Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
M’NTHAŴI zakale anthu a Yehova ankachita mapwando atatu aakulu chaka chilichonse. Mofananamo, m’nthaŵi zamakono anthu a dzina la Yehova amakumana katatu chaka chilichonse kaamba ka mapwando. Amasangalala kusonkhana kaamba ka tsiku la msonkhano wapadera watsiku limodzi, msonkhano wadera wamasiku aŵiri, ndi msonkhano wachigawo wamasiku atatu kapena anayi. Chaka chino, mutu wa msonkhano wachigawo ngwakuti “Amithenga a Mtendere Waumulungu.”
Mmene mutuwo ulili woyenerera nanga! Mulungu wathu, Yehova, ali “Mulungu wa mtendere.” Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, ali “Kalonga wa Mtendere,” ndipo uthenga umene atumiki a Yehova amapereka uli uthenga wa mtendere waumulungu. (Afilipi 4:9; Aroma 15:33; Yesaya 9:6; Nahumu 1:15) Programu yamsonkhano yabwino yakonzedwa imene idzathandiza onse kuzindikira mowonjezereka kufunika kwa mtendere waumulungu.
Chaka chino mu Zambia mokha, mudzakhala misonkhano yachigawo 46, ndipo ina idzakhala ku Malaŵi, Mozambique ndi Zimbabwe. Mofananamo, pafupi ndi inu padzakhala msonkhano wachigawo. Bwanji osafunsa Mboni za Yehova zomwe zili pafupi nanu ponena za tsiku lake lenileni ndi malo ake enieni ndi kupanga makonzedwe akuti mukapezekepo? Onse amene akufuna mtendere weniweni ndi wokhalitsa adzalandiridwa mwachikondi.