidwe oipa asanaphunzire za Mulungu? (Akolose 3:5-7) Kapena tinene kuti atakhala Mkristu, anachita tchimo lalikulu ndipo analangidwa ndi mpingo. (2 Akorinto 7:8-13; Yakobo 5:15-20) Eya, ngati walapadi ndipo wasintha njira zake, iye ‘wasambitsidwa.’ (1 Akorinto 6:9-11) Zimene zinachitika nzakale. Sangaiŵaledi kwenikweni zimene anachita—indedi, angakhale wanzeru kuphunzira pachochitikacho kotero kuti asabwereze tchimolo. Ndiponso, ‘amaiŵala’ m’lingaliro la kusadziimba mlandu nthaŵi zonse. (Yerekezerani ndi Yesaya 65:17.) Atakhululukidwa pamaziko a nsembe ya Yesu, amayesetsa kuiŵala zakale.
Pa Afilipi 3:13, 14, Paulo akudzifotokoza monga wothamanga makani, “kutambalitsira zamtsogolo” kuti afike pa chonulirapo chake. Wothamanga amayang’ana kutsogolo, osati kumbuyo. Momwemonso, Mkristu ayenera kuyang’ana madalitso a mtsogolo, osati zinthu zosiyidwa kumbuyo. Paulo akunenanso kuti: “Ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu.” (Afilipi 3:15) Motero, pempherani kwa Mulungu kuti akuthandizeni kukulitsa lingaliro limeneli. Dzazani maganizo anu ndi malingaliro a Mulungu opezeka m’Baibulo. (Afilipi 4:6-9) Sinkhasinkhani pa chikondi cha Yehova pa inu ndi pa madalitso amene mumakhala nawo chifukwa cha icho. (1 Yohane 4:9, 10, 17-19) Pamenepo, kudzera mwa mzimu woyera Yehova adzakuthandizani kusadera nkhaŵa za zinthu zimene munasiya kumbuyo. M’malo mwake, mudzayang’ana mtsogolo mwaulemerero monga Paulo.—Afilipi 3:17.